Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 28

‘Inu Nokha Ndinu Wokhulupirika’

‘Inu Nokha Ndinu Wokhulupirika’

1, 2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti sizinali zachilendo kwa Mfumu Davide kuona anthu ena akusiya kukhala okhulupirika kwa iye?

 SIZINALI zachilendo kwa Mfumu Davide kuona anthu ena akusiya kukhala okhulupirika kwa iye. Pa nthawi ina anthu a mtundu wake omwe, anaukira ulamuliro wake umenenso unkakumana ndi mavuto ambiri. Pa nthawi inanso anzake ena apamtima anasonyeza kusakhulupirika. Taganizirani za Mikala, mkazi wake woyamba. Poyamba, iye “ankakonda Davide” ndipo ayenera kuti ankamuthandiza. Koma patapita nthawi Mikala “anayamba kumunyoza mumtima mwake” mpaka kufika pomamuona kuti anali “munthu wopanda nzeru.”​—1 Samueli 18:20; 2 Samueli 6:16, 20.

2 Ndiye panalinso Ahitofeli yemwe anali mlangizi wa Davide. Anthu ankaona kuti malangizo ake ndi mawu ochokera kwa Yehova. (2 Samueli 16:23) Koma kenako mnzake wapamtima ameneyu anagwirizana ndi gulu limene linaukira ufumu wa Davide. Kodi ndi ndani amene anayambitsa gulu limeneli? Anali Abisalomu, mwana weniweni wa Davideyo. Abisalomu “anapitiriza kukopa anthu mu Isiraeli” ndipo anadziika kukhala mfumu m’malo mwa Davide. Anthu ambiri anakhala kumbali ya Abisalomu moti Mfumu Davide inakakamizika kuthawa poopa kuphedwa.​—2 Samueli 15:1-6, 12-17.

3. Kodi Davide sankakayikira za chiyani?

3 Koma kodi panalibe aliyense amene anapitiriza kukhala wokhulupirika kwa Davide? M’mavuto ake onse, Davide ankadziwa kuti panali winawake yemwe anali wokhulupirika kwa iye. Ameneyu anali Yehova Mulungu. Ponena za Yehova, Davide anati: “Munthu wokhulupirika, mumamuchitira mokhulupirika.” (2 Samueli 22:26) Kodi kukhulupirika n’kutani, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi?

Kodi Munthu Wokhulupirika Amatani?

4, 5. (a) Kodi munthu “wokhulupirika” amatani? (b) Kodi kukhala wokhulupirika kumasiyana bwanji ndi kudalirika?

4 M’Malemba a Chiheberi, mawu akuti “kukhulupirika,” amatanthauza kumamatira munthu amene umamukonda n’kumapitirizabe kumuthandiza. Munthu amachita zimenezi osati chifukwa chongoti n’zimene ayenera kuchita koma chifukwa cha chikondi. a Choncho kukhala wokhulupirika n’kosiyana ndi kungokhala wodalirika. Mwachitsanzo, wolemba masalimo anati mwezi ndi “mboni yokhulupirika yamumlengalenga” chifukwa nthawi zonse umakhalapo. (Salimo 89:37) Choncho tinganene kuti mwezi ndi wokhulupirika, kapena kuti wodalirika. Koma sikuti mwezi umasonyeza kukhulupirika kofanana ndi kumene munthu amasonyeza. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa choti mwezi sungasonyeze chikondi.

Mwezi umatchulidwa kuti mboni yokhulupirika, koma anthu ndi angelo okha ndi omwe angasonyeze kukhulupirika kofanana ndi kumene Yehova amasonyeza

5 Baibulo limasonyeza kuti munthu wokhulupirika amakhalanso wachikondi. Ndipotu munthu akakhala wokhulupirika kwa munthu wina, zimasonyeza kuti munthu winayo ndi mnzake. Munthu woteroyo amakhala wokhulupirika nthawi zonse ndipo sakhala ngati mafunde apanyanja amene amangokankhika ndi mphepo iliyonse. Munthu wokhulupirika, kapena kuti wachikondi chokhulupirika, samasintha zivute zitani.

6. (a) Kodi masiku ano zinthu zili bwanji m’dzikoli pa nkhani ya kukhulupirika, nanga Baibulo linasonyeza bwanji kuti zimenezi zizidzachitika? (b) Kodi njira yabwino yomwe ingatithandize kumvetsa tanthauzo la kukhulupirika ndi iti, ndipo n’chifukwa chiyani?

