Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 8

Mphamvu Zobwezeretsa​—Yehova ‘Akupanga Zinthu Zonse Kuti Zikhale Zatsopano’

Mphamvu Zobwezeretsa​—Yehova ‘Akupanga Zinthu Zonse Kuti Zikhale Zatsopano’

1, 2. Kodi anthu masiku ano amataya zinthu ziti, nanga zimenezi zimatikhudza bwanji?

 TIYEREKEZE kuti mwana wataya kapena wawononga chidole chake chimene amachikonda kwambiri ndipo akulira momvetsa chisoni. Mayi kapena bambo ake nawonso akumva chisoni kumuona akulira choncho. Koma kenako bambo kapena mayi akewo apeza kapenanso kukonza chidolecho ndipo mwanayo akusangalala kwambiri. Makolowo sangavutike kupeza chidolecho kapena kuchikonza. Koma kwa mwanayo, zimene makolowo achita n’zodabwitsa kwambiri. Tsopano iye azithanso kuseweretsa chidolecho ngakhale kuti poyamba amaganiza kuti sadzakhala nachonso.

2 Yehova, yemwe ndi Bambo wabwino kwambiri, ali ndi mphamvu zobwezeretsa zinthu zimene ana ake apadziko lapansi angaone ngati sizingatheke kuzibwezeretsa. Koma apa sikuti tikunena zidole. Mu “nthawi yapadera komanso yovuta” ino, timataya zinthu zofunika kwambiri. (2 Timoteyo 3:1-5) Nthawi iliyonse anthu akhoza kutaya nyumba kapena katundu wawo, ntchito ikhoza kuwathera komanso akhoza kuyamba kudwala. Timadanso nkhawa tikaganizira kuwonongedwa kwa zinthu zachilengedwe komwe kukuchititsa kuti mitundu yambiri ya zamoyo itheretu. Koma palibe chimene chimatiwawa kwambiri kuposa imfa ya munthu yemwe timam’konda. Timamva kuti tataya chinthu chofunika kwambiri ndipo timasowa mtengo wogwira.​—2 Samueli 18:33.

3. Kodi ndi mfundo yolimbikitsa iti yomwe ili pa Machitidwe 3:21, nanga Yehova adzagwiritsa ntchito chiyani kuti akwaniritse zimenezi?

3 Choncho n’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova ali ndi mphamvu zobwezeretsa zinthu. M’mutuwu tiona kuti pali zinthu zambiri zokhudza ana ake apadziko lapansi zimene Mulungu angabwezeretse ndiponso zomwe adzabwezeretse. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti Yehova akufuna ‘kudzabwezeretsa zinthu zonse.’ (Machitidwe 3:21) Kuti akwaniritse zimenezi, iye adzagwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya, womwe wolamulira wake ndi Mwana wake, Yesu Khristu. Umboni umasonyeza kuti Ufumu umenewu unayamba kulamulira kumwamba mu 1914. a (Mateyu 24:3-14) Koma kodi Yehova adzabwezeretsa zinthu ziti? Tiyeni tikambirane chinthu china chimene wabwezeretsa kale m’nthawi yathu ino komanso zina zomwe adzabwezeretse m’tsogolo, zimene zidzakhudze anthu onse. Zinthu zonsezi ndi zikuluzikulu.

Kubwezeretsa Kulambira Koona

4, 5. N’chiyani chinachitikira anthu a Mulungu mu 607 B.C.E., ndipo kodi Yehova anawalonjeza chiyani?

4 Chinthu china chimene Yehova wabwezeretsa kale ndi kulambira koona. Kuti timvetse bwino zimenezi, tiyeni tikambirane mwachidule mbiri ya ufumu wa Yuda. Kuchita zimenezi kutithandiza kumvetsa bwino mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu zake zobwezeretsa.​—Aroma 15:4.

5 Taganizirani mmene Ayuda okhulupirika anamvera mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa mu 607 B.C.E. Mzinda umene ankaukonda kwambiriwu unagumulidwa ndipo mpanda wake unagwetsedwa. Koma chomvetsa chisoni kwambiri chinali chakuti kachisi wokongola amene Solomo anamanga anawonongedwanso. Kachisiyu anali likulu la kulambira koona padziko lonse. (Salimo 79:1) Anthu amene anapulumuka anawatenga kupita nawo ku ukapolo ku Babulo ndipo dziko lawo analisiya lili bwinja moti nyama zakutchire zinayamba kukhalamo. (Yeremiya 9:11) Mwina Ayuda ankaona kuti palibenso chiyembekezo. (Salimo 137:1) Koma Yehova, yemwe anali atanena kale kuti mzindawu udzawonongedwa, analonjeza kuti adzabwezeretsa zinthu.

