Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 3

Kondani Anthu Amene Mulungu Amakonda

Kondani Anthu Amene Mulungu Amakonda

“Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu.”—MIYAMBO 13:20.

1, 2. Ndi mfundo yosatsutsika iti imene Baibulo limafotokoza?

ANTHUFE tili ngati thonje limene limayamwa zinthu zamadzi zilizonse zimene mwaliviikamo ndi kutengela mtundu wake. Mofananamo, munthu angatengele mosavuta maganizo ndi makhalidwe a anthu amene amaceza nao.

2 Baibulo limachula mfundo yosatsutsika yakuti: “Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu, koma wocita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” (Miyambo 13:20) Mwambi umenewu sukamba za kuceza wamba. Mau akuti “woyenda ndi” angatanthauze kuyanjana kwa nthawi zonse. * Pothilila ndemanga pavesi limeneli, buku lina lofotokozela Baibulo linati: “Kuyenda ndi munthu wina kumatanthauza kukondana ndi kugwilizana naye.” Kodi si zoona kuti timatengela zocita za anthu amene timakonda? N’zoona, cifukwa cakuti timagwilizana kwambili ndi anthu amene timakonda, io angatisonkhezele kucita zabwino kapena zoipa.

3. (a) Kodi tingasankhe motani mabwenzi amene angatilimbikitse kucita zabwino?

3 Kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu, tifunika kupeza mabwenzi amene angatilimbikitse kucita zabwino. Kodi tingacite bwanji zimenezo? Mwacidule, tiyenela kukonda anthu amene Mulungu amakonda, kupanga mabwenzi a Mulungu kukhala mabwenzi athu. Tangoganizilani, kodi pangakhalenso mabwenzi ena abwino kuposa amene ali ndi makhalidwe amene Yehova amafuna? Tsopano tiyeni tione kuti ndi anthu a makhalidwe otani amene Mulungu amakonda. Tikadziŵa anthu amene Yehova amakonda, tidzakhala okonzeka kusankha mabwenzi abwino.

ANTHU AMENE YEHOVA AMAKONDA

4. N’cifukwa ciani m’pake kuti Yehova sasankha mabwenzi cisankhesankhe? N’cifukwa ciani Yehova anacha Abulahamu kuti “bwenzi langa”?

4 Pankhani yosankha mabwenzi, Yehova sasankha cisankhesankhe. Iye amasankha mosamala kwambili. Popeza kuti iye ndi Ambuye Wamkulu Koposa m’cilengedwe, kukhala bwenzi lake ndi mwai wamtengo wapatali kwambili. Nanga ndi anthu otani amene iye amasankha kukhala mabwenzi ake? Yehova amasankha anthu amene amam’dalila ndi kum’khulupilila kwathunthu. Mwacitsanzo, ganizilani za kholo lakale Abulahamu amene anali wokhulupilika kwambili. Kwa munthu aliyense, palibe ciyeso ca cikhulupililo cimene cingapose kumuuza kuti apeleke mwana wake nsembe. * Koma kwa Abulahamu “zinali ngati wapeleka kale Isaki nsembe,” cifukwa anakhulupilila ndi mtima wonse kuti “Mulungu ali ndi mphamvu zomuukitsa kwa akufa.” (Aheberi 11:17-19) Popeza kuti Abulahamu anaonetsa cikhulupililo ca mtundu umenewo ndi kumvela, Yehova mwacikondi anamucha kuti “bwenzi langa.”—Yesaya 41:8; Yakobo 2:21-23.

5. Kodi Yehova amawaona bwanji anthu amene amamumvela mokhulupilika?

5 Yehova amaona kuti kumumvela mokhulupilika n’cinthu cofunika kwambili. Iye amakonda anthu amene amaona kukhulupilika kukhala kofunika kuposa ciliconse. (Ŵelengani 2 Samueli 22:26.) Monga mmene tinaphunzilila m’Nkhani 1 ya buku lino, Yehova amakondwela kwambili ndi anthu amene amamumvela cifukwa comukonda. Lemba la Miyambo 3:32 limakamba kuti iye “amakonda anthu oongoka mtima.” Anthu amene amatsatila malangizo a Mulungu mokhulupilika amaitanidwa ndi Yehova kuti akhale alendo “m’cihema” cake. Ndipo iye amawalola kuti azimulambila ndi kukamba naye m’pemphelo momasuka.—Salimo 15:1-5.

