Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 1

Izi Ndi Zimene “Kukonda Mulungu Kumatanthauza”

Izi Ndi Zimene “Kukonda Mulungu Kumatanthauza”

“Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”—1 YOHANE 5:3.

1, 2. N’ciani cimakupangitsani kukonda Yehova Mulungu?

KODI inu mumam’konda Mulungu? Ngati munadzipeleka kale kwa Yehova Mulungu, ndiye kuti mungayankhe ndi mtima wonse kuti, inde! Mwacibadwa, timakonda Yehova. Timamukonda cifukwa iye ndiye anayamba kutikonda. Ndiye cifukwa cake Baibulo limakamba kuti: “Ife timasonyeza cikondi, cifukwa iye [Yehova] ndi amene anayamba kutikonda.”—1 Yohane 4:19.

2 Yehova ndiye anayamba kutionetsa cikondi. Anatipatsa dziko lapansi kukhala mudzi wathu wokongola.  Amatigaŵilanso zosoŵa zathu zakuthupi. (Mateyu 5:43-48) Koma cofunika kwambili n’cakuti amatigaŵila zosoŵa zathu za kuuzimu. Watipatsa Mau ake, Baibulo. Amatilangizanso kuti tizipemphela kwa iye ndi cidalilo cakuti adzamva mapemphelo athu, ndi kutinso adzatipatsa mzimu wake woyela kuti utithandize. (Salimo 65:2; Luka 11:13) Koposa zonse, anatitumizila Mwana wake wokondedwa kwambili kuti adzatiombole ku ucimo ndi imfa. Cimeneci ndi cikondi cacikulu cimene Yehova wationetsa.—Ŵelengani Yohane 3:16; Aroma 5:8.

3. (a) Kodi tifunika kucita ciani kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu? (b) Kodi ndi funso lofunika kwambili liti limene tifunika kuliganizila? Nanga yankho lake tingalipeze kuti?

3 Yehova amafuna kuti tipindule ndi cikondi cake kwamuyaya. Koma kaya tidzapinduladi naco kapena ai, zili kwa ife. Mau a Mulungu amatilangiza kuti: ‘‘Khalanibe m’cikondi ca Mulungu . . . [kuti mukalandile] moyo wosatha.’’ (Yuda 21, Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulila Malemba Achigiriki Achikhristu.) Liu lakuti “khalanibe” limaonetsa kuti tiyenela kucitapo kanthu kuti tipitilize kukhala m’cikondi ca Mulungu. Tiyenela kuonetsa kuti timayamikila cikondi ca Mulungu mwa zocita zathu. Conco, tifunika kuganizila funso lofunika lakuti, ‘Kodi ndingaonetse bwanji kuti ndimam’konda Mulungu?’ Yankho timalipeza m’mau ouzilidwa a mtumwi Yohane akuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.” (1 Yohane 5:3) Tiyenela kupenda mosamalitsa tanthauzo la mau amenewa, cifukwa tifuna kumuonetsa Mulungu kuti timam’konda kwambili.

IZI NDI ZIMENE “KUKONDA MULUNGU KUMATANTHAUZA”

4, 5. (a) Kodi “kukonda Mulungu” kumatanthauza ciani? (b) Fotokozani mmene cikondi canu pa Yehova cinayambila kukula mumtima mwanu.

4 Kodi mtumwi Yohane anali kutanthauza ciani pamene analemba mau akuti “kukonda Mulungu”? Anali kutanthauza mmene timamvelela kucokela pansi pa mtima wathu ponena za Mulungu. Kodi munamva bwanji pamene cikondi canu pa Yehova cinayamba kukula mumtima mwanu?

Kudzipeleka ndi ubatizo ndi ciyambi ca umoyo womvela Yehova cifukwa timam’konda

5 Ganizilani pamene munayamba kuphunzila coonadi ca Yehova ndi zolinga zake, ndiponso pamene munayamba kukhala ndi cikhulupililo. Munamvetsetsa kuti ngakhale kuti munabadwa ocimwa, ndipo simunali pa ubwenzi ndi Mulungu, Yehova kupyolela mwa Kristu anakutsegulilani njila yakuti mukapeze moyo wangwilo umene Adamu anataya, ndi kuti mukalandile moyo wosatha. (Mateyu 20:28; Aroma 5:12, 18) Munayamba kumvetsetsa kukula kwa nsembe imene Yehova anapeleka potumiza Mwana wake wokondedwa kudzatifela. Munakhudzika mtima kwambili cakuti munayamba kum’konda Mulungu, cifukwa anakuonetsani cikondi cacikulu cimeneci.—Ŵelengani 1 Yohane 4:9, 10.