6-8. (a) Kodi ndi nkhani iti imene aneneri a Chiheberi anailemba mobwerezabwereza, nanga maulosi amenewa anakwaniritsidwa bwanji koyamba? (b) Kodi maulosi amenewa akukwaniritsidwa bwanji munthawi yathu ino?

6 Ndipotu aneneri a Chiheberi analemba mobwerezabwereza nkhani yokhudza kubwezeretsa zinthu. b Kudzera mwa aneneriwa, Yehova analonjeza kuti dzikolo lidzabwereranso mwakale, muzidzakhalanso anthu, lidzakhala lachonde ndiponso lotetezeka ku nyama zolusa ndi adani. Iye ananena kuti dziko lawolo lidzakhala lokongola kwambiri. (Yesaya 65:25; Ezekieli 34:25; 36:35) Chofunika kwambiri chinali choti kulambira koona kudzayambiranso ndipo kachisi adzamangidwanso. (Mika 4:1-5) Maulosiwa anathandiza Ayuda kukhala ndi chiyembekezo komanso kupirira ukapolo wawo kwa zaka 70 ku Babulo.

7 Kenako inadzafika nthawi yoti Yehova abwezeretse zinthu. Ayuda anamasulidwa ku Babulo ndipo anabwerera ku Yerusalemu n’kukamanganso kachisi wa Yehova. (Ezara 1:1, 2) Kulambira kwawo kukakhala koyera, Yehova ankawadalitsa, kuchititsa kuti dziko lawo likhale lachonde komanso ankawapatsa zinthu zina zambiri. Ankawateteza kwa adani awo ndiponso nyama zolusa zomwe zinakhala m’dzikolo kwa zaka zambiri. Iwo ayenera kuti anasangalala kwambiri chifukwa cha mphamvu zobwezeretsa za Yehova. Komabe zinthu zimenezi zinali kukwaniritsidwa koyamba ndiponso kochepa kwambiri kwa maulosi okhudza kubwezeretsedwa kwa zinthu. Kukwaniritsidwa kwakukulu kunali koti kudzachitika munthawi yathu ino, yomwe ndi “masiku otsiriza,” pamene mbadwa ya Mfumu Davide imene Mulungu analonjeza kalekale inayamba kulamulira.​—Yesaya 2:2-4; 9:6, 7.

8 Yesu atangoyamba kulamulira mu Ufumu wakumwamba mu 1914, anayamba kuthandiza anthu okhulupirika padzikoli kuti ayambirenso kulambira Mulungu moyenera. Mofanana ndi zomwe Koresi, mfumu ya Perisiya anachita pomasula Ayuda ku Babulo mu 537 B.C.E., Yesu anamasulanso Ayuda auzimu, omwe ndi otsatira ake. Anawamasula m’Babulo Wamkulu yemwe ndi zipembedzo zonse zonyenga. (Aroma 2:29; Chivumbulutso 18:1-5) Kungochokera mu 1919, Akhristu oona anayambiranso kulambira Yehova m’njira imene iye amafuna. (Malaki 3:1-5) Kuyambira nthawi imeneyo, anthu a Yehova akhala akumulambira m’kachisi wake wauzimu woyeretsedwa, yemwe amaimira dongosolo la kulambira koyera limene Mulungu anakhazikitsa. N’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika kwa ife masiku ano?

N’chifukwa Chiyani Kubwezeretsa Kulambira Koona Kuli Kofunika?

9. Atumwi onse atafa, kodi matchalitchi amene amati ndi a Chikhristu anachita zotani pa nkhani yolambira Mulungu, koma kodi Yehova wachita chiyani m’nthawi yathu ino?