6. Tingaonetse bwanji kuti timam’konda Yesu? Nanga Yehova amawaona bwanji anthu amene amakonda Mwana wake?

6 Yehova amakonda anthu amene amakonda Yesu, mwana wake wobadwa yekha. Yesu anati: “Ngati munthu amandikonda ine, adzasunga mau anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo tidzapita kwa io ndi kukakhala nao.” (Yohane 14:23) Kodi tingaonetse bwanji kuti timam’konda Yesu? Mwa kumvela malamulo ake, kuphatikizapo lamulo lakuti tizilalikila uthenga wabwino ndi kupanga ophunzila. (Mateyu 28:19, 20; Yohane 14:15, 21) Timaonetsanso kuti timam’konda Yesu mwa ‘kutsatila mapazi ake mosamala kwambili,’ kumutsatila m’mau ndi m’zocita zathu mmene tingathele monga anthu opanda ungwilo. (1 Petulo 2:21) Mtima wa Yehova umakondwela ndi anthu amene amayesayesa kutsatila citsanzo ca Kristu cifukwa cokonda Mwanayo.

7. N’cifukwa ciani ndi kwanzelu kupalana ubwenzi ndi mabwenzi a Yehova?

7 Makhalidwe ena amene Yehova amafuna mwa mabwenzi ake ndi cikhulupililo, kukhulupilika, kumvela, ndi kukonda Yesu ndi njila zake. Conco, aliyense wa ife ayenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi mabwenzi anga ali ndi makhalidwe amenewa? Kodi ndapanga mabwenzi a Yehova kukhala mabwenzi anga?’ Kucita zimenezi n’kofunika. Anthu amene amakulitsa makhalidwe aumulungu, ndi kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu mokangalika, angatithandize kuti tipitilize kukondweletsa Mulungu.—Onani kabokosi kakuti “ Kodi Bwenzi Labwino Limakhala Lotani?

 

KUTENGELAPO PHUNZILO PA CITSANZO CA M’BAIBULO

8. N’ciani cimakucititsani cidwi ndi ubwenzi wa (a) Naomi ndi Rute? (b) anyamata atatu aciheberi? (c) Paulo ndi Timoteyo?

8 M’Malemba muli zitsanzo zambili za anthu amene anapindula cifukwa cosankha mabwenzi abwino. Mungaŵelenge za ubwenzi wa Naomi ndi mpongozi wake Rute, ubwenzi wa anyamata atatu aciheberi amene sanatayane pamene anali ku Babulo, ndi ubwenzi wa Paulo ndi Timoteyo. (Rute 1:16; Danieli 3:17, 18; 1 Akorinto 4:17; Afilipi 2:20-22) Koma tiyeni tikambilane citsanzo cimodzi ca ubwenzi wapadela kwambili wa pakati pa Davide ndi Yonatani.

9, 10. N’ciani cinapangitsa kuti ubwenzi wa Davide ndi Yonatani ukhale wolimba?

9 Baibulo limakamba kuti pamene Davide anapha Goliyati, “Yonatani anagwilizana kwambili ndi Davide, moti anayamba kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondela yekha.” (1 Samueli 18:1) Apa ndiye panayambila ubwenzi wathithithi ngakhale kuti io anali osiyana kwambili zaka zakubadwa. Ndipo ubwenzi umenewu unapitililabe mpaka pamene Yonatani anaphedwa kunkhondo. * (2 Samueli 1:26) N’ciani cinapangitsa kuti ubwenzi wa anthu aŵili amenewa ukhale wolimba kwambili?

10 Cimene cinapangitsa kuti Davide ndi Yonatani akhale pa ubwenzi wolimba cinali cikondi cao pa Mulungu ndi mtima wofunitsitsa kukhalabe okhulupilika kwa iye. Onse aŵili anali ofunitsitsa kukondweletsa Mulungu. Aliyense wa io anali ndi makhalidwe okondweletsa mnzake. Mosakaikila, Yonatani anacita cidwi ndi kulimba mtima ndi kukangalika kwa Davide wacinyamatayo pa kuteteza dzina la Yehova mopanda mantha. Nayenso Davide analemekeza mwamuna wacikulileyo, amene anacilikiza makonzedwe a Yehova mokhulupilika, ndi kuika zofuna za Davide patsogolo pa zake mopanda dyela. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika kwa Davide pamene anali wolefuka ndi wothaŵathaŵa m’cipululu poopa Mfumu yoipa Sauli, atate ake a Yonatani. Pofuna kuonetsa kukhulupilika kwake, Yonatani anacitapo kanthu mwa “kupita kwa Davide. . . kuti akalimbikitse Davide kudalila Yehova.” (1 Samueli 23:16) Tangoganizilani mmene Davide anamvelela pamene mnzake wapamtima anabwela kudzam’thandiza ndi kumulimbikitsa! *

