Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 8

Mulungu Amakonda Anthu Oyela

Mulungu Amakonda Anthu Oyela

“Kwa munthu wokhalabe woyela, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyela.”—SALIMO 18:26.

1-3. (a) N’cifukwa ciani amai amaonetsetsa kuti mwana wao ndi waukhondo ndiponso wooneka bwino? (b) N’cifukwa ciani Yehova amafuna alambili ake kukhala oyela? Ndipo n’ciani cimatilimbikitsa kuti tikhalebe oyela?

AMAI akonzekeletsa mwana wao kuti apite kwina kwake. Iwo aonetsetsa kuti mwanayo wasamba, ndipo zovala zake ndi zaukhondo ndi zooneka bwino. Amaiwo amadziŵa kuti ukhondo ndi wofunika kuti mwanayo akhale wathanzi. Amadziŵanso kuti maonekedwe a mwana amaonetsanso mmene makolo ake alili.

2 Atate wathu wakumwamba Yehova, amafuna kuti atumiki ake akhale oyela. Mau ake amati: “Kwa munthu wokhalabe woyela, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyela.” * (Salimo 18:26) Yehova amatikonda; amadziŵa kuti tidzapindula kwambili tikakhala oyela. Ndiponso iye amayembekezela ife monga Mboni zake kupeleka cithunzi cabwino ca mmene iye alili. Ndithudi, maonekedwe athu oyela ndi makhalidwe athu abwino, amabweletsa ulemu osati citonzo kwa Yehova ndi dzina lake loyela.—Ezekieli 36:22; ŵelengani 1 Petulo 2:12.

3 Kudziŵa kuti Mulungu amakonda anthu oyela, kumatilimbikitsa kukhalabe oyela. Timafuna kuti makhalidwe athu azilemekeza Mulungu cifukwa timam’konda. Ndiponso timafuna kukhalabe m’cikondi cake. Conco, tiyeni tsopano tikambilane cifukwa cake tiyenela kukhala oyela, zimene kukhala oyela kumaphatikizapo, ndi zimene tingacite kuti tikhalebe oyela. Kupenda zinthu zimenezi kudzatithandiza kudziŵa ngati pali pena pamene tiyenela kuongolela.

N’CIFUKWA CIANI TIYENELA KUKHALA OYELA?

4, 5. (a) N’cifukwa cacikulu citi cimene tiyenela kukhalila oyela? (b) Kodi ciyelo ca Yehova cimaonekela bwanji m’zinthu zimene analenga?

4 Njila imodzi imene Yehova amatitsogolela ndi mwa kutipatsa citsanzo. Ndiye cifukwa cake, Mau ake amatilimbikitsa kuti ‘tizitsanzila Mulungu.’ (Aefeso 5:1) Cifukwa cacikulu cimene tiyenela kukhalila oyela n’cakuti Yehova Mulungu amene timalambila, ndi woyela m’mbali zonse.—Ŵelengani Levitiko 11:44, 45.

5 Mofanana ndi makhalidwe ambili a Yehova ndi njila zake, ciyelo cake cimaonekelanso mu zimene analenga. (Aroma 1:20) Dziko lapansi linalengedwa kuti likhale malo oyela okhalamo anthu. Yehova anapanga zinthu zimene zimathandiza kuyeletsa mpweya ndi madzi. Ndithudi, dziko lapansi lili ndi mphamvu yodziyeletsa lokha. N’zomveka kuti ciyelo ndi nkhani yofunika kwa “amene anapanga dziko lapansi.” (Yeremiya 10:12) Conco, ciyelo ndi nkhani yofunikanso kwa ife.

6, 7. Kodi Cilamulo ca Mose cinagogomeza bwanji kuti anthu olambila Yehova afunika kukhala oyela?

