Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu 36

Kodi Ndani Adzauka kwa Akufa? Nanga Adzakhala Kuti?

Kodi Ndani Adzauka kwa Akufa? Nanga Adzakhala Kuti?

MU MITU iŵiri yathayi, kodi tinamva kuti ndi anthu angati amene anaukitsidwa kwa akufa?— Tinamva kuti ndi anthu faifi. Nanga ana analipo angati?— Anali atatu. Ndipo wafolo anali mnyamata. Kodi ukuganiza kuti zonsezi zikutiuza chiyani?—

Eya, zikungotiuza kuti Mulungu amakonda ana ndi achinyamata. Ndipo iye adzaukitsanso akufa ena ambiri. Kodi Mulungu adzangoukitsa anthu okha amene anachita zabwino?— Mwina tingaganize zimenezo. Komatu anthu ambiri sanaphunzirepo choonadi cha Yehova Mulungu ndi Mwana wake. Choncho iwo anachita zoipa chifukwa chakuti anaphunzitsidwa zinthu zolakwika. Kodi ukuganiza kuti Yehova adzaukitsa anthu ngati ameneŵa kwa akufa?—

Baibulo limanena kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Kodi ndi chifukwa chiyani anthu osalungama, kapena kuti amene sanachite zabwino, adzaukitsidwa?— Ndi chifukwa chakuti iwo analibe mwayi wophunzira za Yehova ndi zimene iye amafuna kuti anthu achite.

Kodi ndi chifukwa chiyani Mulungu adzaukitsa anthu ena amene sanali kuchita zabwino?

Kodi ukuganiza kuti anthu adzaukitsidwa liti?— Ukukumbukira, Lazaro atamwalira Yesu analonjeza Marita kuti: “Mlongo wako adzauka.” Marita anayankha kuti: “Ndidziŵa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.” (Yohane 11:23, 24) Kodi Marita anatanthauza chiyani pamene ananena kuti Lazaro adzauka “tsiku lomaliza”?—

Kodi Paradaiso amene Yesu akuuza munthu uyu ali kuti?

Chabwino, apa Marita anali atamvapo kale lonjezo la Yesu lakuti: ‘Onse ali m’manda adzatulukamo.’ (Yohane 5:28, 29) Choncho “tsiku lomaliza” ndi pamene onse amene Mulungu akuwakumbukira adzaukitsidwa kukhalanso ndi moyo. Tsiku lomaliza limeneli si la maola 24 ayi. Lidzakhala tsiku la zaka wanisauzande. Pa tsiku limeneli, Baibulo limati, ‘Mulungu adzaweruza anthu okhala padziko.’ Anthu amene adzaweruza akuphatikizapo amene adzaukitsidwa kwa akufa.—Machitidwe 17:31; 2 Petro 3:8.

Koma ndiye tsiku limeneli lidzakhala losangalatsatu kwambiri! M’kati mwa tsiku limeneli la zaka wanisauzande, anthu mamiliyoni ambiri amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo. Yesu anati malo amene iwo adzakhalako ndi moyo ndi Paradaiso. Tiye tione kumene Paradaisoyu adzakhala ndi mmene zinthu zidzakhalira mmenemo.

Kutatsala pafupifupi maola atatu kuti Yesu afe pamtengo wozunzirapo, iye analankhula za Paradaiso kwa mwamuna wina amenenso anali pamtengo pafupi naye. Munthu ameneyu anali kuphedwa chifukwa chophwanya malamulo. Koma pamene munthu ameneyu anali kuyang’ana Yesu ndi kumva zimene anthu anali kunena za Iye, anayamba kukhulupirira Yesuyo. Kenako munthuyo anati: “Ndikumbukireni mmene muloŵa Ufumu wanu.” Ndiye Yesu anayankha kuti: ‘Indetu, ndinena ndi iwe lerolino, udzakhala ndi ine m’Paradaiso.’—Luka 23:42, 43.

Kodi tikamaŵerenga za Paradaiso tiziganiza za chiyani?

Kodi Yesu anali kutanthauza chiyani pamene ananena zimenezi? Kodi Paradaiso ali kuti?— Taganiza kaye, kodi poyamba Paradaiso anali kuti?— Ndiganiza ukukumbukira kuti Mulungu anapatsa munthu woyamba, Adamu, ndi mkazi wake paradaiso woti akhalemo pompano padziko lapansi. Paradaiso ameneyo anali kutchedwa munda wa Edene. Mu munda umenewo munali nyama, koma sizinawapweteke. Munalinso mitengo yambiri yobala zipatso zokoma, ndipo munali mtsinje waukulu. Malo amenewo anali osangalatsa kukhalamo!—Genesis 2:8-10.

