Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 18

“Mawu a Mulungu” Amasonyeza Kuti Iye Ndi Wanzeru

“Mawu a Mulungu” Amasonyeza Kuti Iye Ndi Wanzeru

1, 2. Kodi ndi “kalata” iti imene Yehova anatilembera, ndipo n’chifukwa chiyani?

 KODI mukukumbukira nthawi yomaliza imene munalandira kalata yochokera kwa munthu amene mumam’konda yemwe amakhala kutali? Timasangalala kwambiri tikalandira kalata yochokera kwa munthu wotereyu yokhala ndi mawu ochokera pansi pa mtima. Timasangalala kumva kuti ali bwanji, zimene zikumuchitikira ndiponso zimene akufuna kuchita. Kulankhulana m’njira imeneyi kumachititsa kuti anthu azikondana kwambiri ngakhale kuti akukhala motalikirana.

2 N’chifukwa chake timasangalala kwambiri kulandira uthenga wolembedwa wochokera kwa Mulungu amene timamukonda. Tinganene kuti Yehova anatilembera “kalata,” pamene anatipatsa Mawu ake, Baibulo. M’Mawu akewa amatiuza zokhudza iyeyo, zimene anachita, zimene akufuna kuchita komanso zina zambiri. Yehova anatipatsa Mawu ake chifukwa amafuna kuti tikhale anzake apamtima. Njira yolankhulira nafe imene Mulungu wathu wanzeru zonse anasankhayi, ndi yabwino kwambiri. Mmene Baibulo linalembedwera ndiponso zimene zili m’Baibulo, zimasonyeza kuti iye ndi wanzeru kwambiri.

N’chifukwa Chiyani Anachita Kulemba?

3. Kodi Yehova anagwiritsa ntchito njira iti popereka Chilamulo kwa Mose?

3 Ena angafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova sanagwiritse ntchito njira yochititsa chidwi kwambiri polankhula ndi anthu? Mwachitsanzo, bwanji sanalankhule nafe mwachindunji kuchokera kumwamba?’ Nthawi zina Yehova ankalankhuladi ndi anthu kuchokera kumwamba kudzera mwa angelo. Mwachitsanzo, anachita zimenezi pamene ankapereka Chilamulo kwa Aisiraeli. (Agalatiya 3:19) Mawu amene anachokera kumwambawo anali ochititsa mantha kwambiri moti Aisiraeli anapempha Yehova kuti asalankhule nawonso m’njira imeneyi, koma kudzera mwa Mose. (Ekisodo 20:18-20) Choncho Yehova analankhula ndi Mose ndipo anamuuza malamulo onse oposa 600 omwe anali m’Chilamulo.

4. Fotokozani chifukwa chake njira yongouzana pakamwa sikanakhala yodalirika popereka malamulo a Mulungu ku mibadwo yonse.

4 Koma kodi chikanachitika n’chiyani Chilamulocho chikanapanda kulembedwa? Kodi Mose akanatha kukumbukira mawu onse a m’Chilamulocho, chomwe chinali ndi mfundo zambirimbiri, n’kuwafotokozera Aisiraeli mosalakwitsa chilichonse? Nanga bwanji mibadwo yam’tsogolo? Kodi iwo akanangodalira zowauza ndi pakamwa? Imeneyo sikanakhala njira yodalirika yothandiza anthu kudziwa molondola malamulo a Mulungu. Taganizirani zomwe zingachitike ngati mutakhala ndi nkhani yoti mufotokozere anthu omwe ali pa mzere wautali. Mwafotokozera munthu woyambirira kuti nayenso afotokozere mnzake mpaka nkhaniyo ikafike kwa munthu wakumapeto. Zimene munthu womalizirayo angamve zingakhale zosiyana kwambiri ndi mmene nkhaniyo inalili poyamba. Koma Chilamulo cha Mulungu sichinakumane ndi vuto limeneli.

5, 6. Kodi Yehova anauza Mose kuti achite chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo ndi mphatso yamtengo wapatali?

