Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zimene Zikuchitikazi Ndi Zomwe Mulungu Ankafuna?

Kodi Zimene Zikuchitikazi Ndi Zomwe Mulungu Ankafuna?

MUKAMAWERENGA nyuzipepala, kuonera TV kapena kumvetsera wailesi, nkhani zimene mumamva nthawi zambiri ndi zokhudza kuphwanya malamulo, nkhondo komanso uchigawenga. Kuwonjezera pamenepo, ganizirani mavuto amene inuyo mukukumana nawo. Mwina muli ndi nkhawa komanso chisoni chifukwa cha matenda kapena imfa ya mnzanu kapena wachibale wanu. Zimenezi zingakuchititseni kumva ngati mmene Yobu anamvera. Iye ananena kuti: “Ndachita manyazi kwambiri ndipo ndadzazidwa ndi mavuto.”—Yobu 10:15.

Dzifunseni kuti:

  • Kodi Mulungu ankafuna kuti moyo wanga komanso wa anthu ena onse ukhale wotere?

  • Kodi ndingapeze kuti thandizo kuti ndithe kulimbana ndi mavuto anga?

  • Kodi nthawi ina zidzatheka kuti anthu azikhala mwamtendere padziko lapansili?

Baibulo lili ndi mayankho ogwira mtima a mafunso amenewa.

BAIBULO LIMAPHUNZITSA KUTI MULUNGU ADZACHITA ZINTHU ZOTSATIRAZI PADZIKO LAPANSI.

“Adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:4

“Munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo.”—Yesaya 35:6

“Maso a anthu akhungu adzatsegulidwa.”—Yesaya 35:5

“Onse ali m’manda achikumbutso . . . adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29

“Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24

“Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri.”—Salimo 72:16

ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA ZIKHOZA KUKUTHANDIZANI

Musafulumire kuganiza kuti zimene zafotokozedwa m’masamba apitawa ndi zinthu zosatheka. Mulungu walonjeza kuti adzachita zimenezi ndipo Baibulo limafotokoza mmene adzazichitire.

Kuwonjezera pa kufotokoza zimenezi, Baibulo limafotokozanso za zinthu zimene zingakuthandizeni kukhala ndi moyo wosangalala ngakhale panopa. Ganizirani za mavuto amene muli nawo. Mwina muli ndi mavuto a zachuma, a m’banja, matenda ndiponso mwina wachibale wanu kapena mnzanu anamwalira. Baibulo likhoza kukuthandizani kupirira mavuto anu panopa komanso lingakuthandizeni kupeza mayankho a mafunso ngati awa:

  • N’chifukwa chiyani timakumana ndi mavuto?

  • Kodi tingapirire bwanji mavuto amene timakumana nawo?

  • Kodi tingatani kuti banja lathu lizikhala mosangalala?

  • Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

  • Kodi tidzawaonanso anzathu komanso achibale athu amene anamwalira?

  • Kodi n’chiyani chingatithandize kutsimikizira kuti zimene Mulungu analonjeza zidzachitikadi?

Kuwerenga bukuli komwe mukuchitaku ndi umboni woti mukufuna kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa. Bukuli likuthandizani kwambiri. Onani kuti ndime iliyonse ili ndi funso lake m’munsi mwa tsamba lililonse. Anthu ambiri amasangalala akamaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova pogwiritsa ntchito njira ya mafunso ndi mayankho. Tikukhulupirira kuti inunso musangalala kwambiri ndi njira imeneyi. Mulungu adzakudalitsani pamene mukuyesetsa kuti mudziwe zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni.