Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 3

Muzikonda Anthu Amene Mulungu Amawakonda

Muzikonda Anthu Amene Mulungu Amawakonda

“Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.”—MIYAMBO 13:20.

1-3. (a) Kodi Baibulo limafotokoza mfundo yosatsutsika iti? (b) Kodi tingasankhe bwanji mabwenzi amene angatilimbikitse kuchita zabwino?

ANTHUFE tili ngati thonje. Likaikidwa m’madzi, limayamwa madziwo. Nafenso timakonda kutengera anthu otizungulira. Ndipo n’zosavuta kutengera maganizo, mfundo ndi makhalidwe a anthu amene timacheza nawo kwambiri.

2 Baibulo limafotokoza mfundo yosatsutsika imeneyi motere: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” (Miyambo 13:20) Mwambi umenewu umanena za anthu amene amagwirizana kwambiri. Mawu akuti ‘kuyenda ndi,’ akunena za anthu amene amacheza limodzi nthawi zonse. Ponena za lembali, buku lina lofotokoza Baibulo linati: “Kuyenda ndi munthu kumatanthauza kukondana naye ndi kumukhulupirira kwambiri.” Kodi simukuvomereza kuti nthawi zambiri timatengera zochita za anthu amene timawakonda? Popeza timakhulupirira kwambiri anthu amene timawakonda, zimakhala zosavuta kutengera makhalidwe awo abwino kapena oipa.

3 Kuti Mulungu apitirize kutikonda, tiyenera kupeza mabwenzi amene angatilimbikitse kuchita zabwino. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi? Kunena mwachidule, tingachite zimenezi ngati timakonda anthu amene Mulungu amawakonda, kapena kugwirizana ndi mabwenzi a Mulungu. Taganizirani izi: Kodi mungapezenso mabwenzi abwino kuposa amene Yehova amawaona kuti ndi oyenera kukhala mabwenzi ake? Nanga kodi Mulungu amakonda anthu otani? Tiyeni tikambirane zimenezi, ndipo tikadziwa zimene Yehova amaona posankha mabwenzi, tidzatha kusankha mabwenzi oyenera.

ANTHU AMENE MULUNGU AMAWAKONDA

4. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova amasamala posankha mabwenzi, ndipo n’chifukwa chiyani anamutchula Abulahamu kuti “bwenzi langa”?

4 Yehova amakhala wosamala kwambiri posankha mabwenzi. Ndipo mpake kuti amatero. Pajatu iye ndi Ambuye Wamkulu Koposa m’chilengedwe chonse, moti kukhala naye pa ubwenzi ndi mwayi wosayerekezeka. Ndiyeno, kodi iye amasankha anthu otani kuti akhale mabwenzi ake? Yehova amakonda anthu amene amamudalira ndi kumukhulupirira ndi mtima wonse. Mwachitsanzo, taganizirani za Abulahamu, munthu amene anali ndi chikhulupiriro cholimba. Ndi zovuta kwambiri kuti kholo lipereke mwana wake nsembe. Koma izi n’zimene Abulahamu anapemphedwa kuchita. * Ndipo iye anali wokonzeka ‘kupereka Isaki nsembe’ chifukwa ankakhulupirira “kuti Mulungu ali ndi mphamvu zomuukitsa kwa akufa.” (Aheberi 11:17-19) Apatu Abulahamu anasonyeza chikhulupiriro ndi mtima womvera, ndipo Yehova anamutchula mochokera pansi pa mtima kuti “bwenzi langa.”—Yesaya 41:8; Yakobo 2:21-23.

5. Kodi Yehova amawaona bwanji anthu amene amamumvera mokhulupirika?

5 Yehova amaona kuti kukhulupirika ndi kumvera n’kofunika kwambiri. Iye amakonda anthu amene akufuna kukhala okhulupirika kwa iye zivute zitani. (Werengani 2 Samueli 22:26.) Monga mmene tinaonera m’mutu 1 wa bukuli, Yehova amakondwera kwambiri ndi anthu amene amasankha kumumvera chifukwa chomukonda. Lemba la Miyambo 3:32 limasonyeza kuti iye amakonda kwambiri anthu “owongoka mtima.” Yehova amalandira mokoma mtima anthu amene amatsatira malamulo ake mokhulupirika monga alendo “m’chihema” chake, kutanthauza kuti amawalola kumulambira komanso kupemphera kwa iye.—Salimo 15:1-5.

6. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yesu, ndipo Yehova amamva bwanji akamaona anthu amene amakonda Mwana wake?