11. N’ciani cimene mwaphunzilapo pa ubwenzi wa Davide ndi Yonatani?

11 Kodi tikuphunzila ciani pa citsanzo ca Davide ndi Yonatani? Tiphunzilapo kuti cinthu cofunika kwambili pakati pa mabwenzi ndico kukonda zinthu za kuuzimu. Ngati tigwilizana ndi anthu amene timafanana nao cikhulupililo ndi makhalidwe, ndiponso amene amafuna kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu monga ife, tingayambe kugwilizana maganizo, kukonda zinthu zofanana, ndi kulimbikitsana. (Ŵelengani Aroma 1:11, 12.) Mabwenzi okonda zinthu za kuuzimu amenewo timawapeza pakati pa olambila anzathu. Koma kodi zimenezi zitanthauza kuti aliyense amene timasonkhana naye ku Nyumba ya Ufumu ndi bwenzi labwino? Osati kwenikweni.

MMENE TINGASANKHILE MABWENZI ENIENI

12, 13. (a) N’cifukwa ciani tifunika kukhala osamala posankha mabwenzi ngakhale pakati pa Akristu anzathu? (b) Kodi m’mipingo ya m’nthawi ya atumwi munali vuto lotani? Nanga vutolo linapangitsa kuti Paulo apeleke uphungu wamphamvu uti?

12 Ngakhale mumpingo, tiyenela kusamala kuti tisankhe mabwenzi amene angatilimbikitse mwakuuzimu. Kodi zimenezi ziyenela kutidabwitsa? Osati kwenikweni. Akristu ena mumpingo angatenge nthawi yaitali kuti akhwime mwakuuzimu, monga mmene zipatso zina mu mtengo zimatengela nthawi yaitali kuti zipse. Conco, mumpingo uliwonse mumapezeka Akristu amene ali pa misinkhu yosiyanasiyana kuuzimu. (Aheberi 5:12–6:3) Komabe, tiyenela kukhala oleza mtima ndi acikondi kwa atsopano kapena ofooka, kuti tiwathandize kukula mwakuuzimu.—Aroma 14:1; 15:1.

13 Koma nthawi zina mumpingo mungacitike zinthu zimene zingafune kuti tizikhala osamala posankha anthu oyanjana nao. Anthu ena angayambe kucita zinthu zokaikitsa kwambili. Ena angayambe kukulitsa mzimu wokonda kusuliza kapena kudandaula. M’mipingo ya m’nthawi ya atumwi munalinso vuto limeneli. Ngakhale kuti ambili anali okhulupilika, panali anthu ena amene makhalidwe ao sanali abwino. Cifukwa cakuti ena mumpingo wa ku Korinto sanali kuvomeleza ziphunzitso zina zacikristu, mtumwi Paulo anacenjeza mpingowo kuti: “Musasoceletsedwe. Kugwilizana ndi anthu oipa kumaononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:12, 33) Paulo anacenjeza Timoteyo kuti, ngakhale pakati pa Akristu, pangakhale ena ocita zinthu zosayenela. Timoteyo anauzidwa kuti apewe anthu otelo, ndi kuti asakhale nao paubwenzi.—Ŵelengani 2 Timoteyo 2:20-22.

14. Tingagwilitsile nchito bwanji mfundo imene ikupezeka m’malangizo a Paulo pankhani yokhudza mabwenzi?

14 Kodi mfundo imene ikupezeka m’malangizo amene Paulo anapeleka tingaigwilitsile nchito bwanji? Mwa kupewa kupalana ubwenzi ndi aliyense mumpingo kapena kunja kwa mpingo amene angatisoceletse. (2 Atesalonika 3:6, 7, 14) Tiyenela kuteteza ubwenzi wathu ndi Yehova. Kumbukilani kuti monga mmene thonje limacitila, ife anthu timatengela maganizo ndi zocita za mabwenzi amene timaceza nao. Sitingayembekezele thonje kukhala loyela ngati taliviika m’madzi akuda. Mofananamo, sitingakhale ndi makhalidwe abwino ngati timaceza ndi anthu amene ali ndi makhalidwe oipa.—1 Akorinto 5:6.

