Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 11

‘Cikwati Cikhale Colemekezeka’

‘Cikwati Cikhale Colemekezeka’

“Usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako.” —MIYAMBO 5:18.

1, 2. Kodi tidzakambitsilana funso liti? Ndipo n’cifukwa ciani?

KODI ndinu wokwatila? Ngati ndi conco, kodi mukusangalala ndi cikwati canu, kapena mumakumana ndi mavuto aakulu? Nanga cikondi canu cacepa poyelekezela ndi kale? Ngati n’telo, ndiye kuti simukusangalala cifukwa cimwemwe cimene munali naco kale cacepa. Pokhala Mkristu, mwacionekele mukufuna kuti cikwati canu cizipeleka ulemelelo kwa Yehova, Mulungu amene mumakonda. Mwina mavuto amene mumakumana nao tsopano angakudetseni nkhawa ndi kukumvetsani cisoni. Ngakhale ndi conco, musataye mtima.

2 Pali Akristu ena amene ali pabanja omwe kale anali kungokhalila kupilila. Koma tsopano anapeza njila yolimbitsila cikwati cao. Inunso mungapeze cimwemwe m’cikwati canu. Motani?

KONDANI MULUNGU NDI MNZANU

3, 4. N’cifukwa ciani anthu okwatilana amakondana kwambili akamayandikila Mulungu? Pelekani fanizo.

3 Inu ndi mnzanu wa m’cikwati mudzakondana kwambili ngati mumayesetsa kuyandikila Mulungu. N’cifukwa ciani tikutelo? Tiyeni tifanizile motele: Tinene kuti pali phili losongoka kumwamba, koma lalikulu kwambili munsi mwake. Ndiye mwamuna waimilila munsi kumbali ina, ndipo mkazi waimilila kumbali ina ya phililo. Onse aŵili ayamba kukwela phili limenelo. Pamene onse ali munsi mwa phililo amakhala otalikilana. Koma akayamba kuyandikila nsonga ya phililo, io amayamba kuyandikilana. Ndi mfundo yotani imene tikuphunzilapo m’fanizoli?

4 Khama limene mumacita potumikila Yehova mokwanila tingaliyelekezele ndi kukwela phili. Popeza mumakonda Yehova, tinganene kuti mukuyesetsa mwamphamvu kukwela phili. Koma mukaleka kukondana, zili ngati mwakhala ku mbali zosiyana za phililo. Koma n’ciani cingacitike ngati muyamba kukwela phililo? N’zoona kuti poyamba mungakhale motalikilana kwambili. Komabe, pamene mucita khama kuyandikila Mulungu, zimakhala ngati mukukwela pamwamba pa phili. Zikatelo, mumakondana kwambili ndi mnzanu. Ndithudi, kuyandikila Mulungu ndi kumene kungakuthandizeni kukondana m’banja. Koma kodi mungacite bwanji zimenezo?

Kugwilitsila nchito nzelu za m’Baibulo kudzatithandiza kulimbitsa cikwati cathu.

5. (a) Ndi njila imodzi iti imene ingatithandize kuyandikilila kwa Yehova ndi kwa mnzathu wa m’cikwati? (b) Kodi Yehova amaciona motani cikwati?

5 Njila imodzi yofunika yokwelela phili lophiphilitsa limeneli, ndi yakuti inuyo ndi mnzanu muyenela kutsatila uphungu wa m’Mau a Mulungu wokhudza cikwati. (Salimo 25:4; Yesaya 48:17, 18) Onani uphungu wina wosapita m’mbali umene Paulo anapeleka. Iye anati: “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse.” (Aheberi 13:4) Kodi mau amenewa amatanthauza ciani? Liu lakuti “wolemekezeka” limaonetsa kuti cinthuco ndi camtengo wapatali. Umu ndi mmene Yehova amaonela cikwati. Amaciona kuti ndi camtengo wapatali.

KUKONDA YEHOVA NDI MTIMA WONSE KUMALIMBITSA CIKWATI

6. Kodi zimene Paulo anakamba popeleka uphungu wonena za cikwati zimaonetsa ciani? Ndipo n’cifukwa ciani zimenezo n’zofunika kuzikumbukila?

6 Monga atumiki a Mulungu, inu ndi mnzanu mumadziŵa kuti cikwati ndi camtengo wapatali ndipo ndi copatulika. Yehova iye mwini ndi amene anayambitsa cikwati. (Ŵelengani Mateyu 19:4-6.) Koma ngati muli ndi mavuto m’cikwati canu, kungodziŵa cabe kuti cikwati ndi copatulika sikungakupangitseni kuti muzikondana ndi kulemekezana. Nanga n’ciani cingakuthandizeni kucita zimenezo? Kumbukilani mmene Paulo anafotokozela nkhani yokhudza kulemekezana. Iye sananene kuti “cikwati ndi colemekezeka;” koma anati ‘cikwati cikhale colemekezeka.’ Paulo sanali kungofotokoza mfundo, koma anali kupeleka malangizo. * Kukumbukila mfundo zimenezi kudzakuthandizani kuti muyambenso kulemekeza mnzanu. Motani?

7. (a) Ndi malamulo a m’Malemba ati amene timamvela? Nanga n’cifukwa ciani? (b) Ndi mapindu otani amene timapeza tikakhala omvela?

7 Taganizilani mmene mumaonela malamulo ena a m’Malemba, monga lakuti tizipanga ophunzila kapena lakuti tizisonkhana. (Mateyu 28:19; Aheberi 10:24, 25) N’zoona kuti nthawi zina kucita zimenezi kumakhala kovuta. Mwacitsanzo, anthu ena amene mumawalalikila ndi otsutsa, kapena nchito imene mumagwila imakutopetsani cakuti mumafunika kucita khama kwambili kuti mupezeke pa misonkhano. Ngakhale n’telo, mumayesetsa kulalikila uthenga wa Ufumu, ndi kupezeka pa misonkhano. Palibe angakuletseni kucita zimenezo, ngakhale Satana amene sangakwanitse kukuletsani. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti kukonda kwanu Yehova kocokela pansi pa mtima kumakulimbikitsani kumvela malamulo ake. (1 Yohane 5:3) Nanga mapindu ake amakhala otani? Kugwila nchito yolalikila ndi kupezeka pa misonkhano kumakupatsani mtendele wa mumtima ndi cimwemwe ceniceni cifukwa codziŵa kuti mukucita cifunilo ca Mulungu. Ndipo zimenezi zimakulimbikitsani. (Nehemiya 8:10) Kodi pamenepa tikuphunzilapo ciani?

8, 9. (a) N’ciani cingatilimbikitse kumvela malangizo akuti tizilemekeza cikwati? Nanga n’cifukwa ciani? (b) Ndi mfundo ziŵili ziti zimene tidzakambilana?

8 Kukonda kwambili Mulungu kumakulimbikitsani kumvela malamulo ake akuti muzilalikila ndi kusonkhana ngakhale mukukumana ndi mavuto. Mofananamo, kukonda kwanu Yehova kungakulimbikitseni kumvela malangizo a m’Malemba akuti, ‘cikwati [canu] cikhale colemekezeka’ ngakhale zinthu zitakhala zovuta. (Aheberi 13:4; Salimo 18:29; Mlaliki 5:4) Ndiponso, monga mmene Mulungu amadalitsila khama lanu polalikila ndi posonkhana, Yehova amaona khama limene mumacita polemekeza cikwati ndipo adzakudalitsani.—1 Atesalonika 1:3; Aheberi 6:10.

9 Nanga mungacite ciani kuti cikwati canu cikhale colemekezeka? Muyenela kupewa zinthu zimene zingaononge cikwati canu. Komanso muyenela kucita zinthu zimene zingalimbitse cikwati canu.

PEWANI KALANKHULIDWE NDI KHALIDWE LOSALEMEKEZA CIKWATI

10, 11. (a) Kodi ndi khalidwe lotani limene sililemekeza cikwati? (b) Ndi funso liti limene anthu okwatilana ayenela kuliganizila?

10 Mlongo wina anati: “Ndimapemphela kwa Yehova kuti andithandize kupilila.” Kupilila ciani? Iye anafotokoza kuti: “Amuna anga amandinyoza. Ngakhale kuti ndilibe zipsela zenizeni, koma mau ao okhadzula monga akuti ‘Wandilemetsa’ ndi akuti ‘Ndiwe wacabecabe’ amandipweteka mtima.” Mkaziyu anachula vuto lina lalikulu limene limakhala m’cikwati. Vutolo ndi kulankhula mau acipongwe.