5 Chifukwa cha nzeru zake, Yehova anasankha kuti mawu ake alembedwe. Anauza Mose kuti: “Ulembe mawuwa chifukwa ine ndikuchita pangano ndi iwe komanso Isiraeli mogwirizana ndi mawu amenewa.” (Ekisodo 34:27) Chimenechi chinali chaka cha 1513 B.C.E. ndipo ndi chaka chimene Baibulo linayamba kulembedwa. Kwa zaka 1,610 zotsatira, Yehova “ankalankhula . . . m’njira zosiyanasiyana” kwa anthu pafupifupi 40 amene kenako analemba Baibulo. (Aheberi 1:1) Pa nthawi yomweyinso alembi odzipereka ankakopera zolembedwazo mosamala ndiponso molondola kwambiri kuti uthenga wa m’Baibulo usungike.​—Ezara 7:6; Salimo 45:1.

6 Kunena zoona, Baibulo ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova. Kodi munalandirapo kalata yomwe inakusangalatsani kwambiri mwina chifukwa choti inakulimbikitsani moti munaisunga n’kumaiwerenga mobwerezabwereza? Ndi mmenenso zilili ndi “kalata” imene Yehova anatilemberayi. Chifukwa chakuti Yehova analemba mawu ake, timawawerenga nthawi zonse n’kumaganizira mozama zomwe tawerengazo. (Salimo 1:2) ‘Malembawa amatilimbikitsa’ nthawi iliyonse imene tikufunika kulimbikitsidwa.​—Aroma 15:4.

N’chifukwa Chiyani Anagwiritsa Ntchito Anthu?

7. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ndi wanzeru pogwiritsa ntchito anthu kuti alembe Mawu ake?

7 Popeza ndi wanzeru, Yehova anagwiritsa ntchito anthu kuti alembe Mawu ake. Taganizirani izi: Yehova akanagwiritsa ntchito angelo kuti alembe Baibulo, kodi bwenzi likutifika pamtima ngati mmene zilili panopa? Angelo akanafotokoza zokhudza Yehova m’njira yapamwamba kwambiri ngati mmene iwowo amamudziwira. Akanafotokozanso zimene amachita posonyeza kudzipereka kwa iye ndiponso zokhudza anthu ena okhulupirika. Koma kodi zomwe angelo akanafotokozazo tikanatha kuzimvetsa? Pajatu angelo ndi angwiro, amadziwa zambiri komanso ndi amphamvu kuposa ifeyo.​—Aheberi 2:6, 7.

8. Kodi Yehova analola kuti anthu amene analemba Baibulo achite chiyani? (Onaninso mawu am’munsi.)

8 Pogwiritsa ntchito anthu kuti alembe Mawu ake, Yehova anatipatsa buku ‘louziridwa ndi Mulungu’ koma lofotokoza zinthu zowafika pamtima anthu. Buku lotereli ndi limenedi timafunikira. (2 Timoteyo 3:16) Koma kodi anachita bwanji zimenezi? Zikuoneka kuti nthawi zambiri, ankalola anthu amene ankalembawo kugwiritsa ntchito luso lawo loganiza posankha “mawu osangalatsa” ndiponso “olondola a choonadi.” (Mlaliki 12:10, 11) N’chifukwa chake nkhani za m’Baibulo zinalembedwa mosiyanasiyana ndipo zimasonyeza makhalidwe a wolembayo komanso mmene zinthu zinalili pa moyo wake. a Komabe anthu amenewa “analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” (2 Petulo 1:21) Choncho zimene analembazo ndi “mawu a Mulungu.”​—1 Atesalonika 2:13.

“Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu”

9, 10. N’chifukwa chiyani uthenga wa m’Baibulo umatikhudza mtima kwambiri?

9 Baibulo ndi losangalatsa komanso uthenga wake umatifika pamtima chifukwa choti linalembedwa ndi anthu. Olembawo anali anthu ngati ife tomwe. Popeza sanali angwiro, ankakumana ndi mayesero komanso mavuto omwe nafenso timakumana nawo. Nthawi zina mzimu wa Yehova unkawatsogolera kuti alembe mmene akumvera ndiponso mavuto amene akukumana nawo. (2 Akorinto 12:7-10) Choncho ankalemba mosonyeza kuti nkhaniyo ikuchitikira iwowo ndipo palibe mngelo yemwe akanachita zimenezi.