9 Taganizirani zimene zakhala zikuchitika. Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankasangalala ndi madalitso ambiri auzimu. Koma Yesu ndi atumwi analosera kuti anthu adzasiya kulambira Mulungu m’njira yoyenera. (Mateyu 13:24-30; Machitidwe 20:29, 30) Atumwi onse atafa, panayambika matchalitchi omwe amati ndi a Chikhristu. Atsogoleri a matchalitchiwa anatengera ziphunzitso ndi miyambo yachikunja. Anachititsanso kuti anthu aziona ngati n’zosatheka kupemphera kwa Mulungu. Iwo ankauza anthu kuti Mulungu ndi Utatu wosamvetsetseka. Ankawaphunzitsanso kuti aziulula machimo awo kwa ansembe komanso azipemphera kwa Mariya ndi kwa “oyera mtima” osiyanasiyana m’malo mopemphera kwa Yehova. Ndiye popeza kuti ziphunzitso zabodzazi zakhala zilipo kwa zaka zambiri, kodi Yehova wachita chiyani? Ngakhale kuti panopa padzikoli pali mfundo zambiri zabodza zachipembedzo komanso anthu ali ndi makhalidwe osonyeza kuti saopa Mulungu, iye wabwezeretsa kulambira koona. Choncho sikungakhale kukokomeza kunena kuti kubwezeretsa kulambira koonaku ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri zomwe zachitika m’nthawi yathu ino.

10, 11. (a) Kodi m’paradaiso wauzimu muli mbali ziwiri ziti, nanga mungatani kuti inunso mukhale m’paradaisoyu? (b) Kodi Yehova wasonkhanitsa anthu otani kuti akhale m’paradaiso wauzimu, nanga anthuwa adzakhala ndi mwayi woona chiyani?

10 Choncho masiku ano Akhristu oona ali m’paradaiso wauzimu yemwe akupitiriza kukula komanso kukongola. Kodi m’paradaiso ameneyu muli zinthu ziti? Muli mbali ziwiri zikuluzikulu. Mbali yoyamba ndi kulambira Yehova Mulungu woona movomerezeka. Iye watithandiza kuti tizimulambira popanda kusocheretsedwa ndi mabodza achipembedzo. Komanso amatipatsa chakudya chauzimu. Zimenezi zimatithandiza kuti tiziphunzira za Atate wathu wakumwamba, tizichita zinthu zomusangalatsa ndiponso kuti akhale mnzathu. (Yohane 4:24) Mbali yachiwiri ya paradaiso wauzimu ikukhudza anthu. Mogwirizana ndi zimene Yesaya analosera, “m’masiku otsiriza” ano Yehova waphunzitsa anthu ake zimene angachite kuti azikhala mwamtendere. Watiphunzitsa kuti tisamamenye nawo nkhondo. Ngakhale kuti si ife angwiro, amatithandiza kuvala ‘umunthu watsopano.’ Tikamayesetsa kuchita zabwino, amatidalitsa potipatsa mzimu wake woyera umene umatithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino. (Aefeso 4:22-24; Agalatiya 5:22, 23) Mukamachita zinthu mogwirizana ndi mzimu wa Mulungu, mumasonyeza kuti mulidi m’paradaiso wauzimu.

11 Yehova wasonkhanitsa m’paradaiso wauzimu ameneyu anthu amene amawakonda. Anthuwa amamukonda, amakonda mtendere ndiponso “amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyu 5:3) Anthu amenewa ndi omwe adzakhale ndi mwayi woona kubwezeretsa kwina kwapadera. Kubwezeretsa kumeneku kudzakhudza anthu onse pa nthawiyo ndiponso dziko lonse lapansi.

“Taonani! Zinthu Zonse Zimene Ndikupanga Ndi Zatsopano”

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani maulosi okhudza kubwezeretsa zinthu akuyenera kukwaniritsidwa m’njira inanso? (b) Kodi m’munda wa Edeni Yehova anasonyeza kuti ali ndi cholinga chotani chokhudza dziko lapansi, nanga kudziwa zimenezi kungatithandize bwanji kukhala ndi chiyembekezo?

12 Maulosi ambiri onena za kubwezeretsa zinthu sikuti amangonena za kubwezeretsa kwauzimu kokha. Mwachitsanzo, Yesaya analemba kuti nthawi ina odwala, olumala komanso amene ali ndi vuto losaona ndiponso losamva adzachiritsidwa ndipo ngakhale imfa sidzakhalaponso. (Yesaya 25:8; 35:1-7) Malonjezo amenewa sanakwaniritsidwe ku Isiraeli wakale. Ndipo ngakhale kuti m’nthawi yathu ino taona maulosiwa akukwaniritsidwa m’paradaiso wauzimu, tili ndi zifukwa zomveka zokhulupirira kuti m’tsogolomu adzakwaniritsidwa padziko lonse. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?

