Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu 38

Chifukwa Chake Tiyenera Kukonda Yesu

Chifukwa Chake Tiyenera Kukonda Yesu

YEREKEZERA kuti uli mu boti limene likumira. Kodi ungafune kuti munthu wina akupulumutse?— Bwanji ngati munthuyo wachita kutaya moyo wake kuti apulumutse iwe?— Eya, izitu ndi zimene Yesu Kristu anachita. Ndiganiza ukukumbukira kuti mu Mutu 37 tinaphunzira kuti iye anapereka moyo wake kukhala dipo kuti ife tipulumutsidwe.

Ndi zoona kuti Yesu sakutipulumutsa kuti tisamire m’madzi. Kodi paja akutipulumutsa ku chiyani? Kodi ukukumbukira?— Akutipulumutsa ku uchimo ndi imfa zimene tonse tinatengera kwa Adamu. Ngakhale kuti anthu ena amachita zinthu zoipa kwambiri, nawonso Yesu anawafera. Kodi iwe ungaike moyo wako pachiswe pofuna kupulumutsa anthu oterowo?—

Baibulo limati: ‘Ndi zovuta kuti wina afere munthu wolungama; kapena wina angalimbe mtima kufera munthu wabwino.’ Komatu Baibulo limafotokoza kuti Yesu ‘anafera anthu osapembedza.’ Zimenezitu zikuphatikizapo anthu amene satumikira Mulungu! Baibulo limanenanso kuti: ‘Pamene tinali ochimwabe [tinali kuchitabe zinthu zoipa], Kristu anatifera ife.’—Aroma 5:6-8.

Panali mtumwi wina amene anachitapo zinthu zoipa kwambiri, kodi ungamukumbukire?— Mtumwi ameneyo analemba kuti: ‘Kristu Yesu anabwera ku dziko lapansi kupulumutsa ochimwa. Mwa ochimwaŵa ine ndine wochimwa kwambiri.’ Mtumwi amene ananena mawu ameneŵa ndi Paulo. Ananena kuti ‘kale anali wopusa’ ndipo anali kuchita ‘zoipa.’—1 Timoteo 1:15; Tito 3:3.

Koma ndiye Mulungu analitu ndi chikondi kwambiri potumiza Mwana wake kudzafera anthu ngati amenewo! Tatenga Baibulo tiŵerenge zimenezi pa Yohane chaputala 3, vesi 16. Vesili likuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi [kutanthauza anthu amene amakhala padziko lapansi] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”

Kodi Yesu anavutika ndi zotani pamene anapereka moyo wake chifukwa cha ife?

Yesu anaonetsa kuti anali kutikonda mofanana ndi mmene Atate ake amatikondera. Ndiganiza ukukumbukira kuti mu Mutu 30 wa buku lino tinaŵerenga za zina zimene Yesu anavutika nazo usiku umene anagwidwa. Anapita naye kunyumba kwa Mkulu wa Ansembe Kayafa, komwe anamuweruza. Panali mboni zonama zimene zinanena zabodza za Yesu, ndipo anthu anamumenya. Pajatu ndi nthaŵi imeneyi pamene Petro anakana kuti Yesu samudziŵa. Tsopano tiye tiyerekeze kuti tinali pomwepo ndipo m’maganizo mwathu tikuona zonse zimene zinachitika.

Unali m’maŵa. Yesu sanagone usiku wonse. Chifukwa chakuti usikuwo sanamuweruze moyenerera, ansembe anafulumira kusonkhanitsa mamembala a Sanihedirini, kapena kuti khoti lalikulu la Ayuda, ndi kuyambanso kumuweruza. Apanso ananena kuti Yesu analakwira Mulungu.

Kenako ansembewo anamanga Yesu ndi kupita naye kwa Pilato, yemwe anali nduna ya Roma. Anauza Pilato kuti: ‘Yesu amatsutsa boma. Afunika kuphedwa.’ Koma Pilato anaona kuti ansembewo akunena zabodza. Ndiye Pilato anawauza kuti: ‘Sindikuona kuti munthu uyu ndi wolakwa. Ndimumasula azipita.’ Atanena zimenezi ansembe ndi anthu ena anakuwa kuti: ‘Osamumasula! Aphedwe!’