Ndiye tikamaŵerenga zoti munthu uja wophwanya malamulo adzakhala mu Paradaiso, tiziganiza za dziko lathuli litasanduka malo okongola kwambiri osangalatsa kukhalamo. Kodi zikutanthauza kuti Yesu adzakhala padziko lapansi pano mu Paradaiso limodzi ndi munthu ameneyu amene kale anali wophwanya malamulo?— Ayi. Kodi ukudziŵa chifukwa chake?—

Ndi chifukwa chakuti Yesu adzakhala akulamulira kumwamba monga Mfumu ya Paradaiso wa padziko lapansi. Choncho Yesu adzakhala ndi munthu ameneyo m’njira yakuti adzamuukitsa kwa akufa ndi kumupatsa zosoŵa zake. Koma nanga ndi chifukwa chiyani Yesu adzalola munthu amene kale anali kuphwanya malamulo kukhala mu Paradaiso?— Tiye tione ngati tingapeze yankho.

Kodi munthu ameneyu asanalankhule ndi Yesu, anali kudziŵa zolinga za Mulungu?— Ayi, sanali kudziŵa. Iye anali kuchita zinthu zoipa chifukwa chakuti sanali kudziŵa choonadi cha Mulungu. Ndiye mu Paradaiso adzaphunzitsidwa zolinga za Mulungu. Kenako adzakhala ndi mpata wosonyeza kuti amakondadi Mulungu mwa kuchita zimene Mulunguyo amafuna.

Kodi munthu aliyense amene adzauka kwa akufa adzakhala mu Paradaiso padziko lapansi pano?— Ayi, sadzatero. Kodi ukudziŵa chifukwa chake?— Ndi chifukwa chakuti ena amene adzauka kwa akufa adzakhala ndi Yesu kumwamba. Iwo adzalamulira dziko lapansi la Paradaiso limodzi ndi Yesu monga mafumu. Tiye tione mmene tikudziŵira zimenezi.

Usiku woti maŵa lake Yesu aphedwa, iye anauza atumwi ake kuti: ‘M’nyumba ya Atate wanga kumwamba, muli malo okhalamo ambiri, ndipo ndipita kukukonzerani malo.’ Kenako Yesu anawalonjeza kuti: ‘Ndidzabweranso, ndipo ndidzakulandirani; kuti kumene kuli Ine, inunso mukakhale kumeneko.’—Yohane 14:2, 3.

Kodi Yesu anapita kuti atauka kwa akufa?— Inde, anapita kumwamba kukakhalanso ndi Atate ake. (Yohane 17:4, 5) Choncho Yesu anali kulonjeza atumwi ake ndi anthu ena omutsatira kuti adzawaukitsa kwa akufa kuti akakhale ndi iye kumwamba. Kodi kumwambako adzakhala akuchita chiyani limodzi ndi Yesu?— Baibulo limanena kuti ophunzira ake amene adzauka pa “kuuka koyamba” adzakhala kumwamba ndi kulamulira dziko lapansi monga ‘mafumu pamodzi ndi Iye zaka wanisauzande.’—Chivumbulutso 5:10; 20:6; 2 Timoteo 2:12.

Kodi ndi anthu angati amene adzauka pa “kuuka koyamba” kenako kukalamulira ndi Yesu monga mafumu?— Yesu anauza ophunzira ake kuti: ‘Musaope, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.’ (Luka 12:32) “Kagulu ka nkhosa” kameneka, ka anthu amene adzauka kwa akufa kukakhala ndi Yesu mu Ufumu wa kumwamba, kali ndi chiŵerengero chake. Baibulo limasonyeza kuti amene adzauka kuchoka padziko lapansi kupita kumwamba ndi 144,000.—Chivumbulutso 14:1, 3.

Kodi ouka kwa akufa adzakhala kuti, ndipo adzachita chiyani?

Nanga ndi anthu angati amene adzakhala mu Paradaiso padziko lapansi?— Baibulo silinena. Mulungu anauza Adamu ndi Hava pamene anali m’munda wa Edene kuti abale ana ndi kudzaza dziko lapansi. Koma iwo analephera zimenezo. Ndiye Mulungu adzaonetsetsa kuti cholinga chake chakuti dziko lapansi lidzaze anthu abwino chakwaniritsidwa.—Genesis 1:28; Yesaya 45:18; 55:11.

Koma ndiye kukhala mu Paradaiso kudzasangalatsa kwambiri! Dziko lonse lapansi lidzakhala lokongola ngati munda wa maluŵa. Mudzakhala mbalame zambiri ndi nyama, komanso lidzakongola ndi mitengo ndi maluŵa a mtundu uliwonse. Palibe amene adzamva kupweteka m’thupi chifukwa chodwala, ndipo wina aliyense sadzafa. Anthu onse adzakhala mabwenzi. Ngati tikufuna kukhala ndi moyo wosatha mu Paradaiso, nthaŵi yokonzekera ndi ino.

Ŵerengani zinanso zokhudza cholinga cha Mulungu pa dziko lapansi, pa Miyambo 2:21, 22; Mlaliki 1:4; Yesaya 2:4; 11:6-9; 35:5, 6; ndi 65:21-24.