Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 14

Chitani Zinthu Zonse Moona Mtima

Chitani Zinthu Zonse Moona Mtima

“Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”—AHEBERI 13:18.

1, 2. N’chifukwa chiyani Yehova amasangalala akamationa tikuyesetsa kukhala oona mtima? Perekani chitsanzo.

AMAYI akutuluka ndi mwana wawo m’sitolo. Mwadzidzidzi, mwanayo waima ndipo akuoneka wokhumudwa kwambiri. Iye wanyamula kachidole kamene watenga m’sitoloyo. Ayenera kuti anaiwala kubwezera pamalo pake kapena anaiwala kuwapempha mayi ake kuti am’gulire. Posowa chochita mwanayo akuyamba kulira. Mayi akewo akumuuza kuti asadandaule ndipo akubwerera ku sitoloko kuti iye akabweze kachidoleko komanso kuti akapepese. Pamene akubwerera, mayiwo akusangalala ndiponso akunyadira kwambiri. N’chifukwa chiyani mayiwo akusangalala?

2 Chinthu chimodzi chimene chimasangalatsa kwambiri makolo n’kudziwa kuti ana awo amazindikira kuti kuona mtima n’kofunika kwambiri. N’chimodzimodzinso ndi Atate wathu wakumwamba, yemwe ndi “Mulungu wachoonadi.” (Salimo 31:5) Mulungu amasangalala akamaona kuti tikukula mwauzimu ndipo tikuyesetsa kukhala oona mtima. Popeza tikufuna kumusangalatsa komanso kuchita zinthu zomwe zingachititse kuti Mulungu apitirize kutikonda, maganizo athu ndi ofanana ndi amene mtumwi Paulo anasonyeza ponena kuti: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.” (Aheberi 13:18) Tiyeni tikambirane mbali 4 zofunika kwambiri pa moyo wathu zimene nthawi zina zingativute kukhala oona mtima. Kenako tikambirana madalitso ena amene amabwera chifukwa chokhala oona mtima.

DZIFUFUZENI MOONA MTIMA

3-5. (a) Kodi Mawu a Mulungu amatichenjeza kuti kudzinamiza n’koopsa bwanji? (b) Kodi n’chiyani chingatithandize kudzifufuza moona mtima?

3 Vuto lathu lalikulu n’lakuti timalephera kudzifufuza tokha moona mtima. N’kosavuta kwambiri kwa anthu opanda ungwirofe kudzinamiza. Mwachitsanzo, Yesu anauza Akhristu a ku Laodikaya kuti ankadzinamiza poganiza kuti anali olemera pomwe anali ‘osauka, akhungu, ndi a maliseche’ mwauzimu. Zimenezitu ndi zomvetsa chisoni. (Chivumbulutso 3:17) Kudzinamiza kwawo kunangowawonjezera mavuto.

4 Mungakumbukirenso kuti wophunzira Yakobo anachenjeza kuti: “Ngati munthu akudziona ngati wopembedza, koma salamulira lilime lake, ndipo akupitiriza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.” (Yakobo 1:26) Ngati timaganiza kuti Yehova angavomereze kulambira kwathu ngakhale titamagwiritsa ntchito lilime lathu molakwika, ndiye kuti tikungodzinamiza. Kulambira kwathu kungakhale kopanda phindu. Kodi n’chiyani chingatithandize kupewa zinthu zomvetsa chisoni zimenezi?

5 M’chaputala chomwechi, Yakobo anayerekezera choonadi cha m’Mawu a Mulungu ndi galasi. Iye akutilangiza kuti tiziyang’anitsitsa m’lamulo langwiro la Mulungu ndi kusintha zimene sitikuchita bwino. (Werengani Yakobo 1:23-25.) Baibulo lingatithandize kudzifufuza moona mtima komanso kuona zinthu zimene tikufunika kusintha. (Maliro 3:40; Hagai 1:5) Komanso tingathe kupempha Yehova kuti atifufuze, atithandize kuona ndi kusintha makhalidwe oipa amene tili nawo. (Salimo 139:23, 24) Kusaona mtima ndi vuto limene silionekera mwamsanga, ndipo tiyenera kudana ndi khalidwe limeneli ngati mmene Atate wathu wakumwamba amachitira. Lemba la Miyambo 3:32 limati: “Munthu wochita zachiphamaso [kapena, wachinyengo] Yehova amanyansidwa naye, koma amakonda anthu owongoka mtima.” Yehova angatithandize kuti tiziona zinthu mmene iye amazionera komanso kuti tizidziona mmene iye amationera. Kumbukirani kuti Paulo ananena kuti: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.” Panopo sizingatheke kukhala angwiro, komabe timafunitsitsa ndipo timayesetsa kukhala oona mtima.