6 Yehova amakonda anthu amene amakonda Yesu, yemwe ndi Mwana wake wobadwa yekha. Yesu anati: “Ngati munthu amandikonda, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo tidzapita kwa iwo ndi kukakhala nawo.” (Yohane 14:23) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yesu? Tingachite zimenezi posunga malamulo ake ndipo limodzi mwa malamulo akewa ndi loti tizilalikira uthenga wabwino ndi kuphunzitsa anthu. (Mateyu 28:19, 20; Yohane 14:15, 21) Tingasonyezenso kuti timakonda Yesu ngati ‘timatsatira mapazi ake mosamala kwambiri.’ Zimenezi zikutanthauza kuti anthu opanda ungwirofe tiyenera kuyesetsa kumutsanzira, m’zolankhula ndi zochita zathu. (1 Petulo 2:21) Yehova akamaona anthu amene akuyesetsa kukhala ngati Khristu chifukwa chomukonda, mtima wake umasangalala kwambiri.

7. Kodi n’chifukwa chiyani ndi nzeru kusankha mabwenzi a Yehova kuti akhale mabwenzi athu?

7 Ena mwa makhalidwe amene Yehova amafuna kuti mabwenzi ake akhale nawo ndi chikhulupiriro, kukhulupirika, kumvera ndiponso kukonda Yesu. Aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi mabwenzi anga apamtima ali ndi makhalidwe amenewa? Kodi ndasankha mabwenzi a Yehova kukhalanso mabwenzi anga?’ Ndi nzeru kuchita zimenezi. Anthu amene ali ndi makhalidwe amene Mulungu amafuna ndipo amalalikira uthenga wabwino wa Ufumu mwakhama, angatithandize kwambiri. Iwo angatilimbikitse kusasiya kukondweretsa Mulungu.—Onani bokosi lakuti: “ Kodi Bwenzi Labwino Limakhala Lotani?

CHITSANZO CHA M’BAIBULO

8. Kodi n’chiyani chikukuchititsani chidwi ndi ubwenzi wa (a) Naomi ndi Rute? (b) anyamata atatu achiheberi? (c) Paulo ndi Timoteyo?

8 M’Malemba muli zitsanzo zambiri za anthu amene zinthu zinawayendera bwino kwambiri chifukwa chosankha mabwenzi oyenera. Mungathe kuwerenga za ubwenzi wa Naomi ndi mpongozi wake Rute, za ubwenzi wa anyamata atatu achiheberi amene anali ogwirizana kwambiri ku Babulo, komanso za ubwenzi wa Paulo ndi Timoteyo. (Rute 1:16; Danieli 3:17, 18; 1 Akorinto 4:17; Afilipi 2:20-22) Koma panopo tiyeni tikambirane za chitsanzo china chabwino kwambiri, cha ubwenzi wa Davide ndi Yonatani.

9, 10. Kodi n’chifukwa chiyani Davide ndi Yonatani ankakondana kwambiri?

9 Baibulo limanena kuti Davide atapha Goliyati, “Yonatani anagwirizana kwambiri ndi Davide, moti anayamba kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondera yekha.” (1 Samueli 18:1) Apa m’pamene panayambira ubwenzi wawo wolimba kwambiri. Ngakhale kuti iwo anali osiyana kwambiri zaka, ubwenzi wawo unapitirira mpaka pamene Yonatani anakaphedwa kunkhondo. * (2 Samueli 1:26) Kodi n’chifukwa chiyani ubwenzi wa anthu awiriwa unali wolimba choncho?

10 Davide ndi Yonatani ankagwirizana kwambiri chifukwa chakuti onse ankakonda Mulungu ndiponso ankafunitsitsa kukhalabe okhulupirika kwa iye. Amuna awiri onsewa ankakonda zinthu zauzimu. Iwo ankakondana chifukwa aliyense ankasirira makhalidwe a mnzake. Mosakayika Yonatani anachita chidwi ndi kulimba mtima komanso kudzipereka kumene mnyamatayu anasonyeza poteteza dzina la Yehova mopanda mantha. Nayenso Davide ayenera kuti ankalemekeza kwambiri munthu wachikulireyu amene anagonjera mokhulupirika zimene Yehova anakonza komanso analibe nsanje ndipo ankam’funira zabwino. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika pamene Davide anali wokhumudwa kwambiri. Nthawi imeneyi iye ankakhala m’chipululu pothawa Sauli, bambo ake a Yonatani, omwe anali mfumu yoipa imene inkafuna kumupha. Apa Yonatani anasonyeza kukhulupirika kwambiri pamene ananyamuka ‘ndi kupita kwa Davide  . . . , kuti akamulimbikitse kudalira Mulungu.’ (1 Samueli 23:16) Davide ayenera kuti anasangalala kwambiri bwenzi lake Yonatani atabwera kudzamulimbikitsa. *

