Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 17

Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu

Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
  • N’chifukwa chiyani tiyenera kumapemphera kwa Mulungu?

  • Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu azimva mapemphero athu?

  • Kodi Mulungu amayankha bwanji mapemphero athu?

“Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi” amafunitsitsa kumva mapemphero athu

1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kuona pemphero kukhala mwayi waukulu kwambiri, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhaniyi?

DZIKO LAPANSILI ndi laling’ono kwambiri tikaliyerekezera ndi zinthu zina zimene Yehova analenga. Ndipotu Yehova, “Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi,” amaona kuti mitundu ya anthu ili ngati kadontho ka madzi kochokera mumtsuko. (Salimo 115:15; Yesaya 40:15) Komabe Baibulo limanena kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’choonadi, ndipo anthu amene amamuopa adzawachitira zokhumba zawo, adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.” (Salimo 145:18, 19) Taganizirani zimene lembali likutanthauza. Likutanthauza kuti Mlengi wamphamvuyonse ali nafe pafupi ndipo adzamva ‘tikamamuitana m’choonadi.’ Choncho tili ndi mwayi waukulu woyankhula ndi Mulungu m’pemphero.

2 Koma ngati tikufuna kuti Yehova azimva mapemphero athu, tiyenera kupemphera m’njira imene amafuna. Komatu sitingathe kupemphera m’njira yoyenera ngati tisakudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza pemphero. Tiyenera kudziwa zimene Malemba amanena pa nkhaniyi chifukwa pemphero ndi lomwe lingatithandize kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUPEMPHERA KWA YEHOVA?

3. Kodi chifukwa chachikulu chopempherera kwa Yehova n’chiyani?

3 Chifukwa chachikulu chopempherera kwa Yehova n’choti iyeyo amatiuza kuti tizipemphera. Mawu ake amatiuza kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Umenewu ndi mwayi wapadera kwambiri womwe Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse watipatsa ndipo sitiyenera kuunyalanyaza.

4. Kodi kupemphera kwa Yehova nthawi zonse kumathandiza bwanji kuti tikhale naye pa ubwenzi?

4 Chifukwa china n’choti kupemphera kwa Yehova nthawi zonse kumathandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi wolimba. Anthu amene amagwirizana kwambiri amalankhulana nthawi zonse, osati akangofuna kupemphana chinachake. Amaderana nkhawa komanso amafotokozerana zakukhosi momasuka, zomwe zimachititsa kuti azikondana kwambiri. N’chimodzimodzinso ndi ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu. Bukuli lakuthandizani kudziwa zimene Baibulo limanena zokhudza Yehova, monga makhalidwe ake ndiponso zolinga zake. Panopa mukudziwa kuti Mulungu alipodi. Pemphero limakupatsani mwayi wofotokozera Atate wanu wakumwamba zinthu zimene zili mumtima mwanu. Mukamachita zimenezi, mumayamba kumukonda kwambiri Yehova.—Yakobo 4:8.

ZIMENE TIYENERA KUCHITA KUTI MULUNGU AZIMVA MAPEMPHERO ATHU

5. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yehova samamvetsera mapemphero onse?

5 Kodi Yehova amamvetsera mapemphero onse? Taganizirani zimene anauza Aisiraeli amene sankatsatira malamulo ake m’nthawi ya mneneri Yesaya. Iye anawauza kuti: “Ngakhale mupereke mapemphero ambiri, ine sindimvetsera. Manja anu adzaza magazi amene mwakhetsa.” (Yesaya 1:15) Zimenezi zikusonyeza kuti zinthu zina zimene timachita zingapangitse kuti Mulungu asamamvetsere mapemphero athu. Choncho pali zimene tiyenera kuchita kuti Mulungu azimva komanso kuyankha mapemphero athu.

6. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili ndi chikhulupiriro, nanga chikhulupiriro n’chofunika bwanji?

6 Chinthu chofunika kwambiri ndi kukhala ndi chikhulupiriro. (Werengani Maliko 11:24.) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Popanda chikhulupiriro n’zosatheka kukondweretsa Mulungu. Pakuti aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” (Aheberi 11:6) Kukhala ndi chikhulupiriro n’kosiyana ndi kungodziwa kuti Mulungu alipo ndiponso kuti amamva ndi kuyankha mapemphero. Zochita zathu n’zimene zingasonyeze kuti tili ndi chikhulupiriro. Choncho zinthu zimene timachita tsiku ndi tsiku ziyenera kusonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro.—Yakobo 2:26.

7. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza ulemu tikamalankhula ndi Yehova m’pemphero? (b) Pamene tikupemphera, kodi tingasonyeze bwanji kudzichepetsa?