10 Mwachitsanzo, taganizirani za Davide mfumu ya Isiraeli. Atachita machimo akuluakulu, analemba nyimbo yofotokoza mmene ankamvera ndipo anapempha Mulungu kuti amukhululukire. Iye analemba kuti: “Mundisambitse bwinobwino n’kuchotsa cholakwa changa, ndiyeretseni ku tchimo langa. Chifukwa zolakwa zanga ndikuzidziwa bwino, ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse. Taonani! Ndinabadwa ndili wochimwa, ndipo ndine wochimwa kuchokera pamene mayi anga anatenga pakati panga. Musandichotse pamaso panu n’kunditaya. Ndipo musandichotsere mzimu wanu woyera. Nsembe zimene Mulungu amasangalala nazo ndi kudzimvera chisoni mumtima. Inu Mulungu, simudzakana mtima wosweka ndi wophwanyika.” (Salimo 51:2, 3, 5, 11, 17) Tikamawerenga zimenezi timachita kudziwiratu kuti Davide ankadzimvera chisoni kwambiri. Munthu yemwe si wangwiro yekha ndi amene akananena mawu ochokera pansi pa mtimawa.

N’chifukwa Chiyani Limanena za Anthu?

11. Kodi m’Baibulo muli nkhani zotani zomwe zinalembedwa “kuti zitilangize”?

11 Palinso chinthu china chimene chimapangitsa Baibulo kukhala losangalatsa. Muli nkhani zambiri zomwe zimanena za anthu enieni, amene ankatumikira Mulungu komanso omwe sankamutumikira. Timawerenga zokhudza mavuto amene anakumana nawo ndiponso zinthu zosangalatsa zomwe zinawachitikira. Timaonanso zotsatira za zimene anasankha pa moyo wawo. Nkhanizi zinalembedwa “kuti zitilangize.” (Aroma 15:4) Pogwiritsa ntchito zitsanzo za anthu amenewa, Yehova amatiphunzitsa motifika pamtima. Taonani zitsanzo izi.

12. Kodi nkhani za m’Baibulo zonena za anthu osakhulupirika zimatithandiza bwanji?

12 Baibulo limatiuza za anthu osakhulupirika ndiponso oipa komanso zomwe zinawachitikira. Tikamawerenga nkhanizi, timaona mmene munthu amasonyezera makhalidwe oipa, choncho timamvetsa mosavuta. Mwachitsanzo, Baibulo likanatha kungofotokoza kuti si bwino kukhala wosakhulupirika kwa mnzathu. Koma kodi mumamva bwanji mukamawerenga mmene Yudasi anasonyezera kusakhulupirika popereka Yesu? (Mateyu 26:14-16, 46-50; 27:3-10) Nkhani ngati zimenezi zimatikhudza mtima kwambiri ndipo zimatithandiza kuzindikira makhalidwe oipa n’kumawapewa.

13. Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kuti timvetse zokhudza makhalidwe abwino n’kumawasonyeza?

13 Baibulo limafotokozanso za atumiki a Mulungu ambiri okhulupirika. Timawerenga zokhudza kudzipereka ndiponso kukhulupirika kwawo. Timaona zitsanzo za anthu omwe anasonyeza makhalidwe amene timafunika kukhala nawo kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Mwachitsanzo, taganizirani za chikhulupiriro. Baibulo limafotokoza tanthauzo la chikhulupiriro ndiponso kuti n’chofunika kwambiri kuti tizisangalatsa Mulungu. (Aheberi 11:1, 6) Koma m’Baibulo mulinso zitsanzo za anthu amene anasonyeza chikhulupiriro. Taganizirani chikhulupiriro chimene Abulahamu anasonyeza pamene ankafuna kupereka nsembe Isaki. (Genesis, chaputala 22; Aheberi 11:17-19) Nkhani ngati zimenezi zimatithandiza kumvetsa bwino tanthauzo la “chikhulupiriro.” Choncho sikuti Yehova amangotiuza kuti tikhale ndi makhalidwe abwino, koma amatipatsanso zitsanzo za anthu omwe anasonyeza makhalidwewa. Zimenezi zimasonyeza kuti iye ndi wanzeru kwambiri.

