Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 7

Mphamvu Zoteteza​—“Mulungu Ndi Pothawira Pathu”

Mphamvu Zoteteza​—“Mulungu Ndi Pothawira Pathu”

1, 2. Kodi Aisiraeli anakumana ndi mavuto otani pamene ankalowa m’dera la Sinai m’chaka cha 1513 B.C.E., nanga Yehova anawalimbikitsa bwanji?

 AISIRAELI anakumana ndi mavuto pamene ankalowa m’dera la Sinai chakumayambiriro kwa chaka cha 1513 B.C.E. Ankayembekezera kuyenda ulendo woopsa wodutsa ‘m’chipululu chachikulu ndi chochititsa mantha, chokhala ndi njoka zapoizoni ndiponso zinkhanira.’ (Deuteronomo 8:15) Akanathanso kuukiridwa ndi anthu a mitundu ina omwe ankadana nawo. Yehova ndiye anachititsa kuti anthu ake akumane ndi zimenezi. Popeza kuti iye anali Mulungu wawo, kodi akanatha kuwateteza?

2 Zimene Yehova anawauza zinawalimbikitsa kwambiri. Iye anati: “Inu munaona nokha zimene ndinachitira Aiguputo, kuti ndikunyamuleni pamapiko a chiwombankhanga n’kukubweretsani kwa ine.” (Ekisodo 19:4) Yehova anakumbutsa anthu akewo kuti anawapulumutsa ku Iguputo ngati mmene chiwombankhanga chimanyamulira ana ake n’kukawasiya kumalo otetezeka. Palinso zifukwa zina zomwe zimachititsa kuti “mapiko a chiwombankhanga” akhale chitsanzo chabwino chofotokoza mmene Yehova anatetezera anthu ake.

3. N’chifukwa chiyani “mapiko a chiwombankhanga” ndi chitsanzo chabwino chofotokoza mmene Yehova amatetezera anthu ake?

3 Sikuti chiwombankhanga chimangogwiritsa ntchito mapiko ake, omwe ndi aatali komanso amphamvu pouluka m’mwamba kwambiri, koma chimawagwiritsanso ntchito m’njira zina. Kukatentha kwambiri, chiwombankhanga chachikazi chimatambasula mapiko ake, omwe angakwane mamita awiri, kuti chipange mthunzi wotetezera ana ake kuti asapse ndi dzuwa. Nthawi zina chimafungatira ana ake m’mapiko powateteza ku mphepo yozizira. Yehova ankateteza mtundu wa Aisiraeli womwe unali watsopano, ngati mmene chiwombankhanga chimatetezera ana ake. Pamene anthu a Yehova anali m’chipululu, akanapitiriza kukhala otetezeka mumthunzi wa mapiko ake amphamvu ngati akanakhalabe okhulupirika. (Deuteronomo 32:9-11; Salimo 36:7) Koma kodi masiku ano Mulungu amatetezanso anthu ake?

Yehova Amalonjeza Kuti Aziteteza Atumiki Ake

4, 5. N’chifukwa chiyani sitingakayikire ngakhale pang’ono lonjezo la Mulungu lakuti adzateteza anthu ake?

4 Yehova amakwanitsa kuteteza atumiki ake. Iye ndi “Mulungu Wamphamvuyonse” ndipo dzina laudindo limeneli limasonyeza kuti ali ndi mphamvu zambiri moti palibe amene angamuletse kuchita zomwe akufuna. (Genesis 17:1) Mofanana ndi mafunde omwe sangaimitsidwe, palibe amene angaletse mphamvu za Yehova. Popeza iye amatha kuchita chilichonse chimene wafuna, tingafunse kuti, ‘Kodi Yehova ndi wofunitsitsa kugwiritsa ntchito mphamvu zake poteteza anthu ake?’

5 Yankho ndi lakuti inde. Yehova amatitsimikizira kuti adzateteza anthu ake. Lemba la Salimo 46:1 limati: “Mulungu ndi pothawira pathu komanso mphamvu yathu, thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya mavuto.” Popeza Mulungu “sanganame,” sitingakayikire ngakhale pang’ono lonjezo lake lakuti adzateteza anthu ake. (Tito 1:2) Tiyeni tione mawu ena oyerekezera zinthu amene Yehova amagwiritsa ntchito pofotokoza mmene amatetezera anthu ake.

6, 7. (a) Kodi kale abusa ankateteza bwanji nkhosa zawo? (b) Kodi Baibulo limayerekezera zochita za Yehova ndi za ndani posonyeza kuti Yehovayo amafunitsitsa kuteteza nkhosa zake ndiponso kuzisamalira?

