Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 6

Mmene Mungasankhile Zosangulutsa Zabwino

Mmene Mungasankhile Zosangulutsa Zabwino

“Citani zonse ku ulemelelo wa Mulungu.” —1 AKORINTO 10:31.

1, 2. Kodi tingafunike kupanga zosankha zotani pankhani ya zosangulutsa?

YELEKEZELANI kuti mufuna kudya cipatso cokoma kwambili, koma muona kuti mbali yake ina ndi yoola. Kodi mungacite ciani? Ngati mufuna mungadye cipatso conseco, pamodzi ndi mbali yoolayo kapena mungataye cipatso conseco kapenanso mungaceke ndi kucotsako mbali yoolayo ndi kudya mbali yabwino. Kodi inuyo mungasankhe kucita ciani?

2 Zosangulutsa zili ngati cipatso. Nthawi zina, mungafune kusangalalako, koma mumaona kuti zosangulutsa zambili zimene zilipo masiku ano ndi zoipa kwambili ngati cipatso coola. Nanga inu mungacite bwanji? Ena amakonda zosangulutsa zilizonse zoipa za m’dzikoli. Ena amapewelatu zosangulutsa zonse kuti asakhudzidwe ndi zinthu zilizonse zovulaza. Enanso amapewa zosangulutsa zoipa, koma amakhala ndi nthawi ya zosangulutsa zabwino. Kuti mukhalebe m’cikondi ca Mulungu, kodi muyenela kupanga cosankha citi?

3. Kodi tidzakambitsilana ciani m’nkhani ino?

3 Ambili a ife tingasankhe njila yacitatu. Timadziŵa kuti zosangulutsa n’zofunika, koma timafuna kusankha zosangulutsa zabwino zokhazokha. Conco, tidzakambilana mmene tingadziŵile zosangulutsa zabwino ndi zoipa. Koma coyamba, tiyeni tikambitsilane mmene zosangulutsa zimene timasankha zingakhudzile kulambila kwathu Yehova.

“CITANI ZONSE KU ULEMELELO WA MULUNGU”

4. Kodi kudzipeleka kwathu kuyenela kukhudza bwanji zosangulutsa zimene timasankha?

4 Mboni ina yacikulile imene inabatizidwa mu 1946 inati: “Ndimaonetsetsa kuti ndapezeka pankhani ya ubatizo iliyonse ndi kuimvetsela mwachelu, monga kuti ndine amene ndipita ku ubatizo.” N’cifukwa ciani amatelo? M’baleyo anafotokoza kuti, “Kukumbukila kuti ndinadzipeleka kwa Mulungu kwandithandiza kukhalabe wokhulupilika.” Mosakaikila, inunso mungavomeleze zimene m’baleyu anakamba. Kukumbukila kuti munalonjeza Yehova kuti mudzamutumikila kwa umoyo wanu wonse, kumakuthandizani kupilila. (Ŵelengani Mlaliki 5:4.) Ndipo kusinkhasinkha pa kudzipeleka kwanu kudzakhudza mmene mumaonela utumiki wanu, komanso mmene mumaonela mbali zonse za umoyo wanu kuphatikizapo zosangulutsa. Mtumwi Paulo anagogomezela mfundo imeneyi pamene analembela Akristu a m’nthawi yake kuti; “Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukucita cina ciliconse, citani zonse ku ulemelelo wa Mulungu.”—1 Akorinto 10:31.

5. Kodi lemba la Levitiko 22:18-20, lingatithandize bwanji kuzindikila cenjezo la pa Aroma 12:1?

5 Zinthu zilizonse zimene mumacita paumoyo wanu zimakhudza kulambila kwanu Yehova. M’kalata imene Paulo analembela Aroma, iye anagwilitsila nchito mau amphamvu kuti atsindike mfundo imeneyi kwa okhulupilila anzake. Anawalimbikitsa kuti: “Mupeleke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyela ndi yovomelezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwilitsa nchito luntha la kuganiza.” (Aroma 12:1) Thupi lanu limaphatikizapo nzelu zanu, mtima wanu ndi mphamvu zanu. Zonsezi mumazigwilitsila nchito potumikila Mulungu. (Maliko 12:30) Paulo ananena kuti utumiki umenewu, umene timacita ndi moyo wathu wonse uli ngati nsembe. Liu lakuti nsembe limeneli ndi cenjezo, ngakhale kuti silinachulidwe mwacindunji. M’Cilamulo ca Mose, Mulungu anali kukana nsembe zolemala. (Levitiko 22:18-20) Mofananamo, ngati nsembe ya kuuzimu ya Mkristu ndi yodetsedwa mwa njila iliyonse, Mulungu amaikana. Koma, kodi zimenezi zingacitike bwanji?