6. Kodi cikondi ceniceni tingacionetse bwanji? Ndipo cikondi canu kwa Mulungu cinakupangitsani kucita ciani?

6 Kukhudzika mtima kumeneko, kunali poyambila cabe pa cikondi canu kwa Yehova. Cikondi ceniceni kwa Mulungu si mmene munthu amamvelela cabe mumtima, kapena kungokamba pakamwa kuti: “Ndimakonda Yehova.” Mofanana ndi cikhulupililo, cikondi ceniceni kwa Mulungu cimaonekela m’zocita zathu. (Yakobo 2:26) Timaonetsa cikondi cathu mwa kucita zimene zimakondweletsa munthu amene timakonda. Conco, pamene cikondi canu pa Yehova cinazika mizu mumtima mwanu, munayamba kucita zinthu zokondweletsa mtima wa a Atate wanu wakumwamba. Kodi ndinu Mboni yobatizidwa? Ngati mwayankha kuti inde, ndiye kuti cikondi canu cacikulu kwa Yehova ndi kukhulupilika kwanu kwa iye, n’zimene zinakucititsani kupanga cosankha cofunika kwambili paumoyo wanu. Munadzipeleka kwa Yehova kuti mucite cifunilo cake, ndipo munaonetsa kuti munadzipeleka kwa iye mwa kubatizidwa. (Ŵelengani Aroma 14:7, 8.) Kukwanilitsa lonjezo lalikulu limeneli la kucita cifunilo ca Yehova, kumaphatikizapo kucita zimene mtumwi Yohane anachula m’mau ake otsatila.

“KUSUNGA MALAMULO AKE”

7. Kodi malamulo ena a Mulungu ndi ati? Nanga kuwasunga kumaphatikizapo ciani?

7 Yohane anafotokoza zimene kukonda Mulungu kumatanthauza pamene anati: ‘Tisunge malamulo ake.’ Kodi malamulo a Mulungu ndi ati? Yehova watipatsa malamulo osiyanasiyana kupyolela m’Mau ake, Baibulo. Mwacitsanzo, amaletsa zinthu monga, kuledzela, dama, kupembedza mafano, kuba, ndi kunama. (1 Akorinto 5:11; 6:18; 10:14; Aefeso 4:28; Akolose 3:9) Kusunga malamulo a Mulungu kumaphatikizapo kucita zinthu mogwilizana ndi mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino pa umoyo wathu.

8, 9. Tingadziŵe bwanji zimene zimakondweletsa Yehova pa nkhani zimene palibe malamulo acindunji a m’Baibulo? Pelekani citsanzo.

8 Koma kuti tikondweletse Yehova, tiyenela kucita zambili kuposa kumvela cabe malamulo ake olembedwa. Yehova safuna kutipanikiza mwa kutiikila malamulo pa zocita zonse paumoyo wathu. Conco, tsiku lililonse, tingakumane ndi zocitika zimene Baibulo silinapelekepo malamulo acindunji. Tingadziŵe bwanji zimene zingakondweletse Yehova pa zocitika zimenezo? Baibulo lili ndi mfundo zomveka bwino zoonetsa mmene Mulungu amaonela zinthu. Pamene tiphunzila Baibulo, timadziŵa zimene Yehova amakonda ndi zimene amadana nazo. (Ŵelengani Salimo 97:10; Miyambo 6:16-19) Timafika pa kudziŵa makhalidwe ndi zocita zimene amagwilizana nazo. Pamene tiphunzila zambili za makhalidwe a Yehova ndi njila zake, m’pamene timalola maganizo ake kutitsogolela pa zosankha ndi zocita zathu. Conco, ngakhale pankhani zimene palibe malamulo acindunji a m’Baibulo, tingathe kudziŵa “cifunilo ca Yehova.”—Aefeso 5:17.

9 Mwacitsanzo, m’Baibulo mulibe lamulo lacindunji loletsa kupenyelela mafilimu kapena mapulogalamu a pa TV amene amaonetsa zinthu zaciwawa kapena zaciwelewele. Koma kodi timafunikiladi lamulo lacindunji loletsa kupenyelela zinthu zimenezi? Timadziŵa mmene Yehova amaonela zinthu zimenezi. Mau ake amatiuza mosapita m’mbali kuti “[Yehova] amadana kwambili ndi aliyense wokonda ciwawa.” (Salimo 11:5) Baibulo limatiuzanso kuti: “Mulungu adzaweluza adama ndi acigololo.” (Aheberi 13:4) Kuganizila mau amenewa, kungatithandize kuzindikila mosavuta cimene cili cifunilo ca Yehova. Ndiye cifukwa cake timapewa kupenyelela zinthu zoipa zimene Mulungu wathu amadana nazo. Timadziŵa kuti Yehova amasangalala ngati tipewa zinthu zonyansa zimene dzikoli limaonetsa kukhala ngati zosangulutsa zabwino. *

10, 11. N’cifukwa ciani timasankha kumvela Yehova? Nanga kumvela kwathu kuyenela kukhala kotani?

10 N’cifukwa cacikulu citi cimene timamvelela malamulo a Mulungu? N’cifukwa ciani nthawi zonse timafuna kukhala ndi moyo mogwilizana ndi maganizo a Mulungu? Timamvela Mulungu osati cabe kuti tipewe cilango kapena mavuto amene anthu osacita cifunilo ca Mulungu amakumana nao. (Agalatiya 6:7) M’malo mwake, timaona kumvela Yehova kukhala mwai wapadela woonetsa kuti timam’konda. Monga mmene mwana amafunila kukondweletsa atate wake, ifenso timafuna kukondweletsa Yehova. (Salimo 5:12) Iye ndi Atate wathu, ndipo timam’konda. Palibe cinthu cimene  cimatikondweletsa ndi kutikhutilitsa kuposa kudziŵa kuti zocita zathu zimapangitsa ‘Yehova kukondwela nafe.’—Miyambo 12:2.

11 Conco, sitimvela Mulungu mokakamizika. * Siticita kusankha malamulo akuti tiwamvele, kapena kumvela cabe amene tiona kuti adzatithandiza pa zofuna zathu, kapenanso amene tiona kuti ndi osavuta. M’malo mwake, ‘timamvela mocokela pansi pa mtima.’ (Aroma 6:17) Timamvela mofanana ndi wamasalimo amene analemba kuti: “Ndidzakondwela ndi malamulo anu amene ndimawakonda.” (Salimo 119:47) Inde, timakonda kumvela Yehova. Timadziŵa kuti iye ndi woyenela kumumvela ndi mtima wonse osati mokakamizika. (Deuteronomo 12:32) Timafuna kuti Yehova azikamba za ife mmene Mau ake amakambila za Nowa. Ponena za kholo lokhulupilika lakaleli, limene linakonda Mulungu mwa kumumvela kwa zaka zambili, Baibulo limati: “Nowa anacita zonse motsatila zimene Mulungu anam’lamula. Anacitadi momwemo.”—Genesis 6:22.

12. Ndi kumvela kwa mtundu wotani kumene kumakondweletsa mtima wa Yehova?

12 Kodi Yehova amamva bwanji tikamamumvela mwaufulu? Mau ake amanena kuti tikacita zimenezo ‘timakondweletsa mtima wake.’ (Miyambo 27:11) Kodi kumvela kwathu Ambuye Wamkulu koposa m’cilengedwe conse kumakondweletsadi mtima wake? Inde, ndipo ali ndi zifukwa zabwino zokhalila wokondwela. Yehova anatilenga ndi ufulu wosankha. Izi zikutanthauza kuti tili ndi ufulu wosankha kumvela Mulungu kapena kusamumvela. (Deuteronomo 30:15, 16, 19, 20) Tikasankha kumvela Yehova mwaufulu cifukwa cakuti timam’konda ndi mtima wonse, iye monga Atate wathu wakumwamba amakondwela kwambili. (Miyambo 11:20) Tikacita zimenezo, ndiye kuti tasankha umoyo wabwino koposa.

‘MALAMULO AKE SI OLEMETSA’

13, 14. N’cifukwa ciani tingakambe kuti ‘malamulo a Mulungu si olemetsa?’ Nanga pali citsanzo cotani?

13 Mtumwi Yohane anatiuza mfundo yolimbikitsa kwambili yokhudza malamulo a Yehova. Iye anati: ‘Malamulo akewo si olemetsa.’ Liu la Cigiriki lotembenuzidwa kuti ‘olemetsa’ pa 1 Yohane 5:3 limatanthauza “colema.” * Baibulo lina limati: “Malamulo ake satipondeleza.” (New English Translation) Malamulo a Yehova si opanikiza kapena otopetsa. Malamulo a Mulungu si ovuta kwambili mwakuti anthu opanda ungwilo angalephele kuwatsatila.

14 Tifanizile mwa njila iyi. Mnzanu wa pamtima wakupemphani kuti mum’thandize kusamukila ku nyumba ina. Ali ndi katundu wambili wakuti asamutse. Katundu wina ndi wopepuka mwakuti munthu mmodzi anganyamule mosavuta, koma wina ndi wolema ndipo pangafunike anthu aŵili kuti aunyamule. Mnzanuyo afuna kukupatsani katundu wakuti munyamule. Kodi angakupatseni katundu wofunika kunyamula anthu aŵili? Iyai. Sangafune kuti mudzipweteke pokupatsani katundu wolema kuti munyamule nokha. Mofananamo, Mulungu wathu wacikondi ndi wacifundo, satipatsa malamulo amene sitingakwanitse kuwatsatila. (Deuteronomo 30:11-14) Sangafune kuti tinyamule katundu wolema conco. Yehova amadziŵa kupeleŵela kwathu. Popeza “iye akudziŵa bwino mmene anatiumbila, amakumbukila kuti ndife fumbi.”—Salimo 103:14.