6 Yehova ndi M’busa wathu ndipo ife “ndife anthu ake komanso nkhosa zimene akuweta.” (Salimo 23:1; 100:3) Pali nyama zochepa zomwe zimafuna kuthandizidwa kwambiri ngati mmene zilili ndi nkhosa. Kale abusa ankafunika kukhala olimba mtima kuti ateteze nkhosa zawo kwa mikango, mimbulu, zimbalangondo komanso akuba. (1 Samueli 17:34, 35; Yohane 10:12, 13) Koma nthawi zina m’busa ankafunika kuchita zinthu mwachikondi poteteza nkhosa. Nkhosa ikaberekera kutali ndi khola, m’busa wachikondi ankayang’anira nkhosa yofunika kuthandizidwayo ndipo kenako ankanyamula kamwana kongobadwa kumeneko n’kupita nako kukhola.

“Adzawanyamulira pachifuwa pake”

7 Podziyerekezera ndi m’busa, Yehova amatitsimikizira kuti ndi wofunitsitsa kutiteteza. (Ezekieli 34:11-16) Kumbukirani zimene lemba la Yesaya 40:11 limafotokoza zokhudza Yehova. Lembali linafotokozedwa m’Mutu 2 wa bukuli ndipo limati: “Iye adzasamalira gulu la nkhosa zake ngati m’busa. Ndi dzanja lake, adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa, ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.” Kodi zimatheka bwanji kuti kamwana kankhosa kakhale “pachifuwa” cha m’busa, kapena kuti pachovala chake chakumtunda chomwe wachipinda? Kamwanako kangafike pamene pali m’busayo, mwinanso n’kumakhudza mwendo wake. Komabe m’busayo ndi amene amayenera kuwerama n’kukanyamula ndiponso kukaika mosamala pachifuwa chake pomwe kangakhale motetezeka. Zimenezitu zikusonyeza bwino kuti M’busa wathu wamkulu amafunitsitsa kutiteteza.

8. (a) Ndi ndani amene Mulungu amalonjeza kuti aziwateteza, ndipo lemba la Miyambo 18:10 likusonyeza bwanji mfundo imeneyi? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tizitetezedwa ndi dzina la Mulungu?

8 Koma Mulungu amalonjeza kuti aziteteza anthu okhawo amene amafuna kukhala naye pa ubwenzi. Lemba la Miyambo 18:10 limati: “Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba. Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.” Kale, nthawi zina anthu ankamanga nsanja m’chipululu kuti azithawiramo. Koma munthu yemwe moyo wake uli pangoziyo ndi amene ankafunika kuthamangira kunsanjako kuti apulumuke. N’chimodzimodzinso ndi kutetezedwa ndi dzina la Mulungu. Dzina la Mulungu lilibe mphamvu zamatsenga, choncho kungolitchula mobwerezabwereza si kumene kungatiteteze. M’malomwake, timafunika kudziwa ndiponso kukhulupirira Mwiniwake wa dzina limeneli n’kumayesetsa kutsatira mfundo zake pa moyo wathu. Yehova anatikomera mtima kwambiri potitsimikizira kuti tikamamukhulupirira, azititeteza mofanana ndi mmene nsanja imatetezera.

“Mulungu Wathu . . . Akhoza Kutipulumutsa”

9. Kuwonjezera pa kulonjeza kuti aziteteza anthu ake, kodi Yehova wachitanso chiyani?

9 Sikuti Yehova amangolonjeza kuteteza anthu ake. M’Baibulo muli nkhani zimene zimasonyeza kuti iye ankachita zodabwitsa posonyeza kuti akhoza kuwateteza. Mwachitsanzo, nthawi zambiri Yehova ankagwiritsa ntchito “dzanja” lake lamphamvu poteteza Aisiraeli kwa adani awo amphamvu. (Ekisodo 7:4) Komabe, Yehova ankagwiritsanso ntchito mphamvu zake zoteteza pothandiza munthu aliyense payekha.

10, 11. Kodi ndi zitsanzo za m’Baibulo ziti zimene zimasonyeza mmene Yehova anagwiritsira ntchito mphamvu zake poteteza anthu ena?

