Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu 5

“Uyu Ndiye Mwana Wanga”

“Uyu Ndiye Mwana Wanga”

ANA akachita zinthu zabwino, amene amawasamalira amakondwera. Ngati mtsikana kapena mnyamata amachita bwino zinthu zinazake, atate ake amanyadira kuuza anzawo kuti: “Uyu ndi mwana wanga.”

Nthaŵi zonse Yesu amachita zimene zimakondweretsa Atate ake. Ndipotu Atate ake amamunyadira. Kodi ukukumbukira zimene anachita Atate ake a Yesu tsiku lina pamene Yesu anali ndi anzake atatu?— Inde, Mulungu analankhula kuchokera kumwamba ndi kuwauza kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.”—Mateyu 17:5.

Nthaŵi zonse Yesu amasangalala kuchita zinthu zimene zimakondweretsa Atate ake. Kodi ukudziŵa chifukwa chake? Ndi chifukwa chakuti Atate ake amawakonda kwambiri. Ngati munthu achita zinthu mokakamizika, zinthuzo zimavuta kuchita. Koma sizivuta ngati munthuyo akufunitsitsa kuzichita. Kodi ukudziŵa kuti kufunitsitsa n’kutani?— Kufunitsitsa ndi kukhala wokonzeka kuchita zinthu ndi mtima wonse.

Ngakhale asanabwere padziko lapansi, Yesu anali wofunitsitsa kuchita chilichonse chimene Atate ake anamuuza kuti achite. Anali kutero chifukwa chakuti amakonda Atate ake, Yehova Mulungu. Yesu anali ndi malo abwino kwambiri ndi Atate ake kumwamba. Koma Mulungu anali ndi ntchito yapadera imene anafuna kuti Yesu achite. Kuti agwire ntchito imeneyo, Yesu anafunika kuchokako kumwamba. Anafunika kubadwa monga mwana wakhanda padziko lapansi. Yesu anali wofunitsitsa kuchita zimenezi chifukwa ndi zimene Yehova anafuna kuti iye achite.

Kodi mngelo Gabrieli anamuuza chiyani Mariya?

Kuti Yesu abadwe ngati mwana wakhanda padziko lapansi, anafunika kukhala ndi amayi ake. Kodi ukudziŵa kuti amayi ake anali ndani?— Dzina lawo linali Mariya. Yehova anatumiza mngelo wake Gabrieli kuchokera kumwamba kuti akalankhule ndi Mariya. Gabrieli anauza Mariya kuti adzakhala ndi mwana wamwamuna. Mwanayo adzamupatsa dzina lakuti Yesu. Nanga ndani amene adzakhala atate ake a mwanayo?— Mngeloyo anati Atate ake a mwanayo adzakhala Yehova Mulungu. Ndicho chifukwa chake Yesu anatchedwa kuti Mwana wa Mulungu.

Kodi ukuganiza kuti Mariya anamva bwanji ndi nkhani imeneyi?— Kodi iye ananena kuti, “Sindifuna kukhala amayi ake a Yesu”? Ayi, Mariya anali wokonzeka kuchita zimene Mulungu anafuna. Koma kodi zikanatheka bwanji kuti Mwana wa Mulungu kumwamba adzabadwe monga khanda padziko lapansi? Kodi kubadwa kwa Yesu kunasiyana motani ndi kubadwa kwa ana ena onse? Kodi iwe umadziŵa?—

Eya, Mulungu anapanga makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, kuti azitha kukhala pamodzi mwa njira yodabwitsa. Akatero, mwana amayamba kukula m’mimba mwa amayi ake. Anthu amati izi ndi zozizwitsa! Ndikhulupirira kuti iwenso ukuvomereza.

Tsonotu Mulungu anachita chinthu china chimene chinali chodabwitsa kwambiri kuposa pamenepo. Anatenga moyo wa Mwana wake kumwamba ndi kuuika m’mimba mwa Mariya. Mulungu anali asanachitepo zimenezi, ndipo sanazichitenso mpaka pano. Zitachitika zodabwitsa izi, Yesu anayamba kukula m’mimba mwa Mariya mofanana ndi mmene ana ena onse amakulira m’mimba mwa amayi awo. Kenako Mariya anakwatiwa ndi Yosefe.

Nthaŵi itakwana yoti Yesu abadwe, Mariya ndi Yosefe anali akucheza m’mudzi wa Betelehemu. Koma m’mudzimo munafika anthu ambiri. M’nyumba zonse munali anthu moti Mariya ndi Yosefe anachita kukagona mu khola. Mariya anabereka mwana wake mmenemo, ndipo Yesu anamuika m’chodyeramo ziŵeto, monga ukuonera pachithunzi ichi.