KHALANI OONA MTIMA M’BANJA

Kukhala wokhulupirika kumatithandiza kupewa kuchita zinthu mobisa

6. N’chifukwa chiyani anthu apabanja ayenera kukhala okhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wawo, nanga kodi angapewe mavuto otani akamachita zimenezi?

6 Mabanja achikhristu ayenera kudziwika ndi khalidwe loona mtima. Choncho, mwamuna ndi mkazi wake ayenera kulankhulana moona mtima komanso sayenera kubisirana chilichonse. Mkhristu wapabanja safunika kukhala ndi makhalidwe oipa monga kukopana ndi munthu amene si mkazi kapena mwamuna wake, kukhala ndi zibwenzi zachinsinsi pa Intaneti, kapena kuonera zinthu zolaula. Akhristu ena apabanja achita zoipa ngati zimenezi mobisira mwamuna kapena mkazi wawo. Kumeneku ndi kusakhulupirika. Onani mawu amene Mfumu Davide yokhulupirika inanena, akuti: “Sindinakhale pansi pamodzi ndi anthu achinyengo. Ndipo sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wawo.” (Salimo 26:4) Ngati ndinu wapabanja, musamachite zinthu zimene zingakupangitseni kubisa umunthu wanu kwa mwamuna kapena mkazi wanu.

7, 8. Kodi ndi zitsanzo za m’Baibulo ziti zimene zingathandize ana kudziwa kuti kukhala oona mtima n’kofunika?

7 Pophunzitsa ana awo kufunika kokhala oona mtima, makolo angachite bwino kugwiritsa ntchito zitsanzo za m’Baibulo. Pali zitsanzo za anthu amene anali osaona mtima monga Akani, amene anaba ndi kuyesa kubisa zimene anabazo; komanso Gehazi, amene ananama pofuna kupeza ndalama; ndiponso Yudasi, amene anaba ndi kunamizira kukhala mnzake wa Yesu.—Yoswa 6:17-19; 7:11-25; 2 Mafumu 5:14-16, 20-27; Mateyu 26:14, 15; Yohane 12:6.

8 Palinso zitsanzo za anthu amene anasonyeza kuona mtima monga Yakobo. Iye analimbikitsa ana ake kubweza ndalama zimene anazipeza m’matumba awo poganiza kuti ndalamazo zinaikidwamo mwangozi. Chitsanzo china ndi cha Yefita ndi mwana wake wamkazi. Mwanayu anagwirizana ndi zimene bambo ake analumbira ngakhale kuti zinali zomuvuta kwambiri. Chitsanzo chinanso ndi cha Yesu. Iye analimba mtima kudziulula ku gulu la anthu achiwawa amene anabwera kudzamugwira. Iye anachita zimenezi pofuna kukwaniritsa ulosi ndiponso kuteteza anzake. (Genesis 43:12; Oweruza 11:30-40; Yohane 18:3-11) Zitsanzo zochepa zimenezi zingathandize makolo kudziwa nkhani zofunika kwambiri za m’Mawu a Mulungu zimene zingawathandize kuphunzitsa ana awo kuti azikonda ndiponso aziona kuti kukhala oona mtima n’kofunika kwambiri.

9. Kodi makolo ayenera kupewa kuchita chiyani kuti apereke chitsanzo chabwino kwa ana awo pa nkhani ya kukhala okhulupirika, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika?

9 Makolo amakhalanso ndi udindo waukulu akamaphunzitsa ana awo kukhala oona mtima. Mtumwi Paulo anafunsa kuti: “Kodi iwe wophunzitsa enawe, sudziphunzitsa wekha? Iwe amene umalalikira kuti ‘Usabe,’ umabanso kodi?” (Aroma 2:21) Makolo ena amasokoneza ana awo powaphunzitsa kuti azikhala oona mtima pamene makolowo ali osaona mtima. Iwo angamabe zinthu zazing’ono ku ntchito n’kumati, “Mabwana athu amadziwa kuti anthu amatenga zinthu zimenezi.” Kapenanso amanena zonama n’kumanena kuti, “Sindikunama kwenikweni. Komanso imeneyi ndi nkhani yaing’ono.” Koma kunena zoona, kuba ndi kuba basi, zilibe kanthu kuti mwaba chinthu chaching’ono bwanji. Ndipo kunama ndi kunama basi, zilibe kanthu kuti nkhaniyo ndi yaing’ono bwanji. * (Werengani Luka 16:10.) Ana sachedwa kudziwa ngati munthu akuchita zinthu mwachinyengo, ndipo zimenezi zingapangitse anawo kudzakhalanso anthu osakhulupirika. (Aefeso 6:4) Komabe, ana akaphunzira kukhala okhulupirika poona zochita za makolo awo, angakule akulemekeza Yehova m’dziko la anthu achinyengoli.—Miyambo 22:6.