11 N’zomvetsa cisoni kumva Akristu ena okwatilana akulankhulana mau oipa ndi opweteka mtima amene amatenga nthawi kuiŵala. Ndithudi, ngati mwamuna ndi mkazi amanyozana, cikwati cao cimakhala cosalemekezeka. Kodi inu mumalankhulana bwanji m’banja? Cimene cingakuthandizeni kudziwa mmene mumalankhulila ndi kufunsa mnzanu modzicepetsa kuti: “Kodi mau anga amakukhudzani bwanji?” Ngati mnzanuyo anena kuti mau anu kaŵilikaŵili amam’pweteka mtima, muyenela kukhala wokonzeka kusintha ndi kuongolela khalidwe lanu.—Agalatiya 5:15; ŵelengani Aefeso 4:31.

12. Kodi kulambila kwathu kungakhale bwanji kopanda pake pamaso pa Mulungu?

12 Kumbukilani kuti mmene mumagwilitsilila nchito lilime lanu m’banja, zimakhudza ubwenzi wanu ndi Yehova. Baibulo limati: “Ngati munthu akudziona ngati wopembedza, koma salamulila lilime lake, ndipo akupitiliza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.” (Yakobo 1:26) Kalankhulidwe kanu kamakhudza kwambili kulambila kwanu. Baibulo silicilikiza mfundo yakuti zilizonse zimene munthu amacita kunyumba zilibe kanthu, malinga ngati akutumikila Mulungu. Musadzinamize, nkhani imeneyi ndi yaikulu kwambili. (Ŵelengani 1 Petulo 3:7.) Mungakhale ndi luso ndi cangu, koma ngati mumalankhula mau oipa kwa mnzanu, ndiye kuti simulemekeza makonzedwe a cikwati ndipo kulambila kwanu kungakhale kopanda pake kwa Mulungu.

13. Kodi munthu wokwatila angayambitse bwanji mavuto m’banja?

13 Anthu okwatilana ayenelanso kusamala kuti asamapweteke mnzao mosadziŵa. Ganizilani zitsanzo ziŵili izi: Mai wosakwatiwa amatumila foni m’bale wokwatila wa mumpingo kupempha thandizo ndipo amakambitsilana kwa nthawi yaitali. M’bale wosakwatila amapita muulaliki mlungu uliwonse ndi mlongo wokwatiwa. M’zitsanzo zimenezi anthu okwatilawo angakhale ndi zolinga zabwino, koma kodi khalidwe lao lingakhudze bwanji mnzao? Mkazi wina wokwatiwa amene anali ndi vuto limeneli anati: “Zimandiŵaŵa kwambili ndikaona kuti mwamuna wanga kaŵilikaŵili amatenga nthawi yaitali pothandiza mlongo wina mumpingo. Ndimadzimva kukhala wacabecabe.”

14. (a) Kodi ndi udindo uti wochulidwa pa Genesis 2:24 umene anthu okwatilana ali nao? (b) Nanga tiyenela kudzifunsa ciani?

14 N’zomveka kuti mkaziyu ndi ena amene amakumana ndi mavuto amenewa m’banja apwetekedwe mtima. Anzao a m’cikwati amanyalanyaza mfundo ya Mulungu  yokhudza cikwati yakuti: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mai ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake.” (Genesis 2:24) N’zoona kuti anthu okwatila amalemekezabe makolo ao, koma  udindo wao waukulu wocokela kwa Mulungu ndi kusamalila mnzao. Mofananamo, Akristu amakonda okhulupilila anzao, koma udindo wao waukulu ndi kusamalila mwamuna kapena mkazi wao. Conco, ngati Akristu  okwatila amathela nthawi yaitali kapena  pkuzoloŵelana kwambili ndi Akristu ena, makamaka amene si amuna kapena akazi anzao, amaika banja lao pa mavuto. Kodi mwina  zimenezi ndi  zimene zabweletsa vuto m’banja lanu? Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimaceza mokwanila ndi mnzanga, kumusamalila ndi  kumuonetsa cikondi cimene amafunikila?’

15. Malinga ndi Mateyu 5:28, n’cifukwa ciani Mkristu wokwatila ayenela kupewa kuthela nthawi yaitali ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzao?

15 Ndiponso, Mkristu wokwatila amene amathela nthawi yaitali ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wake amadziika pangozi. N’zacisoni kuti Akristu ena okwatila amayamba kukondana ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wao cifukwa cozoloŵelana kwambili. (Mateyu 5:28) Ndipo zimenezi, zacititsa khalidwe losalemekeza cikwati. Onani zimene mtumwi Paulo anakamba pankhani imeneyi.