Mungapeze mabwenzi abwino pakati pa Akristu anzanu

15. N’ciani cimene mungacite kuti mupeze mabwenzi okonda zinthu za kuuzimu mumpingo?

15 Koma ubwino wake ndi wakuti tingapeze mabwenzi enieni pakati pa Akristu anzathu. (Salimo 133:1) Kodi mungawapeze bwanji mabwenzi okonda zinthu za kuuzimu mumpingo? Mukakhala ndi makhalidwe aumulungu, mosakaikila ena amene ali ndi makhalidwe ofanana ndi anu, adzafuna kukhala mabwenzi anu. Koma inunso mufunika kucitapo kanthu kuti mupeze mabwenzi atsopano. (Onani kabokosi kakuti “ Mmene Ndinapezela Mabwenzi Abwino,” Sankhani mabwenzi amene ali ndi makhalidwe amene inunso mumakonda. Tsatilani uphungu wa m’Baibulo wakuti “futukulani mtima wanu,” mwa kufunafuna mabwenzi pakati pa okhulupilila anzanu, mosayang’ana mtundu wao, dziko lao, kapena cikhalidwe cao. (2 Akorinto 6:13; ŵelengani 1 Petulo 2:17.) Musamaceze cabe ndi anthu a msinkhu wanu. Kumbukilani kuti Yonatani anali wamkulu kwambili kuposa Davide. Mukakhala ndi mabwenzi acikulile, mungapindulenso kwambili cifukwa io amadziŵa zambili ndipo ali ndi nzelu.

 

PAKABUKA MAVUTO

16, 17. N’cifukwa ciani sitifunika kuleka kusonkhana ngati Mkristu mnzathu watikhumudwitsa?

16 Popeza mumpingo muli anthu a maumunthu osiyanasiyana ndipo anakula mosiyanasiyana, nthawi zina pangabuke mavuto. Mkristu mnzathu angakambe kapena kucita zinthu zimene zingatikwiitse. (Miyambo 12:18) Nthawi zina mavuto amabuka cifukwa ca kusiyana kwa khalidwe, kusamvana, kapena kusiyana maganizo. Kodi tidzakhumudwa cifukwa ca zimenezi ndi kuleka kusonkhana? Ngati timakondadi Yehova ndi anthu amene iye amakonda, sitingacite zimenezo.

17 Popeza Yehova ndi Mlengi wathu ndipo amatipatsa zinthu zofunikila pa moyo wathu, tiyenela kum’konda ndi kudzipeleka kwa iye ndi mtima wonse. (Chivumbulutso 4:11) Tiyenelanso kucilikiza mokhulupilika mpingo umene iye amaugwilitsila nchito. (Aheberi 13:17) Cotelo, ngati Mkristu mnzathu watilakwila kapena kutikhumudwitsa, sitidzaleka kusonkhana poonetsa kusakondwa. Kodi tingacitilenji zimenezo monga kuti Yehova ndiye watikhumudwitsa? Ngati timakonda Yehova, sitidzamusiya kapena kusiya anthu ake.—Ŵelengani Salimo 119:165.

18. (a) N’ciani cimene tingacite kuti tilimbitse mtendele mumpingo? (b) Ndi madalitso otani amene timapeza ngati timakhululukila ena ngati m’poyenela kutelo?

18 Kukonda Akristu anzathu kumatilimbikitsa kukhala mwamtendele ndi onse mumpingo. Yehova sayembekezela mabwenzi ake kucita zinthu mwa ungwilo, ifenso tisamacite zimenezo. Cikondi cimatithandiza kuiŵala zolakwa zing’onozing’ono za ena, ndi kukumbukila kuti tonse ndife opanda ungwilo ndipo timalakwa. (Miyambo 17:9; 1 Petulo 4:8) Cikondi cimatithandiza kupitiliza “kukhululukilana ndi mtima wonse.” (Akolose 3:13) Nthawi zina kutsatila uphungu umenewu kumavuta. Ngati tilola mkwiyo kutilamulila, tingayambe kusunga cakukhosi, ndi kuganiza kuti kucita zimenezo ndi njila imodzi yokhaulitsila amene watilakwila. Koma kukamba zoona, kusunga cakukhosi kumavulaza. Kukhululukila ena ngati pali cifukwa comveka, kumabweletsa madalitso osaneneka. (Luka 17:3, 4) Kumatipangitsa kukhala ndi mtendele wa mumtima, kumathandiza kuti mpingo ukhale pamtendele, ndipo koposa zonse kumateteza ubwenzi wathu ndi Yehova.—Mateyu 6:14, 15; Aroma 14:19.

