Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu 23

Chifukwa Chake Anthufe Timadwala

Chifukwa Chake Anthufe Timadwala

KODI pali munthu wodwala amene ukumudziŵa?— Nthaŵi zina nawenso umadwala. Mwina umadwala chifuwa, kapena umamva m’mimba kupweteka. Anthu ena amadwala kwambiri. Satha kuimirira okha popanda wina kuwagwira. Kaŵirikaŵiri izi zimachitika anthu akakalamba kwambiri.

Aliyense amadwala nthaŵi zina. Kodi ukudziŵa chifukwa chake anthu amadwala, kukalamba, ndi kufa?— Tsiku lina anthu ena anatenga munthu wina amene sanali kutha kuyenda ndi kupita naye kwa Yesu, ndipo Yesu anasonyeza chifukwa chake anthu amadwala ndi kufa. Taleka ndikuuze nkhani yake.

Yesu anali kukhala m’nyumba inayake m’mudzi womwe unali pafupi ndi nyanja ya Galileya. Anthu ambiri anabwera kudzamuona. Panafika anthu ochuluka kwambiri moti m’nyumbamo munalibe malo oti anthu ena ndi kutha kuloŵanso. Munthu anali kulephera ngakhale kufika pakhomo. Koma anthu anali kubwerabe! Kagulu kena ka anthu kanabwera ndi munthu wofa ziwalo yemwe sanali kutha kuyenda. Anthu aamuna folo anachita kumunyamulira pa kabedi kamene anali kugonapo.

Kodi ukudziŵa chifukwa chake iwo anafuna kupita kwa Yesu ndi munthu wodwalayu?— Iwo anali ndi chikhulupiriro kuti Yesu akamuthandiza. Anali kukhulupirira kuti Yesu akamuchiritsa matendawo. Kodi ukudziŵa kuti munthu wofa ziwaloyu anafika naye bwanji kwa Yesu pamene m’nyumbamo munali modzaza anthu?—

Eya, chithunzi ichi chili apa chikuonetsa mmene anachitira zimenezo. Iwo choyamba anakweza munthuyu padenga. Linali denga lafulati. Kenako anabowola dengalo malo aakulu ndithu. Atatero munthu wodwala uja ali pa kabedi kake kaja, anamuloŵetsa m’nyumbamo kudzera pa chibowo anabowolacho. Komatu anali ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri!

Anthu onse m’nyumbamo anadabwa poona zimene zinali kuchitika. Munthu wofa ziwalo uja ali pa kabedi kake anafika pagulupo. Kodi ukuganiza kuti Yesu anakwiya poona zimene anthuŵa anachita?— Sanakwiye ngakhale pang’ono! Iye anasangalala kuona kuti iwo anali ndi chikhulupiriro. Anauza munthu wofa ziwaloyo kuti: ‘Machimo ako akhululukidwa.’

Kodi Yesu anauza munthu wofa ziwalo uyu kuti achite chiyani?

Anthu ena m’gululo anaganiza kuti Yesu sanayenere kunena mawu ameneŵa. Iwo anali kuganiza kuti Yesu sangakhululukire munthu machimo. Motero kuti asonyeze kuti akhozadi kukhululukira machimo, Yesu anauza munthu uja kuti: ‘Nyamuka, tenga bedi lako uzipita kwanu.’

Yesu atanena zimenezi, munthu uja anachira! Ziwalo zake sizinalinso zakufa. Ndiye anatha kudzuka yekha ndi kumayenda. Anthu amene anaona zodabwitsa zimenezi anadabwadi kwambiri. Chibadwire chawo anali asanaonepo zodabwitsa zoterozo! Analemekeza Yehova powapatsa Mphunzitsi Waluso ameneyu, amene anali kuchiritsanso anthu odwala.—Marko 2:1-12.

Kodi chodabwitsa ichi chikutiphunzitsa chiyani?

Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zodabwitsa zimenezi?— Tikuphunzira kuti Yesu ali ndi mphamvu zokhululukira machimo ndi kuchiritsa anthu odwala. Koma tikuphunziraponso mfundo ina yofunika kwambiri. Tikuphunzira kuti anthu amadwala chifukwa cha uchimo.

