Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 10

“Muzitsanzira Mulungu” Mukamagwiritsa Ntchito Mphamvu

“Muzitsanzira Mulungu” Mukamagwiritsa Ntchito Mphamvu

1. Kodi anthu omwe si angwirofe timakodwa mosavuta mumsampha uti?

 “MUNTHU aliyense amene wapatsidwa mphamvu, pakapita nthawi amakodwa mumsampha wosaonekera.” Mawu amenewa ananena ndi wandakatulo wina wa m’zaka za m’ma 1800, ndipo amanena za vuto linalake lomwe ndi kugwiritsa ntchito mphamvu molakwika. N’zomvetsa chisoni kuti anthu omwe si angwirofe timakodwa mosavuta mumsampha umenewu. Kuyambira kalekale, “munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Munthu waudindo akamagwiritsa ntchito mphamvu zake mopanda chikondi, anthu ambiri amavutika.

2, 3. (a) Kodi chochititsa chidwi n’chiyani ndi mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu? (b) Kodi anthufe tili ndi mphamvu zotha kuchita chiyani, nanga tiyenera kuzigwiritsa ntchito bwanji?

2 Ndiye kodi si zochititsa chidwi kuti Yehova Mulungu, amene ali ndi mphamvu zopanda malire, sagwiritsa ntchito mphamvuzo molakwika? Monga taonera m’mitu yapitayi, nthawi zonse amagwiritsa ntchito mphamvu zake zotha kulenga zinthu, kuwononga, kuteteza kapena kubwezeretsa pa zifukwa zabwino komanso mwachikondi. Tikamaganizira mozama mmene amagwiritsira ntchito mphamvu zake, timafunitsitsa kuti akhale mnzathu. Zimenezi zingatichititse kuti ‘tizimutsanzira’ tikamagwiritsa ntchito mphamvu zathu. (Aefeso 5:1) Komabe anthufe ndife otsika poyerekezera ndi Mulungu. Ndiye kodi tili ndi mphamvu zotani?

3 Kumbukirani kuti munthu analengedwa “m’chifaniziro cha Mulungu” ndipo ndi wofanana naye. (Genesis 1:26, 27) Choncho ifenso tili ndi mphamvu ndithu. Tili ndi mphamvu zotha kukwaniritsa zinazake, kugwira ntchito, kuuza ena zochita kapena kuwalamulira ndiponso kulimbikitsa ena kuchita zinazake, makamaka amene amatikonda. Tithanso kukhala ndi thupi lamphamvu kapenanso kukhala ndi chuma n’kumatha kuchita zinazake. Ponena za Yehova, wolemba masalimo wina anati: “Inu ndinu kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9) Choncho mphamvu zilizonse zomwe tili nazo, Mulungu ndi amene amatipatsa kapena kutilola kuti tikhale nazo. N’chifukwa chake timafuna kuti azisangalala ndi mmene timazigwiritsira ntchito. Ndiye kodi tingachite bwanji zimenezi?

Chinsinsi Chake Ndi Chikondi

4, 5. (a) Kodi chinsinsi chogwiritsa ntchito bwino mphamvu n’chiyani, nanga chitsanzo cha Mulungu chimasonyeza bwanji zimenezi? (b) Kodi chikondi chingatithandize bwanji kuti tizigwiritsa ntchito bwino mphamvu?

4 Chinsinsi chogwiritsa ntchito mphamvu moyenera ndi chikondi. Timaona zimenezi tikaganizira chitsanzo cha Mulungu. Kumbukirani zomwe tinakambirana m’Mutu 1 zokhudza makhalidwe 4 akuluakulu a Mulungu, omwe ndi mphamvu, chilungamo, nzeru komanso chikondi. Pa makhalidwe amenewa, kodi lalikulu kwambiri ndi liti? Chikondi. Lemba la 1 Yohane 4:8 limati, “Mulungu ndi chikondi.” Choncho khalidwe lalikulu la Yehova ndi chikondi ndipo zonse zimene amachita, amazichita chifukwa cha chikondi komanso kuti zithandize anthu amene amamukonda.