KHALANI OKHULUPIRIKA MUMPINGO

10. Kodi tiyenera kusamala ndi chiyani pa nkhani yolankhula zoona ndi Akhristu anzathu?

10 Kusonkhana pamodzi ndi Akhristu anzathu kumatipatsa mpata wosonyeza kukhulupirika. Monga tinaphunzirira m’mutu 12, m’pofunika kusamala ndi mmene timagwiritsira ntchito mphatso yolankhula, makamaka tikakhala ndi abale ndi alongo athu auzimu. Tikamacheza, n’zosavuta kuti tiyambe miseche, kapenanso mabodza. Tikamauza ena nkhani imene tilibe nayo umboni, ndiye kuti tikuthandiza kufalitsa bodza, choncho ndi bwino kungokhala chete. (Miyambo 10:19) Komanso ngakhale tikudziwa zoona za nkhani inayake, sindiye kuti tiziuza anthu. Mwachitsanzo, nkhaniyo ingakhale yoti siikutikhudza, kapenanso kuifalitsa kungakhale kusam’ganizira munthu amene ikum’khudzayo. (1 Atesalonika 4:11) Anthu ena amanena zochotsera anzawo ulemu n’kumati iwowo akungonena chilungamo basi. Komatu zimene timanena ziyenera kukhala zachisomo ndi zachikondi nthawi zonse.—Werengani Akolose 4:6.

11, 12. (a) Kodi anthu ena amene amachita machimo aakulu amakulitsa bwanji vuto lawo? (b) Kodi mabodza ena a Satana okhudza machimo aakulu ndi ati, nanga tingawapewe bwanji? (c) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife okhulupirika ku gulu la Yehova?

11 M’pofunika kwambiri kukhala oona mtima makamaka kwa amene amatitsogolera mumpingo. Anthu ena amene amachita machimo aakulu amakulitsa vuto lawolo pobisa machimowo ndiponso amanama akafunsidwa ndi akulu mumpingo. Anthu amenewa amayamba kukhala moyo wachiphamaso, ponamizira kutumikira Yehova uku akuchita machimo aakulu. Zimenezi zimapangitsa munthuyo kukhala wabodza. (Salimo 12:2) Anthu ena akafunsidwa ndi akulu amangoulula zochepa n’kubisa zinthu zina zofunika kwambiri. (Machitidwe 5:1-11) Kumeneku n’kusakhulupirika ndipo nthawi zambiri anthu amachita zimenezi chifukwa chokhulupirira mabodza a Satana.—Onani bokosi lakuti “ Mabodza a Satana Okhudza Machimo Aakulu.”

12 M’pofunikanso kukhala wokhulupirika ku gulu la Yehova polemba mafomu osiyanasiyana. Mwachitsanzo, tikamalemba lipoti la utumiki wakumunda, tiyenera kusamala kuti tisalembe zabodza. Komanso, polemba mafomu ofunsira utumiki winawake wapadera, sitiyenera kubisa chilichonse chokhudza thanzi lathu kapenanso chilichonse chimene chingafunike pa fomuyo.—Werengani Miyambo 6:16-19.