“POGONA PAKHALE POSAIPITSIDWA”

16. Kodi Paulo anapeleka lamulo lotani lokhudza cikwati?

16 Pambuyo pakuti Paulo wanena kuti “ukwati ukhale wolemekezeka,” iye anacenjezanso kuti: “Pogona pa anthu okwatilana pakhale posaipitsidwa, pakuti Mulungu adzaweluza adama ndi acigololo.” (Aheberi 13:4) Mau amene Paulo anagwilitsila nchito akuti “pogona pa anthu okwatilana” amatanthauza kugonana. Kugonana kumakhala ‘kosaipitsidwa’ kapena koyela kokha ngati kumacitikila m’cikwati. Ndiye cifukwa cake Akristu amatsatila mau ouzilidwa akuti: “Usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako.”—Miyambo 5:18.

17. (a) N’cifukwa ciani Akristu satengela maganizo a anthu pa nkhani ya cigololo? (b) Ndipo tingatsatile motani citsanzo ca Yobu?

17 Anthu amene amagonana ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wao, salemekeza malamulo a Mulungu a makhalidwe abwino ngakhale pang’ono. N’zoona kuti ambili masiku ano amaona cigololo monga khalidwe lovomelezeka. Komabe, mosasamala kanthu za mmene anthu ena amaonela cigololo, Akristu sayenela kutengela zimenezo. Iwo amazindikila kuti potsilizila pake “Mulungu adzaweluza adama ndi acigololo.” (Aheberi 10:31; 12:29) Conco, Akristu oona amatsatila zimene Yehova amanena pankhani imeneyi. (Ŵelengani Aroma 12:9.) Kumbukilani zimene Yobu ananena. Iye anati: “Ndacita pangano ndi maso anga.” (Yobu 31:1) Ndithudi, kuti Akristu oona apewe zinthu zimene zingawapangitse kucita cigololo, amalamulila maso ao ndipo sayang’ana mokhumbila munthu amene si mkazi kapena mwamuna wao.—Onani Zakumapeto mutu wakuti “Zimene Baibulo Limanena Pankhani ya Kusudzulana ndi Kupatukana.”

18. (a) Kodi cigololo ndi nkhani yaikulu motani kwa Yehova? (b) Nanga pali kufanana kotani pakati pa kucita cigololo ndi kulambila mafano?

18 Kodi cigololo ndi nkhani yaikulu bwanji kwa Yehova? Cilamulo ca Mose cimatithandiza kudziŵa mmene Yehova amaionela nkhaniyi. Mu Isiraeli, cigololo ndi kupembedza mafano anali macimo amene cilango cake cinali imfa. (Levitiko 20:2, 10) Kodi mwaona kufanana kumene kulipo pakati pa macimo aŵiliŵa? Mwisiraeli amene anali kulambila mafano, anali kuphwanya pangano lake ndi Yehova. Mofananamo, Mwisiraeli akacita cigololo anali kuphwanya pangano ndi mwamuna kapena mkazi wake. Cotelo onse aŵili anali acinyengo. (Ekisodo 19:5, 6; Deuteronomo 5:9; ŵelengani Malaki 2:14.) Anthuwo anali onyansa pamaso pa Yehova, Mulungu wokhulupilika ndi wodalilika.—Salimo 33:4.

19. N’ciani cimene cingathandize Mkristu kupewa cigololo? Ndipo n’cifukwa ciani?

19 N’zoona kuti Akristu satsatila Cilamulo ca Mose. Koma kukumbukila kuti m’nthawi ya Aisiraeli cigololo cinali chimo lalikulu, kungathandize Akristu kupewa chimo limeneli. Cifukwa ciani? Tiyelekezele motele: Kodi mungaloŵe m’chalichi, kugwada, ndi kupembedza fano? Munganene kuti: ‘Ine sindingacite zimenezo.’ Koma ngati akuuzani kuti akupatsani ndalama mukacita zimenezo, kodi mungatelo? Munganene kuti: ‘Izo n’zosatheka.’ Ndithudi, Mkristu akangoganizila za kupembedza fano amanyansidwa cifukwa amadziŵa kuti kucita zimenezo ndi kusakhulupilika kwa Yehova. Mofananamo, Akristu ayenela kunyansidwa akaganiza zokhala osakhulupilika kwa Mulungu wao, Yehova, ndi kwa mnzao wa m’banja mwa kucita cigololo mosasamala kanthu za cimene cingawakope kuti acimwe. (Salimo 51:1, 4; Akolose 3:5) Tisayese ngakhale pang’ono kucita zinthu zimene zingasangalatse Satana, ndi kunyozetsa Yehova ndi makonzedwe ake opatulika a cikwati.