5 Nafenso chikondi chingatithandize kuti tisamagwiritse ntchito mphamvu molakwika. Ndipotu Baibulo limatiuza kuti chikondi “n’chokoma mtima” komanso “sichisamala zofuna zake zokha.” (1 Akorinto 13:4, 5) Choncho ngati tili ndi chikondi, anthu amene tikuwalamulira sitingawachitire zinthu mosawaganizira kapena mwankhanza. M’malomwake timawalemekeza n’kumaganizira kwambiri zofuna zawo osati zathu.​—Afilipi 2:3, 4.

6, 7. (a) Kodi kuopa Mulungu n’kutani, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti khalidweli lingatithandize kuti tizigwiritsa ntchito bwino mphamvu? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kuopa kukhumudwitsa Mulungu n’kogwirizana ndi kumukonda.

6 Chikondi chimagwirizananso ndi khalidwe lina limene lingatithandize kuti tisamagwiritse ntchito mphamvu molakwika, lomwe ndi kuopa Mulungu. Kodi kuopa Mulungu n’kofunika bwanji? Lemba la Miyambo 16:6 limati: “Chifukwa choopa Yehova, munthu amapewa kuchita zoipa.” Chimodzi mwa zinthu zoipa zimene tiyenera kupewa ndi kugwiritsa ntchito mphamvu molakwika. Ngati timaopa Mulungu, sitingamazunze anthu amene timawalamulira. Chifukwa chiyani? Chifukwa chimodzi n’chakuti timadziwa kuti tidzayankha kwa Mulungu pa nkhani ya mmene timachitira zinthu ndi anthu amenewa. (Nehemiya 5:1-7, 15) Koma palinso chifukwa china chofunika kwambiri. Mawu a chilankhulo choyambirira omwe anawamasulira kuti “kuopa,” nthawi zambiri amatanthauza kulemekeza kwambiri Mulungu. Choncho Baibulo limasonyeza kuti timafunika kukonda Mulungu kuti tizimulemekeza kwambiri. (Deuteronomo 10:12, 13) Tikamalemekeza Mulungu kwambiri chonchi, timapewa kuchita zimene zingamukhumudwitse osati chifukwa chongoopa zotsatira zake, koma chifukwa choti timamukonda.

7 Mwachitsanzo, taganizirani za mnyamata wamng’ono amene amagwirizana kwambiri ndi bambo ake. Mnyamatayo amadziwa kuti bambo akewo amamukonda komanso amasangalala naye. Koma amadziwanso zimene bambo akewo amafuna kuti iye azichita ndiponso kuti akachita zosayenera akhoza kumupatsa chilango. Mnyamatayu sachita mantha ndi bambo akewo koma amawakonda kwambiri ndipo amafunitsitsa kumachita zimene zimawasangalatsa. Ndi zimenenso zimachitika munthu akamaopa Mulungu. Chifukwa choti timakonda Yehova, yemwe ndi Bambo wathu wakumwamba, timaopa kuchita chilichonse chimene chingamukhumudwitse. (Genesis 6:6) M’malomwake, timafunitsitsa kuti tizisangalatsa mtima wake. (Miyambo 27:11) N’chifukwa chake timafuna kuti tizigwiritsa ntchito bwino mphamvu zathu. Tiyeni tione mmene tingachitire zimenezi.

M’banja

8. (a) Kodi amuna ali ndi udindo wotani m’banja, nanga ayenera kumachita bwanji zinthu? (b) Kodi mwamuna angasonyeze bwanji kuti amalemekeza mkazi wake?

