Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 31

“Yandikirani Mulungu Ndipo Iyenso Adzakuyandikirani”

“Yandikirani Mulungu Ndipo Iyenso Adzakuyandikirani”

1-3. (a) Kodi tingaphunzire chiyani tikaona zimene zimachitika pakati pa makolo ndi mwana wawo wakhanda? (b) Kodi timatani mwachibadwa munthu wina akamatikonda, nanga ndi funso lofunika liti limene tingadzifunse?

 MAKOLO amasangalala kuona mwana wawo wakhanda akumwetulira. Nthawi zambiri amaika nkhope yawo pafupi ndi nkhope ya mwanayo n’kumasewera naye kwinaku akumumwetulira. Amafunitsitsa kuona mwanayo nayenso akuwamwetulira. Ndipo pasanapite nthawi zimachitikadi, mwanayo amamwetulira mosangalatsa. Akachita zimenezi, amakhala kuti akusonyeza chikondi ndipo chimakhala chiyambi chakuti nayenso aziwasonyeza makolo akewo kuti amawakonda.

2 Kumwetulira kwa mwana kumatikumbutsa mfundo yofunika kwambiri yokhudza zimene anthufe timachita mwachibadwa. Munthu wina akasonyeza kuti amatikonda, nafenso timayamba kusonyeza kuti timamukonda. (Salimo 22:9) Tikamakula, timayambanso kudziwa njira zina zimene tingasonyezere chikondi kwa anthu omwe amatikonda. Mwina mungakumbukire mmene makolo anu, achibale anu, kapena anzanu ankakukonderani muli mwana. Izi zinachititsa kuti muzisangalala nawo ndipo kenako nanunso munayamba kuwakonda. Kodi zimenezi ndi zomwe zikuchitikanso pa ubwenzi wanu ndi Yehova?

3 Baibulo limati: “Ife timasonyeza chikondi, chifukwa Mulungu ndi amene anayamba kutikonda.” (1 Yohane 4:19) Mu Gawo 1 mpaka 3 m’bukuli takumbutsidwa kuti Yehova Mulungu amasonyeza mphamvu, chilungamo ndiponso nzeru zake mwachikondi kuti akuthandizeni. Ndipo mu Gawo 4 mwaona kuti iye amawasonyeza anthu chikondi, kuphatikizapo inuyo panokha m’njira zapadera kwambiri. Ndiye mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndingatani posonyeza kuti ndimayamikira chikondi cha Mulungu?’ Limeneli ndi funso lofunika kwambiri limene aliyense ayenera kudzifunsa.

Zimene Kukonda Mulungu Kumatanthauza

4. Kodi anthu ambiri amaganiza kuti kukonda Mulungu kumatanthauza chiyani?

4 Yehova, yemwe ndi amene anayambitsa chikondi, amadziwa kuti munthu akamasonyezedwa chikondi, akhoza kumachita zinthu zabwino kwambiri. Choncho ngakhale kuti anthu osakhulupirika akupitirizabe kusonyeza kuti sakufuna kumamumvera, iye amakhulupirira kuti anthu ena aziyamikira chikondi chake. Ndipo ndi zimenedi anthu mamiliyoni ambiri akuchita. Komabe, n’zomvetsa chisoni kuti zipembedzo zambiri m’dziko loipali zachititsa anthu kuti asamadziwe kuti kukonda Mulungu kumatanthauza chiyani. Anthu ambiri amati amakonda Mulungu, koma zikuoneka kuti amaganiza kuti kungonena kuti, ‘Ndimakonda Mulungu’ n’kokwanira. N’zoona kuti chimenechi chingakhale chiyambi chabwino ngati mmene poyamba mwana wakhanda angasonyezere kuti amakonda makolo ake powamwetulira. Komabe tikamadziwa zambiri zokhudza chikondi, timafunika kuchita zambiri kuposa pamenepa.

5. Kodi Baibulo limati kukonda Mulungu kumatanthauza chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kumasangalala ndi zimenezi?