11. Kodi chitsanzo cha Yonatani ndi Davide chakuphunzitsani chiyani pa nkhani yosankha mabwenzi?

11 Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Yonatani ndi Davide? Mfundo yaikulu imene tikuphunzira ndi yoti, chinthu chofunika kwambiri kwa mabwenzi n’chakuti onsewo azikonda zinthu zauzimu. Tizikondana ndi anthu amene ali ndi zikhulupiriro, makhalidwe komanso amene amafuna kukhala okhulupirika kwa Mulungu ngati ifeyo. Zimenezi zingathandize kuti tizigwirizana maganizo, kukonda zinthu zofanana ndiponso kuti tiziuzana zinthu zolimbikitsana. (Werengani Aroma 1:11, 12.) Tingapeze mabwenzi oterewa pakati pa Akhristu anzathu. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti aliyense amene amabwera kudzasonkhana ku Nyumba ya Ufumu ndi bwenzi labwino? Ayi.

TIZISANKHA MABWENZI MOSAMALA

12, 13. (a) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kusamala posankha mabwenzi ngakhale pakati pa Akhristu anzathu? (b) Kodi mipingo ya m’nthawi ya atumwi inakumana ndi vuto lotani, ndipo zimenezi zinachititsa Paulo kupereka machenjezo amphamvu otani?

12 Ngakhale mumpingo, tiyenera kusamala ngati tikufuna kupeza mabwenzi amene angatilimbikitse mwauzimu. Kodi tiyenera kudabwa nazo zimenezi? Ayi. Akhristu ena mumpingo amatenga nthawi yaitali kuti akhwime mwauzimu, mofanana ndi mmene zipatso zina mumtengo zingatengere nthawi yaitali kuti zipse. Choncho mumpingo uliwonse, muli Akhristu amene misinkhu yawo ndi yosiyanasiyana mwauzimu. (Aheberi 5:12–6:3) Komabe, timakhala oleza mtima ndi achikondi kwa anthu atsopano kapena osalimba, chifukwa timafuna kuwathandiza kuti akule mwauzimu.—Aroma 14:1; 15:1.

13 Nthawi zina, mumpingo mungachitike zinthu zina zimene zingafune kuti tisamale ndi anthu amene timacheza nawo. Anthu ena angayambe kuchita zinthu zokayikitsa. Ena angakhale ndi mtima woipidwa ndi zinthu zina kapena wokonda kudandaula. Mipingo ya m’nthawi ya atumwi inakumananso ndi vuto lofanana ndi limeneli. Ambiri anali okhulupirika, koma panalinso ena amene khalidwe lawo silinali labwino. Mwachitsanzo, ena mumpingo wa ku Korinto sankakhulupirira ziphunzitso zina zachikhristu. N’chifukwa chake mtumwi Paulo anachenjeza mpingowo kuti: “Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:12, 33) Paulo anachenjeza Timoteyo kuti ngakhale pakati pa Akhristu, pangakhale Akhristu ena amene zochita zawo si zabwino. Timoteyo anauzidwa kuti asamagwirizane kwambiri ndi anthu oterowo kapena aziwapeweratu.—Werengani 2 Timoteyo 2:20-22.

14. Kodi tingamvere bwanji machenjezo a Paulo pa nkhani yosankha anthu ocheza nawo?

14 Kodi tingamvere bwanji machenjezo a Paulo? Tingachite zimenezi tikamapewa kugwirizana kwambiri ndi wina aliyense amene angakhale ndi makhalidwe oipa, kaya mumpingo kapena kunja kwa mpingo. (2 Atesalonika 3:6, 7, 14) Tiyenera kuteteza moyo wathu wauzimu. Kumbukirani kuti mofanana ndi thonje, timatengera maganizo ndi makhalidwe a mabwenzi athu apamtima. Tikaika thonje m’madzi akuda, sitingayembekezere kuti litulukamo loyera. Choncho sizingatheke kutengera makhalidwe abwino ngati timagwirizana ndi anthu amene ali ndi makhalidwe oipa.—1 Akorinto 5:6.