8 Choyamba, taganizirani za m’banja. Lemba la Aefeso 5:23 limati: “Mwamuna ndi mutu wa mkazi wake.” Kodi mwamuna ayenera kumagwiritsa ntchito bwanji mphamvu zimene Mulungu anamupatsazi? Baibulo limauza amuna kuti azikhala ndi akazi awo “mowadziwa bwino” komanso ‘aziwapatsa ulemu chifukwa akazi ali ngati chiwiya chosachedwa kusweka.’ (1 Petulo 3:7) Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “kupatsa ulemu” amatanthauza kuona kuti chinthu ndi “chodula, chofunika kwambiri, . . . cholemekezeka.” Mawu ena ochokera ku mawu amenewa amamasulidwanso kuti “mphatso” ndiponso “chamtengo wapatali.” (Machitidwe 28:10; 1 Petulo 2:7) Mwamuna amene amalemekeza mkazi wake samumenya, kumuchititsa manyazi kapena kumunyoza. Kumuchitira zimenezi kungachititse kuti mkaziyo azidziona kuti ndi wosafunika. Koma amazindikira kuti mkazi wakeyo ndi wofunika kwambiri ndipo amamupatsa ulemu. Kaya ali kwa okha kapena pagulu, zolankhula komanso zochita zake zimasonyeza kuti amaona kuti mkazi wake ndi wamtengo wapatali kwa iye. (Miyambo 31:28) Mwamuna wotereyu, mkazi wake amamukonda komanso kumulemekeza ndiponso chofunika kwambiri n’choti Mulungu amasangalala naye.

Mwamuna ndi mkazi wake amagwiritsa ntchito bwino mphamvu zawo akamakondana komanso kulemekezana

9. (a) Kodi akazi ali ndi mphamvu zotani m’banja? (b) N’chiyani chingathandize mkazi kuti azigwiritsa ntchito maluso ake pothandiza mwamuna wake, ndipo zotsatira zake zingakhale zotani?

9 Akazi nawonso ali ndi mphamvu m’banja. Baibulo limatiuza za akazi oopa Mulungu amene molemekeza mutu wabanja, anathandiza amuna awo kuchita zabwino kapenanso kuti asasankhe zinthu molakwika. (Genesis 21:9-12; 27:46–28:2) Mkazi akhoza kukhala wanzeru kwambiri komanso kuti amachita bwino zinthu zina kuposa mwamuna wake. Komabe ayenera ‘kumalemekeza kwambiri’ mwamuna wake ndiponso ‘kumugonjera ngati mmene amagonjerera Ambuye.’ (Aefeso 5:22, 33) Mkazi akakhala ndi cholinga chosangalatsa Mulungu, amagwiritsa ntchito maluso ake pothandiza mwamuna wake m’malo momupeputsa kapena kufuna kuti azimulamulira. ‘Mkazi wanzeru’ ameneyu amachita zinthu mogwirizana ndi mwamuna wakeyo polimbitsa banja lawo. Choncho amapitiriza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu.​—Miyambo 14:1.

10. (a) Kodi Mulungu anapereka udindo wotani kwa makolo? (b) Kodi mawu akuti “malangizo” amatanthauza chiyani, nanga makolo ayenera kulangiza bwanji ana awo? (Onaninso mawu am’munsi.)

10 Nawonso makolo ali ndi udindo umene Mulungu anawapatsa. Baibulo limati: “Inu abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma pitirizani kuwalera powapatsa malangizo komanso kuwaphunzitsa mogwirizana ndi zimene Yehova amanena.” (Aefeso 6:4) M’Baibulo, mawu akuti “malangizo” angatanthauze “kulera, kuphunzitsa ndiponso kulangiza.” Ana amafunika kulangizidwa. Amakula bwino akamapatsidwa malamulo komanso malangizo omveka bwino. Baibulo limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa kulangiza mwana ndi kumukonda. (Miyambo 13:24) Choncho ‘ndodo yolangira’ siyenera kukhala yochitira nkhanza mwana kapena kumuopsezera. a (Miyambo 22:15; 29:15) Makolo akamapereka chilango chokhwima, chankhanza ndiponso mopanda chikondi ndiye kuti akugwiritsa ntchito molakwika udindo wawo. Chilango choterocho chingakwiyitse mwana. (Akolose 3:21) Koma chilango choyenera chingathandize ana kudziwa kuti makolo awo amawakonda ndiponso amawafunira zabwino.