PAMENE TIFUNIKA KULEKA KUYANJANA NDI MUNTHU WINA

19. Kodi tiyenela kuleka kuyanjana ndi munthu wina mumpingo pa zifukwa ziti?

19 Nthawi zina tingafunike kuleka kuyanjana ndi munthu amene anali Mkristu mnzathu mumpingo. Zimenezi zimacitika ngati munthu amaphwanya malamulo a Mulungu mwadala ndipo wacotsedwa mumpingo, kapena ngati wakana cikhulupililo mwa kuphunzitsa ziphunzitso zabodza, kapenanso ngati wadzilekanitsa ndi mpingo. Mau a Mulungu amatiuza mosapita m’mbali kuti ‘lekani kuyanjana ndi aliyense’ wocita zimenezi. * (Ŵelengani 1 Akorinto 5:11-13; 2 Yohane 9-11) Zingakhale zovuta kwambili kuleka kuyanjana ndi munthu amene anali mnzathu kapena wacibanja wathu. Tiyenela kutsatila malangizo amenewa molimba mtima ndi kuonetsa kuti timaona kukhulupilika kwathu kwa Yehova ndi malamulo ake olungama kukhala zofunika kuposa cina ciliconse. Musaiŵale kuti Yehova amaona kukhulupilika ndi kumvela kukhala zinthu zofunika kwambili.

20, 21. (a) N’cifukwa ciani ndi makonzedwe acikondi kucotsa anthu osalapa mumpingo? (b) N’cifukwa ciani tifunika kusankha mabwenzi athu mwanzelu?

20 Kucotsa munthu mumpingo ndi makonzedwe acikondi a Yehova. Motani? Kucotsa munthu wosalapa kumaonetsa kuti timakonda Yehova, dzina lake loyela ndi miyezo yake. (1 Petulo 1:15, 16) Kuonjezela pamenepo, kucita zimenezi kumateteza mpingo. Anthu okhulupilika mumpingo amatetezeka kuti asatengele makhalidwe oipa a anthu ocimwila dala. Ndipo amapitiliza kulambila Yehova momasuka ali ndi cidalilo cakuti mpingo ndi malo acitetezo m’dziko loipali. (1 Akorinto 5:7; Aheberi 12:15, 16) Kupeleka cilango camphamvu cimeneci kumasonyeza cikondi kwa munthu wocimwayo. Cilangoci cingathandize wocimwayo kuona kuti afunika kusintha khalidwe lake ndi kubwelela kwa Yehova.—Aheberi 12:11.

21 N’zodziŵikilatu kuti ife anthu, timatengela kwambili zocita za mabwenzi athu apamtima. Conco, tiyenela kusankha mabwenzi athu mwanzelu. Mwa kupanga mabwenzi a Yehova kukhala mabwenzi athu, ndi kukonda anthu amene Mulungu amakonda, tidzakhala ndi mabwenzi abwino kwambili. Zimene timatengela kwa io zingatithandize kupitiliza kukondweletsa Yehova.

^ par. 2 Liu la Ciheberi lotembenuzidwa kuti “kucita zinthu ndi,” latembenuzidwanso kuti “kukhala ndi,” ndiponso ‘kugwilizana.’—Oweruza 14:20; Miyambo 22:24.

^ par. 4 Mwa kuuza Abulahamu kucita zimenezi, Yehova anapeleka cithunzi ca nsembe ya mwana wake wobadwa yekha, imene iye anali kudzapeleka. (Yohane 3:16) Pankhani ya Abulahamu, Yehova analoŵelelapo, ndipo anapeleka nkhosa kuti ipelekedwe nsembe m’malo mwa Isaki.—Genesis 22:1, 2, 9-13.

^ par. 9 Davide anali mnyamata, kapena kuti “mwana,” pamene anapha Goliyati, ndipo anali ndi zaka pafupifupi 30 pamene Yonatani anafa. (1 Samueli 17:33; 31:2; 2 Samueli 5:4) Yonatani anali ndi zaka pafupifupi 60 pamene anafa. Mwacionekele iye anali wamkulu kuposa Davide ndi zaka pafupifupi 30.

^ par. 10 Malinga ndi lemba la 1 Samueli 23:17, Yonatani anakamba zinthu zisanu kuti alimbikitse Davide: (1) Analimbikitsa Davide kuti asacite mantha. (2) Anatsimikizila Davide kuti zocita za Sauli zidzalephela. (3) Anakumbutsa Davide kuti adzapatsidwa ufumu monga mmene Mulungu analonjezela. (4) Analonjeza kuti adzapitiliza kukhala wokhulupilika kwa Davide. (5) Yonatani anauza Davide kuti ngakhale Sauli anali kudziŵa kuti iye ndi wokhulupilika kwa Davide.

^ par. 19 Kuti mudziŵe zambili za mmene mungacitile ndi munthu wocotsedwa kapena wodzilekanitsa, onani Zakumapeto mutu wakuti “Kodi Tiyenela Kucita Bwanji ndi Munthu Wocotsedwa?.”