6, 7. Kodi Mkristu angadetse bwanji thupi lake? Nanga zotsatilapo zake zingakhale zotani?

6 Paulo analimbikitsa Akristu a ku Roma kuti: “Musapeleke ziwalo zanu [“ziwalo za thupi,” New International Version] ku uchimo.” Paulo anawauzanso kuti: ‘Muphe zocita za thupi.’ (Aroma 6:12-14; 8:13) Panthawi ina m’kalata yake, iye anapeleka zitsanzo zina za “zocita za thupi” zimenezi. Ponena za anthu ocimwa, timaŵelenga kuti: “M’kamwa mwao mwadzaza mau otukwana.” “Mapazi ao amathamangila kukhetsa magazi.” “Maso ao saona cifukwa coopela Mulungu.” (Aroma 3:13-18) Mkristu angadetse thupi lake ngati agwilitsila nchito “ziwalo” za thupi kucita nchito za thupi zimenezi. Mwacitsanzo, masiku ano ngati Mkristu mwadala amaonelela zinthu zoipa monga zamalisece kapena zaciwawa, ndiye kuti ‘apeleka [maso ake] ku ucimo’ ndipo akudetsa thupi lake lonse. Kulambila kwake konse kumakhala nsembe yodetsedwa ndi yosavomelezeka kwa Mulungu. (Deuteronomo 15:21; 1 Petulo 1:14-16; 2 Petulo 3:11) Limenelo ndi tsoka lalikulu limene munthu angakumane nalo ngati amasankha zosangulutsa zoipa.

7 Conco, zosangulutsa zimene Mkristu angasankhe zingakhale ndi zotsatilapo zoopsa. Ndiye cifukwa cake tiyenela kusankha zosangulutsa zimene zingapangitse nsembe yathu kwa Mulungu kukhala yabwino osati yodetsedwa. Tiyeni tsopano tikambilane mmene tingadziŵile zosangulutsa zoyenela ndi zosayenela.

“NYANSIDWANI NDI COIPA”

8, 9. (a) Kodi zosangulutsa zingagaŵidwe m’magulu aŵili ati? (b) Kodi ndi zosangulutsa ziti zimene tiyenela kupewa? Nanga n’cifukwa ciani?

8 Mwacidule, zosangulutsa zingagaŵidwe m’magulu aŵili. Gulu loyamba ndi zosangulutsa zimene Akristu amapewa, ndipo gulu lina ndi zosangulutsa zimene Akristu ayenela kudzisankhila okha. Tiyeni tikambilane gulu loyamba limene ndi zosangulutsa zimene Akristu amapewa.

9 Monga mmene tinaphunzilila m’Nkhani 1, zosangulutsa zina zimakhala ndi zinthu zimene Baibulo limaletsa mwacindunji. Mwacitsanzo, ganizilani mawebusaiti, mafilimu, mapulogilamu a pa TV, ndi nyimbo zokhudza zinthu za mizimu kapena zamalisece ndiponso zimene zimacilikiza zaciwelewele. Zosangulutsa zimenezi zimacititsa kuti zinthu zosemphana ndi mfundo ndi malamulo a m’Baibulo zizioneka ngati zabwino. Conco, Akristu oona ayenela kuzipewa. (Machitidwe 15:28, 29; 1 Akorinto 6:9, 10; Chivumbulutso 21:8) Mwa kupewa zosangulutsa zoipa zimenezi, mumatsimikizila Yehova kuti ‘mumanyansidwa ndi coipa’ ndipo nthawi zonse ‘mumapatuka pa zinthu zoipa.’ Mukacita zimenezo, ndiye kuti muli ndi “cikhulupililo copanda cinyengo.”—Aroma 12:9; Salimo 34:14; 1 Timoteyo 1:5.

10. Kodi ndi maganizo ati okhudza zosangulutsa amene ndi oopsa? Ndipo n’cifukwa ciani ndi oopsa?

10 Akristu ena angaganize kuti kupenyelela zosangulutsa zimene zimaonetsa zaciwelewele kulibe vuto. Iwo angakambe kuti ‘Ndingapenyelele zinthu zimenezi m’mafilimu kapena pa TV, koma ine sindingacite zimenezo.’ Maganizo amenewo ndi onyenga ndipo ndi oopsa. (Ŵelengani Yeremiya 17:9.) Ngati timakonda kupenyelela zinthu zimene Yehova amadana nazo, kodi tinganene kuti ‘tikunyansidwa ndi coipa’? Ngati timapenyelela zoipa mobwelezabweleza zikhoza kuononga maganizo athu. (Salimo 119:70; 1 Timoteyo 4:1, 2) Kucita zimenezo kungayambukile zimene timacita kapena mmene timaonela khalidwe loipa la ena.