13 M’munda wa Edeni, Yehova anasonyeza bwino cholinga chake chokhudza dziko lapansi. Iye ankafuna kuti padzikoli pakhale anthu osangalala, athanzi ndiponso ogwirizana. Ankafuna kuti anthu azisamalira zinyama komanso dziko lapansili mpaka lonse likhale paradaiso. (Genesis 1:28) Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi mmene zinthu zilili panopa. Komabe tizikhulupirira ndi mtima wonse kuti zofuna za Yehova sizilephereka. (Yesaya 55:10, 11) Yesu, yemwe ndi Mesiya komanso Mfumu yosankhidwa ndi Yehova, ndi amene adzabweretse Paradaiso ameneyu padziko lonse lapansi.​—Luka 23:43.

14, 15. (a) Kodi Yehova adzapanga bwanji ‘zinthu zonse kuti zikhale zatsopano’? (b) Kodi moyo udzakhala wotani m’Paradaiso, nanga inuyo n’chiyani chomwe mukuyembekezera mwachidwi?

14 Mukuganiza kuti mudzamva bwanji mukadzaona dziko lonseli lili Paradaiso? Ponena za nthawi imeneyo, Yehova ananena kuti: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.” (Chivumbulutso 21:5) Taganizirani tanthauzo la zimenezi. Yehova akadzamaliza kugwiritsa ntchito mphamvu zake kuwononga dziko loipali, chimene chidzatsale ndi “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” Izi zikutanthauza kuti boma latsopano lakumwamba lizidzalamulira anthu padziko lapansi omwe amakonda Yehova n’kumachita zimene iye amafuna. (2 Petulo 3:13) Satana ndi ziwanda zake adzaletsedwa kuchita chilichonse. (Chivumbulutso 20:3) Ndiyeno kwa nthawi yoyamba pambuyo pa zaka masauzande ambiri, anthu sazidzasokonezedwanso ndi zochita za Satana ndiponso ziwanda zake. Imeneyitu idzakhala nthawi yosangalatsa kwambiri.

15 Pa nthawi imeneyo tizidzasamalira dziko lokongolali ngati mmene Yehova ankafunira poyamba. Dzikoli lili ndi mphamvu zotha kubwezeretsa zinthu zachilengedwe. Mwachitsanzo, nyanja ndi mitsinje zomwe zaipitsidwa zikhoza kudzikonza ngati chomwe chikuchititsa kuti ziwonongekecho chitachotsedwa. Malo amene anawonongeka chifukwa cha nkhondo akhoza kukhalanso bwinobwino ngati nkhondozo zitatha. Tidzasangalalatu kwambiri kugwira nawo ntchito yokonza dziko lonse lapansi kuti likhale Paradaiso ngati mmene unalili munda wa Edeni, ndipo lidzakhala ndi zomera ndiponso nyama zamitundumitundu. M’malo momawononga mwadala nyama ndi zomera, anthu sazidzawononga zinthu zimenezi. Ngakhalenso ana sazidzaopa nyama zakutchire.​—Yesaya 9:6, 7; 11:1-9.

16. Kodi ndi kubwezeretsa kuti m’Paradaiso kumene kudzakhudze munthu aliyense wokhulupirika?

16 Yehova adzabwezeretsanso zinthu kwa munthu aliyense payekha. Padziko lonse, anthu onse amene adzapulumuke pa Aramagedo adzachiritsidwa modabwitsa. Mofanana ndi mmene anachitira ali padziko lapansi, Yesu adzagwiritsa ntchito mphamvu zimene Mulungu anamupatsa ndipo adzachiritsa anthu olumala, odwala komanso amene ali ndi vuto losaona ndi losamva. (Mateyu 15:30) Achikulire adzasangalala kukhalanso achinyamata amphamvu komanso athanzi. (Yobu 33:25) Makwinya adzatha ndipo manja, miyendo ndiponso minofu izidzagwiranso ntchito bwino ngati kale. Anthu onse okhulupirika adzazindikira kuti mavuto amene amabwera chifukwa choti ndife ochimwa komanso siife angwiro akutha. Tidzathokoza kwambiri Yehova Mulungu chifukwa cha mphamvu zake zazikulu zobwezeretsa zinthu. Tsopano tiyeni tikambirane chinthu china chosangalatsa kwambiri chimene chidzachitike pa nthawi yobwezeretsa zinthu imeneyi.

