Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZAKUMAPETO

Mmene Ulosi wa Danieli Unasonyezera Nthawi Imene Mesiya Adzafike

Mmene Ulosi wa Danieli Unasonyezera Nthawi Imene Mesiya Adzafike

MNENERI Danieli anakhala ndi moyo zaka zoposa 500 Yesu asanabadwe. Komabe Yehova anamuululira Danieli zinthu zimene zinathandiza anthu kudziwa nthawi yeniyeni imene Yesu adzadzozedwe, kapena kuti kusankhidwa, kukhala Mesiya, kapena kuti Khristu. Danieli anauzidwa kuti: “Uyenera kudziwa ndi kuzindikira kuti kuchokera pamene mawu adzamveka onena kuti Yerusalemu akonzedwe ndi kumangidwanso, kufika pamene Mesiya Mtsogoleri adzaonekere, padzadutsa milungu 7, komanso milungu 62.”—Danieli 9:25.

Kuti tidziwe nthawi yeniyeni yofikira Mesiya, choyamba tiyenera kudziwa kuti kuwerengera nthawiyi kukuyambira pati. Malinga ndi ulosiwu, nthawiyi ikuyambira “pamene mawu adzamveka onena kuti Yerusalemu akonzedwe ndi kumangidwanso.” Kodi mawu amenewa anamveka liti? Malinga ndi zimene Nehemiya ananena, mawu oti mpanda wa Yerusalemu umangidwenso anamveka “m’chaka cha 20 cha mfumu Aritasasita.” (Nehemiya 2:1, 5-8) Olemba mbiri yakale amatsimikizira kuti Aritasasita anayamba kulamulira m’chaka cha 475 B.C.E. Choncho, chaka cha 20 cha ulamuliro wake chinali chaka cha 455 B.C.E. Tsopano tapeza poyambira kuwerengera nthawi yonena za kubwera kwa Mesiya, kuti ndi chaka cha 455 B.C.E.

Danieli anasonyezanso kutalika kwa nthawi imene idzadutse kuti “Mesiya Mtsogoleri” aonekere. Ulosi wake unanena za “milungu 7, komanso milungu 62,” yomwe ikaphatikizidwa ndi milungu 69. Kodi nthawi imeneyi ndi yaitali bwanji? Mabaibulo ambiri amasonyeza kuti milungu imeneyi si ya masiku 7 okha, koma ndi milungu ya zaka. Choncho mlungu umodzi ukuimira zaka 7. Zomanena kuti zaka 7 ndi mlungu umodzi, sizinali zachilendo kwa Ayuda akale. Mwachitsanzo, chaka cha 7 chilichonse chinali chaka chawo cha Sabata. (Ekisodo 23:10, 11) Choncho mlungu uliwonse unkakhala ndi zaka 7, zomwe zikusonyeza kuti milungu 69 imeneyi ndi zaka zokwanira 483.

Apatu chatsala n’kuwerengetsera. Kuwerengetsera zaka 483 kuchokera m’chaka cha 455 B.C.E., kukutifikitsa mu 29 C.E. Chaka chimenechi ndi chimene Yesu anabatizidwa n’kukhala Mesiya. * (Luka 3:1, 2, 21, 22) Kumenekutu n’kukwaniritsidwa kochititsa chidwi kwa ulosi wa m’Baibulo.

^ ndime 2 Kuchokera mu 455 B.C.E. kufika mu 1 B.C.E panadutsa zaka 454. Kuchokera mu 1 B.C.E. kufika 1 C.E. panali chaka chimodzi chokha. Ndipo kuchokera mu 1 C.E. kufika mu 29 C.E. panadutsa zaka 28. Tikaphatikizira, zaka zimenezi zikukwana zaka 483. Yesu ‘anaphedwa’ m’chaka cha 33 C.E., womwe ndi mlungu wa 70. (Danieli 9:24, 26) Onani buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli! Mutu 11, ndi Kukambitsirana za m’Malemba, tsamba 231-233. Mabukuwa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.