6 N’zoona kuti masiku ano anthu si okhulupirika chonchi. Nthawi zambiri anthu amene amagwirizana amakhala “okonzeka kuchitirana zoipa.” Timamvanso za anthu amene athawa akazi kapena amuna awo. (Miyambo 18:24; Malaki 2:14-16) Anthu ambiri amachita zachinyengo moti tinganenenso mawu amene mneneri Mika ananena akuti: “Anthu okhulupirika atha padziko lapansi.” (Mika 7:2) Ngakhale kuti nthawi zambiri anthu amalephera kukhala okhulupirika, Yehova amasonyeza kwambiri khalidwe lapadera limeneli. Ndipotu njira yabwino yomwe ingatithandize kumvetsa tanthauzo la kukhulupirika, ndi kuphunzira mmene Yehova amasonyezera khalidweli lomwe ndi logwirizana kwambiri ndi chikondi chake.

Yehova Ndi Wokhulupirika Kuposa Aliyense

7, 8. N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti Yehova yekha ndiye wokhulupirika?

7 Baibulo limati: “Inu nokha Yehova ndinu wokhulupirika.” (Chivumbulutso 15:4) N’chifukwa chiyani limanena zimenezi? Kodi anthu ndiponso angelo ena sanasonyezepo m’njira yapadera kuti ndi okhulupirika? (Yobu 1:1; Chivumbulutso 4:8) Nanga bwanji Yesu Khristu? Pajatu iye ndi “wokhulupirika” wa Mulungu. (Salimo 16:10) Ndiye n’chifukwa chiyani Baibulo limati Yehova yekha ndiye wokhulupirika?

8 Choyamba, kumbukirani kuti kukhulupirika ndi mbali imodzi ya chikondi. Popeza “Mulungu ndi chikondi” ndipo iye ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi, ndaninso angakhale wokhulupirika kwambiri kuposa iyeyo? (1 Yohane 4:8) N’zoona kuti angelo komanso anthu akhoza kusonyeza makhalidwe a Mulungu, komatu Yehova yekha ndi amene ali wokhulupirika kwambiri kuposa aliyense. Popeza ndi “Wamasiku Ambiri,” iye wakhala akusonyeza kukhulupirika kwa nthawi yaitali kuposa zolengedwa zonse. (Danieli 7:9) Choncho Yehova ndi amene amasonyeza kwambiri kukhulupirika kuposa aliyense ndipo palibe angafanane naye. Taonani zitsanzo izi.

9. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi “wokhulupirika pa chilichonse chimene amachita”?

9 Yehova ndi “wokhulupirika pa chilichonse chimene amachita.” (Salimo 145:17) Kodi amachita bwanji zimenezi? Yankho likupezeka mu Salimo 136. Salimo limeneli limatchula zinthu zingapo zimene Yehova anachita populumutsa anthu ake, kuphatikizapo kupulumutsa Aisiraeli pa Nyanja Yofiira. N’zochititsa chidwi kuti vesi lililonse la mu salimoli limamaliza ndi mawu akuti: “Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.” Salimo limeneli lilinso m’bokosi lakuti “ Mafunso Ofunika Kuwaganizira” lomwe lili patsamba 289. Tikamawerenga Salimoli timachita chidwi kwambiri ndi njira zosiyanasiyana zimene Yehova anasonyezera anthu ake chikondi chokhulupirika. Inde, Yehova amasonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa atumiki ake powamvetsera akamapempha kuti awathandize ndipo amawathandizadi pa nthawi yoyenera. (Salimo 34:6) Yehova sasiya kusonyeza atumiki ake chikondi chokhulupirika ngati iwo akupitirizabe kukhala okhulupirika.

10. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wokhulupirika pa nkhani yotsatira mfundo zake?

10 Njira inanso imene Yehova amasonyezera kuti ndi wokhulupirika kwa atumiki ake, ndi yoti mfundo zake sizisintha. Mosiyana ndi anthu amene chifukwa chotengeka maganizo amasinthasintha pa nkhani yokhudza chabwino ndi choipa, Yehova sasintha. Mwachitsanzo, iye sanasinthe mmene amaonera kukhulupirira zamizimu, kulambira mafano komanso kupha munthu. Kudzera mwa mneneri wake Yesaya, iye anati: “Ngakhale mudzakalambe, ine ndidzakhala chimodzimodzi.” (Yesaya 46:4) Choncho, sitikayikira kuti zinthu zidzatiyendera bwino tikamatsatira malangizo omveka bwino opezeka m’Mawu a Mulungu.​—Yesaya 48:17-19.

11. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti Yehova amakwaniritsa malonjezo ake.

11 Yehova amasonyezanso kuti ndi wokhulupirika pokwaniritsa zimene walonjeza. Akanena kuti chinachake chidzachitika, chimadzachitikadi. Choncho iye anati: “Mawu otuluka pakamwa panga sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake, koma adzachitadi chilichonse chimene ine ndikufuna, ndipo zimene ndinawatumizira kuti achite zidzachitikadi.” (Yesaya 55:11) Akamachita zimene walonjeza, Yehova amasonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa anthu ake. Sawachititsa kuti azidikirira zinthu zomwe akudziwa kuti sizichitika. Pa nkhaniyi, Yehova ali ndi mbiri yabwino moti mtumiki wake Yoswa ananena kuti: “Palibe lonjezo limene silinakwaniritsidwe, pa malonjezo onse abwino amene Yehova analonjeza nyumba ya Isiraeli. Onse anakwaniritsidwa.” (Yoswa 21:45) Choncho timakhulupirira kuti sitidzagwiritsidwa fuwa lamoto chifukwa choti Yehova walephera kukwaniritsa malonjezo ake.​—Yesaya 49:23; Aroma 5:5.

12, 13. Kodi chikondi chokhulupirika cha Yehova chidzakhalapo mpaka kalekale m’njira ziti?

12 Monga taonera kale, Baibulo limatiuza kuti chikondi chokhulupirika cha Yehova “chidzakhalapo mpaka kalekale.” (Salimo 136:1) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Choyamba, zikukhudza zimene Yehova amachita akatikhululukira machimo. Monga tinaonera m’Mutu 26, Yehova akakhululukira munthu, m’tsogolo sakumbutsanso zimene anakhululukazo. Popeza “anthu onse ndi ochimwa ndipo amalephera kusonyeza bwinobwino ulemerero wa Mulungu,” tiyenera kumayamikira kuti chikondi chokhulupirika cha Yehova chimakhalapo mpaka kalekale.​—Aroma 3:23.

13 Koma Yehova amasonyeza m’njira inanso kuti chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale. Mawu ake amanena kuti wolungama “adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa ngalande za madzi, umene umabereka zipatso mʼnyengo yake, umenenso masamba ake safota. Ndipo zonse zimene amachita zimamuyendera bwino.” (Salimo 1:3) Taganizirani za mtengo waukulu womwe masamba ake ndi wobiriwira ndipo safota. Nafenso tikamakonda Mawu a Mulungu, timakhala ndi moyo wautali, wamtendere komanso zinthu zimatiyendera bwino. Yehova amapatsa atumika ake madalitso osatha ndipo amachita zimenezi mokhulupirika. Ndithudi, m’dziko latsopano, anthu omvera Yehova adzawasonyeza chikondi chake chokhulupirika mpaka kalekale.​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Yehova “Sadzasiya Anthu Ake Okhulupirika”

14. Kodi Yehova amamva bwanji atumiki ake akamamutumikira mokhulupirika?

14 Yehova wakhala akusonyeza mobwerezabwereza kuti ndi wokhulupirika. Ndipo popeza iye sasintha, sadzasiya kukhala wokhulupirika kwa atumiki ake. Wolemba masalimo anati: “Ndinali mwana ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha chakudya. Chifukwa Yehova amakonda chilungamo, ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika.” (Salimo 37:25, 28) N’zoona kuti timayenera kulambira Yehova popeza ndi Mlengi. (Chivumbulutso 4:11) Komabe chifukwa choti ndi wokhulupirika, amayamikira kwambiri tikamamutumikira mokhulupirika.​—Malaki 3:16, 17.