6 Cifukwa cina cokhalila woyela n’cakuti Yehova, Mfumu yathu ya Cilengedwe Conse, amafuna kuti olambila ake akhale oyela. M’Cilamulo cimene Yehova anapatsa Aisiraeli, ciyelo ndi kulambila zinali kuyendela limodzi. Cilamulo cinanenelatu kuti pa Tsiku Lophimba Macimo, mkulu wa ansembe anayenela kusamba osati kamodzi, koma kaŵili. (Levitiko 16:4, 23, 24) Ansembe amene anali kutsogolela anali kufunikila kusamba m’manja ndi mapazi asanapeleke nsembe kwa Yehova. (Ekisodo 30:17-21; 2 Mbiri 4:6) Cilamulo cimeneci cinachula zinthu zina zokwana 70 zimene zinali kudetsa munthu. Mwiisraeli wodetsedwa sanali kutengako mbali pa kulambila koona kulikonse, ndipo nthawi zina anali kufunika kuphedwa. (Levitiko 15:31) Munthu aliyense amene anali kukana kucita mwambo womuyeletsa, umene unali kuphatikizapo kusamba ndi kucapa zovala, anayenela ‘kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa mpingo.’—Numeri 19:17-20.

7 Ngakhale kuti sitili pansi pa Cilamulo ca Mose, Cilamuloci cimatithandiza kudziŵa maganizo a Mulungu pankhani zosiyanasiyana. Mosapita m’mbali, Cilamulo cinagogomeza mfundo yakuti anthu olambila Mulungu afunika kukhala oyela. Yehova sanasinthe. (Malaki 3:6) Iye amavomeleza kulambila kwathu kokha ngati ndi “koyela ndi kosaipitsidwa.” (Yakobo 1:27) Conco, tiyenela kudziŵa zimene tiyenela kucita kuti kulambila kwathu kukhale koyela.

ZIMENE KUKHALA WOYELA PAMASO PA MULUNGU KUMATANTHAUZA

8. Kodi Yehova amafuna kuti tikhale oyela m’mbali ziti?

8 Mfundo ya m’Baibulo yokamba za kukhala oyela, siikhudza cabe ciyelo cakuthupi. Kukhala woyela kumakhudza mbali zonse za moyo wathu. Yehova amafuna kuti tikhale oyela m’mbali zinai. Mbali zimenezi ndi kukhala oyela mwakuuzimu, mwamakhalidwe, mwamaganizo ndi mwakuthupi. Kodi mbali iliyonse imeneyi imaphatikizapo ciani? Tiyeni tikambilane.

9, 10. Kodi kukhala oyela kuuzimu kumatanthauza ciani? Ndipo Akristu oona ayenela kupewa ciani?

9 Kukhala oyela mwakuuzimu. M’mau osavuta, kukhala oyela mwakuuzimu kumatanthauza kusasakaniza kulambila koona ndi konama. Pamene Aisiraeli anacoka ku Babulo ndi kubwelela ku Yerusalemu, io anafunika kutsatila lamulo louzilidwa lakuti: “Tulukani mmenemo! Musakhudze cinthu ciliconse codetsedwa . . . Khalani oyela.” (Yesaya 52:11) Cifukwa cacikulu cimene Aisiraeli anali kubwelela kwao cinali cakuti akayambilenso kulambila Yehova. Kulambila kumeneko kunafunikila kukhala koyela, osati kodetsedwa ndi ziphunzitso, makhalidwe ndi miyambo ya cipembedzo conama yosalemekeza Mulungu.

10 Masiku ano, ife Akristu oona tiyenela kukhala osamala kwambili kuti tisaipitsidwe ndi cipembedzo conama. (Ŵelengani 1 Akorinto 10:21.) Kukhala chelu n’kofunika pankhani imeneyi cifukwa cipembedzo conama cili paliponse. M’maiko ambili, miyambo yosiyanasiyana ndi zocita zina zimagwilizana ndi ziphunzitso za cipembedzo conama, monga ciphunzitso cakuti munthu akafa cinacake m’thupi cimatuluka ndipo sicimafa. (Mlaliki 9:5, 6, 10) Akristu oona amapewa miyambo yokhudzana ndi ziphunzitso za cipembedzo conama. * Sitidzalola anthu ena kutikakamiza kuphwanya mfundo za m’Baibulo zokhudza kulambila koyela.—Machitidwe 5:29.

11. Kodi kukhala oyela m’makhalidwe kumaphatikizapo ciani? Ndipo n’cifukwa ciani kukhala oyela m’mbali imeneyi n’kofunika?

11 Kukhala ndi khalidwe loyela. Zimenezi zimaphatikizapo kupewa ciwelewele camtundu uliwonse. (Ŵelengani Aefeso 5:5.) Kukhala ndi khalidwe loyela n’kofunika kwambili. Kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu, tiyenela ‘kuthawa dama’ monga mmene tidzaonela m’nkhani yotsatila ya buku lino. Adama osalapa “sadzaloŵa mu ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10, 18) Pamaso pa Mulungu anthu otelo ali pakati pa ao “amenenso amacita zinthu zonyansa.” Ngati alephela kukhala ndi khalidwe loyela, “colandila cao cidzakhala . . . imfa yaciŵili.”—Chivumbulutso 21:8.

