Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu 4

Mulungu Ali ndi Dzina Lake

Mulungu Ali ndi Dzina Lake

KODI ukakumana ndi mnzako nthaŵi yoyamba, umayamba kumufunsa chiyani?— Inde, umafunsa dzina lake. Tonse tili ndi mayina. Mulungu anapatsa dzina munthu wamwamuna woyamba kukhala padziko lapansi. Anamupatsa dzina lakuti Adamu. Mkazi wa Adamu anamupatsa dzina lakuti Hava.

Komatu si anthu okha amene ali ndi mayina. Taganizira zinthu zinanso zimene zili ndi mayina. Munthu wina akakuumbira kapena akakupatsa chidole, umachipatsa dzina, eti?— Inde, kukhala ndi dzina ndi kofunika kwambiri.

Ona nyenyezi zambirimbiri zimene zimaoneka usiku. Kodi ukuganiza kuti zili ndi mayina?— Inde, Mulungu anapatsa dzina nyenyezi iliyonse imene ili kumwamba. Baibulo limatiuza kuti: ‘Amaŵerenga nyenyezi; amazitcha mayina awo zonse.’—Salmo 147:4.

Kodi umadziŵa kuti nyenyezi zonse zili ndi mayina awo?

Kodi unganene kuti munthu wofunika kwambiri kumwamba ngakhalenso padziko lapansi pano ndani?— Inde ndi Mulungu. Kodi ukuganiza kuti ali ndi dzina lake?— Yesu ananena kuti ali nalo. Nthaŵi ina Yesu popemphera kwa Mulungu anati: ‘Ndinadziŵitsa ophunzira anga dzina lanu.’ (Yohane 17:26) Kodi dzina la Mulungu umalidziŵa?— Mulungu iye mwini amatiuza dzina lake. Amati: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli.” Motero dzina la Mulungu ndi YEHOVA.—Yesaya 42:8.

Kodi iwe umamva bwanji anthu ena akakumbukira dzina lako?— Umasangalala, si choncho?— Yehova amafunanso kuti anthu adziŵe dzina lake. Motero tizigwiritsa ntchito dzina lakuti Yehova pamene tikukamba za Mulungu. Mphunzitsi Waluso polankhula kwa anthu anagwiritsa ntchito dzina la Mulungu lakuti Yehova. Nthaŵi ina Yesu anati: “Uzikonda Ambuye [“Yehova,” NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse.”—Marko 12:30.

Yesu anadziŵa kuti dzina lakuti “Yehova” ndi dzina lofunika kwambiri. Choncho anaphunzitsa otsatira ake kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu. Anawaphunzitsa kulankhula za dzina la Mulungu ngakhale popemphera. Yesu anadziŵa kuti Mulungu amafuna kuti anthu onse adziŵe dzina Lake, lakuti Yehova.

Kalekalelo, Mulungu anasonyeza Mose, amene anali Mwisrayeli, kuti dzina lake ndi lofunika zedi. Aisrayeli anali kukhala m’dziko la Igupto. Anthu a m’dziko limenelo anali kudziŵika kuti Aigupto. Iwo anapanga Aisrayeli kukhala akapolo ndipo anali kuwachitira nkhanza kwambiri. Mose atakula, anayesa kuthandiza munthu wina wa anthu a mtundu wake. Izi zinachititsa Farao, yemwe anali mfumu ya Igupto, kukwiya kwambiri. Anafuna kupha Mose! Ndiyeno Mose anathaŵako ku Igupto.

Mose anapita ku dziko lina. Anapita ku Midyani. Kumeneko Mose anakwatira ndipo anakhala ndi ana. Analinso kuŵeta nkhosa. Tsiku lina Mose akudyetsa nkhosa zake pafupi ndi phiri anaona zodabwitsa. Chitsamba chinali kuyaka moto, koma icho osapsa! Mose anapita pafupi kuti akaonetsetse.

Kodi ukudziŵa zimene zinachitika?— Mose anamva mawu akuitana pakati pa chitsamba choyaka motocho. Mawuwo anaitana kuti, “Mose, Mose.” Kodi ukuganiza kuti ndani anali kunena mawu amenewo?— Mulungu ndiye anali kulankhula! Mulungu anali ndi ntchito yambiri yoti Mose achite. Mulungu anati: ‘Tiye tsopano, ndikutume kwa Farao, mfumu ya Igupto, kuti ukatulutse anthu anga, ana a Israyeli mu Igupto.’ Mulungu analonjeza kuthandiza Mose pantchitoyi.

Kodi chinthu chofunika chimene Mose anaphunzira pa chitsamba choyaka moto ndi chiyani?