5 Yehova amatiuza mmene munthu angasonyezere kuti amamukonda. Mawu ake amati: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kutsatira malamulo ake.” Choncho zochita zathu ndi zimene zingasonyeze kuti timakonda Mulungu. Komabe ambiri sasangalala kuti azimvera munthu wina. Komatu vesili limanenanso kuti: “Malamulo [a Mulungu] si ovuta kuwatsatira.” (1 Yohane 5:3) Yehova anatipatsa malamulo ndiponso mfundo zake kuti zizitithandiza osati kutipondereza. (Yesaya 48:17, 18) M’Mawu a Mulungu muli mfundo zambiri zomwe zimatithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. N’chifukwa chiyani tikutero? Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zomwe zimatithandiza kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Zinthu zake ndi kulankhulana naye, kumulambira ndiponso kumutsanzira.

Kulankhulana ndi Yehova

6-8. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikumvetsera Yehova akamalankhula nafe? (b) Kodi tingatani kuti kuwerenga Baibulo kuzitisangalatsa?

6 Mutu 1 unayamba ndi funso lakuti, “Kodi mungamve bwanji mutadziwa kuti Mulungu akufuna kulankhula nanu?” Tinaona kuti zoterezi zinachitikapo. Mose analankhula ndi Mulungu. Nanga bwanji ifeyo? Masiku ano Yehova satumiza angelo ake kuti alankhule ndi anthu. Koma iye ali ndi njira zabwino kwambiri zomwe amagwiritsa ntchito kuti alankhule nafe. Kodi amalankhula nafe bwanji, nanga tingasonyeze bwanji kuti tikumvetsera?

7 Popeza “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu,” timamvetsera zimene Yehova akulankhula tikamawerenga Mawu ake, Baibulo. (2 Timoteyo 3:16) Choncho wolemba masalimo analangiza atumiki a Yehova kuti aziliwerenga “masana ndi usiku.” (Salimo 1:1, 2) Kuti zimenezi zitheke, pamafunika khama. Koma khama limeneli limatithandiza kwambiri. Monga tinaonera m’Mutu 18, Baibulo lili ngati kalata yofunika kwambiri yochokera kwa Atate athu akumwamba. Choncho tisamaone kuti kuliwerenga ndi chintchito. Tiziwerenga Baibulo m’njira yoti lizitisangalatsa. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

8 Muziona m’maganizo mwanu zimene mukuwerengazo. Muziona anthu otchulidwa m’Baibulo ngati anthu enieni. Yesetsani kumvetsa kuti anali anthu otani, mmene zinthu zinaliri pa moyo wawo komanso zolinga zawo pochita zinthu. Kenako muziganizira mozama zimene mukuwerengazo. Muzidzifunsa mafunso ngati akuti: ‘Kodi nkhaniyi ikundiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova? Kodi ndikupezapo khalidwe liti la Yehova? Kodi ndi mfundo iti imene Yehova akufuna kuti ndiphunzire, nanga ndingaigwiritse ntchito bwanji pa moyo wanga?’ Muziwerenga, kuganizira mozama komanso kutsatira zomwe mwawerengazo. Mukamachita zimenezi, kuwerenga Mawu a Mulungu kuzikusangalatsani.​—Salimo 77:12; Yakobo 1:23-25.

9. Kodi “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” ndi ndani, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kumamumvetsera mwatcheru?

9 Yehova amalankhulanso nafe pogwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru.” Mogwirizana ndi zimene Yesu ananeneratu, pali kagulu ka Akhristu odzozedwa kamene kanaikidwa kuti kazipereka ‘chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera’ m’masiku ovuta ano. (Mateyu 24:45-47) Tikamawerenga mabuku omwe amakonzedwa kuti azitithandiza kudziwa mfundo zolondola za m’Baibulo ndiponso tikamafika pa misonkhano yampingo ndi ikuluikulu, timakhala kuti tikudyetsedwa ndi kapoloyu. Popeza kapoloyu ndi wa Khristu, timasonyeza kuti ndife anzeru tikamatsatira mawu a Yesu akuti: “Muzimvetsera mwatcheru kwambiri.” (Luka 8:18) Timamvetsera mwatcheru chifukwa timadziwa kuti kapoloyu ndi imodzi mwa njira zimene Yehova amagwiritsa ntchito polankhula nafe.