12, 13. Kodi zimene timacita ndi zimene timaganiza zimagwilizana bwanji? Ndipo tingacite ciani kuti tikhale ndi maganizo oyela?

12 Kukhala ndi maganizo oyela. Anthufe timacita zimene timaganiza. Ngati tilola maganizo oipa kukhala mumtima mwathu, posapita nthawi tingayambe kucita zinthu zoipa. (Mateyu 5:28; 15:18-20) Koma ngati tidzaza maganizo athu ndi zinthu zoyela, zingatithandize kukhala ndi makhalidwe oyela. (Ŵelengani Afilipi 4:8.) Kodi tingacite bwanji kuti tikhale ndi maganizo oyela? Tifunika kupewa zosangulutsa zilizonse zimene zingadetse maganizo athu. * Kuonjezela pamenepo, tingadzaze maganizo athu ndi zinthu zoyela mwa kuphunzila Mau a Mulungu nthawi zonse.—Salimo 19:8, 9.

13 Kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu, tiyenela kukhala oyela mwakuuzimu, mwamakhalidwe ndi mwamaganizo. Mbali zimenezi zafotokozedwanso m’nkhani zina m’buku lino. Tiyeni tsopano tikambitsilane mbali yacinai imene ndi kukhala oyela mwakuthupi.

KODI TINGACITE CIANI KUTI TIKHALE OYELA MWAKUTHUPI?

14. N’cifukwa ciani kukhala oyela mwakuthupi si nkhani yaumwini cabe?

14 Kukhala oyela mwakuthupi kumatanthauza kusamalila matupi athu ndi nyumba zathu. Kodi kukhala oyela mwakuthupi ndi nkhani yaumwini imene wina sayenela kuloŵelelapo? Alambili a Yehova saona nkhaniyi mwa njila imeneyi. Monga mmene taonela kale, kukhala oyela mwakuthupi ndi nkhani yofunika kwambili kwa Yehova, cifukwa cakuti timapindula komanso timaonetsa mmene iye alili. Ganizilani citsanzo cili kuciyambi kwa nkhani ino. Mwana amene nthawi zonse amakhala wauve ndi wosaoneka bwino, amatipangitsa kukaikila makolo ake. Sitifuna kuti maonekedwe athu kapena makhalidwe athu abweletse citonzo kwa Atate wathu wakumwamba kapena pa uthenga umene timalalikila. Mau a Mulungu amati: “Sitikucita ciliconse cokhumudwitsa, kuti utumiki wathu usapezedwe cifukwa. Koma tikusonyeza mwa njila ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu.” (2 Akorinto 6:3, 4) Nanga tingacite ciani kuti tikhale oyela mwakuthupi?

15, 16. Kodi kukhala waukhondo kumaphatikizapo ciani? Nanga zovala zathu ziyenela kuoneka bwanji?

15 Kukhala oyela mwakuthupi. Ngakhale kuti zikhalidwe ndi umoyo wa anthu zimasiyanasiyana malinga ndi dziko, tingakwanitse kupeza sopo ndi madzi osamba nthawi zonse, ndi kuonetsetsa kuti ife ndi ana athu tili aukhondo. Kukhala waukhondo kumaphatikizapo kusamba m’manja ndi sopo tisanadye kapena tisanagwile cakudya, tikacoka kucimbudzi, ndiponso tikamaliza kusambika kapena kusintha mwana theŵela. Kusamba m’manja ndi sopo kumatichinjiliza ku matenda ndipo kumapulumutsa miyoyo. Kumathandiza kuti tuzilombo tofalitsa matenda tusafalikile, ndipo kumatiteteza kuti tisadwale matenda otsegula m’mimba. M’maiko amene anthu alibe zimbudzi pa nyumba zao, angafocele zonyansa monga mmene zinalili mu Isiraeli wakale.—Deuteronomo 23:12, 13.

