Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutu 41

Ana Amene Amakondweretsa Mulungu

Ana Amene Amakondweretsa Mulungu

KODI ukuganiza kuti ndi mwana uti padziko lapansi amene anakondweretsa Yehova kwambiri?— Ndi Yesu, Mwana wake. Tiye tikambirane zinthu zimene Yesu anachita kuti akondweretse Atate ake akumwamba.

Yesuyo ndi banja lawo lonse anali kukhala m’mudzi umene unali pamtunda wotenga pafupifupi masiku atatu kuyenda kuchokera ku Yerusalemu. Ku Yerusalemuko ndi kumene kunali kachisi wokongola wa Yehova. Yesu anatcha kachisiyo ‘nyumba ya Atate wanga.’ Iye ndi banja lawo lonse anali kupita komweko chaka chilichonse kukapezeka pa Paskha.

Chaka china, Yesu ali ndi zaka 12, banja lonse linayamba ulendo wobwerera kwawo atatha Paskha. Paulendowo, iwo sanadziŵe kuti Yesu palibe, ndi kuti sali ndi achibale awo ndi mabwenzi awo mpaka ataima penapake kuti agone kutada. Pomwepo Mariya ndi Yosefe anabwerera ku Yerusalemu kukafunafuna Yesu. Kodi iwe ukuganiza kuti iye anali kuti?—

Iwo anakapeza Yesu ali m’kachisi. Iyeyo anali kumvetsera kwa aphunzitsi, ndipo anali kuwafunsa mafunso. Komanso aphunzitsiwo akamufunsa mafunso, iye anali kuyankha. Aphunzitsiwo anadabwa kwambiri ndi mayankho ake abwino. Kodi ukuona chifukwa chake Mulungu anakondwera naye Mwana wake ameneyu?—

Pamene Mariya ndi Yosefe anapeza Yesu, mitima yawo inakhala pansi. Koma nthaŵi yonseyo Yesu sanali kuda nkhaŵa. Anadziŵa kuti kachisi ndi malo abwino kukhalapo. Choncho iye anawafunsa kuti: ‘Kodi simunadziŵe kuti ndiyenera kukhala m’nyumba ya Atate wanga?’ Yesu anadziŵa kuti kachisiyo anali nyumba ya Mulungu, ndipo iye anali kufunitsitsa kukhala kumeneko.

Atatero, Mariya ndi Yosefe anatenga Yesu uja wa zaka 12 ndi kupita naye kwawo ku Nazarete. Kodi ukuganiza kuti Yesu anali kuwaona bwanji makolo ake?— Eya, Baibulo limanena kuti iye ‘anapitiriza kuwamvera.’ Kodi ukaganiza, zimenezi zikutanthauza chiyani?— Zikutanthauza kuti Yesu anachita zimene makolo ake anali kumuuza kuchita, ngakhale ngati anamutuma kukatunga madzi kuchitsime.—Luka 2:41-52.

Kodi Yesu ali mwana, anachita chiyani kuti akondweretse Mulungu?

Ndiye tangoganiza: Ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, iye anamvera makolo ake opanda ungwiro. Kodi zimenezi zinakondweretsa Mulungu?— Inde, pakuti Mawu a Mulungu amauza ana kuti: “Mverani akukubalani.” (Aefeso 6:1) Iwenso ngati umvera makolo ako mofanana ndi Yesu, udzakondweretsa Mulungu.

Njira ina imene ungakondweretsere Mulungu ndiyo kuuzako ena za Mulunguyo. Tsono anthu ena angakuuze kuti ana safunika kuchita zimenezi. Koma pamene anthu anafuna kuletsa ana kuchita zimenezo, Yesu anati: ‘Simunaŵerenge kodi m’Malemba kuti, Mulungu adzachititsa m’kamwa mwa ana kufotokoza zolemekeza?’ (Mateyu 21:16) Choncho ngati tikufunadi kutero, ife tonse tingauze ena za Yehova ndi kuti ali Mulungu wabwino kwambiri. Ndipo tikachita zimenezo, tidzakondweretsa Mulungu.

