Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 2

“Yehova Amakonda Chilungamo”

“Yehova Amakonda Chilungamo”

Masiku ano, padzikoli pakuchitika zinthu zopanda chilungamo zambiri ndipo anthu ambiri amanena kuti Mulungu ndi amene amachititsa zimenezi. Koma Baibulo limatiphunzitsa mfundo yolimbikitsa yakuti: “Yehova amakonda chilungamo.” (Salimo 37:28) M’chigawochi tiphunzira mmene iye wasonyezera kuti mawu amenewa ndi oona, zomwe zimapatsa anthu onse chiyembekezo.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 11

“Njira Zake Zonse Ndi Zolungama”

N’chifukwa chiyani chilungamo cha Mulungu ndi khalidwe losangalatsa?

MUTU 12

“Kodi Mulungu Alibe Chilungamo?”

Ngati Yehova amadana ndi zinthu zopanda chilungamo, n’chifukwa chiyani zachuluka kwambiri m’dzikoli?

MUTU 13

‘Malamulo a Yehova Ndi Angwiro’

Kodi malamulo angathandize bwanji anthu kuti azisonyeza chikondi?

MUTU 14

Yehova Anapereka “Dipo Kuti Awombole Anthu Ambiri”

Mfundo yosavuta koma yofunika kwambiri ingathandize kuti Mulungu akhale mnzanu.

MUTU 15

Yesu ‘Akukhazikitsa Chilungamo Padziko Lapansi’

Kodi Yesu analimbikitsa bwanji chilungamo? Kodi panopa akukhazikitsa bwanji chilungamo? Nanga m’tsogolo adzakhazikitsa bwanji chilungamo?

MUTU 16

‘Muzichita Chilungamo’ Poyenda ndi Mulungu

Chilungamo chimaphatikizapo mmene timaonera chabwino ndi choipa komanso mmene timachitira zinthu ndi ena.