14, 15. Kodi Baibulo limatiuza chiyani za mayi wina amene anafika pakachisi, ndipo nkhani imeneyi imatiphunzitsa chiyani za Yehova?

14 Nkhani zokhudza anthu ena zimene zili m’Baibulo nthawi zambiri zimatithandiza kuti timudziwe bwino Yehova. Mwachitsanzo, taganizirani za nkhani yokhudza mayi wina yemwe Yesu anamuona pakachisi. Yesu anakhala pansi pafupi ndi mosungiramo zopereka ndipo ankaona anthu akuponya zopereka zawo. Pankafika anthu ambiri olemera n’kumapereka kuchokera ‘pa zochuluka zimene anali nazo.’ Koma Yesu anayamba kuyang’anitsitsa mkazi wina wamasiye yemwe analinso wosauka. Mayiyu anapereka “timakobidi tiwiri tating’ono, tochepa mphamvu kwambiri.” b Iye anali ndi ndalama zokhazi basi. Zimene Yesu ananena zinasonyeza mmene Yehova ankamuonera mayiyo. Iye anati: “Mkazi wamasiye wosaukayu waponya zochuluka kuposa ena onse amene aponya ndalama moponyera zoperekamo.” Mogwirizana ndi mawu amenewa, mkaziyu anaponya zambiri kuposa kuphatikiza pamodzi zimene ena onse anaponya.​—Maliko 12:41-44; Luka 21:1-4; Yohane 8:28.

15 Kodi si zolimbikitsa kuti pa anthu onse amene anabwera kukachisi tsiku limenelo, mkazi wamasiyeyu ndi amene Yesu anachita naye chidwi komanso anatchulidwa m’Baibulo? Chitsanzo chimenechi chimatiphunzitsa kuti Yehova ndi Mulungu amene amayamikira. Amasangalala ndi zimene timamupatsa popanda kuziyerekezera ndi zochuluka zimene ena angathe kupereka. Apatu Yehova anagwiritsa ntchito njira yabwino kwambiri yotiphunzitsira mfundo ya choonadi yosangalatsayi.

Zimene M’Baibulo Mulibe

16, 17. Kodi Yehova anasonyezanso bwanji kuti ndi wanzeru tikaganizira zimene anasankha kuti zisalembedwe m’Mawu ake?

16 Mukamalemba kalata yopita kwa munthu amene mumamukonda, n’zosatheka kulembamo mfundo zonse zimene muli nazo. Choncho mumasankha mwanzeru zoti mulembe. Nayenso Yehova anasankha zochitika komanso anthu oti nkhani zawo zilembedwe m’Mawu ake. Koma sikuti Baibulo limafotokoza mfundo zonse zokhudza nkhani zimenezi. (Yohane 21:25) Mwachitsanzo, Baibulo likamanena zokhudza chiweruzo chimene Mulungu anapereka, zimene limafotokoza sizingayankhe funso lililonse lomwe tingakhale nalo. Pamene Yehova anasankha kuti zinthu zina zisalembedwe m’Mawu ake, anasonyezanso kuti ndi wanzeru. N’chifukwa chiyani tikutero?

17 Baibulo linalembedwa mwa njira yoti lizitithandiza kudziwa kuti ndife munthu wotani. Lemba la Aheberi 4:12 limati: “Mawu [kapena kuti uthenga] a Mulungu ndi amoyo komanso amphamvu, ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse. Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu . . . amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.” Uthenga wa m’Baibulo umatifika pamtima n’kutithandiza kudziwa zimene timaganiza komanso zolinga zathu pochita zinthu. Anthu amene amawerenga Baibulo pongofuna kulipezera zifukwa, nthawi zambiri amakhumudwa chifukwa choti silinafotokoze zambiri pa nkhani inayake. Mwinanso angamakayikire ngati Yehova alidi wachikondi, wanzeru komanso wachilungamo.

