Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu 14

Chifukwa Chake Tiyenera Kukhululukira Ena

Chifukwa Chake Tiyenera Kukhululukira Ena

KODI munthu wina anayamba wakuchitirapo choipa?— Kodi anakupweteka kapena kukunyoza?— Kodi iwe uyenera kumuchitiranso choipa monga anachitira iye?—

Anthu ambiri amabwezera wina akawapweteka. Komatu Yesu anaphunzitsa kuti tiyenera kukhululukira anthu amene atilakwira. (Mateyu 6:12) Nanga bwanji ngati munthuyo amatilakwira nthaŵi zambiri? Kodi tiyenera kumukhululukira kangati?—

Petro anafuna kudziŵa zimenezi. Ndiye tsiku lina anafunsa Yesu kuti: ‘Kodi ndiyenera kumukhululukira mpaka maulendo seveni?’ Komatu maulendo seveni ndi ochepa. Yesu anati: ‘Uyenera kumukhululukira maulendo 77’ ngati munthuyo wakulakwira kambirimbiri maulendo amenewo.

Kodi Petro anafuna kudziŵa chiyani pa nkhani ya kukhululukira ena?

Ameneŵatu ndi maulendo ambiri zedi! Sitingakumbukire n’komwe zinthu zoipa zochuluka moteromo zimene ena amatichitira, kodi tingakumbukire ngati? Tsono mfundo ya Yesu pamenepa inali yakuti: Sitifunika kukumbukira kuchuluka kwa zoipa zimene ena amatichitira. Iwo akatipempha kuti tiwakhululukire, tiyenera kuwakhululukira.

Yesu anafuna kusonyeza ophunzira ake kuti kukhululukira ena ndi kofunika kwambiri. Choncho atayankha funso la Petro, anawafotokozera nkhani inayake. Kodi ukufuna ndikuuze nkhaniyo?—

Kalekale kunali mfumu ina yabwino. Inali mfumu yokoma mtima zedi. Inali kubwereka akapolo ake ndalama akafunika thandizo. Koma tsiku lina mfumuyo inafuna kuti akapolowo abweze ndalama zimene anabwerekazo. Ndiye panabwera kapolo wina amene anabwereka ndalama zokwana 60,000,000 kwa mfumuyo. Izi ndi ndalama zambiri zedi!

Kodi chinachitika ndi chiyani kapoloyu atapempha mfumu kuti imuyembekeze?

Koma kapoloyo anali atawononga ndalama zonsezo ndipo sanathe kubwezera mfumuyo kalikonse. Motero mfumu ija inalamula kuti amugulitse. Mfumuyo inanenanso kuti agulitse mkazi wake wa kapoloyo ndi ana ake omwe komanso katundu wake yense. Ndiye ndalama zimene zikanapezeka pogulitsa onsewo, akanatha kubwezera mfumu ija tsopano. Kodi ukuganiza kuti kapoloyo anamva bwanji ndi zimenezi?—

Anagwada pamaso pa mfumuyo ndi kupempha kuti: ‘Chonde mundiyembekeze, ndikubwezerani zonse zimene ndinatenga.’ Iweyo ukanakhala kuti ndiwe mfumu imeneyi, kodi kapoloyu ukanamuchita chiyani?— Mfumuyi inamvera chisoni kapolo wake. Motero inamukhululukira. Inauza kapoloyo kuti asabweze ndalama iliyonse, ngakhale imodzi yokha mwa ndalama 60,000,000 zija. Kapoloyo ayenera kuti anasangalala kwambiri ndi zimenezi!

Koma kodi kenako kapoloyo anachita chiyani? Anachoka ndi kukapeza kapolo wina yemwe iye anamubwereka ndalama 100 zokha basi. Anagwira kapolo mnzakeyo pakhosi. Uku akukanyanga pakhosipo, anati: ‘Bwezera ndalama 100 zija unabwereka!’ Kodi ukuganiza kuti munthu wabwinobwino angachitire mnzake zoterezi, makamaka pamene mfumu yamukhululukira ngongole yaikulu kwambiri?—

Kodi kapoloyu anamutani kapolo mnzake atalephera kumubwezera ndalama zake?

