Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 27

“Ubwino Wake Ndi Waukulu Kwambiri!”

“Ubwino Wake Ndi Waukulu Kwambiri!”

1, 2. Kodi ndi ndani amene amapindula chifukwa choti Yehova ndi wabwino, nanga Baibulo limafotokoza zotani zokhudza ubwino wa Yehova?

 MUNTHU wina ndi anzake apamtima akudyera limodzi chakudya panja pomwe dzuwa likulowa. Anthuwa akucheza komanso kuseka pamene akuona kukongola kwa dzuwalo. Kudera lina lakutali, mlimi akuyang’ana munda wake mosangalala chifukwa mvula yayamba kugwa, pambuyo poti mbewu zake zinafota ndi dzuwa. Kudera linanso, mwamuna ndi mkazi wake akusangalala kuona mwana wawo akuyamba kuyenda.

2 Kaya anthuwa akudziwa kapena ayi, onsewa akusangalala ndi zinthu zimenezi chifukwa choti Yehova ndi wabwino. Anthu ambiri opemphera amakonda kunena kuti “Mulungu ndi wabwino.” Koma Baibulo limanena zoposa pamenepa. Limati: “Ubwino wake ndi waukulu kwambiri.” (Zekariya 9:17) Koma zikuoneka kuti masiku ano pali anthu ochepa okha omwe amadziwa zimene mawuwa amatanthauza. Ndiye kodi mfundo yoti Yehova ndi wabwino imatanthauza chiyani, nanga tonsefe timapindula bwanji ndi khalidwe la Mulungu limeneli?

Khalidwe Lomwe Limasonyeza Kuti Yehova Ndi Wachikondi

3, 4. Kodi ubwino n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti mfundo yoti Yehova ndi wabwino imasonyeza kuti iye ndi wachikondi?

3 M’zilankhulo zambiri masiku ano, mawu akuti “ubwino” amangowagwiritsa ntchito pa zilizonse. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti ubwino ndi khalidwe palokha. Nthawi zambiri limatanthauza kukhala ndi makhalidwe abwino kwambiri. Choncho tikhoza kunena kuti Yehova ndi wabwino kwambiri pa chilichonse. Mphamvu zake, chilungamo chake, nzeru zake ndiponso makhalidwe ake ena onse ndi abwino kwambiri. Komabe, tinganene kuti mfundo yoti Yehova ndi wabwino imasonyeza kuti iye ndi wachikondi. N’chifukwa chiyani tikutero?

4 Munthu yemwe ndi wabwino amachitira zinthu zabwino anthu ena. Mtumwi Paulo anasonyeza kuti anthu amasangalala kwambiri ndi munthu wabwino kuposa wolungama. (Aroma 5:7) Munthu wolungama amatsatira malamulo mokhulupirika, koma munthu wabwino amachita zoposa pamenepo. Amayamba ndi iyeyo kuchitapo kanthu ndipo amafufuza njira zothandizira ena. Monga tionere, Yehova ndi wabwino m’njira imeneyi. N’zodziwikiratu kuti iye amasonyeza khalidwe la ubwino chifukwa cha chikondi chake chopanda malire.

5-7. N’chifukwa chiyani Yesu anakana kutchulidwa kuti “Mphunzitsi Wabwino,” ndipo kodi pamenepa anaphunzitsa mfundo ya choonadi yofunika iti?

5 Yehova ndi wabwino kuposa aliyense. Kutatsala nthawi yochepa kuti Yesu aphedwe, munthu wina anapita kukamufunsa funso. Munthuyo anatchula Yesu kuti “Mphunzitsi Wabwino.” Yesu anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino? Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.” (Maliko 10:17, 18) Mwina yankho limeneli lingakudabwitseni kwambiri. N’chifukwa chiyani Yesu anamukonza munthuyo? Kodi m’mesa Yesu analidi “Mphunzitsi Wabwino”?

6 N’zodziwikiratu kuti munthuyo anatchula Yesu kuti “Mphunzitsi Wabwino” popereka ulemu wabodza. Modzichepetsa, Yesu anapereka ulemerero umenewu kwa Atate ake akumwamba, omwe ndi abwino kwambiri kuposa aliyense. (Miyambo 11:2) Koma pamenepa Yesu anaphunzitsanso mfundo yofunika kwambiri. Popeza ndi Wolamulira Wamkulu Kwambiri, Yehova yekha ndi amene ali ndi ufulu wotiuza zinthu zomwe ndi zabwino kapena zoipa. Pamene Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu n’kudya zipatso za mtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa, anasonyeza kuti ankafuna kukhala ndi ufulu umenewu. Koma mosiyana ndi iwowo, modzichepetsa Yesu anavomereza kuti Atate ake okha ndi amene ali ndi ufulu wouza anthu kuti ichi n’chabwino, ichi n’choipa.