11. Kodi ana angatani kuti azigwiritsa ntchito bwino mphamvu zawo?

11 Nanga bwanji ana? Kodi angatani kuti azigwiritsa bwino mphamvu zawo? Lemba la Miyambo 20:29 limati: “Ulemerero wa anyamata ndi mphamvu zawo.” Kunena zoona, palibe njira yabwino kwambiri imene achinyamata angagwiritsire ntchito mphamvu zawo kuposa kutumikira “Mlengi” wathu Wamkulu. (Mlaliki 12:1) Achinyamata ayenera kukumbukira kuti zochita zawo zikhoza kusangalatsa kapena kukhumudwitsa makolo awo. (Miyambo 23:24, 25) Akamamvera makolo awo omwe ndi oopa Mulungu n’kumachita zoyenera, makolowo amasangalala. (Aefeso 6:1) Zimenezi ‘zimasangalatsanso Ambuye.’​—Akolose 3:20.

Mu Mpingo

12, 13. (a) Kodi akulu ayenera kumauona bwanji udindo wawo mumpingo? (b) N’chifukwa chiyani akulu ayenera kusamalira nkhosa mokoma mtima? Perekani chitsanzo.

12 Yehova anatipatsa oyang’anira kuti azitsogolera mumpingo wa Chikhristu. (Aheberi 13:17) Amuna oyenerera amenewa amafunika kugwiritsa ntchito udindo womwe Mulungu wawapatsa pothandiza nkhosa. Kodi oyang’anirawa ali ndi ufulu woti azilamulira abale ndi alongo awo? Ayi ndithu. Akulu amafunika kuti aziona moyenera udindo wawo mumpingo komanso azikhala odzichepetsa. (1 Petulo 5:2, 3) Baibulo limauza oyang’anira kuti: “Muwete mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweni.” (Machitidwe 20:28) Chimenechitu ndi chifukwa chachikulu chochitira zinthu mokoma mtima ndi aliyense mumpingo.

13 Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mnzanu wapamtima wakupemphani kuti mumusungire chinthu chinachake chamtengo wapatali. Mukudziwa kuti mnzanuyo anagula chinthucho modula kwambiri. Kodi simungachisunge mosamala kwambiri kuti chisawonongeke? Mofanana ndi zimenezi, Mulungu anapatsa akulu udindo wosamalira mpingo, womwe ndi chinthu chofunika kwambiri ndipo anthu amumpingowo amayerekezeredwa ndi nkhosa. (Yohane 21:16, 17) Yehova amakonda kwambiri nkhosa zake moti mpaka anazigula ndi magazi amtengo wapatali a Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Khristu. Palibenso mtengo wokwera kuposa pamenepa umene Yehova akanalipira kuti agule nkhosazi. Akulu odzichepetsa amakumbukira zimenezi ndipo amasamalira nkhosa za Yehova mwachikondi.

“Mphamvu ya Lilime”

14. Kodi lilime lili ndi mphamvu yotani?

14 Baibulo limati: “Imfa ndiponso moyo zili mumphamvu ya lilime.” (Miyambo 18:21) Lilime likhozadi kuwononga zinthu. Tonsefe tinakhumudwapo chifukwa choti munthu wina anatilankhula mawu opweteka. Komatu lilime lilinso ndi mphamvu yokonza zinthu. Lemba la Miyambo 12:18 limati: “Lilime la anthu anzeru limachiritsa.” Izitu ndi zoona chifukwa mawu abwino komanso olimbikitsa amakhala ngati mankhwala ndipo angathandize munthu kuti ayambe kumva bwino. Taganizirani zitsanzo izi.

15, 16. Kodi tingagwiritse ntchito lilime lathu m’njira ziti polimbikitsa ena?