10-12. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti pemphero ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova anatipatsa? (b) Kodi tizipemphera bwanji kuti Mulungu azisangalala ndi mapemphero athu, nanga n’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti iye amasangalala ndi mapemphero athu?

10 Taona njira zimene Yehova amagwiritsa ntchito polankhula nafe. Nanga kodi ifeyo timalankhula naye bwanji? Mwina tikhoza kumachita mantha tikaganizira zimenezi. Mutafuna kukaonana ndi pulezidenti wa dziko lanu kuti mukakambirane naye mavuto anu, kodi mungaonane naye mosavuta? M’mayiko ena, kuchita zimenezi kungakhale kuika moyo pachiswe. M’nthawi ya Esitere ndi Moredikayi, munthu ankatha kuphedwa ngati wakaonekera kwa mfumu ya Perisiya asanaitanidwe ndi mfumuyo. (Esitere 4:10, 11) Ndiye kuli bwanji kukaonekera pamaso pa Ambuye Wamkulu Koposa wa chilengedwe chonse yemwe kwa iye anthu, ngakhale amphamvu kwambiri, “ali ngati ziwala”? (Yesaya 40:22) Kodi tiyenera kuchita mantha kwambiri? Ayi.

11 Yehova anakonza njira yosavuta yoti tizigwiritsa ntchito tikafuna kulankhula naye. Njira imeneyi ndi pemphero. Ngakhale mwana wamng’ono kwambiri akhoza kupemphera mwachikhulupiriro kwa Yehova m’dzina la Yesu. (Yohane 14:6; Aheberi 11:6) Komatu pemphero limatithandiza kuti tithe kumuuza zakukhosi kwathu ndiponso nkhawa zathu ngakhalenso zinthu zimene zikutisowetsa mtendere kwambiri moti sitingathe kuzifotokoza bwinobwino. (Aroma 8:26) Tikamapemphera, tisamaganize kuti Yehova angachite chidwi ngati tingagwiritse ntchito mawu ogometsa kapena kupereka mapemphero aatali omangobwerezabwereza. (Mateyu 6:7, 8) Komabe Yehova sanatiikire malire a kutalika kwa nthawi imene tiyenera kulankhula naye komanso kuti tiyenera kulankhula naye kangati. Ndipotu Mawu ake amatiuza kuti ‘tizipemphera nthawi zonse.’​—1 Atesalonika 5:17.

12 Kumbukirani kuti Yehova yekha ndi amene amatchedwa kuti “Wakumva pemphero,” ndipo pamene akumvetsera amakhudzidwa kwambiri. (Salimo 65:2) Kodi iye amaona kuti n’zokwanira kungomvetsera mapemphero a atumiki ake okhulupirika? Ayi, amasangalala ndi mapempherowo. Mawu ake amati mapemphero oterowo ali ngati zofukiza zomwe akazitentha zimatulutsa kafungo konunkhira bwino. (Salimo 141:2; Chivumbulutso 5:8; 8:4) N’zolimbikitsatu kwambiri kudziwa kuti mapemphero athu ochokera pansi pamtima amafanana ndi zimenezi ndipo amasangalatsa Ambuye Wamkulu Koposa. Choncho ngati mukufuna kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, tsiku lililonse muzipemphera kwa iye modzichepetsa ndiponso pafupipafupi. Muzimuuza zakukhosi kwanu. (Salimo 62:8) Iye ndi Atate wanu wakumwamba choncho muzimuuza zimene zikukudetsani nkhawa kapena kukusangalatsani. Komanso muzimuthokoza ndi kumutamanda. Mukamatero, ubwenzi wanu ndi iye udzapitiriza kukhala wolimba.

Kulambira Yehova

13, 14. Kodi kulambira Yehova kumatanthauza chiyani, nanga n’chifukwa chiyani n’zoyenera kuti tizimulambira?