N’chifukwa chiyani Yesu akumuika modyeramo ziŵeto?

Usiku umene Yesu anabadwa kunachitika zosangalatsa. Mngelo anaonekera kwa abusa ena amene anali pafupi ndi ku Betelehemu. Mngeloyu anawauza kuti Yesu anali munthu wofunika kwambiri. Anati: ‘Taonani! Ndikuuzani inu uthenga wabwino womwe udzasangalatsa anthu. Lero kwabadwa munthu amene adzapulumutsa anthu.’—Luka 2:10, 11.

Kodi mmodzi wa angeloŵa wawauza uthenga wabwino wotani abusawo?

Mngeloyo anauza abusa aja kuti Yesu akamupeza ku Betelehemu atagona mu chodyeramo ziŵeto. Ndiyeno mwadzidzidzi, angelo ena kumwamba anayamba kutamanda Mulungu limodzi ndi mngelo woyamba uja. Angelowo anali kuimba kuti: ‘Ulemerero ukhale kwa Mulungu, ndi mtendere pansi pano kwa anthu amene akondwera nawo.’—Luka 2:12-14.

Angelowo atachoka, abusa aja anapita ku Betelehemu nakapeza Yesu. Kumeneko anafotokozera Yosefe ndi Mariya zinthu zabwino zonse zimene anamva. Kodi ukutha kuona mmene Mariya analili wokondwa chifukwa chakuti anafunitsitsa kukhala amayi ake a Yesu?

Pambuyo pake, Yosefe ndi Mariya anakakhala ndi Yesu m’mudzi wa Nazarete. Yesu anakulira kumeneko. Atakula anayamba ntchito yake yaikulu yophunzitsa. Imeneyi inali ina mwa ntchito zimene Yehova Mulungu anafuna kuti Mwana wake agwire padziko lapansi. Yesu anali wofunitsitsa kugwira ntchito imeneyo chifukwa choti Atate ake akumwamba anawakonda kwambiri.

Yesu asanayambe ntchito yake monga Mphunzitsi Waluso, anabatizidwa kaye ndi Yohane Mbatizi mu mtsinje wa Yordano. Ndiyeno panachitika chinthu chodabwitsa! Pamene Yesu anali kutuluka m’madzi, Yehova analankhula kuchokera kumwamba. Anati: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:17) Kodi iwe susangalala makolo ako akakuuza kuti amakukonda?— Yesu nayenso ayenera kuti anasangalala.

Nthaŵi zonse Yesu anali kuchita zabwino. Sanayese kukhala ngati munthu wina. Sanauze anthu kuti anali Mulungu. Mngelo Gabrieli anauza Mariya kuti Yesu adzatchedwa Mwana wa Mulungu. Yesu mwiniyo anati anali Mwana wa Mulungu. Ndipo sanauze anthu kuti amadziŵa zinthu zambiri kuposa Atate ake. Iye anati: ‘Atate ndi wamkulu kuposa Ine.’—Yohane 14:28.

Ngakhale pamene Yesu anali kumwamba, anagwira ntchito iliyonse imene Atate ake anamupatsa. Sanali kunena kuti agwira koma ndi kuchita zina. Atate ake anali kuwakonda. Motero iye anali kumvera zimene Atate akewo anali kunena. Ndiyeno atabwera padziko lapansi, Yesu anachita zimene Atate ake akumwamba anamutumizira kudzachita. Sanathere nthaŵi yake kuchita zinthu zina. Mpake kuti Yehova amakondwera naye Mwana wake!

Ifenso tikufuna kusangalatsa Yehova, si choncho?— Ndiye tifunika kuonetsa kuti timamveradi Mulungu, monga anachitira Yesu. Mulungu amalankhula nafe kudzera m’Baibulo. Si bwino kuchita ngati tikumvera Mulungu pamene tikukhulupirira ndiponso kuchita zinthu zina zosagwirizana ndi Baibulo. Kodi ndi zabwino nanga zimenezo?— Ndipo kumbukira kuti ngati Yehova timamukondadi, tidzafuna kumukondweretsa.

Tsopano ŵerengani malemba ena aŵa a m’Baibulo amene akusonyeza zimene tifunika kudziŵa ndi kukhulupirira ponena za Yesu: Mateyu 7:21-23; Yohane 4:25, 26; ndi 1 Timoteo 2:5, 6.