Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu 29

Kodi Mapwando Onse Amakondweretsa Mulungu?

Kodi Mapwando Onse Amakondweretsa Mulungu?

Ndi chifukwa chiyani chisangalalo ichi chinakondweretsa Mulungu?

KODI umakonda kupita kuphwando?— Nthaŵi zina mapwando amasangalatsa kwambiri. Kodi ukuganiza kuti Mphunzitsi Waluso amafuna kuti tizipita kumapwando?— Eya, iye limodzi ndi ophunzira ake ena anapita ku chikwati cha munthu winawake, ndipo limenelo linali phwando ndithu. Yehova ndi ‘Mulungu wosangalala,’ motero zimamukondweretsa tikamasangalala pamapwando abwino.—1 Timoteo 1:11, NW; Yohane 2:1-11.

Buku lino patsamba 29 linatiuza kuti Yehova anagaŵa Nyanja Yofiira pofuna kuti Aisrayeli adutsepo. Kodi ukukumbukira kuti tinaŵerenga nkhani imeneyi?— Atawoloka, anthuwo anaimba nyimbo, anavina, ndiponso anayamika Yehova. Anali pachisangalalo. Iwo anasangalala kwambiri, ndipo ndi zosakayikitsa kuti Mulungu nayenso anasangalala.—Eksodo 15:1, 20, 21.

Patapita pafupifupi zaka 40, Aisrayeli anapita kuphwando linanso lalikulu. Anthu amene anawaitana ku phwando limeneli sanali kulambira Yehova. Iwo anali kulambira milungu ina ndiponso anali kugonana ndi anthu amene sanakwatirane nawo. Kodi iwe ukuganiza kuti panali bwino ndithu kuti Aisrayeli apite kuphwando lotereli?— Yehovatu sizinamukondweretse, moti Aisrayeliwo anawalanga.—Numeri 25:1-9; 1 Akorinto 10:8.

Baibulo limatchulanso mapwando aŵiri okondwerera tsiku limene anthu ena anabadwa. Kodi phwando limodzi mwa aŵiriwo linali lokondwerera kubadwa kwa Mphunzitsi Waluso?— Ayi. Mapwando aŵiri onsewo anali a anthu amene sanali kutumikira Yehova. Limodzi linali lokondwerera tsiku limene anabadwa Mfumu Herode Antipa. Iye anali kulamulira dera la Galileya panthaŵi imene Yesu anali kukhala kumeneko.

Mfumu Herode inachita zinthu zoipa zambiri. Inakwatira mkazi wa mbale wake. Mkaziyo dzina lake anali Herodiya. Yohane Mbatizi, yemwe anali mtumiki wa Mulungu, anauza Herode kuti analakwa kuchita zimenezo. Izi Herode sanasangalale nazo. Ndiye anatsekera Yohaneyo mu ndende.—Luka 3:19, 20.

Pamene tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode linakwana, Yohane anali kundende kuja. Patsikulo Herode anakonza phwando lalikulu. Anaitana anthu otchuka ambiri. Onsewo anadya ndi kumwa, ndipo anasangalala. Kenako mwana wamkazi wa Herodiya anayamba kuvina. Ndiye anavina bwino kwambiri moti aliyense anasangalala ndipo Mfumu Herode inafuna kumupatsa mphatso yapadera. Herode anauza mtsikanayo kuti: “Chilichonse ukandipempha ndidzakupatsa, kungakhale kukugaŵira ufumu wanga.”

Kodi iye akanapempha kuti amupatse chiyani? Ndalama? zovala zokongola? kapena chinyumba chabwino? Mtsikanayu sanadziŵe chopempha. Ndiye anangopita kwa amayi ake, Herodiya, ndi kuwafunsa kuti: ‘Kodi ndikapemphe chiyani?’

Tsonotu Herodiya anali kudana naye kwambiri Yohane Mbatizi. Moti anauza mwana wakeyo kukapempha mutu wa Yohaneyo. Mtsikana uja anapita kwa mfumu ija ndi kunena kuti: ‘Ndifuna mundipatse mu mbale tsopano apa, mutu wa Yohane Mbatizi.’

Mfumu Herode sinafune kupha Yohane chifukwa chakuti inali kudziŵa kuti Yohane anali munthu wabwino. Koma Herode analonjeza, ndipo anaopa kuti anthu ena amene anali paphwandopo angayambe kuganiza zina ngati iye asintha maganizo ake. Choncho anatuma munthu kupita kundende kukadula mutu wa Yohane. Mosakhalitsa munthuyo anabwerako. Anali ndi mutu wa Yohane mu mbale ndipo anaupereka kwa mtsikana uja. Kenako mtsikanayo anapereka mutuwo kwa amayi ake.—Marko 6:17-29.

Phwando lina lokondwerera tsiku la kubadwa limene Baibulo limasimba nalonso silinali labwino. Linali la mfumu ya ku Igupto. Paphwando ilinso, mfumu inadula mutu wa munthu wina. Kenako, munthu wodulidwa mutuyo anamupachika pamtengo kuti mbalame zidye! (Genesis 40:19-22) Kodi ukuganiza kuti mapwando aŵiri amenewo Mulungu anagwirizana nawo?— Kodi iwe ukanakonda kupita kumapwando amenewo?—

Kodi chinachitika ndi chiyani paphwando lokondwerera tsiku limene Herode anabadwa?

Tikudziŵa kuti chilichonse chimene chili m’Baibulo chili ndi cholinga chake. Baibulo limangotchula mapwando aŵiri okha okondwerera tsiku la kubadwa. Ndipo pamapwando onse aŵiri panachitika zinthu zoipa pamene anthuwo anali kusangalala. Ndiye pamenepa iwe unganene kuti Mulungu akutiuza chiyani za mapwando okondwerera tsiku la kubadwa? Kodi Mulungu amafuna kuti tizikondwerera masiku amene tinabadwa?—

Ndi zoona kuti masiku ano pamapwando otero anthu sadula mutu wa munthu wina. Komatu kukondwerera masiku a kubadwa anakuyambitsa ndi anthu amene sanali kulambira Mulungu woona. Pothirira ndemanga pa mapwando okondwerera masiku a kubadwa otchulidwa m’Baibulo, buku lina limati: “Anthu ochimwa okha ndiwo . . . amasangalalira kwambiri tsiku limene anabadwa.” (The Catholic Encyclopedia) Kodi ife tikufuna kukhala ngati iwowo?—

Nanga bwanji Mphunzitsi Waluso? Kodi naye anakondwerera tsiku limene anabadwa?— Ayi, Baibulo silitchula kuti panali phwando lililonse lokondwerera tsiku limene Yesu anabadwa. Ndipotu, ophunzira oyambirira a Yesu sanakondwerere kubadwa kwake. Kodi ukudziŵa chifukwa chake anthu kenako anasankha kumakondwerera kubadwa kwa Yesu pa December 25?—

Anasankha tsiku limenelo chifukwa chakuti “kuyambira kale patsikuli anthu a ku Roma anali kuchita Phwando la Saturn pokondwerera kubadwa kwa dzuŵa.” (The World Book Encyclopedia) Ukuona tsono, anthu anasankha kukondwerera kubadwa kwa Yesu pa tsiku limene anthu akunja anali kale kukhala ndi holide!

Kodi ukudziŵa chifukwa chake sizingakhale kuti Yesu anabadwa mu December?— Ndi chifukwa chakuti Baibulo limanena kuti panthaŵi imene Yesu anabadwa, abusa anali adakali kutchire usiku. (Luka 2:8-12) Iwotu sakanakhala ali kutchireko m’mwezi wa December pamene kumazizira ndiponso kumagwa mvula.

Ndi chifukwa chiyani sizingakhale kuti Yesu anabadwa pa December 25?

Anthu ambiri amadziŵa kuti Yesu sanabadwe pa tsiku la Khirisimasi. Amadziŵanso kuti pa tsiku limenelo anthu akunja anali kuchita phwando limene Mulungu sanali kukondwera nalo. Ngakhale ndi choncho anthu ambiri amakondwererabe Khirisimasi. Zimene iwo amafuna kwambiri ndi kuchita phwando, koma safuna kudziŵa maganizo a Mulungu pa phwandolo. Komatu ife timafuna kukondweretsa Yehova, si choncho?—

Ndiye pamene tikhala ndi mapwando, tizionetsetsa kuti ndi mapwando amene Yehova amanena kuti ndi abwino. Tingachite mapwando ameneŵa nthaŵi ina iliyonse pachaka. Sitifunika kuchita kudikira tsiku lapadera. Tingadye chakudya chimene sitidya masiku onse komanso tingaseŵere maseŵera osangalatsa. Kodi ungakonde kuchita zimenezi?— Mwina ungakambirane nkhaniyi ndi makolo ako ndi kupangana nawo zoti tsiku lina adzakuthandize kukonza phwando. Zimenezi zingakhale zosangalatsa kwambiri, ukuona bwanji iwe?— Koma usanakonze zokhala ndi phwando, ufunika kuonetsetsa kuti lidzakhala phwando lokondweretsa Mulungu.

Kodi tingachite chiyani kuti mapwando athu azikondweretsa Mulungu?

Nthaŵi zonse ndi pofunika kuchita zimene zimakondweretsa Mulungu, ndipo zimenezi zasonyezedwanso pa Miyambo 12:2; Yohane 8:29; Aroma 12:2; ndi 1 Yohane 3:22.