13 Tikamalankhulana ndi Yehova Mulungu, sikuti timakhala kuti tikungomumvetsera ndiponso kumulankhula ngati mmene zimakhalira ndi mnzathu kapena wachibale. M’malomwake, ndi imodzi mwa njira zimene timasonyezera kuti timamulemekeza kwambiri komanso timamukonda ndi mtima wonse. Timakhalanso kuti tikumupatsa ulemu waukulu umene amafunika kulandira. Kulambira koona kumakhudza chilichonse pa moyo wathu. Kumachititsanso kuti atumiki onse okhulupirika a Yehova akhale ogwirizana, akumwamba ndiponso apadziko lapansi. M’masomphenya, mtumwi Yohane anamva mngelo akulengeza lamulo lakuti: “Lambirani Iye amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja ndi akasupe amadzi.”​—Chivumbulutso 14:7.

14 Koma n’chifukwa chiyani tiyenera kulambira Yehova? Taganizirani makhalidwe amene takambirana m’bukuli, makhalidwe monga kukhala woyera, mphamvu, kudziletsa, chilungamo, kulimba mtima, chifundo, nzeru, kudzichepetsa, chikondi, kumvera ena chisoni, kukhulupirika ndiponso ubwino. Taona kuti Yehova ndi amene amasonyeza kwambiri makhalidwe abwino amenewa kuposa aliyense. Tikamayesetsa kumvetsa njira zosiyanasiyana zimene Yehova amasonyezera makhalidwe ake onse, timazindikira kuti sikuti iye wangokhala winawake wamkulu kwambiri amene amatigometsa. Iye ndi waulemerero komanso wapamwamba kwambiri kuposa ifeyo. (Yesaya 55:9) N’zosachita kufunsa kuti Yehova ndiyedi Wolamulira wathu wamkulu ndipo tikuyenera kumamulambira. Koma kodi tiyenera kumamulambira bwanji?

15. Kodi tingalambire bwanji Yehova “motsogoleredwa ndi mzimu komanso choonadi,” nanga pamisonkhano yathu timakhala ndi mwayi wochita chiyani?

15 Yesu anati: “Mulungu ndi Mzimu, ndipo amene akumulambira akuyenera kumulambira motsogoleredwa ndi mzimu komanso choonadi.” (Yohane 4:24) Kuti tizilambira Mulungu “motsogoleredwa ndi mzimu,” tiyenera kukhala ndi mzimu wake komanso kulola kuti uzititsogolera. Kulambira kwathu kuyeneranso kukhala kogwirizana ndi choonadi, kutanthauza mfundo zolondola zopezeka m’Mawu a Mulungu. Nthawi iliyonse pamene tasonkhana ndi Akhristu anzathu, timakhala ndi mwayi wamtengo wapatali wolambira Yehova “motsogoleredwa ndi mzimu komanso choonadi.” (Aheberi 10:24, 25) Tikamaimba nyimbo zomutamanda, kupemphera limodzi, kumvetsera komanso kutenga nawo mbali tikamakambirana Mawu ake, timasonyeza kuti timamukonda komanso kumulambira m’njira imene amafuna.

Misonkhano yampingo imakhala nthawi yosangalatsa yolambira Yehova

16. Kodi lamulo limodzi mwa malamulo akuluakulu amene Akhristu oona anapatsidwa ndi liti, nanga n’chifukwa chiyani timaona kuti tiyenera kumvera?

16 Timalambiranso Yehova tikamauza ena zokhudza iyeyo ndipo tikamatero timakhala tikumutamanda. (Aheberi 13:15) Ndipotu limodzi mwa malamulo akuluakulu amene Akhristu oona anapatsidwa, ndi loti azilalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Yehova. (Mateyu 24:14) Timamvera lamuloli mofunitsitsa chifukwa timakonda Yehova. Satana Mdyerekezi, yemwe ndi “mulungu wa nthawi ino wachititsa khungu maganizo” a anthu osakhulupirira ndipo amafalitsa mabodza oipa kwambiri okhudza Yehova. Tikaganizira zimenezi, timafunitsitsa kukhala Mboni za Mulungu wathu n’kumauza anthu zoona zokhudza Mulunguyo. (2 Akorinto 4:4; Yesaya 43:10-12) Ndipo tikamaganizira makhalidwe a Yehova ochititsa chidwi timafunitsitsanso kuuza ena zokhudza iyeyo. Kunena zoona, palibe mwayi waukulu kuposa kuthandiza ena kudziwa Atate wathu wakumwamba n’kuyamba kumukonda ngati mmene ifeyo timachitira.