7 Ndiponso, Yesu ankadziwa kuti chinthu chilichonse chabwino chimachokera kwa Yehova. Ndi iyeyo amene amapereka “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” (Yakobo 1:17) Tiyeni tione mmene Yehova amasonyezera kuti ndi wabwino pokhala wowolowa manja.

Umboni Woti Yehova Ndi Wabwino Kwambiri

8. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wabwino kwa anthu onse?

8 Munthu aliyense amene anakhalako ndi moyo anapindulako ndi ubwino wa Yehova. Lemba la Salimo 145:9 limati: “Yehova ndi wabwino kwa aliyense.” Kodi zitsanzo zina zosonyeza kuti iye ndi wabwino kwa anthu onse ndi ziti? Baibulo limati: “Iye sanangokhala wopanda umboni wakuti anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chisangalalo.” (Machitidwe 14:17) Kodi munadyapo chakudya chokoma chomwe munasangalala nacho kwambiri? Zikanakhala kuti Yehova si wabwino ndipo sanakonze zoti padzikoli pazigwa mvula komanso pazikhala ‘nyengo zimene zokolola zimakhala zambiri,’ bwenzi kulibe zakudya. Yehova amachitira aliyense zabwinozi, osati anthu amene amamukonda okha. Yesu anati: “Iye amawalitsira dzuwa lake anthu abwino ndi oipa omwe, ndipo amagwetsera mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.”​—Mateyu 5:45.

9. Kodi maapozi amasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wabwino?

9 Chifukwa chakuti nthawi zonse timakhala ndi dzuwa, mvula ndiponso nyengo ya zipatso, ambiri saona kuti m’pofunika kumayamikira zinthu zimene Yehova amatipatsa mosaumira. Mwachitsanzo, taganizirani za maapozi. Zipatso zimenezi zimapezeka kwambiri m’madera otentha padzikoli. Komatu ndi zipatso zokongola, zokoma komanso zimakhala ndi madzi ambiri ndiponso zinthu zofunika m’thupi. Kodi mukudziwa kuti padzikoli pali mitundu pafupifupi 7,500 ya maapozi owoneka mosiyanasiyana? Ena ndi ofiira, ena agolide, ayelo ndiponso agirini. Maapoziwa amasiyananso kukula kwake, ena amakhala akuluakulu pomwe ena amakhala ang’onoang’ono. Mukatenga kanjere ka apozi m’manja mwanu, zimangokhala ngati palibe chimene mwagwira. Koma kanjereka kakamera, kamakula n’kukhala umodzi wa mitengo yosangalatsa kwambiri. (Nyimbo ya Solomo 2:3) Chaka chilichonse mitengo ya maapozi imachita maluwa okongola ndipo kenako imabereka zipatso. Pa chaka, mtengo wa maapozi umabereka zipatso zokwana makatoni 20, katoni iliyonse yolemera makilogalamu 19 ndipo umachita zimenezi kwa zaka 75.

Yehova ‘amakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri’

Kanjere kakang’ono aka kamamera n’kukhala mtengo umene zipatsa zake anthu amadya komanso kusangalala nazo kwa zaka zambiri

10, 11. Kodi mmene thupi lathu linapangidwira zimasonyeza bwanji kuti Mulungu ndi wabwino?

10 Chifukwa cha ubwino wake wosatha, Yehova anatipatsa thupi ‘lopangidwa modabwitsa,’ limene limatha kuzindikira zomwe Mulungu analenga n’kumasangalala nazo. (Salimo 139:14) Taganiziraninso zitsanzo zomwe tafotokoza m’ndime yoyamba zija. Mukanakhala kuti inuyo munalipo, kodi ndi zinthu ziti zomwe mukanasangalala mutaziona? Kodi ndi kumwetulira kwa mwana yemwe akusangalala, mvula ikugwa m’minda, kapena mitundu yosiyanasiyana imene dzuwa limaonetsa likamalowa? Diso la munthu linapangidwa kuti lizitha kusiyanitsa mitundu ya zinthu mahandiredi masauzande, mwinanso mpaka mamiliyoni. Ndiponso makutu athu amatha kuzindikira mawu abwino amene tikumva kuchokera kwa munthu yemwe timam’konda, kuseka kwa mwana yemwe wasangalala kapenanso kaphokoso kamphepo yomwe ikudutsa m’mitengo. Kodi n’chifukwa chiyani timatha kuona komanso kumva zinthu zimenezi? Baibulo limati: “Khutu lakumva ndiponso diso loona, zonsezi anazipanga ndi Yehova.” (Miyambo 20:12) Koma pali zinthu zinanso zomwe timachita zomwe zimatithandiza kuti tizisangalala ndi moyo.