Popeza kuti tonsefe nthaŵi zina timadwala, kodi ndiye kuti tonse ndife ochimwa?— Inde, Baibulo limanena kuti tonsefe timabadwa ndi uchimo. Kodi umadziŵa kuti kubadwa ndi uchimo kumatanthauza chiyani?— Kumatanthauza kuti timabadwa opanda ungwiro. Nthaŵi zina timachita zinthu molakwika, ngakhale kuti sitikufuna kutero. Kodi ukudziŵa kuti tonsefe tinakhala bwanji ndi uchimo?—

Tinabadwa ochimwa chifukwa chakuti munthu woyamba, Adamu, sanamvere Mulungu. Iye anachimwa pamene anaswa lamulo la Mulungu. Ndiye tonse tinatengera uchimo kwa Adamuyo. Kodi ukudziŵa kuti tinatengera bwanji uchimowo? Taleka ndiyese kukufotokozera moti usavutike kumva.

Kodi zinakhala bwanji kuti tonsefe tikhale ndi uchimo?

Mwinamwake unaonapo munthu akuphika buledi kapena chikondamoyo m’chiwaya. Kodi bulediyo kapena chikondamoyocho chingaoneke motani ngati chiwayacho ndi choloŵa m’kati penapake? Iwe ukuganiza bwanji?— Buledi yense amene angapange m’chiwaya chimenecho adzakhalanso ndi penapake poloŵa m’kati, si choncho?—

Adamu anali ngati chiwaya chimenecho, ndipo ife tili ngati buledi. Ataswa lamulo la Mulungu anakhala wopanda ungwiro. Zinali ngati kuti anakhala ndi penapake poloŵa m’kati, kapena kuti mbali yolakwika. Ndiye atakhala ndi ana, unganene kuti anawo anali otani?— Ana ake onse analandira mbali yolakwika imeneyi ya kupanda ungwiro.

Ana ambiri sabadwa ndi cholakwika chachikulu chimene ungachione. Sabadwa opanda dzanja kapena mwendo. Koma iwo amakhala opanda ungwiro ndithu moti amadwala ndipo m’kupita kwa nthaŵi amafa.

Ndi zoona kuti anthu ena amadwala kaŵirikaŵiri kusiyana ndi ena. Kodi chifukwa chake ndi chiyani? Kodi ndi chifukwa chakuti iwo amabadwa ndi uchimo wambiri?— Ayi, tonse timabadwa ndi uchimo wofanana. Tonse timabadwa opanda ungwiro. Motero m’kupita kwa nthaŵi aliyense amadwala ndithu matenda enaake. Ngakhale anthu amene amamvera malamulo onse a Mulungu ndipo palibe choipa chenicheni chimene amachita, nawonso amadwala.

Kodi tidzakhala ndi moyo wotani

uchimo wathu ukadzachoka?

Nangano ndi chifukwa chiyani anthu ena amadwala kaŵirikaŵiri kusiyana ndi ena?— Pali zifukwa zambiri. Mwina iwo sakhala ndi chakudya chokwanira. Kapena mwina amadya chakudya chosayenera. Nthaŵi zambiri angamadye chakudya chosapatsa thanzi. Chifukwa china chingakhale chakuti amachedwa kugona moti sagona tulo tokwanira. Kapena mwina savala zovala zokwanira kuti azimva kutenthera pamene kukuzizira. Anthu ena matupi awo ndi ofooka kwambiri moti amalephera kulimbana ndi matenda, ngakhale iwo ayesetse bwanji kudzisamalira.

Kodi idzakhalapo nthaŵi yoti sitidzadwalanso? Kodi uchimo udzatichoka?— Eya, kodi munthu wofa ziwalo uja Yesu anamuchitira chiyani?— Yesu anamukhululukira machimo ake ndi kumuchiritsa. Mwa kuchita zimenezi, Yesu anasonyeza zimene tsiku lina adzachitira onse amene amayesetsa kuchita zabwino.

Tikamaonetsa kuti sitifuna kuchimwa ndipo timadana ndi zoipa, Yesu adzatichiritsa. M’tsogolomu iye adzachotsa kupanda ungwiro kumene tili nako. Adzachita zimenezi pokhala kuti iye ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Sadzatichotsera uchimo wonse nthaŵi imodzi. Adzauchotsa pang’onopang’ono kwa kanthaŵi ndithu. Ndiyeno uchimo wathu wonse utatha, sitidzadwalanso. Tonse tidzakhala ndi moyo wangwiro. Zidzakhala zosangalatsatu kwambiri!

Kuti mupeze mfundo zina za mmene uchimo umakhudzira munthu aliyense, ŵerengani Yobu 14:4; Salmo 51:5; Aroma 3:23; 5:12; ndi Aroma 6:23.