7 Yehova amafunanso kuti anthu azipemphera kwa iye modzichepetsa komanso mochokera pansi pa mtima. Pali zinthu zambiri zotichititsa kukhala odzichepetsa tikamalankhula ndi Yehova. Anthu akakhala ndi mwayi wolankhulana ndi mfumu kapena pulezidenti, nthawi zambiri amayesetsa kulankhula mwaulemu posonyeza kuti akudziwa udindo umene munthuyo ali nawo. Ndiye kuli bwanji tikamalankhulana ndi Yehova? (Salimo 138:6) Pajatu iye ndi “Mulungu Wamphamvuyonse.” (Genesis 17:1) Mmene timapempherera kwa Mulungu, ziyenera kusonyeza kuti ndife odzichepetsa ndipo tikudziwa kuti tikulankhulana ndi Mulungu. Kudzichepetsa kotere kungachititsenso kuti mapemphero athu azikhala ochokera mumtima, osati omangobwereza.—Mateyu 6:7, 8.

8. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikuchita zinthu mogwirizana ndi zimene tapempha?

8 Chinthu china chimene chingachititse kuti Mulungu azimva mapemphero athu ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene tapemphazo. Yehova amafuna kuti tiziyesetsa mmene tingathere kuchita zinthu zimene zingatithandize kupeza zinthu zomwe tapemphazo. Mwachitsanzo, ngati titapemphera kuti, “Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero,” timafunika kugwira mwakhama ntchito iliyonse yomwe yapezeka imene tingakwanitse kugwira. (Mateyu 6:11; 2 Atesalonika 3:10) Ngati tapemphera kuti atithandize kulimbana ndi khalidwe linalake, tiyenera kupewa zinthu zimene zingapangitse kuti tichitenso khalidwelo. (Akolose 3:5) Kuwonjezera pa zinthu zimene takambiranazi, palinso mafunso okhudza pemphero amene tikufunikira kudziwa mayankho ake.

MAYANKHO AMAFUNSO ENA OKHUDZA PEMPHERO

9. Kodi tizipemphera kwa ndani, ndipo kudzera mwa ndani?

9 Kodi tiyenera kupemphera kwa ndani? Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kwa “Atate wathu wakumwamba.” (Mateyu 6:9) Choncho, mapemphero athu onse ayenera kupita kwa Yehova Mulungu. Komabe Yehova amafuna kuti tizizindikira udindo umene Mwana wake, Yesu Khristu, ali nawo. Monga tinaphunzirira m’Mutu 5, Mulungu anatumiza Yesu padziko lapansi kuti adzapereke moyo wake ngati dipo lowombola anthu ku uchimo ndi imfa. (Yohane 3:16; Aroma 5:12) Iye anasankhidwa kukhala Mkulu wa Ansembe komanso Woweruza. (Yohane 5:22; Aheberi 6:20) Choncho, Baibulo limatiuza kuti tizipemphera kudzera mwa Yesu. Ndipo Yesu mwiniwakeyo ananena kuti: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Kuti mapemphero athu ayankhidwe, tiyenera kupemphera kwa Yehova yekha kudzera mwa Mwana wake.

10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti palibe kakhalidwe kapadera popemphera?

10 Kodi pali kakhalidwe kenakake kapadera kofunika popemphera? Ayi. Yehova safuna kuti tizichita kuima kapena kukhala mwanjira inayake tikamapemphera. Baibulo limasonyeza kuti tikhoza kuima, kugwada, kukhala kapena kuwerama popemphera. (1 Mbiri 17:16; Nehemiya 8:6; Danieli 6:10; Maliko 11:25) Chofunika kwambiri si mmene munthu waimira kapena wakhalira, koma mmene mtima wake ulili. Ndipotu pamene tikugwira ntchito zathu kapena pamene takumana ndi vuto linalake mwadzidzidzi, tikhoza kupemphera chamumtima kulikonse kumene tili. Yehova amamva mapemphero oterowo, ngakhale kuti anthu ena amene tili nawo limodzi sangadziwe n’komwe kuti tikupemphera.—Nehemiya 2:1-6.

11. Kodi ndi nkhani zina ziti zomwe tingamatchule m’mapemphero athu?

11 Kodi tiyenera kupempherera nkhani ziti? Baibulo limanena kuti: “Chilichonse chimene tingamupemphe [Yehova] mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.” (1 Yohane 5:14) Choncho tikhoza kupempherera chilichonse chogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Kodi iye amafuna kuti tizipempherera mavuto athu komanso zinthu zina zimene ifeyo tikufuna? Inde. Kupemphera kwa Yehova kuli ngati kulankhulana ndi mnzathu wapamtima. Tikhoza kufotokozera Mulungu zinthu momasuka, kapena kuti ‘kumukhuthulira za mumtima mwathu.’ (Salimo 62:8) Ndi bwino kumupempha kuti atipatse mzimu woyera kuti uzitithandiza kuchita zinthu zoyenera. (Luka 11:13) Tingapemphenso kuti azititsogolera kuti tizitha kusankha zinthu mwanzeru ndiponso kuti azitithandiza kupirira mavuto. (Yakobo 1:5) Tikachimwa, tiyenera kupempha kuti atikhululukire pogwiritsa ntchito nsembe ya Khristu. (Aefeso 1:3, 7) Komabe sitiyenera kungopempherera zinthu zathu zokha. Tiyenera kupemphereranso anthu ena, monga achibale athu komanso Akhristu anzathu.—Machitidwe 12:5; Akolose 4:12.