16 Tiyenela kucapa zovala zathu nthawi zonse kuti zizikhala zoyela ndi zooneka bwino. Zovala za Mkristu siziyenela kucita kukhala zodula kapena zamakono, koma ziyenela kukhala zooneka bwino, zaukhondo ndi zaulemu. (Ŵelengani 1 Timoteyo 2:9, 10.) Mosasamala kanthu za kumene timakhala, timafuna kuti maonekedwe athu ‘azikometsela ciphunzitso ca Mpulumutsi wathu, Mulungu.’—Tito 2:10.

17. N’cifukwa ciani nyumba ndi katundu wathu ziyenela kukhala zaukhondo ndi zooneka bwino?

17 Nyumba ndi katundu wathu. Ngakhale kuti nyumba yathu singakhale yapamwamba, iyenela kukhala yaukhondo ndi yooneka bwino malinga ndi mmene zinthu zilili pa umoyo wathu. Galimoto imene timagwilitsila nchito popita kumisonkhano ndi muulaliki iyenelanso kukhala yoyela mkati ndi kunja. Tisaiŵale kuti nyumba ndiponso malo aukhondo zimapeleka umboni wabwino. Ndipo timaphunzitsa anthu kuti Yehova ndi Mulungu woyela, ndi kuti ‘adzaononga amene akuononga dziko lapansi.’ Timaphunzitsanso kuti posacedwapa Ufumu wake udzasintha dziko lapansi kukhala paladaiso. (Chivumbulutso 11:18; Luka 23:43) Ndithudi, timafuna kuti nyumba yathu ndi katundu wathu zizionetsa kuti ngakhale tsopano ndife anthu aukhondo. Kukhala waukhondo n’kofunika kwambili kuti munthu adzakhale m’dziko latsopano limene likubwela.

Kukhala oyela mwakuthupi kumaphatikizapo kusamalila matupi athu ndi katundu wathu.

18. Kodi tingaonetse bwanji kuti timalemekeza Nyumba ya Ufumu?

18 Malo athu olambilila. Kukonda kwathu Yehova kumatilimbikitsa kulemekeza Nyumba ya Ufumu, imene ndi malo olambilila Mulungu woona m’dela lathu. Mabwenzi athu akabwela kudzasonkhana nafe, timafuna kuti azikhala ndi cithunzi cabwino ca malo athu olambilila. Kuyeletsa ndi kukonza nyumba ya Ufumu nthawi zonse n’kofunika kuti izioneka bwino. Timalemekeza Nyumba ya Ufumu mwa kucita zimene tingathe kuti izioneka bwino. Ndi mwai wathu kudzipeleka kuti tizithandiza kuyeletsa ndi ‘kukonza’ malo athu olambilila. (2 Mbiri 34:10) Mfundo imeneyi imagwilanso nchito pamene tili ku Bwalo la Msonkhano kapena malo ena kumene timacitila misonkhano ikuluikulu.

DZIYELETSENI MWA KUPEWA ZIZOLOŴEZI ZODETSA

19. Kuti tikhale oyela mwakuthupi, kodi tiyenela kupewa ciani? Nanga Baibulo limatithandiza bwanji pa mbali imeneyi?

19 Kuti tikhale oyela mwakuthupi, tiyenela kupewa zizoloŵezi zoipa ndi makhalidwe odetsa, monga kukoka fodya, kumwa moŵa kwambili, ndi kugwilitsila nchito mankhwala osokoneza bongo. Baibulo silichula mwacindunji makhalidwe onse odetsa amene ndi ofala masiku ano, koma limapeleka mfundo zimene zingatithandize kudziŵa mmene Yehova amaonela makhalidwe amenewa. Popeza timadziŵa mmene Yehova amaonela zinthu, cikondi cathu pa iye cimatilimbikitsa kucita zimene iye amafuna. Tiyeni tikambilane mfundo zisanu za m’Malemba.

20, 21. Kodi Yehova amafuna kuti tizipewa makhalidwe ati? Ndipo tiyenela kuwapewa pa cifukwa cacikulu citi?

20 “Okondedwanu, popeza talonjezedwa zinthu zimenezi, tiyeni tidziyeletse ndipo ticotse cinthu ciliconse coipitsa thupi kapena mzimu, kwinaku tikukwanilitsa kukhala oyela poopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Yehova amafuna kuti tipewe makhalidwe amene angadetse matupi athu ndi kuononga maganizo athu. Conco, tiyenela kupewa zizoloŵezi zoipa zimene zingaononge thupi lathu ndi maganizo athu.