Kodi zinthu za Mulungu zimene tingauzeko ena timaziphunzira kuti?— Timaziphunzira poŵerenga Baibulo kunyumba. Koma timaphunzira zambiri tikapita ku malo amene anthu a Mulungu amasonkhana kuti aphunzire. Nanga tingawadziŵe bwanji anthu a Mulungu?—

Eya, kodi anthu amachita chiyani pamisonkhano yawo? Kodi amaphunzitsadi zimene zili m’Baibulo? Kodi amaliŵerenga ndi kukambirana mfundo zake? Pajatu imeneyi ndiyo njira imene timamvetsera kwa Mulungu, si choncho kodi?— Ndiponso tikakhala pamisonkhano yachikristu timayembekeza kumva zimene Mulungu akunena, sitero?— Koma bwanji ngati anthu akukuuza kuti sufunika kuchita zimene Baibulo limanena? Kodi unganene kuti iwo ndi anthu a Mulungu?—

Palinso zina zimene ufunika kuganiza. Baibulo limanena kuti anthu a Mulungu adzakhala “anthu a dzina lake.” (Machitidwe 15:14) Ndiye popeza kuti dzina la Mulungu ndi Yehova, tingawafunse anthuwo ngati Yehovayo ndiye Mulungu wawo. Iwo akayankha kuti ayi, pamenepo tidziŵe kuti iwo si anthu ake. Anthu a Mulungu amauzanso ena za Ufumu wa Mulungu. Ndipo amasonyeza kuti amakonda Mulungu mwa kusunga malamulo ake.—1 Yohane 5:3.

Ngati ukudziŵa anthu amene amachita zonsezi, ufunika kusonkhana nawo polambira Mulungu. Ndiyeno uzimvetsera bwinobwino pamisonkhano imeneyi kenako uziyankha akafunsa mafunso. Yesu anachita zomwezo pamene anali m’nyumba ya Mulungu. Ndipo ukachita zimenezi, udzakondweretsa Mulungu, monga momwe Yesu anachitira.

Kodi ungakumbukire ana ena otchulidwa m’Baibulo amene anakondweretsa Mulungu?— Timoteo ndi chitsanzo chabwino kwambiri. Atate ake sanali kukhulupirira Yehova. Koma amayi ake a Yunike, ndi agogo ake a Loisi, anali kukhulupirira Yehova. Timoteo anali kuwamvera iwo ndipo anadziŵa Yehova.

Ngakhale kuti atate ake sanali okhulupirira, kodi Timoteo anafuna kuchita chiyani?

Timoteo atakula, mtumwi Paulo anakacheza mu mudzi umene Timoteoyo anali kukhala. Paulo anaona kuti Timoteo anali kufuna kwambiri kutumikira Yehova. Choncho anapempha Timoteo kuti apite naye kukachita zambiri potumikira Mulungu. Kulikonse kumene iwo anapita, anali kuuza anthu za Ufumu wa Mulungu ndi za Yesu.—Machitidwe 16:1-5; 2 Timoteo 1:5; 3:14, 15.

Koma kodi m’Baibulo muli chabe zitsanzo za anyamata okhaokha amene anakondweretsa Mulungu?— Ayi. Tiye tikambirane za mtsikana wamng’ono wa ku Israyeli amenenso anachita zomwezo. Nthaŵi imene anali ndi moyo, mtundu wa Aaramu ndi mtundu wa Aisrayeli anali adani. Tsiku lina Aaramu aja anachita nkhondo ndi Aisrayeli ndipo anagwira mtsikana uja kupita naye kwawo. Kumeneko anakamupereka kunyumba ya mkulu wa asilikali, dzina lake Namani, ndipo anakhala wantchito wa mkazi wa Namani.

Koma Namani anali kudwala khate. Madokotala onse sanathe kumuthandiza. Koma mtsikana wamng’ono uja wa ku Israyeli anakhulupirira kuti mtumiki wapadera wa Mulungu, kapena kuti mneneri, atha kuthandiza Namani. Tikudziŵa kuti Namani ndi mkazi wake sanali kulambira Yehova. Kodi mtsikanayo anafunikira kuwauza zimene iye anali kudziŵa? Ukanakhala iwe, kodi ukanachita chiyani?—

Kodi mtsikana uyu wa ku Israyeli anachita chiyani kuti akondweretse Mulungu?

Chabwino, mtsikana uja anati: ‘Ngati Namani angapite kwa mneneri wa Yehova ku Israyeli, akhoza kumuchiritisa khate lakelo.’ Namani anamva zimene mtsikanayo ananena, ndipo anapita kwa mneneri wa Yehova. Atachita zimene mneneri anamuuza, anachira. Chifukwa cha zimenezi Namani anayamba kulambira Mulungu woona.—2 Mafumu 5:1-15.

Kodi ungakonde kuthandiza wina kudziŵa Yehova ndi zimene Yehovayo angachite, monga momwe anachitira mtsikanayo?— Kodi ndani amene ungathandize?— Inde, iwo poyamba angaganize kuti safunikira thandizo lako. Koma ungakambirane nawo zinthu zabwino zimene Yehova amachita. Ndipo mwina iwo angamve. Ukatero, udziŵe kuti Mulungu adzakondwera nawe.

Malemba ena amene angalimbikitse ana kukonda kutumikira Mulungu ndi Salmo 122:1; 148:12, 13; Mlaliki 12:1; 1 Timoteo 4:12; ndi Ahebri 10:23-25.