Kubwezeretsa Moyo kwa Anthu Amene Anamwalira

17, 18. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anadzudzula Asaduki? (b) N’chiyani chinachititsa Eliya kupempha Yehova kuti aukitse munthu?

17 Munthawi ya atumwi, atsogoleri achipembedzo ena otchedwa Asaduki sankakhulupirira zoti akufa adzaukitsidwa. Yesu anawadzudzula kuti: “Mukulakwitsa chifukwa simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu.” (Mateyu 22:29) Malemba amasonyezadi kuti Yehova ali ndi mphamvu zotha kubwezeretsa moyo kwa anthu amene anamwalira. Tiyeni tione zitsanzo pa nkhaniyi.

18 Taganizirani zimene zinachitika munthawi ya Eliya. Mayi wamasiye anali atanyamula mwana wake wamwamuna mmodzi yekhayo yemwe anali atamwalira. Mneneri Eliya, yemwe anali mlendo kunyumba kwa mayiyo kwa nthawi ndithu, ayenera kuti zinamuvuta kukhulupirira. Poyamba, iye anathandiza kupulumutsa mwanayu kuti asafe ndi njala. N’kutheka kuti Eliya ankagwirizana kwambiri ndi mnyamatayo. Mayi ake a mwanayo anali ndi chisoni kwambiri. Mwamuna wawo atamwalira, ankatonthozedwa akaona mnyamatayu. Komanso mwina ankaganiza kuti mwana wawoyo ndi amene adzawasamalire akadzakalamba. Chifukwa cha chisoni, mayiwa anayamba kuganiza kuti akulangidwa chifukwa cha zimene analakwitsa m’mbuyomo. Eliya anakhudzidwa kwambiri ndi zimenezi. Choncho anatenga mwanayo kuchokera m’manja mwa mayi ake n’kupita naye kuchipinda kwake ndipo anapempha Yehova Mulungu kuti amuukitse.​—1 Mafumu 17:8-21.

19, 20. (a) Kodi Abulahamu anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira kuti Yehova ali ndi mphamvu zoukitsa anthu amene amwalira, ndipo n’chiyani chinachititsa kuti azikhulupirira zimenezi? (b) Kodi Yehova anadalitsa bwanji Eliya chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro?

19 Eliya sanali woyamba kukhulupirira zoti munthu amene wamwalira akhoza kuukitsidwa. Zaka zambiri m’mbuyomo, Abulahamu ankakhulupirira kuti Yehova ali ndi mphamvu zoukitsa akufa, ndipo iye anali ndi zifukwa zomveka. Abulahamu ali ndi zaka 100 ndipo Sara ali ndi zaka 90, Yehova anabwezeretsa mphamvu zawo zobereka, ndipo Sara anabereka mwana wamwamuna. (Genesis 17:17; 21:2, 3) Kenako mnyamatayo ali wamkulu, Yehova anauza Abulahamu kuti apereke nsembe mwana wakeyo. Abulahamu anasonyeza kuti ankakhulupirira zoti Yehova angachititse kuti Isaki, mwana wake wokondedwayo, akhalenso ndi moyo. (Aheberi 11:17-19) N’chifukwa chake pamene ankapita kuphiri kuti akapereke nsembe Isaki, anatsimikizira antchito ake kuti iye ndi mwana wakeyo abwerera limodzi.​—Genesis 22:5.

“Mwana wanu uja tsopano ali moyo.”

20 Yehova anapulumutsa Isaki, choncho sipanafunike kuti amuukitse. Koma pa nkhani ya Eliya, mwana wa mayi wamasiye uja nali atamwalira kale, koma panali pasanathe nthawi yaitali. Yehova anadalitsa Eliya chifukwa cha chikhulupiriro chake poukitsa mwanayo. Kenako Eliya anapereka mwanayo kwa amayi ake ndipo ananena mawu osaiwalika akuti: “Mwana wanu uja tsopano ali moyo.”​—1 Mafumu 17:22-24.

21, 22. (a) N’chifukwa chiyani Baibulo limafotokoza nkhani za anthu amene anaukitsidwa? (b) Kodi ndi anthu ambiri bwanji amene adzaukitsidwe m’Paradaiso, nanga ndani adzawaukitse?

