Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZAKUMAPETO

Kodi Ndi Zoona Kuti Anthu Ali Ndi Mzimu Umene Sumafa?

Kodi Ndi Zoona Kuti Anthu Ali Ndi Mzimu Umene Sumafa?

MUKAMVA mawu akuti “mzimu,” kodi mumaganiza za chiyani? Anthu ambiri amakhulupirira kuti mawu amenewa amatanthauza chinthu chinachake chosaoneka chimene chimakhala mkati mwa munthu aliyense ndipo chimapitirizabe kukhala ndi moyo munthuyo akamwalira. Iwo amakhulupirira kuti munthu akafa, chinthu chimenechi chimachoka m’thupi mwake n’kumapitiriza kukhala ndi moyo kwinakwake. Popeza kuti maganizo amenewa ndi ofala, anthu ambiri amadabwa akamva kuti zimenezi si zimene Baibulo limaphunzitsa. Ndiye kodi Mawu a Mulungu amanena kuti mzimu n’chiyani?

Polemba nkhani zonena za “mzimu,” olemba Baibulo anagwiritsa ntchito mawu achiheberi akuti ruʹach, kapena achigiriki akuti pneuʹma. Malemba amasonyeza okha zimene mawu amenewa amatanthauza. Mwachitsanzo, lemba la Yakobo 2:26 limanena kuti ‘thupi lopanda mzimu [pneuʹma] limakhala lakufa.’ Choncho pa lemba limeneli, mawu akuti “mzimu” amatanthauza chimene chimachititsa kuti thupi likhale la moyo. Thupi likakhala lopanda mzimu, limakhala lakufa. M’Baibulo, mawu akuti ruʹach amamasuliridwa mosiyanasiyana. Nthawi zina amawamasulira kuti “mzimu” komanso “mpweya wa moyo,” kapena kuti mphamvu ya moyo. Mwachitsanzo, ponena za Chigumula cha nthawi ya Nowa, Mulungu anati: “Ndidzabweretsa chigumula chamadzi padziko lapansi, kuti chiwononge chamoyo chilichonse cha pansi pa thambo, chimene chili ndi mphamvu ya moyo [ruʹach] m’thupi mwake.” (Genesis 6:17; 7:15, 22) Zimenezi zikusonyeza kuti “mzimu” ndi mphamvu yosaoneka (mphamvu ya moyo), imene imachititsa kuti zinthu zikhale ndi moyo.

Thupi limafunikira mzimu kuti likhale ndi moyo, mofanana ndi mmene wailesi imafunikira magetsi kuti igwire ntchito. Taganizirani za wailesi ya mabatire. Mukaika mabatire muwailesi n’kuitsegula, mphamvu yochokera m’mabatirewo imapangitsa kuti wailesiyo iyambe kugwira ntchito. Koma popanda mabatire, wailesiyo imakhala yakufa, kapena kuti siingathe kugwira ntchito. N’chimodzimodzinso ndi wailesi yoyendera magetsi. Ngati mutazula nthambo yake kumagetsi, wailesiyo ingasiye kugwira ntchito. Mofanana ndi zimenezi, mzimu ndi mphamvu imene imapangitsa kuti thupi lathu likhale lamoyo. Ndipo mofanana ndi magetsi, mzimu ndi mphamvu chabe moti suumva kalikonse kapena kuganiza. Koma popanda mzimuwu, kapena kuti mphamvu ya moyo, matupi athu ‘amafa, ndipo timabwerera kufumbi.’—Salimo 104:29.

Ponena za zimene zimachitika munthu akafa, lemba la Mlaliki 12:7 limati: “Fumbi [thupi la munthuyo] lidzabwerera kunthaka kumene linali, ndipo mzimu udzabwerera kwa Mulungu woona amene anaupereka.” Mzimu, kapena kuti mphamvu ya moyo, ukatuluka m’thupi, thupilo limafa n’kubwerera kunthaka kumene linachokera. Nayonso mphamvu ya moyo imabwerera kwa mwiniwake amene anaipereka, yemwe ndi Mulungu. (Yobu 34:14, 15; Salmo 36:9) Zimenezi sizikutanthauza kuti mphamvu ya moyo imayendadi ulendo wopita kumwamba ayi. Koma zikutanthauza kuti munthu amene wamwalirayo kuti adzakhalenso ndi moyo m’tsogolo, zikudalira pa zimene Yehova Mulungu angachite. M’mawu ena, tingati moyo wake umakhala m’manja mwa Mulungu. Izi zili choncho chifukwa Mulungu yekha ndi amene ali ndi mphamvu yobwezeretsanso mzimu wa munthuyo kuti akhalenso ndi moyo.

N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti zimenezi ndi zomwe Mulungu adzachitire anthu onse amene akugona “m’manda achikumbutso.” (Yohane 5:28, 29) Pa nthawi imene azidzaukitsa akufa, Yehova adzapangira munthu aliyense amene akugona mu imfa thupi latsopano, n’kuikamo mzimu kapena kuti mphamvu ya moyo kuti akhalenso ndi moyo. Imeneyitu idzakhaladi nthawi yosangalatsa kwambiri.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhudza mmene mawu akuti “mzimu” anagwiritsidwira ntchito m’Baibulo, mungapeze mfundo zothandiza m’kabuku kakuti Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza? tsamba 12-14, ndiponso tsamba 319-323 m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba. Mabukuwa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.