17. Kodi kulambira Yehova kumakhudzanso zinthu ziti, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kumulambira mokhulupirika?

17 Kulambira Yehova kumakhudzanso zinthu zina zambiri. Kumakhudza mbali iliyonse ya moyo wathu. (Akolose 3:23) Ngati timavomerezadi kuti Yehova ndi Ambuye wathu wamkulu koposa, tidzayesetsa kuchita zimene iye amafuna pa chilichonse kaya ndi m’banja, kuntchito, tikamachita zinthu ndi ena komanso tikakhala kwatokha. Tidzayesetsa kutumikira Yehova “ndi mtima wonse,” kapena kuti mokhulupirika. (1 Mbiri 28:9) Munthu akamalambira Yehova m’njira imeneyi sakhala wachiphamaso kapena wachinyengo, kumaoneka ngati akutumikira Yehova pamene kumbali akuchita machimo akuluakulu. Kukhala wokhulupirika kumachititsa kuti munthu asakhale wachinyengo ndipo kukonda Mulungu kumachititsa kuti azinyansidwa ndi zachinyengo. Kuopa Mulungu kudzatithandizanso kuti tizimutumikira ndi mtima wonse. Baibulo limati kuopa Mulungu kumatithandiza kuti tipitirize kukhala naye pa ubwenzi.​—Salimo 25:14.

Muzitsanzira Yehova

18, 19. N’chifukwa chiyani n’zomveka kuganiza kuti anthu omwe si angwirofe tikhoza kumatsanzira Yehova Mulungu?

18 Chigawo chilichonse cha bukuli chikumamaliza ndi mutu wosonyeza mmene ‘tingatsanzirire Mulungu monga ana ake okondedwa.’ (Aefeso 5:1) N’zofunika kumakumbukira kuti ngakhale kuti si ife angwiro, tikhoza kumatsanzira Yehova pa nkhani yosonyeza mphamvu, chilungamo, nzeru ndiponso chikondi. Kodi timadziwa bwanji kuti n’zothekadi kutsanzira Wamphamvuyonse? Kumbukirani kuti tanthauzo la dzina la Yehova limatiphunzitsa kuti iye akhoza kukhala chilichonse chimene wafuna kuti akwaniritse zofuna zake. Timagoma kwambiri ndi zimenezi. Koma kodi n’zotheka kuti ifenso tizisankha zimene tikufuna kuchita? Inde n’zotheka.

19 Tinapangidwa m’chifaniziro cha Mulungu. (Genesis 1:26) Choncho anthufe ndife osiyana ndi zolengedwa zina zonse padzikoli. Sitichita zinthu pongogwiritsa ntchito nzeru zachibadwa kapena pongotengera zinthu zimene zatizungulira. Yehova anatipatsa mphatso ya mtengo wapatali, yomwe ndi ufulu wosankha zochita. Ngakhale kuti pali zina zimene sitingakwanitse kuchita ndiponso si ife angwiro, tili ndi ufulu wosankha kuti tikhale anthu otani. Komanso tiyenera kukumbukira kuti dzina la Mulungu limatanthauzanso kuti akhoza kuchititsa kuti atumiki ake akhale chilichonse chimene iye wafuna. Ndiye kodi mukufuna kukhala munthu wachikondi, wanzeru ndiponso wachilungamo amene amagwiritsa ntchito bwino mphamvu zake? Mothandizidwa ndi mzimu wa Yehova, n’zotheka kukhala munthu wotero. Taganizirani zabwino zimene mungakwanitse kuchita mutakhala munthu woteroyo.