15. Kodi zimene Yehova anachitira Aisiraeli zimasonyeza bwanji kuti ndi wokhulupirika?

15 Chifukwa choti ali ndi chikondi chokhulupirika, Yehova amathandiza anthu ake akakhala pa mavuto. Wolemba masalimo anati: “Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupirika. Amawapulumutsa mʼmanja mwa oipa.” (Salimo 97:10) Taganizirani zimene anachitira Aisiraeli. Atawapulumutsa modabwitsa pa Nyanja Yofiira, iwo anaimbira Yehova kuti: “Munasonyeza chikondi chanu chokhulupirika potsogolera anthu amene munawawombola.” (Ekisodo 15:13) Apatu Yehova anasonyeza chikondi chokhulupirika. Choncho Mose anauza Aisiraeliwo kuti: “Sikuti Yehova anakusonyezani chikondi ndi kukusankhani chifukwa chakuti munali ochuluka kuposa mitundu yonse, chifukwatu mtundu wanu unali waungʼono mwa mitundu yonse. Koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu kuti akulanditseni mʼnyumba yaukapolo, mʼmanja mwa Farao mfumu ya Iguputo, chifukwa chakuti Yehova anakukondani, komanso chifukwa chosunga lumbiro lake limene analumbirira makolo anu.”​—Deuteronomo 7:7, 8.

16, 17. (a) Kodi Aisiraeli anasonyeza bwanji kuti anali osayamika ngakhale pang’ono, komabe Yehova anawasonyeza bwanji chifundo? (b) Kodi Aisiraeli ambiri anasonyeza bwanji kuti panalibenso “chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa,” nanga tikuphunzirapo chiyani?

16 N’zoona kuti monga mtundu, Aisiraeli analephera kusonyeza kuti ankayamikira chikondi chokhulupirika cha Yehova, chifukwa atapulumutsidwa “anapitiriza kumuchimwira popandukira Wamʼmwambamwamba.” (Salimo 78:17) Kwa zaka mahandiredi ambiri, ankapandukira Yehova mobwerezabwereza ndipo ankalambira mafano komanso kuchita miyambo yachikunja yomwe inkachititsa kuti akhale odetsedwa. Komabe Yehova anapitiriza kusunga pangano lake. Kudzera mwa mneneri Yeremiya, Yehova anachonderera anthu ake kuti: “Bwerera Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyangʼana mokwiya chifukwa ndine wokhulupirika.” (Yeremiya 3:12) Komabe monga tinaonera m’Mutu 25, Aisiraeli ambiri anakana kutsatira malangizowa. Ndipotu iwo “anapitiriza kunyoza atumiki a Mulungu woona, kunyoza mawu ake ndiponso kuseka aneneri ake.” Ndiye kodi zotsatira zake zinali zotani? “Iwo anafika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa. Kenako Yehova anawakwiyira kwambiri nʼkuwalanga.”​—2 Mbiri 36:15, 16.

17 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tikuphunzira kuti ngakhale kuti Yehova ndi wokhulupirika, salekerera zolakwa komanso n’zosatheka kumupusitsa. N’zoona kuti Yehova ndi “wachikondi chokhulupirika chochuluka” ndipo amasangalala kuchitira ena chifundo pakakhala zifukwa zomveka. Koma kodi iye amatani munthu akakhala woipa kwambiri moti sangasinthe? Zikatero amatsatira mfundo zake zolungama ndipo amalanga munthuyo. Mogwirizana ndi zimene anauza Mose, iye ‘salekerera wolakwa osamʼpatsa chilango.’​—Ekisodo 34:6, 7.

18, 19. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova akalanga anthu ochita zoipa amasonyeza kuti ndi wokhulupirika? (b) Kodi Yehova adzasonyeza bwanji kuti ndi wokhulupirika kwa atumiki ake amene amazunzidwa mpaka kuphedwa?

18 Mulungu akalanga anthu ochita zoipa umakhalanso umboni wakuti iye ndi wokhulupirika. N’chifukwa chiyani tikutero? Mfundo imeneyi yafotokozedwa m’buku la Chivumbulutso pamene Yehova analamula angelo 7 kuti: “Pitani, kathireni mbale 7 za mkwiyo wa Mulunguzo padziko lapansi.” Mngelo wachitatu atathira mbale yake “pamitsinje ndi pa akasupe amadzi,” zonse zinasanduka magazi. Ndiyeno mngeloyo anauza Yehova kuti: “Inu Mulungu amene mulipo ndi amene munalipo, inu Wokhulupirika, ndinu wolungama chifukwa mwapereka ziweruzo zimenezi, chifukwa iwo anakhetsa magazi a oyera ndi a aneneri ndipo inu mwawapatsa magazi kuti amwe. Iwo akuyeneradi kulandira chiweruzo chimenechi.”​—Chivumbulutso 16:1-6.