Mungapeze mabwenzi abwino pakati pa Akhristu anzanu

15. Kodi muyenera kuchita chiyani kuti mupeze mabwenzi okonda zinthu zauzimu mumpingo?

15 Komabe chosangalatsa n’chakuti n’zotheka kupeza mabwenzi abwino ambiri pakati pa Akhristu anzathu. (Salimo 133:1) Kodi mungatani kuti mupeze mabwenzi okonda zinthu zauzimu mumpingo? Choyamba, inuyo muyenera kuyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene Mulungu amakondwera nawo. Mukatero, anthu enanso amene akuyesetsa kuchita zimenezi, mosakayikira adzakukondani kwambiri. Komanso, muyenera kuchita zinthu zimene zingakuthandizeni kupeza mabwenzi atsopano. (Onani bokosi lakuti: “ Zimene Ndinachita Kuti Ndipeze Mabwenzi Abwino.”) Pofuna mabwenzi, muziona anthu amene ali ndi makhalidwe omwe inuyo mumafuna kukhala nawo. Muzitsatira malangizo a m’Baibulo akuti “futukulani mtima wanu.” Mungachite zimenezi pofufuza mabwenzi pakati pa okhulupirira anzanu mosayang’ana khungu, mtundu kapena chikhalidwe chawo. (2 Akorinto 6:13; werengani 1 Petulo 2:17.) Musamangocheza ndi anthu amsinkhu wanu okha. Kumbukirani kuti Yonatani anali wamkulu kwambiri kuposa Davide. Popeza kuti anthu achikulire ambiri amadziwa zochuluka ndiponso ali ndi nzeru, kucheza nawo kungakupindulitseni kwambiri.

PAKAKHALA MAVUTO

16, 17. Ngati wolambira mnzathu watilakwira, n’chifukwa chiyani sitiyenera kusiya kusonkhana ndi mpingo?

16 Popeza kuti anthufe tili ndi makhalidwe osiyanasiyana komanso tinakulira kosiyana, nthawi zina mumpingo mungakhale mavuto. Wokhulupirira mnzathu anganene kapena kuchita zinthu zimene zingatikhumudwitse. (Miyambo 12:18) Nthawi zina mavuto amayamba chifukwa cha kusamvetsetsana, kusemphana maganizo kapena chifukwa chosiyana chikhalidwe. Kodi tiyenera kukhumudwa ndi mavuto amenewa n’kusiya kusonkhana ndi mpingowo? Ngati timakondadi Yehova ndi anthu amene amawakonda, sitingachite zimenezi.

17 Yehova ndi Mlengi wathu ndipo ndi amene amatisamalira, choncho, tiyenera kumukonda ndi kudzipereka kwa iye ndi mtima wonse. (Chivumbulutso 4:11) Ndiponso, tiyenera kukhala okhulupirika mumpingo umene amaugwiritsa ntchito. (Aheberi 13:17) Choncho, ngati wolambira mnzathu watilakwira kapena kutikhumudwitsa, sitidzasiya kusonkhana ndi mpingowo pofuna kumusonyeza kukhumudwa kwathu. Ndipo tingachite bwanji zimenezi ngati kuti Yehova ndi amene watilakwira? Sitingalole kum’siya Yehova ndi anthu ake chifukwa chakuti timamukonda.—Werengani Salimo 119:165.

18. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti mumpingo mukhale mtendere? (b) Kodi kukhululukira ena, kumabweretsa madalitso otani?

18 Kukonda Akhristu anzathu kumatithandiza kulimbikitsa mtendere mumpingo. Yehova sayembekezera kuti anthu amene amawakonda azichita zinthu mwangwiro. Nafenso sitiyenera kutero. Chikondi chimatithandiza kunyalanyaza zolakwa zazing’ono, pokumbukira kuti tonsefe ndife opanda ungwiro ndipo timalakwa. (Miyambo 17:9; 1 Petulo 4:8) Chikondi chimatithandizanso kupitiriza “kukhululukirana ndi mtima wonse.” (Akolose 3:13) Koma nthawi zina zimakhala zovuta kutsatira malangizo amenewa. Tikamalola mkwiyo kutilamulira, tingamasunge chakukhosi, mwina n’kumaganiza kuti tikukhaulitsa munthu amene watilakwirayo. Koma kunena zoona, kusunga chakukhosi kumangokhala kudzivulaza tokha. Mosiyana ndi zimenezi, kusankha kukhululukira ena, kumabweretsa madalitso ambiri. (Luka 17:3, 4) Kumatipatsa mtendere wa m’maganizo ndi mumtima, kumathandiza kuti mumpingo mukhale mtendere, ndipo koposa zonse, kumateteza ubwenzi wathu ndi Yehova.—Mateyu 6:14, 15; Aroma 14:19.

