Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

GAWO 3

“Ali Ndi Mtima Wanzeru”

“Ali Ndi Mtima Wanzeru”

Nzeru zenizeni ndi chimodzi mwa zinthu zamtengo wapatali zimene munthu ayenera kuyesetsa kuti akhale nazo. Nzeru zimenezi zimachokera kwa Yehova yekha. M’gawoli tikambirana mozama zokhudza nzeru zopanda malire za Yehova Mulungu, amene pofotokoza za iye, munthu wokhulupirika Yobu, ananena kuti: “Iye ali ndi mtima wanzeru.”​—Yobu 9:4.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 17

‘Nzeru za Mulungu N’zozama’

N’chifukwa chiyani nzeru za Mulungu zimaposa ngakhale zinthu zimene amazidziwa komanso kuzimvetsa?

MUTU 18

“Mawu a Mulungu” Amasonyeza Kuti Iye Ndi Wanzeru

N’chifukwa chiyani Mulungu anagwiritsa ntchito anthu kuti alembe maganizo ake m’buku, nanga ndi zinthu ziti zomwe zinaikidwa m’bukuli komanso zomwe sizinaikidwemo?

MUTU 19

‘Nzeru ya Mulungu Imaonekera mu Chinsinsi Chopatulika’

Kodi chinsinsi chopatulika chimene Mulungu wakhala akuchiulula pang’onopang’ono n’chiyani?

MUTU 20

“Ali ndi Mtima Wanzeru” Koma Ndi Wodzichepetsa

Kodi zingatheke bwanji kuti Ambuye Wamkulu Koposa wa chilengedwe chonse akhale wodzichepetsa?

MUTU 21

Yesu Amatisonyeza “Nzeru za Mulungu”

Yesu ankaphunzitsa mwaluso kwambiri moti nthawi ina alonda omwe anatumidwa kuti akamugwire anabwerera chimanjamanja.

MUTU 22

Kodi Mumagwiritsa Ntchito “Nzeru Yochokera Kumwamba” pa Moyo Wanu?

Baibulo limatchula mfundo 4 zomwe zingakuthandizeni kukhala ndi nzeru za Mulungu.