19 N’chifukwa chiyani pamene ankapereka uthenga wachiweruzo, mngeloyo ananena kuti Yehova ndi “wokhulupirika”? N’chifukwa choti powononga anthu oipa, Yehova akusonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa atumiki ake omwe akhala akuzunzidwa mpaka kuphedwa. Yehova amasonyeza kukhulupirika popitirizabe kuwakumbukira anthu amenewa. Iye amalakalaka ataonanso anthu okhulupirika amene anamwalirawa, ndipo Baibulo limatitsimikizira kuti adzawaukitsa. (Yobu 14:14, 15) Ngakhale kuti atumiki ake okhulupirikawo anamwalira, Yehova sanawaiwale. “Kwa iye onsewa ndi amoyo.” (Luka 20:37, 38) Yehova amafuna kudzapatsanso moyo anthu amene akuwakumbukira ndipo umenewu ndi umboni wamphamvu wakuti ndi wokhulupirika.

Yehova adzakumbukira ndiponso kuukitsa anthu amene anakhala okhulupirika mpaka kuphedwa

Bernard Luimes (pamwamba) ndi Wolfgang Kusserow (pakati) anaphedwa ndi a chipani cha Nazi

Gulu la ndale linabaya Moses Nyamussua ndi mkondo mpaka kumupha

Chikondi Chokhulupirika cha Yehova Chikuthandiza Kuti Tidzapulumuke

20. Kodi “anthu oyenera kuwachitira chifundo” ndi ndani, ndipo Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wokhulupirika kwa anthuwa?

20 Yehova wakhala akusonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa atumiki ake. Ndipotu kwa zaka masauzande ambiri, iye wakhala ‘akulekerera moleza mtima kwambiri anthu oyenera kuwonongedwa.’ Chifukwa chiyani? “Kuti asonyeze kukula kwa ulemerero wake kwa anthu oyenera kuwachitira chifundo, omwe anawakonzeratu kuti alandire ulemerero.” (Aroma 9:22, 23) “Anthu oyenera kuwachitira chifundo” amenewa, ndi Akhristu omwe amadzozedwa ndi mzimu woyera kuti akalamulire limodzi ndi Khristu mu Ufumu wake. (Mateyu 19:28) Pokonza zoti anthuwa adzapulumutsidwe, Yehova anasonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa Abulahamu, yemwe anachita naye pangano lakuti: “Kudzera mwa mbadwa yako, mitundu yonse yapadziko lapansi idzapeza madalitso chifukwa chakuti wamvera mawu anga.”​—Genesis 22:18.

Chifukwa chakuti Yehova ndi wokhulupirika, atumiki ake onse okhulupirika ali ndi chiyembekezo chodalirika

21. (a) Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wokhulupirika kwa “khamu lalikulu” limene lidzapulumuke “chisautso chachikulu”? (b) Kodi mukufunitsitsa kuchita chiyani chifukwa chodziwa kuti Yehova ndi wokhulupirika?

21 Yehova amasonyezanso kuti ndi wokhulupirika kwa “khamu lalikulu” limene lidzapulumuke pa “chisautso chachikulu” n’kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padzikoli. (Chivumbulutso 7:9, 10, 14) Ngakhale kuti atumiki ake si angwiro, mokhulupirika Yehova akuwapatsa mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso. Kodi akuchita bwanji zimenezi? Akuzichita pogwiritsa ntchito dipo, lomwe ndi njira yaikulu kwambiri imene anasonyezera kuti ndi wokhulupirika. (Yohane 3:16; Aroma 5:8) Chifukwa choti Yehova ndi wokhulupirika, anthu amene akufunafuna chilungamo amakopeka naye. (Yeremiya 31:3) Kodi mukumva bwanji mukaganizira mfundo yoti Yehova wakhala akusonyeza kuti ndi wokhulupirika kwambiri ndipo adzapitirizabe kusonyeza khalidweli? Popeza timafunitsitsa kuyandikira Mulungu, tiyeni tizisonyeza kuti timayamikira chikondi chake pokhala otsimikiza mtima kuti tizimutumikira mokhulupirika.

a N’zochititsa chidwi kuti mawu amene anawamasulira kuti “mokhulupirika” pa 2 Samueli 22:26, m’malo ena anawamasulira kuti “chikondi chokhulupirika.”