15 Lemba la 1 Atesalonika 5:14 limati: “Muzilankhula molimbikitsa kwa anthu amene ali ndi nkhawa.” Zoonadi, ngakhalenso atumiki okhulupirika a Yehova nthawi zina amavutika ndi nkhawa. Ndiye kodi tingawathandize bwanji? Muziwayamikira mosapita m’mbali komanso moona mtima, zomwe zingawathandize kuti azidziwa kuti Yehova amawaona kuti ndi amtengo wapatali. Muziwalimbikitsa ndi malemba omwe amasonyeza kuti Yehova amadera nkhawa komanso kukonda anthu a “mtima wosweka” ndiponso “amene akudzimvera chisoni mumtima mwawo.” (Salimo 34:18) Tikamagwiritsa ntchito lilime lathu polimbikitsa ena, timasonyeza kuti tikutsanzira Mulungu wathu wachifundo, yemwe “amalimbikitsa anthu amene ali ndi nkhawa.”​—2 Akorinto 7:6.

16 Tingagwiritsenso ntchito lilime lathu polimbikitsa ena omwe akufunika kwambiri kulimbikitsidwa. Ngati Mkhristu mnzathu waferedwa, tikhoza kumulimbikitsa pomuuza mawu osonyeza kuti ifenso zatikhudza ndipo tikumudera nkhawa. Kodi pali m’bale kapena mlongo wachikulire amene akudziona kuti ndi wosafunika? Tikasankha kulankhula mawu abwino, tingamutsimikizire kuti ndi wofunika kwambiri ndiponso timamuyamikira. Kodi wina akudwala matenda okhalitsa? Mawu abwino amene tingamuuze pafoni, pomulembera kapena pamasom’pamaso angamulimbikitse kwambiri. Mlengi wathu amasangalala tikamalankhula mawu ‘abwino kuti alimbikitse ena.’​—Aefeso 4:29.

17. Kodi tingagwiritse ntchito lilime lathu m’njira yofunika iti pothandiza ena, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi?

17 Palibe njira ina yofunika kwambiri yogwiritsa ntchito mphamvu ya lilime lathu kuposa kuuza ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Lemba la Miyambo 3:27 limati: “Usalephere kuchitira zabwino anthu amene ukuyenera kuwachitira zabwinozo, ngati ungathe kuwathandiza.” Ndi udindo wathu kuuza ena uthenga wabwino wowathandiza kuti adzapulumuke. Si bwino kungosunga uthenga wofunika kulengezedwa mwamsangawu, womwe Yehova watipatsa mowolowa manja. (1 Akorinto 9:16, 22) Koma kodi Yehova amayembekezera kuti tizichita zambiri bwanji pa ntchito imeneyi?

Njira yabwino kwambiri yogwiritsa ntchito mphamvu zathu, ndi kuuza ena uthenga wabwino

Kutumikira Yehova ndi ‘Mphamvu Zathu Zonse’

18. Kodi Yehova amayembekezera kuti tizichita chiyani?

18 Chifukwa chakuti timakonda Yehova, timagwira nawo ntchito yolalikira ndi mtima wonse. Koma kodi Yehova amayembekezera kuti tizichita chiyani? Zimene amayembekezera, aliyense akhoza kukwanitsa kaya zinthu zili bwanji pa moyo wake. Baibulo limati: “Chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse ngati kuti mukuchitira Yehova, osati anthu.” (Akolose 3:23) Pofotokoza lamulo lalikulu kwambiri pa onse, Yesu anati: “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu onse ndi mphamvu zanu zonse.” (Maliko 12:30) Yehova amayembekezera kuti aliyense azimukonda ndiponso kum’tumikira ndi moyo wake wonse.

19, 20. (a) Popeza mawu akuti moyo amaphatikizapo mtima, maganizo ndi mphamvu, n’chifukwa chiyani zimenezi zinatchulidwanso pa Maliko 12:30? (b) Kodi kutumikira Yehova ndi moyo wathu wonse kumatanthauza chiyani?