12. Kodi mapemphero athu angasonyeze bwanji kuti timaona nkhani zokhudza Atate wathu wakumwamba kukhala zofunika kwambiri?

12 Tikamapemphera tiyenera kusonyeza kuti nkhani zokhudza Yehova Mulungu ndi zimene zili zofunika kwambiri. Pali zinthu zambiri zotichititsa kuti tizimutamanda komanso kumuyamikira chifukwa cha zabwino zonse zimene amatichitira. (1 Mbiri 29:10-13) Yesu anatipatsa chitsanzo cha mmene tingapempherere, chomwe chimasonyeza kuti tiyenera kupempherera dzina la Mulungu kuti liyeretsedwe. Chitsanzochi chili pa Mateyu 6:9-13. (Werengani.) Kenako ananena zoti Ufumu wa Mulungu ubwere ndiponso zoti chifuniro chake chichitike padziko lapansi ngati mmene zilili kumwamba. Atatchula zinthu zofunika kwambiri zimenezi, zomwe zikukhudza Yehova ndi Yesu, m’pamene anayamba kutchula zinthu zofunikira pa moyo wathu. Choncho nafenso tingasonyeze kuti sitimangoganizira za zofuna zathu zokha ngati popemphera timayamba n’kutchula zinthu zokhudza Mulungu.

13. Kodi Malemba amati chiyani pa nkhani ya kutalika kwa mapemphero?

13 Kodi mapemphero athu ayenera kukhala aatali bwanji? Baibulo silimaika malire a nthawi imene tingapemphere, kaya ndi pagulu kapena patokha. Tikhoza kupemphera mwachidule pa nthawi ya chakudya ndiponso kupemphera pemphero lalitali patokha ndipo m’pemphero limeneli tingamuuze Yehova zimene zili mumtima mwathu. (1 Samueli 1:12, 15) Komabe, Yesu anadzudzula anthu amene amadziona ngati olungama, omwe amapereka mapemphero ataliatali pagulu pongofuna kudzionetsera. (Luka 20:46, 47) Yehova sasangalala ndi mapemphero a mtundu umenewu. Chimene Yehova amafuna n’choti tizipemphera kuchokera pansi pa mtima. Choncho mapemphero angatalike mosiyanasiyana malinga ndi mmene zinthu zilili.

Mulungu akhoza kumva pemphero lanu kulikonse ndiponso nthawi iliyonse

14. Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamatilimbikitsa kuti ‘tizipemphera mosalekeza,’ ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zolimbikitsa?

14 Kodi tiyenera kupemphera kangati pa tsiku? Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tizipemphera kosalekeza’ ndiponso kuti ‘tizilimbikira kupemphera.’ (Mateyu 26:41; Aroma 12:12; 1 Atesalonika 5:17) Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti tizingokhalira kupemphera kwa Yehova tsiku lonse. Akutanthauza kuti tiyenera kupemphera pafupipafupi, kumuthokoza Yehova chifukwa cha zinthu zabwino zimene amatichitira ndiponso kumupempha kuti azititsogolera komanso kutilimbikitsa. Kodi sizolimbikitsa kudziwa kuti Yehova sanaike malire a mmene pemphero liyenera kutalikira komanso kuti tizipemphera kangati? Choncho, ngati timaona kuti pemphero ndi mwayi wapadera wolankhulana ndi Atate wathu wakumwamba, tidzayesetsa kumapemphera pafupipafupi.

15. N’chifukwa chiyani tiyenera kunena “Ame” pamapeto pa pemphero la patokha kapena la pagulu?

15 N’chifukwa chiyani tiyenera kunena kuti “Ame” pamapeto pa pemphero? Mawu akuti “ame” amatanthauza kuti “zoonadi,” kapena kuti “zikhaledi choncho.” Zitsanzo za m’Baibulo zimasonyeza kuti ndi bwino kunena kuti “Ame” pamapeto pa pemphero la pawekha kapena la pagulu. (1 Mbiri 16:36; Salimo 41:13) Tikamapemphera patokha, kunena kuti “Ame” kumatanthauza kutsimikizira kuti zimene tanenazo ndi zimene zinalidi mumtima mwathu. Ndipo kunena kuti “Ame,” chamumtima kapena mokweza, pambuyo pa pemphero la pagulu loperekedwa ndi munthu wina, kumasonyeza kuti tikugwirizana ndi zimene munthuyo wanena m’pempherolo.—1 Akorinto 14:16.