Panthaŵi ina Pilato anauzanso anthuwo kuti Yesu amumasula. Koma ansembe anauza anthu kuti azikuwa kuti: ‘Mukamumasula ndiye kuti inunso mukutsutsana ndi boma! Ameneyu aphedwe!’ Anthuwo anachita phokoso kwambiri. Kodi ukudziŵa zimene Pilato anachita?—

Analolera zofuna za anthuwo. Ndiye choyamba anakwapula Yesu. Kenako anamupereka kwa asilikali kuti akamuphe. Iwo anaveka Yesu chisoti chaminga ndi kumamuseka pomugwadira. Atatero anapatsa Yesu mtengo waukulu kuti anyamule ndipo anatuluka naye m’mudzimo ndi kupita kumalo ena otchedwa Malo a Bade. Kumeneko anakhomerera manja a Yesu ndi mapazi ake kumtengo uja. Kenako anaimiritsa mtengowo ndipo Yesu anapachikika pamenepo. Anali kutuluka magazi. Anali kumva kupweteka kwambiri.

Yesu sanafe nthaŵi yomweyo. Anangopachikika choncho pamtengopo. Ansembe aakulu anali kumuseka. Ndipo anthu odutsa m’njira anali kunena kuti: ‘Ngati uli Mwana wa Mulungu, tatsika pamtengopo.’ Koma Yesu anali kudziŵa zimene Atate ake anamutumizira kudzachita. Anali kudziŵa kuti ayenera kupereka moyo wake wangwiro kuti ife tithe kukhala ndi moyo wosatha. Ndiyeno cha m’ma fili koloko masana, Yesu anafuula kwa Atate ake ndi kufa.—Mateyu 26:36–27:50; Marko 15:1; Luka 22:39–23:46; Yohane 18:1–19:30.

Yesu analitu wosiyana kwambiri ndi Adamu! Adamu sanakonde Mulungu. Sanamvere Mulungu. Ndiponso Adamu sanatikonde ifeyo. Chifukwa chakuti iye anachimwa, tonsefe tinabadwa ndi uchimo. Koma Yesu anasonyeza kuti Mulungu amamukonda ndiponso kuti ife amatikonda. Anali kumvera Mulungu nthaŵi zonse. Ndipo anapereka moyo wake kuti achotse choipa chimene Adamu anatichitira.

Kodi n’chiyani chimene tingachite posonyeza kuti Yesu timamukonda?

Kodi iwe ukuyamikira zinthu zapamwamba zimene Yesu anachita?— Ukamapemphera kwa Mulungu, kodi umamuthokoza kuti anatipatsa Mwana wake?— Mtumwi Paulo anali kuyamikira zimene Kristu anamuchitira. Paulo analemba kuti Mwana wa Mulungu ‘anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.’ (Agalatiya 2:20) Yesu anaferanso ine ndi iwe. Anapereka moyo wake wangwiro kuti ife tikhale ndi moyo wosatha! Ndithudi ichi ndi chifukwa chachikulu choti ife tizimukonda Yesu.

Mtumwi Paulo analembera a Kristu a ku Korinto kuti: “Chikondi cha Kristu chimatilimbikitsa kugwira ntchito.” Kodi chikondi cha Kristu chiyenera kutilimbikitsa kugwira ntchito yotani? Ukuganiza bwanji iwe?— Taona zimene anayankha Paulo, anati: ‘Kristu anafera onse kuti iwo azikhala ndi moyo wofuna kukondweretsa Iye. Iwo sayenera kukhala ndi moyo wofuna kudzikondweretsa okha.’2 Akorinto 5:14, 15, New Life Version.

Kodi ungaganizire zimene ungachite posonyeza kuti ukukhala ndi moyo wofuna kukondweretsa Kristu?— Eya, njira ina ndiyo kuuza ena zimene waphunzira za iye. Kapena taganizira izi: Mwinamwake ungakhale uli wekha, moti amayi ako kapena atate ako kapenanso munthu wina aliyense sangaone zimene ukuchita. Kodi ungaonerere mapulogalamu enaake a pa TV kapena kuchita zinazake zimene ukudziŵa kuti Yesu sangasangalale nazo?— Uzikumbukira kuti tsopano Yesu ali moyo ndipo amaona zonse zimene timachita!

Kodi ndani amene amaona zonse zimene timachita?

Yesu tiyeneranso kumukonda pachifukwa chakuti tikufuna kukhala ngati Yehova. Yesu ananena kuti: “Atate andikonda Ine.” Kodi ukudziŵa chifukwa chake Yehova amakonda Yesu ndiponso chifukwa chake ifenso tiyenera kumukonda?— Ndi chifukwa chakuti Yesu anali wofunitsitsa kufa kuti zimene Mulungu amafuna zichitike. (Yohane 10:17) Ndiye tiye tizichita izi zimene Baibulo limatiuza: “Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; ndipo yendani m’chikondi monganso Kristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m’malo mwathu.”—Aefeso 5:1, 2.

Kuti tiziyamikira kwambiri Yesu ndi zimene anatichitira, tiye tiŵerenge Yohane 3:35; 15:9, 10; ndi 1 Yohane 5:11, 12.