19 Kodi kutumikira Mulungu ndi moyo wathu wonse kumatanthauza chiyani? Mawu akuti moyo akutanthauza munthu yense, kuphatikizapo mtima, maganizo ndi mphamvu zake. Popeza moyo ukuphatikizapo mtima, maganizo ndi mphamvu, n’chifukwa chiyani zinthu zimenezi zikutchulidwanso pa Maliko 12:30? Taganizirani chitsanzo ichi. Kale munthu ankatha kudzigulitsa, kapena kuti kugulitsa moyo wake, kuti akhale kapolo. Koma kapoloyo akanatha kusankha kuti asamatumikire mbuye wake ndi mtima wonse. Akanathanso kusankha kuti asamagwiritse ntchito mphamvu zake zonse kapena nzeru zake zonse kuti zinthu za mbuye wake ziziyenda bwino. (Akolose 3:22) Choncho n’zodziwikiratu kuti Yesu anatchula mbali zinazi pofuna kutsindika mfundo yoti tisamasiye dala kuchita zambiri potumikira Mulungu. Kutumikira Mulungu ndi moyo wathu wonse kumatanthauza kuchita zonse zomwe tingathe komanso kugwiritsa ntchito mphamvu zathu zonse pomutumikira.

20 Kodi kutumikira Mulungu ndi moyo wathu wonse kukutanthauza kuti tonse tiyenera kumachita zofanana? Ayi. Zimenezi sizingatheke, chifukwa mmene zinthu zilili pa moyo wathu zimasiyana komanso tili ndi maluso osiyana. Mwachitsanzo, wachinyamata amene ndi wamphamvu komanso sadwaladwala akhoza kumalalikira nthawi yaitali kusiyana ndi munthu amene mphamvu zake ndi zochepa chifukwa cha uchikulire. Munthu yemwe sali pa banja angathe kuchita zambiri kusiyana ndi munthu amene ali pa banja chifukwa amakhala ndi udindo wosamalira banjalo. Tiyenera kuthokoza kwambiri ngati tili ndi mphamvu komanso timatha kuchita zambiri mu utumiki. Komabe sitiyenera kumadziyerekezera ndi ena n’kumaganiza kuti sakuchita zonse zomwe angathe. (Aroma 14:10-12) M’malomwake, tizigwiritsa ntchito mphamvu zathu polimbikitsa anzathu.

21. Kodi njira yabwino komanso yofunika kwambiri imene tingagwiritsire ntchito mphamvu zathu ndi iti?

21 Yehova amatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yogwiritsa ntchito mphamvu moyenera. Ngakhale kuti siife angwiro, timafuna kumutsanzira mmene tingathere. Tingagwiritse ntchito bwino mphamvu zathu ngati timalemekeza anthu amene timawayang’anira kapena kuwalamulira. Kuwonjezera pamenepa, timafuna kuti tizigwira ndi mtima wonse ntchito yolalikira imene Yehova watipatsa yomwe imathandiza kuti anthu adzapulumuke. (Aroma 10:13, 14) Kumbukirani kuti Yehova amasangalala mukamachita zonse zomwe inuyo mungakwanitse pomutumikira. Kodi simukufunitsitsa kumachita zonse zimene mungathe potumikira Mulungu yemwe ndi womvetsa komanso wachikondi chonchi? Palibenso njira ina yabwino komanso yofunika kwambiri imene mungagwiritsire ntchito mphamvu zanu kuposa imeneyi.

a Mawu a Chiheberi omwe anawamasulira kuti “ndodo” ankatanthauza kamtengo kamene m’busa ankagwiritsa ntchito poweta nkhosa. (Salimo 23:4) Mofanana ndi zimenezi, mfundo yakuti makolo ayenera kugwiritsa ntchito “ndodo” polangiza ana awo ikusonyeza kuti ayenera kuchita zimenezi mwachikondi, osati mwankhanza.