Koma Mose anati kwa Mulungu: ‘Inde, ine nditati ndafika kwa ana a Israyeli ku Igupto, ndi kuwauza kuti Mulungu wandituma, koma iwo ndi kundifunsa kuti, Dzina lake ndani? Kodi ndikanene chiyani?’ Mulungu anauza Mose kuti akauze ana a Israyeli kuti: ‘Yehova ndiye wandituma kwa inu, ndipo wandiuza kuti Yehova ndilo dzina lake mpaka kalekale.’ (Eksodo 3:1-15) Izi zikusonyeza kuti Mulungu adzakhalabe ndi dzina lakuti Yehova, sadzalisintha. Mulungu anafuna kuti nthaŵi yonse azidziŵika ndi dzina lake limeneli lakuti Yehova.

Kodi Mulungu analidziŵitsa motani dzina lake pa Nyanja Yofiira?

Mose atabwerera ku Igupto, Aigupto anaganiza kuti Yehova anali Mulungu wamng’ono wa Aisrayeli komanso wopanda mphamvu. Sanaganize kuti iye anali Mulungu wa dziko lonse lapansi. Koma Yehova anauza mfumu ya Igupto kuti: ‘Ndidzadziŵitsa dzina langa pa dziko lonse lapansi.’ (Eksodo 9:16) Yehova anadziŵitsadi dzina lake. Kodi ukudziŵa mmene anachitira zimenezi?—

Eya, anauza Mose kutsogolera Aisrayeli kutuluka mu Igupto. Atafika pa Nyanja Yofiira, Yehova anakonza njira mwa kugaŵa nyanjayo. Aisrayeli anayenda mosavutika pansi pouma. Koma Farao ndi asilikali ake onse atayamba kuyenda pansi pa nyanja popanda madzipo, madzi amene anawaimitsa kumbali zonse ziŵiri anagwera Aiguptowo, ndipo onse anafa.

Posakhalitsa, anthu padziko lonse anayamba kumva zimene Yehova anachita pa Nyanja Yofiira. Kodi timadziŵa bwanji kuti anthu anamva nkhani imeneyi?— Eya, patapita zaka pafupifupi 40, Aisrayeli anafika m’dziko la Kanani lomwe Yehova analonjeza kuwapatsa. Kumeneko, mkazi wina dzina lake Rahabi anauza amuna aŵiri a ku Israyeli kuti: ‘Tinamva kuti Yehova anaumitsa madzi a m’Nyanja Yofiira pamaso panu, muja munatuluka mu Igupto.’—Yoswa 2:10.

Masiku ano anthu ambiri ali ngati Aigupto amenewo. Sakhulupirira kuti Yehova ndi Mulungu wa dziko lonse. Ndiye Yehova amafuna kuti anthu ake aziuza anthu ena za iye. Izi ndi zimene anachita Yesu. Ali pafupi kufa padziko lapansi, anauza Yehova m’pemphero kuti: ‘Ndinadziŵitsa iwo dzina lanu.’—Yohane 17:26.

Yesu anadziŵitsa anthu dzina la Mulungu. Kodi ungapeze pamene pali dzina la Mulungu m’Baibulo?

Kodi ukufuna kukhala ngati Yesu? Ndiyetu uziuza ena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Udzaona kuti anthu ambiri sadziŵa zimenezi. Mwina ukhoza kuwasonyeza lemba la m’Baibulo la Salmo 83:18. Tenga Baibulo tsopano ndipo tipeze lemba limeneli. Limati: “Kuti adziŵe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”

Kodi lemba limene taŵerengali likutiphunzitsa chiyani?— Inde, likutiphunzitsa kuti pa mayina onse, dzina lakuti Yehova ndi dzina lofunika kwambiri. Ndi dzina la Mulungu Wamphamvuyonse, Atate ake a Yesu komanso Yemwe anapanga zinthu zonse. Ndipo kumbukira kuti Yesu anati tifunika kukonda Yehova Mulungu ndi mtima wathu wonse. Kodi iwe Yehova umamukonda?—

Kodi tingasonyeze bwanji kuti Yehova timamukonda?— Njira imodzi ndi yakuti timudziŵe monga Bwenzi lathu. Njira ina ndiyo kuuza ena za dzina lake. Tingawasonyeze m’Baibulo kuti dzina lake ndi Yehova. Tingawauzenso zinthu zodabwitsa zimene Yehova anapanga ndiponso zinthu zabwino zimene wachita. Zimenezi Yehova zimamusangalatsa kwambiri chifukwa amafuna kuti anthu amudziŵe. Nafenso tiziuza ena zimenezi, eti?—

Si aliyense amene adzafuna kumvetsera pamene tikuwauza za Yehova. Anthu ambiri sanamvetsere ngakhale pamene Mphunzitsi Waluso, Yesu, anali kuwauza za Iye. Komatu zimenezo sizinalepheretse Yesu kulankhula za Yehova.

Ifenso tikhale ngati Yesu. Tisaleke kulankhula za Yehova. Tikamalankhula za Yehova Mulungu, iye adzakondwera nafe chifukwa chakuti dzina lake timalikonda.

Tsopano ŵerengerani limodzi m’Baibulo malemba ena angapo osonyeza kufunika kwa dzina la Mulungu: Yesaya 12:4, 5; Mateyu 6:9; Yohane 17:6; ndi Yoweli 2:32.