11. N’ciani cikuonetsa kuti lemba la Agalatiya 6:7 limanena zoona pankhani ya zosangulutsa?

11 Zinthu zotelo zacitikapo. Akristu ena anacita zaciwelewele cifukwa ca cizoloŵezi copenyelela zosangulutsa zoipa. Iwo anamva nkhwangwa ili m’mutu kuti “ciliconse cimene munthu wafesa, adzakololanso comweco.” (Agalatiya 6:7) Koma zimenezi n’zotheka kuzipewa. Ngati mufesa zinthu zabwino m’maganizo mwanu, ndiye kuti paumoyo wanu mudzakolola zabwino.—Onani bokosi lakuti “ Kodi Ndisankhe Ziti?

ZOSANKHA ZAUMWINI ZOZIKIDWA PA MFUNDO ZA M’BAIBULO

12. Kodi lemba la Agalatiya 6:5 limakhudza bwanji zosangulutsa? Nanga n’ciani cingatithandize popanga zosankha?

12 Tiyeni tikambilane gulu laciŵili limene ndi zosangulutsa zimene Mau a Mulungu satsutsa kapena kuvomeleza mwacindunji. Posankha zosangulutsa zotelo, Mkristu ayenela kudzisankhila yekha zimene aona kuti n’zabwino. (Ŵelengani Agalatiya 6:5.) Koma sikuti tilibe citsogozo. M’Baibulo muli mfundo za coonadi, zimene zimatithandiza kuzindikila maganizo a Yehova. Mwa kugwilitsila nchito mfundo zimenezi, tidzazindikila “cifunilo ca Yehova” pa zinthu zonse kuphatikizapo zosangulutsa zimene tiyenela kusankha.—Aefeso 5:17.

13. N’ciani cingatithandize kupewa zosangulutsa zimene zingakhumudwitse Yehova?

13 N’zoona kuti Akristu onse alibe luso lofanana pankhani yozindikila coyenela ndi cosayenela. (Afilipi 1:9) Ndiponso, Akristu amadziŵa kuti pankhani ya zosangulutsa amakonda zinthu zosiyanasiyana. Conco, sitingayembekezele kuti Akristu onse angapange zosankha zofanana. Ngakhale ndi conco, pamene tilola mfundo za Mulungu kutsogolela maganizo athu ndi mtima wathu, tidzakhala okonzeka kupewa zosangulutsa zilizonse zimene zingakhumudwitse Yehova.—Salimo 119:11, 129; 1 Petulo 2:16.

14. (a) Kodi tiyenela kuganizila ciani posankha zosangulutsa? (b) N’ciani cimene tingacite kuti zinthu za Ufumu zikhalebe patsogolo?

14 Mfundo ina yofunika imene muyenela kuiganizila posankha zosangulutsa ndi nthawi yanu. Zosangulutsa zimene mumasankha zimaonetsa zinthu zimene mumaona kuti ndi zoyenela, koma nthawi imene mumathela pa zosangulutsazo imaonetsa zimene mumaona kuti n’zofunika. Koma kwa Akristu zinthu za kuuzimu ndiye zofunika kwambili. (Ŵelengani Mateyu 6:33.) Nanga n’ciani cimene mungacite kuti zinthu za Ufumu zikhalebe patsogolo? Mtumwi Paulo anati: “Samalani kwambili kuti mmene mukuyendela si monga anthu opanda nzelu, koma ngati anzelu. Muzigwilitsa nchito bwino nthawi yanu.” (Aefeso 5:15, 16) Ndithudi, kuika malile pa nthawi imene mumathela pa zosangulutsa kudzakuthandizani kuti mupeze nthawi yocita “zinthu zofunika kwambili.” Kucita zinthu zofunika kwambili kudzalimbitsa umoyo wanu wa kuuzimu.—Afilipi 1:10.

15. N’cifukwa n’ciani ndi bwino kukhala osamala kwambili posankha zosangulutsa?

15 Tiyenelanso kukhala osamala kwambili posankha zosangulutsa. Kodi zimenezi zikutanthauza ciani? Ganizilaninso citsanzo cija ca cipatso. Kuti mupewe kudya mosadziŵa mbali yoola, simuceka ndendende pamalo oola, koma mumacekako pang’ono mbali yabwino. Mofananamo, ndi bwino kusamala posankha zosangulutsa. Mkristu wanzelu samangopewa cabe zosangulutsa zimene zimaphwanya mfundo za m’Baibulo. Koma iye amapewanso zosangulutsa zokaikitsa kapena zosangulutsa zokhala ndi mbali zimene zingaononge ubwenzi wake ndi Yehova. (Miyambo 4:25-27) Kutsatila Mau a Mulungu mosamalitsa, kudzakuthandizani kuti mucite zimenezo.