10 Anyamata atatu, Shadireki, Misheki ndi Abedinego, omwe anali Aheberi, atakana kugwadira fano lagolide la Mfumu Nebukadinezara, mfumuyo inakwiya kwambiri ndipo inawaopseza kuti iwaponya m’ng’anjo yotentha kwambiri. Nebukadinezara, yemwe anali mfumu yamphamvu kwambiri padziko lapansi, analankhula monyoza kuti: “Ndi mulungu uti amene angakupulumutseni m’manja mwanga?” (Danieli 3:15) Anyamata atatuwo ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu wawo ali ndi mphamvu zoti atha kuwateteza, koma sanaganize kuti iye achita zimenezo pa nthawiyo. Choncho anayankha kuti: “Mulungu wathu amene tikumutumikira akhoza kutipulumutsa.” (Danieli 3:17) Ndi zimenedi zinachitika, chifukwa ng’anjo yotenthayo, ngakhale kuti anaisonkhezera kuwirikiza ka 7 kuposa nthawi zonse, sinalepheretse kuti Mulungu wawo wamphamvu zonse awapulumutse. Iye anawateteza ndipo mfumuyo inakakamizika kuvomereza kuti: “Palibe mulungu wina amene amatha kupulumutsa anthu ake mofanana ndi ameneyu.”​—Danieli 3:29.

11 Yehova anasonyezanso mochititsa chidwi mphamvu zake zoteteza pamene anasamutsa moyo wa Mwana wake wobadwa yekha n’kuuika m’mimba mwa namwali wa Chiyuda dzina lake Mariya. Mngelo anauza Mariya kuti ‘adzakhala woyembekezera n’kubereka mwana wamwamuna.’ Mngeloyo anafotokoza kuti: “Mzimu woyera udzafika pa iwe ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba.” (Luka 1:31, 35) Pa nthawiyi Mwana wa Mulungu ankafunikira kwambiri kutetezedwa. Popeza kuti mayi ake sanali angwiro, kodi zimenezi zikanachititsa kuti mwanayo abadwe wochimwa? Kodi Satana akanavulaza kapena kupha mwanayo asanabadwe? Ayi, zimenezi zinali zosatheka. Yehova anateteza Mwana wake amene anali m’mimba mwa Mariya kungoyambira pamene Mariyayo anakhala ndi pakati, moti panalibe chilichonse kapena aliyense amene akanamuvulaza. Yehova anapitiriza kuteteza Yesu pa nthawi imene anali mnyamata. (Mateyu 2:1-15) Mulungu anapitirizabe kuteteza Mwana wake mpaka pamene inafika nthawi yoti apereke moyo wake.

12. N’chifukwa chiyani kale Yehova ankateteza anthu ena modabwitsa?

12 N’chifukwa chiyani Yehova ankateteza anthu ena modabwitsa chonchi? Nthawi zambiri Yehova ankateteza anthu ena n’cholinga choti ateteze chinthu chofunika kwambiri, chomwe ndi kukwaniritsidwa kwa cholinga chake. Mwachitsanzo, zinali zofunika kwambiri kuti Yesu ali wakhanda apulumuke kuti cholinga cha Mulungu, chomwe pamapeto pake chidzathandiza anthu onse, chikwaniritsidwe. Nkhani zambiri zimene zimafotokoza mmene Yehova anagwiritsira ntchito mphamvu zake zoteteza, ndi mbali ya Malemba ouziridwa amene ‘analembedwa kuti atilangize. Malembawa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa n’cholinga choti tikhale ndi chiyembekezo.’ (Aroma 15:4) Zitsanzo zimenezi zimatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Mulungu wathu wamphamvu zonse. Koma kodi tingayembekezere kuti Mulungu azititeteza bwanji masiku ano?

Kodi Kutetezedwa ndi Mulungu Sikutanthauza Chiyani?

13. Kodi Yehova amafunika kutiteteza modabwitsa nthawi zonse? Fotokozani.

13 Lonjezo la Mulungu loti aziteteza anthu ake silitanthauza kuti Yehova amafunika kutiteteza modabwitsa nthawi zonse. Mulungu wathu sananene kuti tizikhala moyo wopanda mavuto m’dziko loipali. Atumiki a Yehova ambiri amakumana ndi mavuto aakulu monga umphawi, nkhondo, matenda ndiponso imfa. Yesu anauza ophunzira ake mosapita m’mbali kuti ena a iwo adzaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. N’chifukwa chake iye anatsindika mfundo yakuti tifunika kupirira mpaka mapeto. (Mateyu 24:9, 13) Yehova akanati nthawi zonse azigwiritsa ntchito mphamvu zake kupulumutsa atumiki ake modabwitsa, bwenzi Satana akumunyoza ndiponso kunena kuti timatumikira Mulungu osati chifukwa choti timamukonda koma chifukwa choti amatiteteza.​—Yobu 1:9, 10.

14. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti Yehova sateteza atumiki ake onse mofanana?