11 Umboni wina woti Yehova ndi wabwino ndi woti timatha kumva fungo. Mphuno ya munthu ikhoza kusiyanitsa mitundu yosiyanasiyana ya fungo yofika mpaka 1 thililiyoni. Mwachitsanzo, taganizirani za fungo lomwe mumamva wina akamaphika chakudya chomwe mumachikonda, la maluwa, la masamba ouma omwe athothoka komanso la utsi umene ukuchokera pamoto wonyeka bwino. Thupi lathu limazindikiranso kuti lakhudza kapena lakhudzidwa ndi chinthu chinachake. Mwachitsanzo, timamva kamphepo kayaziyazi kakatiwomba kumaso, timamva bwino wokondedwa wathu akatihaga komanso tikagwira chipatso chosalala. Mukamadya chipatsocho mumamva kukoma kwambiri ndipo kukomako kumamveka mosiyanasiyana m’kamwamu. N’zosachita kufunsa kuti tili ndi zifukwa zomveka zotamandira Yehova kuti: “Ubwino wanu ndi wochuluka kwambiri! Ubwino umenewu mwasungira anthu amene amakuopani.” (Salimo 31:19) Koma kodi zikutanthauza chiyani tikamati Yehova wasungira ubwino anthu amene amamuopa?

Zinthu Zabwino Zomwe Zidzatithandize Mpaka Kalekale

12. Kodi ndi zinthu ziti zimene Yehova amatipatsa zomwe ndi zofunika kwambiri, ndipo n’chifukwa chiyani?

12 Yesu anati: “Malemba amati: ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu alionse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.’” (Mateyu 4:4) Zoonadi, zinthu zauzimu zomwe Yehova amatipatsa zingatithandize kwambiri kuposa zakuthupi, chifukwa zauzimuzi zingatithandize kudzapeza moyo wosatha. M’Mutu 8 wa bukuli, tinaona kuti m’masiku otsiriza ano Yehova akugwiritsa ntchito mphamvu zake zobwezeretsa zinthu, pokhazikitsa paradaiso wauzimu. Mbali yaikulu ya paradaisoyu, ndi chakudya chauzimu chochuluka.

13, 14. (a) Kodi mneneri Ezekieli anaona chiyani m’masomphenya, nanga zimenezo zimatanthauza chiyani? (b) Kodi ndi zinthu ziti zothandiza kudzapeza moyo zimene Yehova akupatsa anthu ake okhulupirika?

13 Mu ulosi wina wofunika kwambiri wonena za kubwezeretsa zinthu, mneneri Ezekieli anaona masomphenya a kachisi waulemerero yemwe anabwezeretsedwa. Madzi ankayenda kuchokera kukachisiyo ndipo ankawonjezereka mpaka anakhala mtsinje. Kulikonse kumene mtsinjewo unkapita, unkabweretsa madalitso. M’mbali mwake munamera mitengo yomwe inkabereka zipatso komanso inkachiritsa anthu. Mtsinjewo unachititsanso Nyanja Yakufa, imene inali yamchere komanso munalibe zamoyo, kuti ikhale ndi zamoyo. (Ezekieli 47:1-12) Koma kodi zonsezi zinkatanthauza chiyani?

14 Masomphenya okhudza kachisiwa ankatanthauza kuti Yehova adzabwezeretsa kulambira koona ndipo anthu azidzamulambiranso mogwirizana ndi mfundo zake zolungama. Ankatanthauzanso kuti mofanana ndi mtsinje wa m’masomphenya uja, zinthu zothandiza kudzapeza moyo wosatha zimene Mulungu adzapatse anthu ake zizidzawonjezereka. Yehova wakhala akuchita zimenezi kungoyambira pamene kulambira koona kunabwezeretsedwa mu 1919. Kodi akuzichita bwanji? Pogwiritsa ntchito Baibulo, mabuku othandiza kumvetsa Baibulo komanso misonkhano ya mpingo ndi ikuluikulu, anthu mamiliyoni ambiri aphunzira choonadi. Yehova amagwiritsa ntchito zinthu zimenezi pophunzitsa anthu mfundo zofunika kwambiri, makamaka yokhudza nsembe ya dipo ya Khristu. Nsembeyi imathandiza anthu amene amakonda komanso kuopa Mulungu kuti Mulunguyo aziwaona kuti ndi olungama ndiponso adzapeze moyo wosatha. a Choncho m’masiku onse otsiriza ano, pamene dzikoli likuvutika ndi njala yauzimu, anthu a Yehova akhala akusangalala ndi phwando lauzimu.​—Yesaya 65:13.

15. Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, kodi Yehova adzasonyeza bwanji ubwino wake kwa anthu okhulupirika?

15 Koma mtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenya sudzasiya kuyenda dziko loipali likadzawonongedwa. Udzapitiriza kuyenda komanso kukula mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu. Pa nthawi imeneyi, kudzera mu Ufumu wa Mesiya, Yehova adzagwiritsa ntchito nsembe ya Yesu pothandiza anthu okhulupirika mpaka anthuwo atakhala angwiro. Zikadzatero tidzasangalalatu kwambiri ndi ubwino wa Yehova.

Mbali Zinanso za Ubwino wa Yehova

16. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yehova alinso ndi makhalidwe ena abwino, nanga ena mwa makhalidwewa ndi ati?

16 Kuwonjezera pa kukhala wowolowa manja, Yehova amasonyeza kuti ndi wabwino m’njira zinanso. Iye anauza Mose kuti: “Ineyo ndidzakuonetsa ubwino wanga wonse, ndipo ndidzalengeza dzina langa lakuti Yehova kwa iwe.” Kenako nkhaniyi imati: “Yehova anadutsa pamaso pa Mose akulengeza kuti: ‘Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka komanso choonadi.’” (Ekisodo 33:19; 34:6, mawu a m’munsi) Choncho popeza Yehova ndi wabwino, alinso ndi makhalidwe ena abwino. Tiyeni tikambirane awiri okha.

17. Kodi munthu wachisomo amakhala wotani, nanga Yehova amasonyeza bwanji khalidweli kwa anthu omwe si angwirofe?

17 “Wachisomo.” Khalidwe limeneli, lomwe limamasuliridwanso kuti “wokoma mtima,” limatiuza zambiri za mmene Yehova amachitira zinthu ndi ena. Nthawi zambiri anthu audindo amakhala aukali komanso ankhanza. Koma Yehova nthawi zonse amachita zinthu modekha ndiponso mokoma mtima. Mwachitsanzo, iye anauza Abulamu kuti: “Takweza maso ako kuchokera pamene ulipo. Uyangʼane kumpoto ndi kumʼmwera, komanso kumʼmawa ndi kumadzulo.” (Genesis 13:14) Akatswiri a Baibulo amanena kuti m’Chiheberi choyambirira, mawu amulembali amasonyeza kuti Yehova ankapempha mwaulemu osati kulamula. Palinso malemba ena omwe Yehova anasonyeza kuti akupempha. (Genesis 31:12; Ezekieli 8:5) Tangoganizani, Wolamulira wa chilengedwe chonse amalankhula mwaulemu kwa anthu wamba. M’dzikoli anthu ambiri ndi olusa, ankhanza ndiponso achipongwe koma n’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu wathu, Yehova, ndi wachisomo.

18. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi ‘wachoonadi chochuluka,’ nanga n’chifukwa chiyani zimenezi ndi zolimbikitsa?

18 ‘Wachoonadi chochuluka.’ Masiku ano anthu ambiri sachita zinthu moona mtima. Koma Baibulo limatikumbutsa kuti: “Mulungu sali ngati munthu amene amanena mabodza.” (Numeri 23:19) Ndipotu lemba la Tito 1:2 limati ‘Mulungu sanganame.’ Iye ndi wabwino kwambiri moti sangachite zimenezo. Choncho malonjezo a Yehova ndi odalirika kwambiri ndipo zimene wanena nthawi zonse zimachitika. Yehova amatchedwa “Mulungu wa choonadi.” (Salimo 31: 5) Sikuti amangopewa kunena zabodza, koma amatiuzanso mfundo zambiri za choonadi. Sabisa zimene amadziwa kapenanso kuchita zinthu mwachinsinsi. Koma mosaumira amauza atumiki ake nzeru zake zopanda malire. b Ndiponso amawauza zimene angachite kuti azitsatira choonadi chimene amawaphunzitsa n’cholinga choti ‘apitirize kuyendabe m’choonadicho.’ (3 Yohane 3) Ndiye kodi tiyenera kutani chifukwa chodziwa kuti Yehova ndi wabwino?