MMENE MULUNGU AMAYANKHIRA MAPEMPHERO ATHU

16. Kodi tiyenera kukhala otsimikizira za chiyani pa nkhani ya pemphero?

16 Kodi n’zoona kuti Yehova amayankha mapemphero athu? Inde, amayankha. Ndipotu Baibulo limanena kuti iye ndi “Wakumva pemphero” ndipo zimenezi zimatitsimikizira kuti amayankha mapemphero ambirimbiri ochokera pansi pa mtima amene anthu amapereka. (Salimo 65:2) Yehova amayankha mapemphero athu m’njira zosiyanasiyana.

17. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Mulungu amagwiritsa ntchito angelo ndiponso atumiki ake a padziko lapansi poyankha mapemphero athu?

17 Yehova amatha kugwiritsa ntchito angelo komanso atumiki ake a padziko lapansi poyankha mapemphero. (Aheberi 1:13, 14) Zachitikapo kambirimbiri kuti munthu wina anapemphera kwa Mulungu kuti amuthandize kumvetsa mfundo inayake ya m’Baibulo ndipo pasanapite nthawi n’kukumana ndi a Mboni za Yehova omwe anamuthandiza. Nkhani ngati zimenezi zimasonyeza umboni wakuti angelo ndi amene amatitsogolera pa ntchito yolalikira. (Chivumbulutso 14:6) Pofuna kuyankha mapemphero athu opempha thandizo linalake, Yehova akhoza kulimbikitsa Mkhristu winawake kuti atithandize.Miyambo 12:25; Yakobo 2:16.

Poyankha mapemphero athu, Yehova angachititse kuti Mkhristu mnzathu atithandize m’njira inayake

18. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji mzimu woyera ndi Mawu ake poyankha mapemphero a atumiki ake?

18 Yehova Mulungu amagwiritsanso ntchito mzimu woyera ndiponso Mawu ake, Baibulo, poyankha mapemphero a atumiki ake. Akhoza kuyankha mapemphero athu opempha kuti atithandize kulimbana ndi mayesero ndipo angatipatse mzimu wake woyera kuti uzititsogolera komanso kutilimbikitsa. (2 Akorinto 4:7) Nthawi zambiri tikapemphera kuti atitsogolere, Yehova amayankha pogwiritsa ntchito Baibulo, lomwe lili ndi mfundo zomwe zimatithandiza kusankha zinthu mwanzeru. Tingapeze mfundo zothandizazi tikamaphunzira Baibulo patokha komanso tikamawerenga mabuku achikhristu, ngati limene tikuphunzirali. Tikhozanso kumva mfundo zofunikira za m’Baibulo pamisonkhano yachikhristu kapena kuchokera kwa mkulu wa mumpingo yemwe amatiganizira.—Agalatiya 6:1.

19. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani ngati nthawi zina timaona ngati Mulungu sakuyankha mapemphero athu?

19 Yehova akamaoneka ngati akuchedwa kuyankha mapemphero athu, sizisonyeza kuti mapempherowo ndi oti sangathe kuwayankha. Tizikumbukira kuti Yehova amayankha mapemphero mogwirizana ndi cholinga chake komanso pa nthawi yake yoyenera. Iye ndi amene amadziwa bwino zimene tikufunikira ndiponso mmene angatipatsire zinthuzo. Koma nthawi zina iye amafuna kuti tizipitirizabe ‘kupempha, kufunafuna, ndi kugogoda.’ (Luka 11:5-10) Kupitirizabe kupempha kotereku kumasonyeza kuti chinthucho tikuchifunadi ndiponso kuti tili ndi chikhulupiriro. Nthawi zinanso Yehova akhoza kuyankha pemphero lathu m’njira imene ifeyo sitimayembekezera. Mwachitsanzo, ngati titapemphera kuti atithandize pa mayesero enaake amene tikukumana nawo, nthawi zina sangatichotsere mayeserowo, koma akhoza kungotipatsa mphamvu kuti tipirire.—Werengani Afilipi 4:13.

20. N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito mwanzeru mwayi womwe tili nawo wopemphera kwa Mulungu?

20 N’zosangalatsa kudziwa kuti Mlengi wa chilengedwe chonse ali pafupi ndi onse amene amayesetsa kupemphera kwa iye moyenerera. (Werengani Salimo 145:18.) Tiyenera kugwiritsa ntchito mwanzeru mwayi wapadera umenewu wopemphera kwa Yehova. Tikamachita zimenezi tidzakhala ndi mwayi wokhala pa ubwenzi ndi Yehova, yemwe ndi Wakumva pemphero.