14 Ngakhalenso kale, Yehova sankagwiritsa ntchito mphamvu zake poteteza mtumiki wake aliyense kuti asaphedwe. Mwachitsanzo, Herode anapha mtumwi Yakobo cha m’ma 44 C.E. koma pasanapite nthawi yaitali, Petulo anapulumutsidwa “m’manja mwa Herode” yemweyo. (Machitidwe 12:1-11) Ndipo Yohane, mchimwene wake wa Yakobo, anakhala ndi moyo nthawi yaitali kuposa Petulo ndi Yakobo. Choncho n’zoonekeratu kuti sitingayembekezere Mulungu wathu kuti aziteteza atumiki ake onse mofanana. Ndiponso “nthawi yatsoka komanso zinthu zosayembekezereka” zimagwera tonsefe. (Mlaliki 9:11) Ndiyeno kodi Yehova amatiteteza bwanji masiku ano?

Yehova Amateteza Moyo Wathu

15, 16. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amateteza atumiki ake ngati gulu? (b) N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova aziteteza atumiki ake panopa komanso adzawateteza pa “chisautso chachikulu”?

15 Choyamba, tiyeni tiganizire mmene Yehova amatetezera moyo wathu. Atumiki a Yehovafe tingayembekezere kuti iye azititeteza ngati gulu. Akanakhala kuti sachita zimenezi, bwenzi Satana akungotipha. Taganizirani izi: Satana, yemwe ndi “wolamulira wa dzikoli,” amafunitsitsa kuthetseratu kulambira koona. (Yohane 12:31; Chivumbulutso 12:17) Maboma ena amphamvu kwambiri akhala akuletsa ntchito yathu yolalikira ndiponso kuyesetsa kuti athetseretu gulu lathu. Koma anthu a Yehova amakhalabe olimba komanso amapitiriza kulalikira. N’chifukwa chiyani maboma amphamvu alephera kuletsa ntchito ya Akhristu omwe amaoneka kuti ndi ochepa komanso opanda chitetezo? N’chifukwa chakuti Yehova amatiteteza ndi mapiko ake amphamvu.​—Salimo 17:7, 8.

16 Nanga kodi Yehova adzatiteteza pa “chisautso chachikulu” chimene chikubwerachi? Sitikufunika kudzachita mantha Mulungu akamadzawononga anthu oipa. Pajatu “Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero. Koma anthu osalungama amawasunga kuti adzawawononge pa tsiku lopereka chiweruzo.” (Chivumbulutso 7:14; 2 Petulo 2:9) Panopa, nthawi zonse tizikhala otsimikiza za zinthu ziwiri izi: Choyamba, Yehova sadzalola kuti Satana aphe atumiki onse a Mulungu okhulupirika. Chachiwiri, adzapereka mphoto ya moyo wosatha kwa anthu okhulupirika m’dziko latsopano lolungama ndipo amene anamwalira adzawaukitsa. Komanso anthu amene akumwalira panopa ndi otetezeka chifukwa Mulungu akuwakumbukira.​—Yohane 5:28, 29.

17. Kodi Yehova amatiteteza bwanji pogwiritsa ntchito Mawu ake?

17 Ngakhale panopa Yehova amatiteteza pogwiritsa ntchito “mawu” ake. Mawu akewa ndi amoyo ndipo ali ndi mphamvu yothandiza munthu kusintha n’kumakhala wosangalala. (Aheberi 4:12) Tikamatsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu, timatetezeka ku zinthu zina zomwe zingawononge moyo wathu. Lemba la Yesaya 48:17 limati: “Ine Yehova . . . ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.” N’zosakayikitsa kuti kutsatira mfundo za m’Mawu a Mulungu kungachititse kuti tikhale ndi thanzi labwino komanso moyo wautali. Mwachitsanzo, chifukwa chotsatira malangizo a m’Baibulo akuti tizipewa chiwerewere ndiponso tiziyesetsa kukhala oyera, timapewa makhalidwe odetsa komanso zizolowezi zoipa zimene zimawononga moyo wa anthu ambiri osaopa Mulungu. (Machitidwe 15:29; 2 Akorinto 7:1) Tikuthokozatu kwambiri kuti Mawu a Mulungu amatiteteza.

Yehova Amatiteteza Mwauzimu

18. Kodi Yehova amatiteteza bwanji mwauzimu?

18 Chofunika kwambiri n’chakuti Yehova amatiteteza mwauzimu. Mulungu wathu wachikondi amatipatsa chilichonse chimene tingafunikire kuti tizipirira mayesero komanso kuti tisawononge ubwenzi wathu ndi iye. Choncho Yehova amatithandiza kuti tikhalebe ndi moyo panopa komanso mpaka kalekale. Taganizirani zinthu zina zimene Mulungu amatipatsa kuti tikhalebe anzake.

19. Kodi mzimu wa Yehova ungatithandize bwanji kupirira mayesero alionse amene tingakumane nawo?

19 Yehova ndi “Wakumva pemphero.” (Salimo 65:2) Tikapanikizika ndi mavuto, kupemphera kwa Yehova ndi mtima wonse kungathandize kuti tiyambe kumvako bwino. (Afilipi 4:6, 7) Iye sangatichotsere mavuto athuwo modabwitsa, koma poyankha pemphero lathu lochokera pansi pamtima, angatipatse nzeru kuti tidziwe zoyenera kuchita. (Yakobo 1:5, 6) Kuwonjezera pamenepo, Yehova amapereka mzimu woyera kwa anthu amene amamupempha. (Luka 11:13) Mzimuwu, womwe ndi wamphamvu kwambiri, ungatithandize kupirira mayesero alionse kapenanso vuto lililonse limene tingakumane nalo. Ungatipatse “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti tipirire mpaka pamene Yehova adzachotse mavuto onse m’dziko latsopano limene lili pafupi kwambiri.​—2 Akorinto 4:7.

20. Kodi Yehova amatiteteza bwanji pogwiritsa ntchito Akhristu anzathu?

20 Nthawi zina, Yehova amatiteteza pogwiritsa ntchito abale ndi alongo athu. Iye wasonkhanitsa anthu ake kuti akhale “gulu la abale” la padziko lonse. (Yohane 6:44; 1 Petulo 2:17) Abale akamasonyezana chikondi, timaona umboni wakuti mzimu wa Mulungu umathandiza anthu kuchita zabwino. Mzimu umenewo umatithandiza kuti tikhale ndi makhalidwe abwino komanso amtengo wapatali monga chikondi, kukoma mtima ndiponso ubwino. (Agalatiya 5:22, 23) Choncho ngati takumana ndi vuto linalake ndipo Mkhristu mnzathu watipatsa malangizo othandiza kapena watiuza mawu olimbikitsa amene timafunikira kwambiri, tiyenera kuthokoza Yehova chifukwa chotithandiza pogwiritsa ntchito Mkhristuyo.

21. (a) Kodi ndi chakudya chauzimu cha pa nthawi yoyenera chiti chomwe Yehova amatipatsa kudzera mwa “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru”? (b) Kodi inuyo mwapindula bwanji ndi zinthu zimene Yehova amatipatsa pofuna kutiteteza mwauzimu?

21 Palinso chinthu china chimene Yehova amatipatsa pofuna kutiteteza, chomwe ndi chakudya chauzimu cha pa nthawi yoyenera. Kuti tizipeza mphamvu kuchokera m’Mawu ake, Yehova wauza “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” kuti azitipatsa chakudya chauzimu. Kapoloyu amagwiritsa ntchito mabuku, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, webusaiti yathu ya jw.org ndiponso misonkhano yampingo, yadera ndi yachigawo kuti azitipatsa “chakudya pa nthawi yoyenera.” Amatipatsa zimene timafunikira komanso pa nthawi yomwe zikufunikira. (Mateyu 24:45) Kodi nthawi ina pamisonkhano yampingo munamvapo mfundo inayake mundemanga, munkhani kapena m’pemphero, imene inakulimbikitsani komanso kukupatsani mphamvu zomwe munkafunikira? Kapena kodi moyo wanu unasintha chifukwa cha nkhani inayake imene munawerenga m’magazini yathu ina? Kumbukirani kuti Yehova amatipatsa zinthu zonsezi kuti azititeteza mwauzimu.

22. Kodi nthawi zonse Yehova amagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zake, nanga n’chifukwa chiyani akamachita zimenezi amakhala kuti akutithandiza?

22 Kunena zoona, Yehova amateteza “onse amene amathawira kwa iye.” (Salimo 18:30) Tikudziwa kuti panopa sagwiritsa ntchito mphamvu zake potiteteza ku mavuto onse amene tingakumane nawo. Komabe, nthawi zonse amagwiritsa ntchito mphamvu zake zoteteza poonetsetsa kuti cholinga chake chikukwaniritsidwa. Ndipo zimene amachitazi pamapeto pake zidzathandiza atumiki ake. Tikakhala pa ubwenzi ndi Yehova n’kumachitabe zinthu zomwe zingachititse kuti azitikonda, iye adzatipatsa moyo wosatha. Popeza tikuyembekezera zimenezi, tingamaone mavuto alionse amene tikukumana nawo m’dzikoli kuti ndi “akanthawi ndiponso aang’ono.”​—2 Akorinto 4:17.