21 Imeneyi ndi nkhani yoyamba m’Baibulo yomwe imasonyeza kuti Yehova anagwiritsa ntchito mphamvu zake poukitsa munthu. Patapita nthawi, Yehova anapatsanso mphamvu Elisa, Yesu, Paulo ndiponso Petulo kuti aukitse anthu. N’zoona kuti anthu amene anaukitsidwawo kenako anamwaliranso. Komabe nkhani za m’Baibulo zimenezi zimatithandiza kudziwa zimene zidzachitike m’tsogolo.

22 M’Paradaiso, Yesu adzakwaniritsa udindo wake monga “kuuka ndi moyo.” (Yohane 11:25) Adzaukitsa anthu mamiliyoni osawerengeka n’kuwapatsa mwayi wokhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padzikoli. (Yohane 5:28, 29) Taganizirani mmene tidzasangalalire tikadzakumana komanso kuhagana ndi anzathu ndiponso achibale amene tinkawakonda kwambiri koma tinasiyana nawo kalekale chifukwa cha imfa. Anthu onse adzatamanda Yehova chifukwa cha mphamvu zake zoukitsa.

23. Kodi ndi chinthu chachikulu chiti chimene Yehova anachita posonyeza mphamvu zake, ndipo zimenezi zimatitsimikizira bwanji kuti akufa adzaukitsidwa?

23 Yehova watithandiza kuti tisamakayikire ngakhale pang’ono zoti akufa adzaukitsidwa. Iye anaukitsa Mwana wake Yesu ndi thupi lauzimu ndipo anamupatsa mphamvu komanso udindo waukulu kuposa angelo onse. Imeneyi inali njira yaikulu kwambiri imene Yehova anasonyezera mphamvu zake. Yesu ataukitsidwa, anthu ambirimbiri anamuona. (1 Akorinto 15:5, 6) Umenewu ndi umboni wokwanira wakuti akufa adzauka, ngakhale kwa anthu amene sakhulupirira zimenezi. Yehova ali ndi mphamvu zobwezeretsa moyo.

24. N’chifukwa chiyani tiyenera kumakhulupirira kuti Yehova adzaukitsa anthu amene anamwalira, nanga ndi chiyembekezo chiti chimene tonsefe tiyenera kuchiona kuti ndi chamtengo wapatali?

24 Sikuti Yehova wangokhala ndi mphamvu zobwezeretsa moyo kwa anthu amene anamwalira, koma ndi wofunitsitsanso kuchita zimenezi. Yobu, yemwe anali wokhulupirika, anauziridwa kunena kuti Yehova amachita kulakalaka kuti adzaukitse anthu amene anamwalira. (Yobu 14:15) Kodi simukufunitsitsa kuti Mulungu wathu, yemwe amalakalaka kugwiritsa ntchito mwachikondi mphamvu zake zobwezeretsa zinthu, akhale mnzanu? Komabe, kumbukirani kuti kuukitsa anthu amene anamwalira ndi mbali imodzi yokha ya ntchito yaikulu yobwezeretsa zinthu imene Yehova adzachite. Pamene mukuyesetsa kulimbitsa ubwenzi wanu ndi iye, nthawi zonse muziona kuti chiyembekezo chanu, choti mukhoza kudzakhalapo Yehova ‘akamadzapanga zonse kuti zikhale zatsopano,’ ndi chamtengo wapatali.​—Chivumbulutso 21:5.

a “Nthawi yobwezeretsa zinthu zonse” inayamba pamene Ufumu wa Mesiya unakhazikitsidwa komanso pamene mbadwa ya Mfumu Davide, yemwe anali wokhulupirika, inakhala Mfumu. Yehova analonjeza Davide kuti mmodzi wa mbadwa zake adzalamulira mpaka kalekale. (Salimo 89:35-37) Koma Ababulo atawononga Yerusalemu mu 607 B.C.E., palibe mbadwa ya Davide iliyonse imene inakhala pampando wachifumu wa Mulungu. Yesu, amene anabadwa monga wolowa ufumu wa Davide, anakhala Mfumu yomwe Mulungu analonjeza kalekale, pamene anapatsidwa Ufumu kumwamba.

b Mwachitsanzo, Mose, Yesaya, Yeremiya, Ezekieli, Hoseya, Yoweli, Amosi, Obadiya, Mika ndi Zefaniya analemba za nkhani imeneyi.