MMENE MUNGALIMBITSILE CIKWATI CANU

20. N’ciani cimene cacitika m’zikwati zina? Pelekani fanizo.

20 Kuonjezela pa kupewa zinthu zimene sizilemekeza cikwati, kodi mungacite ciani kuti muyambenso kulemekeza mnzanu? Kuti tiyankhe, tiyelekezele kuti cikwati ndi nyumba ndipo zinthu zosonyeza kulemekeza mnzanu monga kukamba mau abwino kapena kumucitila zinthu zabwino, zili ngati zinthu zokongoletsa nyumbayo. Ngati mumakondana ndi mnzanu, ndiye kuti cikwati canu cidzafanana ndi nyumba imene muli zinthu zokongoletsa, ndipo nyumba yotelo imakhala yosangalatsa kukhalamo. Koma cikondi canu cikazilala, zokongoletsa zimenezi pang’onopang’ono zimaleka kuoneka bwino, titelo kunena kwake, ndipo cikwati canu cimakhala ngati nyumba imene ilibe zokongoletsa. Popeza mumafuna kumvela lamulo la Mulungu lakuti “ukwati ukhale wolemekezeka,” muyenela kucita khama kuti mukonze zinthu. Ndithudi, cinthu camtengo wapatali ndi colemekezeka cimafunika kucikonza. Kodi mungacite bwanji zimenezo? Mau a Mulungu amati: “Nzelu zimamanga banja la munthu, ndipo kuzindikila kumacititsa kuti lilimbe kwambili. Kudziŵa zinthu kumacititsa kuti zipinda zamkati mwa nyumba zidzaze ndi zinthu zonse zamtengo wapatali ndiponso zosangalatsa.” (Miyambo 24:3, 4) Ganizilani mmene mungagwilitsile nchito mau amenewa m’banja lanu.

21. Kodi tingalimbitse bwanji cikwati cathu pang’onopang’ono? (Onaninso bokosi lakuti “ Ndingacite Ciani Kuti Cikwati Canga Cikhale Cabwino?”)

21 Zinthu zina ‘zamtengo wapatali’ zimene zimadzaza nyumba ndi makhalidwe monga cikondi ceniceni,  kuopa Mulungu, ndi cikhulupililo colimba. (Miyambo 15:16, 17; 1 Petulo 1:7) Makhalidwe amenewa amalimbitsa cikwati. Koma kodi mwaona cimene capangitsa kuti zipinda za nyumba imene yachulidwa m’mwambi uli pamwambapa zidzaze ndi zinthu zamtengo wapatali? Cinthu cimeneco ndi “kudziŵa zinthu.” Inde, kugwilitsila nchito nzelu za m’Baibulo kungathandize anthu okwatilana kusintha maganizo ao ndi kuyamba kukondananso. (Aroma 12:2; Afilipi 1:9) Conco, nthawi zonse pamene muceza ndi mnzanu ndi kukambitsilana mfundo ina ya m’Baibulo, monga lemba la tsiku, kapena nkhani iliyonse ya mu Nsanja ya Mlonda kapena Galamukani! yokhudza cikwati, zimakhala monga kuti mukufufuza cinthu cimene cingakongoletse nyumba yanu. Pamene mugwilitsila nchito malangizo amenewo m’cikwati canu cifukwa cokonda Yehova, zili ngati mukubweletsa zokongoletsa ‘m’zipinda zamkati mwa nyumba yanu.’ Potsilizila pake, mudzayambanso kukondana monga mmene munali kucitila poyamba.

22. Kodi tidzapindula bwanji ngati ticita khama kulimbitsa cikwati cathu?

22 Mosakaikila, zingatenge nthawi yaitali ndi khama kuti mubwezeletse zokongoletsa zimenezo m’malo ake. Koma ngati muyesetsa kucita mbali yanu, mudzasangalala cifukwa comvela lamulo la m’Baibulo lakuti: “Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10; Salimo 147:11) Koposa zonse, mukamayetsetsa kulemekeza cikwati canu, mudzakhalabe m’cikondi ca Mulungu.

^ par. 6 Mfundo zimene Paulo anali kukamba pankhani ya cikwati ndi mbali ya malangizo osiyanasiyana amene iye anapeleka.—Aheberi 13:1-5.