Muzisangalala “Chifukwa cha Ubwino wa Yehova”

19, 20. (a) Kodi Satana anachititsa bwanji kuti Hava azikayikira zoti Yehova ndi wabwino, nanga zotsatira zake zinali zotani? (b) Kodi mumamva bwanji mukaganizira za ubwino wa Yehova, ndipo n’chifukwa chiyani?

19 Pamene Satana ankayesa Hava m’munda wa Edeni, mochenjera kwambiri anamuchititsa kuti ayambe kukayikira kuti Yehova ndi wabwino. Yehova anali atauza Adamu kuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa mʼmundamu uzidya mmene ungafunire.” Pa mitengo yonse yambirimbiri imene inali m’mundawo, Yehova anangowaletsa mtengo umodzi wokha. Koma taonani funso loyamba limene Satana anafunsa Hava. Anati: “Eti nʼzoona kuti Mulungu ananena kuti musadye zipatso za mtengo uliwonse wamʼmundamu?” (Genesis 2:9, 16; 3:1) Satana anapotoza mawu a Yehova n’cholinga choti Hava aziganiza kuti Yehova sankafuna kumupatsa zinthu zina zabwino. N’zomvetsa chisoni kuti zimene ankafunazi zinachitikadi. Mofanana ndi anthu ambiri amene pambuyo pake anachitanso zomwezi, Hava anayamba kukayikira zoti Mulungu, yemwe anali atamupatsa chilichonse, ndi wabwino.

20 Tikudziwa kuti kukayikira kumeneku kunabweretsa mavuto ambirimbiri. Choncho tisamaiwale mawu a pa Yeremiya 31:12 akuti: “Nkhope zawo zidzawala chifukwa cha ubwino wa Yehova.” Zoonadi, nkhope zathu ziyenera kumawala, kapena kuti tiyenera kumasangalala kwambiri chifukwa cha zinthu zabwino zimene Yehova amatichitira. Tisamakayikire zolinga za Mulungu wathu yemwe ndi wabwino pa chilichonse. Tingamudalire ndi mtima wonse chifukwa nthawi zonse amafunira zabwino anthu amene amamukonda.

21, 22. (a) Kodi mukufuna kumachita zinthu ziti potsanzira ubwino wa Yehova? (b) Kodi m’mutu wotsatira tidzakambirana khalidwe liti, nanga limasiyana bwanji ndi ubwino?

21 Timasangalalanso tikapeza mwayi wouza ena za ubwino wa Mulungu. Ponena za anthu a Mulungu lemba la Salimo 145:7 limati: “Iwo azidzalankhula mosangalala akadzakumbukira ubwino wanu wochuluka.” Tsiku lililonse timapindula ndi ubwino wa Yehova m’njira inayake. Bwanji osakonza zoti tsiku lililonse muzithokoza Yehova pa zabwino zimene wakuchitirani, n’kumatchula mwachindunji zinthuzo? Kuganizira ubwino wa Yehova, kumuthokoza tsiku lililonse komanso kumauzako ena zokhudza khalidweli, kungatithandize kuti tizitsanzira Mulungu wathu wabwinoyu. Ndipo tikamayesetsa kuchita zabwino ngati Yehova, ubwenzi wathu ndi iye umalimba. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Wokondedwa, usamatsanzire anthu ochita zoipa, m’malomwake uzitsanzira anthu amene amachita zabwino. Amene amachita zabwino amayendera maganizo a Mulungu.”​—3 Yohane 11.

22 Palinso makhalidwe ena amene amayendera limodzi ndi ubwino wa Yehova. Mwachitsanzo, Mulungu ndi “wachikondi chokhulupirika chochuluka.” (Ekisodo 34:6) Mosiyana ndi ubwino, khalidwe limeneli ndi lapadera chifukwa Yehova amalisonyeza kwa atumiki ake okhulupirika okha. M’mutu wotsatira, tidzaphunzira mmene amachitira zimenezi.

a Dipo ndi chitsanzo chachikulu kwambiri chosonyeza kuti Yehova ndi wabwino. Pa angelo mamiliyoni ambiri omwe alipo, iye anasankha Mwana wake wokondedwa ndiponso wobadwa yekha kuti adzatifere.

b N’chifukwa chake Baibulo limagwirizanitsa choonadi ndi kuwala. Wolemba masalimo anaimba kuti: “Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu.” (Salimo 43:3) Yehova amapereka kuwala kwakukulu kwauzimu kwa anthu amene amafuna kuti iye awaunikire, kapena kuti awaphunzitse.​—2 Akorinto 4:6; 1 Yohane 1:5.