13. Kodi tingatani kuti tipitirize kukhala oona mtima ngati talemba kapena kulembedwa ntchito ndi Mkhristu mnzathu?

13 Tiyeneranso kukhala okhulupirika kwa Akhristu anzathu pa nkhani ya ntchito. Nthawi zina abale ndi alongo achikhristu angathe kulembana ntchito. Koma ayenera kusamala kuti asamaphatikize nkhani zantchito yawo ndi kulambira, akakhala ku Nyumba ya Ufumu kapena mu utumiki wakumunda. Tikalemba ntchito abale kapena alongo, tiyenera kuwachitira zinthu moona mtima. Mwachitsanzo, tiyenera kuwalipira malipiro amene tinapangana nawo pa nthawi yake, ndiponso tiyenera kuwachitira zonse zimene malamulo a boma amafuna. (1 Timoteyo 5:18; Yakobo 5:1-4) Komanso, ngati talembedwa ntchito ndi m’bale kapena mlongo, tizigwira ntchito mokhulupirika moganizira kuti timalandira malipiro. (2 Atesalonika 3:10) Sitiyenera kuyembekezera kuti azitichitira zinthu mokondera chifukwa cha ubale wathu wauzimu. Palibe chifukwa choyembekezera kuti azitipatsa nthawi yambiri yopuma kuposa anthu ena, kapena kutichitira zinthu zina zimene sachitira antchito ake ena.—Aefeso 6:5-8.

14. Akhristu akafuna kuchitira bizinesi limodzi, kodi ndi nzeru kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

14 Nanga bwanji ngati abale apangana zoti achitire bizinesi inayake limodzi kapena kukongozana ndalama? Baibulo lili ndi mfundo yofunika ndiponso yothandiza pa nkhani imeneyi. Mfundo yake ndi yakuti: Muzilemberana zonse zimene mwagwirizana. Mwachitsanzo, Yeremiya atagula malo, analemba zikalata ziwiri pamaso pa mboni ndipo iye anasungapo chikalata chimodzi kuti chidzakhale ngati umboni m’tsogolo. (Yeremiya 32:9-12; onaninso Genesis 23:16-20.) Mukamachita bizinesi ndi Akhristu anzanu, muzilemba zonse bwinobwino, n’kusainirana ndipo pazikhala mboni. Sikuti kuchita zimenezi n’kusakhulupirirana, koma zimathandiza kupewa kusamvetsetsana, kukhumudwitsana, ndiponso kusagwirizana kumene kumayambitsa magawano. Akhristu amene akuchitira bizinesi limodzi ayenera kudziwa kuti kukhala mogwirizana ndi mwamtendere mumpingo ndi komwe kuli kofunika kwambiri kuposa bizinesi yawoyo. *1 Akorinto 6:1-8.

KHALANI OKHULUPIRIKA POCHITA ZINTHU NDI ANTHU A M’DZIKOLI

15. Kodi Yehova amakuona bwanji kuchita chinyengo pa malonda, nanga Akhristu amatani ndi chinyengo chimene chafala pochita malonda?

15 Akhristu sayenera kukhala okhulupirika mumpingo mokha. Paulo ananena kuti: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.” (Aheberi 13:18) Mlengi wathu amafuna kuti tizikhala okhulupirika tikamachita malonda ndi anthu ena. M’buku la Miyambo lokha, muli malo angapo onena za miyezo yachinyengo. (Miyambo 11:1; 20:10, 23) Kale pochita malonda, zinali zofala kugwiritsa ntchito masikelo pofuna kuyeza zinthu zimene anthu agula ndiponso ndalama zimene ayenera kulipira. Ogulitsa achinyengo ankagwiritsa ntchito miyezo iwiri yosiyana ndiponso sikelo zachinyengo kuti azibera anthu ogula. * Yehova amanyansidwa ndi zimenezi. Kuti Mulungu apitirize kutikonda, tiyenera kupeweratu chinyengo pa malonda.

16, 17. Kodi ndi zinthu zachinyengo ziti zimene zafala m’dzikoli, ndipo kodi Akhristu oona atsimikiza mtima kuchita chiyani?

16 Sitimadabwa tikamaona kuti anthu ambiri m’dzikoli ndi achinyengo chifukwa timadziwa kuti Satana ndi amene akulamulira dzikoli. Tsiku lililonse timayesedwa kuti tichite zachinyengo. Mwachitsanzo, anthu akamalemba makalata ofunsira ntchito amakonda kulemba zabodza ndiponso amafotokoza mbiri yawo mokokomeza. Iwo amanama kuti ali ndi masatifiketi enaake ndiponso kuti agwira ntchitoyo kwa nthawi yaitali. Anthu akamalemba mafomu opempha ziphaso zolowera kapena kutuluka m’dziko, a msonkho, a inshuwalansi ndi zina zotero, amakonda kulemba zabodza pofuna kuti zimene akufunazo zitheke. Ana a sukulu ambiri amaonera mayeso, ndipo kusukuluko akapatsidwa homuweki, amakafufuza pa Intaneti n’kukopera zimene ena analemba, ndipo amanama kuti alemba okha. Ndipo nthawi zambiri anthu ena amapereka ziphuphu kwa anthu achinyengo ogwira ntchito m’boma kuti zimene akufunazo zitheke. Zimenezi si zodabwitsa chifukwa anthu ambiri m’dzikoli ndi “odzikonda, okonda ndalama, . . . [komanso] osakonda zabwino.”—2 Timoteyo 3:1-5.