18, 19. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kukhumudwa ngati nkhani ina ya m’Baibulo yachititsa kuti tikhale ndi mafunso amene sitingapeze mayankho ake nthawi yomweyo? (b) Kodi timafunika kuchita chiyani kuti timvetse Mawu a Mulungu, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti umenewu ndi umboni wakuti Yehova ndi wanzeru kwambiri?

18 Koma mosiyana ndi zimenezi, tikamaphunzira Baibulo mosamala kwambiri ndiponso tili ndi zolinga zabwino, timatha kumudziwa bwino Yehova mogwirizana ndi zimene Baibulo lonse limanena zokhudza iyeyo. Choncho sitikhumudwa ngati nkhani ina yachititsa kuti tikhale ndi mafunso amene sitingapeze mayankho ake nthawi yomweyo. Mwachitsanzo, ngati tikusonkhanitsa pamodzi mapisi a chithunzi chachikulu kuti tipangenso chithunzicho, mwina poyamba sitingapeze pisi ina kapenanso sitingadziwe kuti kapisi kena tikaike pati. Komatu, tikhoza kukhala kuti tasonkhanitsa mapisi okwanira amene angatithandize kudziwa mmene chithunzi chonsecho chimaonekera. Mofanana ndi zimenezi, tikamaphunzira Baibulo, pang’ono ndi pang’ono timayamba kudziwa kuti Yehova ndi wotani ngakhale kuti pangakhale zina zomwe sitinazidziwe. Ngakhale kuti poyamba sitingamvetse nkhani inayake kapenanso kuona kuti ikugwirizana bwanji ndi makhalidwe a Mulungu, zinthu zokhudza Yehova zimene taphunzira kale m’Baibulo zatithandiza kuona kuti nthawi zonse iye amachita zinthu mwachikondi komanso mwachilungamo.

19 Choncho kuti timvetse Mawu a Mulungu, tiyenera kuwawerenga ndi kuwaphunzira tili ndi maganizo oyenera komanso mtima wofuna kuphunzira zinthu. Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova ndi wanzeru kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Anthu anzeru akhoza kulemba mabuku amene “anthu anzeru ndi ozindikira” okha ndi amene angawamvetse. Koma Yehova yekha, mwanzeru zake, ndi amene angathe kulemba buku limene angalimvetse ndi anthu a mitima yabwino okha.​—Mateyu 11:25.

Buku la “Nzeru Zopindulitsa”

20. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova yekha ndi amene angatiuze zoyenera kuchita kuti tikhale ndi moyo wabwino kwambiri, nanga m’Baibulo muli chiyani chimene chingatithandize?

20 M’Mawu ake, Yehova amatiuza zoyenera kuchita kuti tikhale ndi moyo wabwino kwambiri. Popeza ndi Mlengi wathu, amadziwa bwino zimene timafunikira kuposa mmene ifeyo timadziwira. Munthu aliyense amafuna kukondedwa, kukhala wosangalala, kukhala ndi banja labwino komanso kukhala ndi anzake apamtima. Ndipo zimenezi sizinasinthe kuchokera pamene Baibulo linalembedwa. M’Baibulo muli “nzeru zopindulitsa” zomwe zingatithandize kukhala ndi moyo wabwino. (Miyambo 2:7) Gawo lililonse la bukuli lili ndi mutu umene ukusonyeza mmene tingagwiritsire ntchito malangizo a nzeru a m’Baibulo. Koma tiyeni tione chitsanzo chimodzi.

21-23. Kodi ndi malangizo anzeru ati amene angatithandize kuti tisamapitirize kukwiyira ena komanso kuwasungira chakukhosi?