15. N’cifukwa ciani tingakhale ndi cidalilo cakuti malamulo a Yehova angatipindulitse?

15 Malamulo a Yehova si olemetsa ngakhale pang’ono; ndipo amatipindulitsa. (Ŵelengani Yesaya 48:17) Ndiye cifukwa cake Mose anauza Aisiraeli akale kuti: “Yehova anatilamula kuti tizitsatila malangizo onsewa, tiziopa Yehova Mulungu wathu ndi kupindula nthawi zonse, kuti tikhale ndi moyo monga mmene zilili lelo.” (Deuteronomo 6:24) Nafenso tingakhale ndi cidalilo cakuti pamene Yehova anatipatsa malamulo ake, amafuna kuti zinthu zizitiyendela bwino nthawi zonse. Ndithudi n’zosatheka kuti Yehova atipatse malamulo ovuta cifukwa iye ali ndi nzelu zopanda malile. (Aroma 11:33) Motelo iye amadziŵa bwino zimene zingatipindulitse. Kuonjezela pamenepo, Yehova ndiye mwini cikondi. (1 Yohane 4:8) Cikondi ndi khalidwe lake lalikulu, ndipo cimasonkhezela zokamba ndi zocita zake zonse. Cikondi ndiye maziko a malamulo onse amene iye amapatsa atumiki ake.

16. N’cifukwa ciani n’zotheka kukhala omvela mosasamala kanthu za mzimu woipa wa dzikoli ndi thupi lathu lopanda ungwilo?

16 Koma zimenezi sizitanthauza kuti kumvela Mulungu n’kopepuka nthawi zonse. Tifunika kupewa mzimu wa dziko loipali, limene “lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Tifunikanso kulimbana ndi thupi lathu lopanda ungwilo, limene limatipangitsa kuphwanya malamulo a Mulungu. (Aroma 7:21-25) Koma cikondi cathu pa Mulungu cingatithandize kugonjetsa mzimu woipa wa dzikoli ndi thupi lathu lopanda ungwilo. Yehova amadalitsa anthu amene amaonetsa cikondi cao pa iye mwa kukhala omvela. Amapeleka mzimu wake woyela kwa “omumvela monga wolamulila.” (Machitidwe 5:32) Mzimu umenewu umabala cipatso cokongola mwa ife, cimene ndi makhalidwe abwino amene angatithandize kukhalabe omvela.—Agalatiya 5:22, 23.

17, 18. (a) Tidzaphunzila ciani m’buku lino? Ndipo tiyenela kukumbukila ciani pamene tiphunzila zimenezo? (b) Kodi m’nkhani yotsatila tidzaphunzila ciani?

17 M’buku lino, tidzaphunzila mfundo za Yehova ndi miyezo yake ya makhalidwe abwino, ndi zinthu zina zimene zingatithandize kudziŵa cifunilo cake. Pamene tiphunzila zimenezo, tiyenela kukumbukila mfundo zingapo zofunika. Tizikumbukila kuti Yehova satikakamiza kutsatila malamulo ake ndi mfundo zake. M’malomwake, iye amafuna kuti tizimumvela mocokela pansi pa mtima. Tisaiŵale kuti Yehova amafuna kuti tizicita zinthu zimene zingatibweletsele madalitso tsopano ndi moyo wamuyaya mtsogolo. Ndipo tiyenela kuzindikila kuti kumvela kwathu ndi mtima wonse ndi mwai wamtengo wapatali woonetsa Yehova kuti timam’konda kwambili.

18 Kuti atithandize kusiyanitsa cabwino ndi coipa, Yehova mwacikondi cake anatilenga ndi cikumbumtima. Koma kuti cikumbumtima cathu cizititsogolela bwino, tiyenela kuciphunzitsa. Zimenezi ndi zimene tidzaphunzila m’nkhani yotsatila.

^ par. 11 Ngakhale ziŵanda nthawi zina zimamvela, koma mokakamizika. Pamene Yesu analamula ziŵanda kuti zituluke mwa anthu, izo zinakakamizika kuzindikila ulamulilo wake ndi kumumvela monyinyilika.—Maliko 1:27; 5:7-13.

^ par. 13 Pa Mateyu 23:4, liu la Cigiriki limenelo analigwilitsila nchito kutanthauza ‘akatundu olema,’ kapena kuti malamulo ambilimbili ndi miyambo ya anthu. Alembi ndi Afalisi anali kukakamiza anthu wamba kutsatila zimenezo. Liu limenelo analitembenuzanso kuti “opondeleza” pa Machitidwe 20:29, 30, ndipo limatanthauza ampatuko ankhanza amene anali “kulankhula zinthu zopotoka” ndi colinga cakuti apatutse ena.