“ZINTHU ZILIZONSE ZOYELA”

Kugwilitsila nchito mfundo za Mulungu posankha zosangulutsa kumatiteteza kuuzimu

16. (a) Kodi mungaonetse bwanji kuti muli ndi maganizo a Yehova pankhani ya makhalidwe? (b) Mungacite ciani kuti kutsatila mfundo za m’Baibulo kukhale cizoloŵezi canu?

16 Posankha zosangulutsa, coyamba Akristu oona amaganizila mmene Yehova amaonela zinthu. Baibulo limafotokoza mmene Yehova amaonela zinthu ndi miyezo yake. Mwacitsanzo, Mfumu Solomo inachula zinthu zingapo zimene Yehova amadana nazo, monga “lilime lonama, manja okhetsa magazi a anthu osalakwa, mtima wokonzela ena ziwembu, mapazi othamangila kukacita zoipa.” (Miyambo 6:16-19) Kodi kudziŵa mmene Yehova amaonela zinthu kuyenela kukhudza motani mmene inu mumaonela zinthu? Wamasalimo anatilangiza kuti: “Inu okonda Yehova danani naco coipa.” (Salimo 97:10) Zosangulutsa zanu ziyenela kuonetsa kuti mumadanadi ndi zimene Yehova amadana nazo. (Agalatiya 5:19-21) Ndiponso kumbukilani kuti zimene mumacita mseli, ndizo zimene zimaonetsa umunthu wanu weniweni kuposa zimene mumacita pagulu. (Salimo 11:4; 16:8) Motelo, ngati pa umoyo wanu wonse mumafunadi kuonetsa kuti muli ndi maganizo a Yehova pa nkhani ya makhalidwe, nthawi zonse mudzasankha zinthu mogwilizana ndi mfundo za m’Baibulo. Ndipo cimeneci cidzakhala cizoloŵezi canu.—2 Akorinto 3:18.

17. Kodi ndi mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa tisanasankhe zosangulutsa?

17 Ndi zinthu zina ziti zimene mungacite kuti muonetse kuti mumatsatila njila za Yehova pankhani yosankha zosangulutsa? Dzifunseni kuti: ‘Kodi zimenezi zidzandikhudza bwanji, ndipo zidzakhudza bwanji ubwenzi wanga ndi Mulungu?’ Mwacitsanzo, musanasankhe filimu yakuti mupenyelele, mungadzifunse kuti, ‘Kodi zimene zili mufilimu imeneyi zidzakhudza bwanji cikumbumtima canga?’ Tiyeni tikambilane mfundo zimene mungagwilitsile nchito pankhaniyi.

18, 19. (a) Kodi mfundo yopezeka pa Afilipi 4:8 ingatithandize bwanji kudziŵa ngati zosangulutsa zathu ndi zabwino? (b) Ndi mfundo zina ziti zimene zingakuthandizeni kusankha zosangulutsa zabwino? (Onani mau a munsi.)

18 Mfundo yofunika kwambili ikupezeka pa lemba la Afilipi 4:8 imene imati: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambili, zilizonse zolungama, zilizonse zoyela, zilizonse zacikondi, zilizonse zoyamikilika, khalidwe labwino lililonse, ndi ciliconse cotamandika, pitilizani kuganizila zimenezi.” N’zoona kuti Paulo sanali kukamba nkhani ya zosangulutsa, koma anali kukamba za kusinkhasinkha kwa mtima kumene kumakondweletsa Mulungu. (Salimo 19:14) Koma mau a Paulo amenewa amagwilanso nchito pankhani ya zosangulutsa. Motani?

19 Dzifunseni kuti, ‘Kodi mafilimu, maseŵela a pavidiyo, nyimbo kapena zosangulutsa zina zimene ndimasankha zimadzaza maganizo anga ndi “zilizonse zoyela”?’ Mwacitsanzo, kodi mumakhala ndi maganizo otani pambuyo popenyelela filimu ina yake? Ngati mumakhala ndi maganizo abwino, oyela, ndi otsitsimula, ndiye kuti zosangulutsa zanu zinali zoyenela. Koma ngati filimuyo imakusiyani ndi maganizo oipa, ndiye kuti zosangulutsa zimenezo zinali zosayenela, ngakhale zovulaza kumene. (Mateyu 12:33; Maliko 7:20-23) N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti kuganizila zinthu zoipa, kungasokoneze mtendele wanu wa m’maganizo, kungavulaze cikumbumtima canu cophunzitsidwa Baibulo ndipo kungaononge unansi wanu ndi Mulungu. (Aefeso 5:5; 1 Timoteyo 1:5, 19) Popeza kuti zosangulutsa zimenezo zingakuonongeni, onetsetsani kuti mukuzipewa. * (Aroma 12:2) Khalani monga wamasalimo amene anapemphela kwa Yehova kuti: “Cititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.”—Salimo 119:37.