21 Kodi munaonapo kuti anthu amene amasunga chakukhosi komanso amene amapitirizabe kukhala okhumudwa nthawi zambiri amadzivulaza okha? Tikamapitiriza kukwiyira munthu, zimakhala ngati tanyamula chimtolo cholemera. Maganizo athu onse amakhala pa zimenezo ndipo timasowa mtendere komanso sitikhala osangalala. Asayansi anapeza kuti munthu yemwe amapitiriza kukwiya akhoza kudwala matenda amtima komanso ena okhalitsa. Kalekale kwambiri asayansi asanatulukire zimenezi, Baibulo linapereka malangizo anzeru akuti: “Usapse mtima ndipo uzipewa kukwiya.” (Salimo 37:8) Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?

22 Mawu a Mulungu amapereka malangizo anzeru awa: “Kuzindikira kumachititsa kuti munthu abweze mkwiyo wake, ndipo kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa kukhala wokongola.” (Miyambo 19:11) Kuzindikira ndi luso lotha kudziwa mfundo zina osangoti zokhazo zimene zikuonekeratu. Munthu wozindikira amathanso kumvetsa chifukwa chake mnzake analankhula kapena kuchita zinazake. Tikayesetsa kumvetsa zolinga za munthu, mmene akumvera komanso mmene zinthu ziliri pa moyo wake, zingatithandize kuti tisamuganizire zoipa kapena kumukwiyira.

23 Baibulo limatipatsanso malangizo akuti: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse.” (Akolose 3:13) Mawu akuti “pitirizani kulolerana” akusonyeza kuti tiyenera kukhala oleza mtima n’kumayesetsa kuti tisamakhumudwe ngakhale kuti anthu ena ali ndi makhalidwe enaake omwe satisangalatsa. Zimenezi zingatithandize kuti tizipitirizabe kuchita nawo zinthu m’malo mowakwiyira. Mawu akuti “kukhululukirana” angatanthauzenso kuti sitiyenera kupitiriza kukwiyira munthu. Mulungu wathu wanzeru amadziwa kuti timafunika kukhululukira ena pakakhala chifukwa chomveka chowakhululukira. Sikuti zimenezi zimangothandiza iwowo, koma zimathandizanso ifeyo kuti tikhale ndi mtendere wamumtima. (Luka 17:3, 4) Zonsezi zikusonyeza kuti m’Mawu a Mulungu muli nzeru zothandiza kwambiri.

24. Kodi chimachitika n’chiyani tikamatsatira nzeru za Mulungu pa moyo wathu?

24 Chifukwa chakuti amatikonda kwambiri, Yehova anakonza zoti azilankhula nafe. Anasankha njira yabwino kwambiri yochitira zimenezi yomwe ndi kutilembera “kalata” pogwiritsa ntchito anthu omwe ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera. M’kalata imeneyi timapezamo nzeru za Yehova ndipo nzeruzi ndi “zodalirika kwambiri.” (Salimo 93:5) Tikamazitsatira pa moyo wathu komanso kuuzako ena, timakhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu wathu wanzeru zonse. M’mutu wotsatira, tidzakambirana chitsanzo china chosonyeza kuti Yehova ali ndi nzeru zotha kuoneratu zam’tsogolo ndiponso kukwaniritsa zimene akufuna.

a Mwachitsanzo, Davide yemwe anali m’busa, anagwiritsa ntchito zitsanzo za zimene zimachitika ku ubusa. (Salimo 23) Mateyu, yemwe poyamba anali wokhometsa msonkho, nthawi zambiri ankatchula manambala ndiponso kuchuluka kwa ndalama. (Mateyu 17:27; 26:15; 27:3) Luka, yemwe anali dokotala, anagwiritsa ntchito mawu osonyeza kuti ankadziwa zachipatala.​—Luka 4:38; 14:2; 16:20.

b Ndalama zimenezi zinali timalepitoni, ndalama ya Chiyuda yaing’ono kwambiri imene ankagwiritsa ntchito pa nthawiyo. Munthu ankangofunika kugwira ntchito 15 minitsi kuti alandire malepitoni awiri. Tindalama tiwiri timeneti tinali tosakwanira kugula ngakhale mpheta imodzi yomwe inali mbalame yotchipa kwambiri imene anthu osauka ankadya.