20. Kodi ndi zinthu zabwino ziti zomwe zimachitika tikamatsanzira Yehova?

20 Mudzasangalatsa mtima wa Atate wanu wakumwamba. (Miyambo 27:11) Mukhozanso ‘kumamusangalatsa pa chilichonse’ chifukwa amadziwa zimene mungakwanitse ndi zimene simungakwanitse kuchita. (Akolose 1:9, 10) Ndipo mukamapitiriza kutsanzira makhalidwe abwino a Atate wanu wokondedwa, mudzakhala ndi mwayi wina wapadera. M’dziko lamdimali lomwe anthu ambiri sadziwa Mulungu, mukhoza kuwathandiza kuti aone kuwala kwa choonadi. (Mateyu 5:1, 2, 14) Mukamasonyeza makhalidwe abwino a Yehova, anthu ena akhoza kudziwa kuti iye ndi Mulungu wabwino kwambiri. Umenewutu ndi mwayi waukulu kwambiri.

“Yandikirani Mulungu Ndipo Iyenso Adzakuyandikirani”

Muziyandikira Yehova nthawi zonse

21, 22. Kodi anthu onse okonda Yehova adzapitiriza kuchita chiyani mpaka kalekale?

21 Zimene timauzidwa pa Yakobo 4:8, si zinthu zongochita kamodzi kokha kapena kwa nthawi yochepa. Tidzazichita kwa moyo wathu wonse ngati tingakhalebe okhulupirika. Tidzapitiriza kuyandikira Yehova. Ndipotu nthawi zonse pamakhala kuti pali zambiri zofunika kuti tiphunzire zokhudza iye. Tisaganize kuti bukuli latiphunzitsa zonse zokhudza Mulungu wathu Yehova. Apa tangoyambapo kukambirana zimene Baibulo limanena. Ndipo ngakhalenso Baibulo silitiuza zonse zokhudza Yehova. Mtumwi Yohane ananena kuti zonse zimene Yesu anachita pa utumiki wake ali padzikoli zikanati zilembedwe, “mipukutu yolembedwayo sikanakwana mʼdzikoli.” (Yohane 21:25) Ngati zili choncho ponena za Mwana, ndiye kuli bwanji za Atate?

22 Ngakhale pamene tidzakhale ndi moyo wosatha, sitidzamaliza kuphunzira za Yehova. (Mlaliki 3:11) Ndiye taganizirani zomwe tikuyembekezera m’tsogolomu. Pambuyo pokhala ndi moyo kwa zaka mahandiredi ambiri, masauzande, mamiliyoni, ngakhalenso mabiliyoni, tidzadziwa zinthu zambiri zokhudza Yehova Mulungu kuposa mmene tikudziwira panopa. Koma tizidzaonabe kuti pakanali zinthu zambiri zodabwitsa zoti tiziphunzire. Tizidzafunitsitsa kuphunzira zambiri chifukwa nthawi zonse tizidzakhala ndi zifukwa zotichititsa kumva ngati mmene wolemba masalimo anamvera, yemwe anaimba kuti: “Kwa ine, kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.” (Salimo 73:28) Moyo m’Paradaiso udzakhala wosangalatsa kwambiri kuposa mmene tingaganizire komanso tidzakhala ndi zochita zosiyanasiyana. Ndipo nthawi zonse chinthu chosangalatsa kwambiri chizidzakhala kuyandikira Yehova.

23. Kodi mukulimbikitsidwa kuchita chiyani?

23 Popeza Yehova amakukondani, yesetsani kuti nanunso muzimukonda ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu onse ndiponso mphamvu zanu zonse. (Maliko 12:29, 30) Muzimukonda ndi chikondi chokhulupirika. Tsiku lililonse mukamasankha zinthu, kaya zikuluzikulu kapena zing’onozing’ono, muzisonyeza kuti nthawi zonse mumafunitsitsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Atate wanu wakumwamba. Koposa zonse, nthawi zonse muziyesetsa kuyandikira Yehova ndipo iyenso adzakuyandikirani mpaka kalekale.