FUNANI ZOPINDULITSA ENA

20, 21. Kodi lemba la 1 Akorinto 10:23, 24, lingatithandize bwanji posankha zosangulutsa zabwino?

20 Paulo anachula mfundo yofunika kwambili ya m’Baibulo imene tiyenela kuiganizila pamene tipanga zosankha zaumwini. Iye anati: “Zinthu zonse ndi zololeka, koma si zonse zimene zili zolimbikitsa. Aliyense asamangodzifunila zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.” (1 Akorinto 10:23, 24) Kodi mfundo imeneyi imagwilizana bwanji ndi nkhani yosankha zosangulutsa zabwino? Muyenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi ena amaziona bwanji zosangulutsa zimene ndimasankha?’

21 Cikumbumtima canu cingakuloleni kusangalala ndi zosangulutsa zimene inu mungaone kuti ndi “zololeka” kapena zovomelezeka. Komabe, ngati muona kuti cikumbumtima ca Akristu anzanu siciwalola kusangalala ndi zosangulutsa zimenezo, mungasankhe kuzileka. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti simufuna ‘kucimwila abale anu,’ kapena ‘kucimwila Kristu’ mwa kucita zinthu zimene zingalepheletse anzanu kukhala okhulupilika kwa Mulungu. Zimenezi n’zimene Paulo anakamba. Tiyenela kukumbukila cenjezo lakuti: “Pewani kukhala okhumudwitsa.” (1 Akorinto 8:12; 10:32) Masiku ano, Akristu oona amamvela uphungu wabwino ndi wanzelu wa Paulo mwa kupewa zosangulutsa zimene zingakhale “zololeka” koma “zosamangilila.”—Aroma 14:1; 15:1.

22. N’cifukwa ciani Akristu amalola kukhala ndi maganizo osiyanasiyana pankhani zaumwini?

22 Koma palinso mbali ina imene tiyenela kuiganizila pankhani yofuna kupindulitsa ena. Mkristu amene cikumbumtima cake cimamutsutsa pa zosangulutsa zina, sayenela kuumilila kuti onse mumpingo azisankha zosangulutsa zimene iye amaona kuti ndizo zoyenela. Ngati iye acita zimenezo, angakhale ngati dalaivala amene afuna kuti madalaivala onse pamseu aziyendela paliŵilo limene iye afuna. Kucita zimenezo ndi kusaganizila ena. Cifukwa cokonda Akristu anzao, anthu amene ali ndi cikumbumtima cimene cimawaletsa kucita zinthu zina, ayenela kulemekeza Akristu anzao amene angasankhe zosangulutsa zosiyana ndi zao, koma zimene ndi zogwilizana ndi mfundo zacikristu. Mwa njila imeneyi, io amaonetsa kwa ‘anthu onse kuti ndi ololela.’—Afilipi 4:5; Mlaliki 7:16.

23. Kodi mungatsimikize bwanji kuti zosangulutsa zimene mumasankha ndi zoyenela?

23 Malinga ndi zimene takambilana, kodi mungatsimikize bwanji kuti zosangulutsa zimene mumasankha ndi zoyenela? Pewani zosangulutsa zilizonse zimene zimaonetsa zinthu zoipa, zimene Mau a Mulungu amaletsa. Tsatilani mfundo za m’Baibulo zimene tingagwilitsile nchito pa zosangulutsa zosiyanasiyana zimene Baibulo silichula mwacindunji. Pewani zosangulutsa zimene zingavulaze cikumbumtima canu ndiponso zimene zingakhumudwitse ena, makamaka Akristu anzanu. Onetsetsani kuti zosankha zanu zikupeleka ulemelelo kwa Mulungu ndi kukuthandizani kuti inu ndi banja lanu mukhalebe m’cikondi cake.

^ par. 19 Mfundo zina zoonjezela zokhudza zosangulutsa zimapezeka pa Miyambo 3:31; 13:20; Aefeso 5:3, 4; ndi Akolose 3:5, 8, 20.