Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu 1

Chifukwa Chake Yesu Anali Mphunzitsi Waluso

Chifukwa Chake Yesu Anali Mphunzitsi Waluso

ZAKA zoposa 2,000 zapitazo, kunabadwa mwana wapadera amene anakula n’kukhala munthu wodziŵika kwambiri kuposa wina aliyense. Kalelo kunalibe munthu amene anali ndi ndege kapena galimoto. Kunalibe ma TV kapenanso mawailesi.

Mwanayo anapatsidwa dzina lakuti Yesu. Atakula anali ndi nzeru kuposa munthu wina aliyense amene anakhalako padziko lapansi pano. Yesu analinso wodziŵa kuphunzitsa kuposa wina aliyense. Anali kufotokoza zinthu zovuta m’njira imene anthu angathe kumva bwino.

Yesu anaphunzitsa anthu kulikonse kumene anakumana nawo. Anawaphunzitsa ali m’mbali mwa nyanja komanso m’maboti. Anawaphunzitsa panyumba zawo ndiponso pamene anali kuyenda. Yesu analibe galimoto, komanso sanali kuyenda pabasi kaya pasitima. Yesu anali kuyenda pansi popita kumalo osiyanasiyana kukaphunzitsa anthu.

Timaphunzira zinthu zambiri kwa anthu ena. Koma tingaphunzire zinthu zofunika kwambiri kwa Mphunzitsi Waluso, Yesu. M’Baibulo ndi mmene timapezamo mawu a Yesu. Tikamamva mawu amenewo m’Baibulo, zimangokhala ngati kuti Yesu akulankhula nafe.

Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anali Mphunzitsi Waluso choncho? Chifukwa choyamba ndi chakuti Yesu naye anaphunzitsidwa ndi winawake. Ndipo iye anali kudziŵa kuti kumvetsera ndi kofunika. Koma kodi Yesu anamvetsera kwa ndani? Kodi unganene kuti ndani amene anamuphunzitsa?— Atate ake ndiwo anamuphunzitsa. Ndipotu Atate ake a Yesu ndi Mulungu.

Yesu asanakhale munthu padziko lapansi pano, anali ndi Mulungu kumwamba. Motero Yesu anali wosiyana ndi anthu ena chifukwa palibe munthu wina aliyense amene anakhalako kumwamba asanabadwe padziko lapansi. Yesu anali Mwana wabwino kumwamba, anali kumvera Atate ake. Choncho Yesu anali wokhoza kuphunzitsa anthu zimene anaphunzira kwa Mulungu. Mwa kumvera atate ako ndi amayi ako, iwenso ungakhale ngati Yesu.

Yesu analinso Mphunzitsi Waluso chifukwa chakuti anali kukonda anthu. Anafuna kuthandiza anthu kuphunzira za Mulungu. Yesu anali kukonda anthu akuluakulu, komanso anali kukonda ana. Ndipo ana anali kukonda kukhala ndi Yesu chifukwa Yesu anali kucheza nawo.

N’chifukwa chiyani ana anali kukonda kukhala ndi Yesu?

Tsiku lina makolo ena anapita kwa Yesu ndi ana awo. Koma anzake a Yesu anaganiza kuti Mphunzitsi Walusoyu analibe nthaŵi yocheza ndi ana. Ndiye anawauza kuti abwerere. Kodi ukuganiza kuti Yesu anati chiyani?— Yesu anati: ‘Lolani ana abwere kwa Ine; musawaletse.’ Inde, Yesu anafuna kuti ana abwere kwa iye. Tsono ungaone kuti ngakhale Yesu anali munthu wanzeru kwambiri komanso wofunika zedi, anapeza nthaŵi yophunzitsa ana aang’ono.—Marko 10:13, 14.

Kodi ukudziŵa chifukwa chake Yesu anali kuphunzitsa ana komanso kucheza nawo? Ndi chifukwa chakuti anafuna kuti anawo azisangalala pa kumva za Mulungu, Atate wake wakumwamba. Kodi iweyo anthu ungawasangalatse motani?— Ungawasangalatse mwa kuwauza za Mulungu zimene waphunzira.

Nthaŵi ina Yesu pophunzitsa anzake mfundo yofunika kwambiri anagwiritsa ntchito mwana wamng’ono. Anatenga mwanayo ndi kumuika pakati pa ophunzira Ake. Kenako Yesu anati anthu akuluakulu ameneŵa ayenera kusintha khalidwe lawo ndi kukhala ngati kamwana kameneka.

Kodi ana okulirapo komanso anthu akuluakulu angaphunzire chiyani kwa mwana wamng’ono?

Kodi Yesu anatanthauza chiyani ponena zimenezi? Kodi iweyo umadziŵa mmene munthu wamkulu, kapena mwana wamkulupo, angakhalire ngati kamwana?— Eya, mwana wamng’ono sadziŵa zinthu zambiri ngati munthu wamkulu ndipo iye amafuna kuphunzira. Apatu Yesu anali kunena kuti ophunzira ake afunika kukhala odzichepetsa, ngati mmene ana alili. Inde, tonse tikhoza kuphunzira zinthu zambiri kwa anthu ena. Ndipo tonse tifunika kuzindikira kuti zimene Yesu anaphunzitsa ndi zofunika kwambiri kuposa zimene timaganiza.—Mateyu 18:1-5.

Yesu analinso Mphunzitsi Waluso chifukwa chakuti anali kudziŵa kufotokoza zinthu m’njira yoti zisangalatse anthu. Anafotokoza zinthu mosavuta kumva. Analankhula za mbalame ndi maluŵa ndiponso zinthu zina zimene anthu anali kuzidziŵa pofuna kuwathandiza kumvetsa za Mulungu.

Tsiku lina Yesu ali m’mbali mwa phiri, anthu ambiri anabwera pomwepo. Yesu anakhala pansi ndi kumawakambira nkhani, kapena kuti ulaliki, monga ukuonera apamu. Nkhani imeneyi imatchedwa kuti Ulaliki wa pa Phiri. Iye anati: ‘Onani mbalame m’mwamba. Izo sizilima. Sizisunga chakudya m’nkhokwe. Koma Mulungu wakumwamba amazidyetsa. Kodi inu sindinu ofunika kuposa mbalamezo?’

Kodi Yesu anali kuphunzitsa chiyani pamene analankhula za mbalame ndi maluŵa?

Yesu ananenanso kuti: ‘Phunzirani pa maluŵa akuthengo. Iwo amakula koma sagwira ntchito. Ndipo onani mmene alili okongola! Ngakhale Mfumu Solomo amene anali wolemera kwambiri sanavale zovala zokongola kuposa maluŵa akuthengo ameneŵa. Ndiye ngati Mulungu amasamalira maluŵa amene amamera, kodi iye sadzakusamalirani inunso?’—Mateyu 6:25-33.

Kodi waona mfundo imene Yesu anali kuphunzitsa?— Sanafune kuti tizivutika kuganiza kuti chakudya tidzachipeza kuti kaya kuti tidzavala chiyani. Mulungu amadziŵa kuti timafunika zinthu zonsezo. Yesu sanaletse kugwira ntchito kuti munthu apeze chakudya ndi zovala. Koma iye ananena kuti tiziika Mulungu patsogolo pochita zinthu. Ngati tichita zimenezi, Mulungu adzaonetsetsa kuti tikupeza chakudya ndi zovala. Kodi iweyo ukukhulupirira zimenezi?—

Kodi ukuganiza kuti anthu anatani Yesu atamaliza kulankhula?— Baibulo limanena kuti iwo anadabwa kwambiri ndi mmene Yesu anaphunzitsira. Zinali zosangalatsa kwambiri kumvetsera pamene iye anali kulankhula. Zimene iye ananena zinathandiza anthu kuchita zabwino.—Mateyu 7:28.

Choncho ndi bwino kuti ife tiphunzire kwa Yesu. Kodi ukuganiza kuti zimenezi tingazichite bwanji?— Eya, zimene iye ananena zinalembedwa m’buku. Kodi buku limene analembamo zimenezo dzina lake n’chiyani?— Ndi Baibulo Lopatulika. Zimenezi zikutanthauza kuti tingamvetsere Yesu mwa kuchita zinthu zimene timaŵerenga m’Baibulo. Ndipotu Baibulo lili ndi nkhani yosangalatsa yonena za mmene Mulungu mwiniyo anatiuzira kuti tizimvera Yesu. Tiye tione zimene zinachitika.

Tsiku lina Yesu anapita kuphiri ndi anzake atatu. Mayina awo anali Yakobo, Yohane, ndi Petro. Tidzaphunzira zambiri za amuna ameneŵa m’tsogolomu popeza kuti onse atatu anali anzake zedi a Yesu. Koma panthaŵi yapadera imeneyi, nkhope ya Yesu inayamba kuwala kwambiri. Nazonso zovala zake zinawala zedi, ngati mmene ukuonera apa.

“Uyu ndiye Mwana wanga . . . Mverani Iye”

Kenako, Yesu ndi anzakewo anamva mawu ochokera kumwamba. Mawuwo anati: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.” (Mateyu 17:1-5) Kodi ukuganiza kuti ndani analankhula mawu amenewo?— Anali mawu a Mulungu! Inde, anali Mulungu amene ananena kuti iwo ayenera kumvera Mwana wake.

Nanga bwanji ifeyo masiku ano? Kodi tidzamvera Mulungu ndi Mwana wake, Mphunzitsi Waluso?— Zimenezi ndi zimene tonse tifunika kuchita. Kodi ukukumbukira mmene tingachitire zimenezi?—

Inde, tingamvetsere kwa Mwana wa Mulungu mwa kuŵerenga nkhani za m’Baibulo zonena za moyo wake. Pali zinthu zosangalatsa zambiri zoti Mphunzitsi Waluso atiuze. Udzasangalala kuphunzira zinthu zimenezi zolembedwa m’Baibulo. Ndiponso udzakhala wokondwa ukamauza anzako zinthu zabwino zimene ukuphunzira.

Kuti mupeze mfundo zina zabwino zosonyeza phindu lomvera Yesu, tsegulani Baibulo lanu ndi kuŵerenga Yohane 3:16; 8:28-30; ndi Machitidwe 4:12.