17 Akhristu oona ndi otsimikiza mtima kupewa zinthu ngati zimenezi. Nthawi zina chimene chimalepheretsa anthu kukhala okhulupirika n’chakuti, anthu amene amachita zachinyengo amaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino ndipo nthawi zina amapezadi chuma chambiri. (Salimo 73:1-8) Koma Akhristu angavutike pa nkhani ya zachuma chifukwa chofuna kuchita “zinthu zonse” moona mtima. Ndiye kodi kukhala munthu wokhulupirika n’kothandizadi? Inde, n’kothandiza. Koma kodi kukhala wokhulupirika kuli ndi ubwino wotani?

UBWINO WOKHALA WOKHULUPIRIKA

18. Kodi kukhala okhulupirika n’kofunika bwanji?

18 Kukhala ndi mbiri yakuti ndife anthu okhulupirika komanso odalirika ndi kofunika kwambiri kuposa chilichonse chimene tingakhale nacho pa moyo wathu. (Onani bokosi lakuti “ Kodi Ndimachita Zinthu Zonse Moona Mtima?”) Ndipotu munthu aliyense angathe kukhala ndi mbiri imeneyi. Kuti mukhale ndi mbiri imeneyi, sizikudalira luso linalake, chuma, maonekedwe, kochokera kapena zinthu zina zapadera. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri amalephera kukhala ndi mbiri yabwino imeneyi, yomwe ili ngati chuma chamtengo wapatali. Anthu okhulupirika ndi ochepa padzikoli. (Mika 7:2) Anthu ena angakunyozeni chifukwa chakuti ndinu wokhulupirika. Komabe, anthu ena angakuyamikireni, ndipo zimenezi zingachititse kuti azikudalirani ndi kukulemekezani. Anthu ambiri a Mboni za Yehova aona kuti kukhala okhulupirika kumawathandiza pa nkhani ya zachuma. Kumawathandizanso kuti asachotsedwe ntchito kampani ikamachotsa ntchito anthu achinyengo. Amathanso kupeza ntchito mosavuta ngati pantchitopo akufuna anthu okhulupirika.

19. Kodi kukhala wokhulupirika kumakhudza bwanji chikumbumtima chathu ndiponso ubwenzi wathu ndi Yehova?

19 Kukhala okhulupirika n’kothandiza kwambiri m’njira zinanso. Kumakuthandizani kukhala ndi chikumbumtima choyera. Paulo analemba kuti: “Tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choona.” (Aheberi 13:18) Komanso, mukamachita zinthu mokhulupirika, Atate wathu wakumwamba, yemwe ndi wachikondi, amaona zimenezi ndipo amayamba kukukondani chifukwa amakonda anthu okhulupirika. (Werengani Salimo 15:1, 2; Miyambo 22:1.) Choncho, kukhala wokhulupirika kumathandiza kuti Mulungu azitikonda, ndipo palibe mphoto yoposa imeneyi. Koma kodi Yehova amaiona bwanji nkhani yokhudza kugwira ntchito? Mutu wotsatirawu ufotokoza zimenezi.

^ ndime 9 Ngati wina mu mpingo ali ndi chizolowezi chonena mabodza n’cholinga chofuna kuika ena m’mavuto, akulu angaone ngati nkhaniyo ikufunikira komiti ya chiweruzo.

^ ndime 14 Ngati mukufuna kudziwa zimene muyenera kuchita bizinesi ikapanda kuyenda bwino, onani Zakumapeto, “Kuthetsa Kusamvana pa Nkhani za Bizinezi.”

^ ndime 15 Iwo ankagwiritsa ntchito muyezo wina pogula ndiponso wina pogulitsa, n’cholinga choti apikule motchipa koma agulitse modula kwambiri. Ankagwiritsanso ntchito sikelo ya ndodo yaitali mbali imodzi kapena yolemera kwambiri mbali imodzi n’cholinga choti azibera anthu.