NTHAWI YOYENERA KUSIYA KUGWIRIZANA NDI WINAWAKE

19. Kodi ndi nthawi iti pamene tiyenera kusiya kugwirizana ndi munthu wina?

19 Nthawi zina timalangizidwa kusiya kugwirizana ndi munthu amene timasonkhana naye mumpingo. Zimenezi zimachitika ngati munthu amene amaswa malamulo a Mulungu popanda kulapa wachotsedwa mumpingo, kapena pamene wina wakana chikhulupiriro n’kuyamba kuphunzitsa chiphunzitso chonyenga, kapenanso pamene wina wadzilekanitsa ndi mpingo. Mawu a Mulungu amatilamula momveka bwino kuti ‘tileke kuyanjana’ ndi anthu otere. * (Werengani 1 Akorinto 5:11-13; 2 Yohane 9-11) Zingakhale zovuta kwambiri kuti tizipewa munthu amene anali mnzathu wapamtima kapenanso wachibale. Kodi zikatere, tidzalimba mtima kusonyeza kuti timafuna kukhala okhulupirika kwa Yehova ndi malamulo ake olungama zivute zitani? Kumbukirani kuti Yehova amaona kuti kukhulupirika komanso kumvera n’kofunika kwambiri.

20, 21. (a) Kodi n’chifukwa chiyani dongosolo lochotsa munthu mumpingo limasonyeza chikondi cha Yehova? (b) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kusankha mabwenzi mwanzeru?

20 Dongosolo lochotsa munthu mumpingo limasonyeza chikondi cha Yehova. Chifukwa chiyani zili choncho? Kuchotsa munthu wosalapa mumpingo kumasonyeza kuti timakonda dzina loyera la Yehova ndi zonse zimene dzinalo limaimira. (1 Petulo 1:15, 16) Komanso kuchotsa munthu mumpingo kumateteza mpingowo. Anthu okhulupirika mumpingomo amatetezedwa kuti asatengere makhalidwe oipa a anthu ochimwa mwadala ndipo amapitiriza kulambira kwawo akudziwa kuti mpingo ndi malo achitetezo m’dziko loipali. (1 Akorinto 5:7; Aheberi 12:15, 16) Chilango chokhwima chimenechi chimasonyeza chikondi kwa wolakwayo. Ndiponso, mwina n’chimene chingamuthandize kudzidzimuka ndi kuzindikira kulakwa kwake ndipo kenako kupeza zoyenera kuchita kuti abwerere kwa Yehova.—Aheberi 12:11.

21 Kaya tifune kapena tisafune, timatengera makhalidwe a anthu amene timagwirizana nawo. Choncho, tiyenera kusankha mabwenzi athu mwanzeru. Ngati timasankha mabwenzi a Yehova kuti akhale mabwenzi athu ndiponso ngati timakonda anthu amene Mulungu amawakonda, tidzakhala ndi mabwenzi abwino kwambiri. Makhalidwe amene tingatengere kwa iwo adzatithandiza kusasiya kukondweretsa Yehova.

^ ndime 4 Popempha Abulahamu kuchita zimenezi, Yehova anafuna kusonyeza kuti iyenso adzapereka nsembe Mwana wake wobadwa yekha. (Yohane 3:16) Komabe, Abulahamu sanapereke mwana wake nsembe chifukwa Yehova anamuletsa ndipo anam’patsa nkhosa yamphongo imene anapereka m’malo mwa mwana wake Isaki.—Genesis 22:1, 2, 9-13.

^ ndime 9 Davide anali wachinyamata kapena “mwana” pamene anapha Goliyati, koma pa nthawi imene Yonatani anaphedwa, Davide anali ndi zaka pafupifupi 30. (1 Samueli 17:33; 31:2; 2 Samueli 5:4) Zikuoneka kuti Yonatani ndi Davide ankasiyana ndi zaka pafupifupi 30, chifukwa Yonatani anafa ali ndi zaka pafupifupi 60.

^ ndime 10 Lemba la 1 Samueli 23:17 limasonyeza kuti Yonatani ananena zinthu 5 polimbikitsa Davide. Zinthu zake ndi izi: (1) Analimbikitsa Davide kuti asachite mantha. (2) Anatsimikizira Davide kuti Sauli adzamulephera. (3) Anakumbutsa Davide kuti adzakhala mfumu, monga mmene Mulungu analonjezera. (4) Analumbira kuti iye adzakhala wokhulupirika kwa Davide. (5) Anauza Davide kuti ngakhale bambo ake, Sauli, ankadziwa kuti Yonataniyo anali wokhulupirika kwa Davide.

^ ndime 19 Kuti mudziwe zambiri za mmene tiyenera kuchitira ndi anthu ochotsedwa kapena odzilekanitsa, onani Zakumapeto Mmene Tiyenera Kuchitira ndi Munthu Wochotsedwa.”