21 Baibulo limatiuza cifukwa cacikulu cimene tiyenela ‘kudziyeletsela ndi kucotsa cinthu ciliconse coipitsa.’ Onani kuti lemba la 2 Akorinto 7:1 limayamba ndi mau akuti: “Popeza talonjezedwa zinthu zimenezi.” Kodi talonjezedwa ciani? Monga mmene mavesi apamwamba pa lembali amasonyezela, Yehova akulonjeza kuti: “Ndidzakulandilani. Ndidzakhala atate wanu.” (2 Akorinto 6:17, 18) Tangoganizilani! Yehova wakulonjezani kuti adzakusamalilani ndi kukukondani monga mmene tate amakondela mwana wake. Koma Yehova adzakwanilitsa malonjezo amenewa kokha ngati mupewa zodetsa za “thupi kapena mzimu.” Conco kungakhale kupusa kulola khalidwe lililonse lonyansa kuononga ubwenzi wathu wamtengo wapatali ndi Yehova.

22-25. Kodi ndi mfundo ziti za m’Malemba zimene zingatithandize kupewa makhalidwe odetsa?

22 “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mateyu 22:37) Yesu anati lamulo limeneli ndi lalikulu kuposa malamulo onse. (Mateyu 22:38) Yehova ndi woyeneleladi kum’konda conco. Kuti timukonde ndi mtima wathu, moyo wathu, ndi maganizo athu, tiyenela kupewa makhalidwe amene angafupikitse moyo wathu kapena kutilepheletsa kugwilitsila nchito nzelu zimene Mulungu anatipatsa.

23 [Yehova] amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:24, 25) Moyo ndi mphatso yocokela kwa Mulungu. Popeza kuti Mpatsi wa moyo timam’konda, tiyenela kuonetsa kuti timalemekeza mphatsoyo. Timapewa zizoloŵezi zimene zingaononge thanzi lathu, cifukwa cakuti timadziŵa kuti zizoloŵezi zotelo zimaonetsa kusalemekeza mphatso ya moyo.—Salimo 36:9.

24 “Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” (Mateyu 22:39) Nthawi zambili zizoloŵezi zoipa zimakhudza osati cabe munthu amene akucita zinthuzo, komanso anthu ena. Mwacitsanzo ngati muli pafupi ndi munthu amene akukoka fodya, inuyo ndi amene mungavulale kwambili. Munthu amene amavulaza anthu amene ali naye, amaphwanya lamulo la Mulungu lakuti tizikonda anzathu. Mwa zocita zake amaonetsa kuti ndi wabodza ngakhale akambe kuti amakonda Mulungu.—1 Yohane 4:20, 21.

25 “Pitiliza kuwakumbutsa kuti azigonjela ndi kumvela maboma ndiponso olamulila.” (Tito 3:1) M’maiko ambili, kupezeka ndi mankhwala enaake kapena kuwaseŵenzetsa ndi mlandu. Monga Akristu oona, sitiyenela kupezeka kapena kuseŵenzetsa mankhwala oletsedwa.—Aroma 13:1.

26. (a) Kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu, kodi tiyenela kucita ciani? (b) N’cifukwa ciani kukhala oyela pamaso pa Mulungu ndi njila yabwino koposa?

26 Kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu, tiyenela kukhala oyela, osati cabe m’mbali zina, koma m’mbali zonse. Kuleka makhalidwe odetsa ndi kuwapewa kungakhale kovuta, koma n’kotheka. * Ndipo kucita zimenezo ndi njila yabwino, cifukwa Yehova amatiphunzitsa nthawi zonse kuti tipindule. (Ŵelengani Yesaya 48:17.) Koposa zonse, kukhala oyela kumatipangitsa kukhala osangalala cifukwa timadziŵa kuti tikupeleka cithunzi cabwino ca Mulungu amene timakonda. Kucita zimenezo kudzatihandiza kukhalabe m’cikondi cake.

^ par. 2 Mau Aciheberi otembenuzidwa kuti “kuyela,” amakamba za ciyelo ca kuthupi, ca makhalidwe ndi ca kuuzimu.

^ par. 26 Onani bokosi lakuti “ Kodi Ndimalimbikila Kucita Zabwino?” komanso lakuti “ Zinthu Zonse N’zotheka ndi Mulungu,” limene lili pamwambapa.

^ par. 67 Maina asinthidwa.