Tsonotu kapolo amene anabwereka ndalama 100 uja anali wosauka. Sakanatha kubweza ndalamazo nthaŵi yomweyo. Motero anagwada pansi ndi kupempha kapolo mnzakeyo kuti: ‘Chonde mundiyembekeze, ndidzakubwezerani ndalama zanu.’ Kodi munthuyu anafunika kuyembekeza kapolo mnzakeyo kuti apeze ndalama?— Kodi ukanakhala iwe ukanatani?—

Munthuyu anali woipa mtima, anasiyana ndi mfumu ija. Anafuna kuti amupatse ndalama zake pomwepo. Ndipo popeza kapolo mnzakeyo sanathe kumupatsa ndalamazo, anamuika mu ndende. Akapolo ena anaona zonse zimene zinachitika, ndipo sanasangalale nazo. Anawamvetsa chisoni kapolo yemwe anaikidwa m’ndendeyo. Choncho anakanena nkhaniyi kwa mfumu ija.

Mfumunso sinagwirizane nazo. Inakwiya naye kapolo wosakhululukira mnzakeyo. Moti inaitanitsa kapoloyo ndi kumuuza kuti: ‘Kapolo woipa iwe, kodi ine sindinakukhululukire zimene ndinakubwereka? Nanga bwanji iwe sunakhululukire kapolo mnzako?’

Kodi mfumu imamutani kapolo wosakhululukira mnzake?

Kapolo wosakhululukira enayo anafunika kutengapo phunziro pa zimene mfumu yabwinoyo inachita. Koma ayi ndithu sanaphunzirepo kalikonse. Ndiye chifukwa cha zimenezi mfumuyo inaika kapoloyo m’ndende kuti akhale momwemo mpaka atabweza ndalama zonse zija 60,000,000. Ndipotu kundende sakanapeza ndalama zoti abwezere mfumu. Zinangoonetsa kuti akakhala kumeneko mpaka kufa.

Yesu pomaliza kufotokoza nkhaniyi, anauza ophunzira ake kuti: ‘Atate wanga wakumwamba adzakuchitirani zomwezi, ngati simukhululukira abale anu ndi mtima wonse.’—Mateyu 18:21-35.

Tonsefe Mulungu watichitira zambiri. Inde, moyo wathuwu umachokera kwa Mulunguyo! Motero poyerekeza ndi zimene ife timalakwira Mulungu, zimene anthu ena amatilakwira ndi zochepa zedi. Zimene iwo amatilakwira zili ngati ndalama 100 zija zimene kapolo wina anabwereka kwa mnzake. Koma zimene ife timalakwira Mulungu chifukwa cha zoipa zimene timachita, zili ngati ndalama 60,000,000 zija zimene kapolo anabwereka kwa mfumu.

Mulungu ndi wokoma mtima kwambiri. Amatikhululukira ngakhale kuti timachita zinthu zoipa. Satiuza kuti tilipire zolakwa zathu mwa kutilanda moyo mpaka kalekale. Komatu tifunika kukumbukira mfundo iyi: Mulungu amatikhululukira pokhapokha ngati ifeyo timakhululukira anthu amene amatilakwira. Imeneyitu ndi mfundo yofunika kwambiri, si choncho?—

Kodi iwe udzachita chiyani munthu wina akakupempha kuti umukhululukire?

Ndiye ngati munthu wina atakupweteka koma ndi kukupepesa, kodi iwe udzachita chiyani? Kodi udzamukhululukira?— Nanga bwanji zitachitika maulendo ambiri? Kodi udzamukhululukirabe?—

Ngati titakhala ifeyo amene tikufuna kuti munthu wina atikhululukire, tidzafunitsitsa ndithu kuti munthuyo atikhululukire, si choncho?— Ndiye ifenso tiyenera kumukhululukira. Tizikhululukadi zenizeni kuchokera pansi pa mtima, osangonena pakamwa pokha. Tikamachita zimenezi timaonetsa kuti tikufunadi kukhala ophunzira a Mphunzitsi Waluso.

Kuti timvetse kufunika kwa kukhululukira ena, tiye tiŵerengenso Miyambo 19:11; Mateyu 6:14, 15; ndi Luka 17:3, 4.