Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZAKUMAPETO

Mmene Tiyenera Kuchitira ndi Munthu Wochotsedwa

Mmene Tiyenera Kuchitira ndi Munthu Wochotsedwa

Zimapweteka kwambiri wachibale kapena mnzathu wapamtima akachotsedwa mumpingo chifukwa chosalapa. Mmene timachitira ndi zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi zingasonyeze ngati timakonda kwambiri Mulungu kapena ayi ndiponso ngati timatsatira malamulo ake mokhulupirika. * Taganizirani ena mwa mafunso amene amakhalapo pa nkhani imeneyi.

Kodi tiyenera kuchita bwanji zinthu ndi munthu wochotsedwa? Baibulo limati: “Muleke kuyanjana ndi aliyense wotchedwa m’bale, amene ndi wadama, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, wolalata, chidakwa, kapena wolanda, ngakhale kudya naye munthu wotereyu ayi.” (1 Akorinto 5:11) Ponena za munthu aliyense amene “amachita zosemphana ndi zimene Khristu amaphunzitsa,” timawerenga kuti: “Musamulandire m’nyumba zanu kapena kumupatsa moni. Aliyense amene wamupatsa moni akugawana naye ntchito zake zoipazo.” (2 Yohane 9-11) Sitiyenera kucheza ndi anthu ochotsedwa kapena kukambirana nawo nkhani zokhudza kulambira. Nsanja ya Olonda ya March 15, 1982, patsamba 24, inanena kuti: ‘Kungomupatsa munthu moni, pangakhale poyambira kucheza naye ngakhalenso kukhala naye pa ubwenzi. Kodi tingafune kuchita zimenezi ndi munthu wochotsedwa?’

Kodi m’pofunika kupeweratu kuchita naye chilichonse? Inde, ndipo pali zifukwa zingapo zochitira zimenezi. Choyamba, kuchita zimenezi kumasonyeza kuti ndife okhulupirika kwa Mulungu ndi Mawu ake. Timamvera Yehova, osati pa nthawi yokha imene taona kuti n’zosavuta kuchita zimenezo, koma ngakhalenso pamene n’zovuta kwambiri. Kukonda Mulungu kumatipangitsa kuti tizimvera malamulo ake onse, podziwa kuti iye ndi wachilungamo ndi wachikondi ndiponso kuti malamulo ake ndi opindulitsa kwambiri. (Yesaya 48:17; 1 Yohane 5:3) Chachiwiri, kusiya kucheza ndi munthu wosalapa kumateteza ifeyo, ndi mpingo wonse, kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu komanso makhalidwe athu zisawonongeke. Kumathandizanso kuti mbiri ya mpingo isaipe. (1 Akorinto 5:​6, 7) Chachitatu, kutsatira mfundo za m’Baibulo pa nkhani ya munthu wochotsedwa kungathandize munthuyo. Tikamagwirizana ndi zimene komiti ya chiweruzo yagamula, zingam’khudze munthu wolakwayo amene walephera kulandira thandizo la akulu mumpingo. Poona kuti wasiya kugwirizana ndi anthu amene amamukonda, zingamuthandize kuti ‘nzeru zim’bwerere,’ aone kukula kwa tchimo lakelo ndi kuchita zotheka kuti abwerere kwa Yehova.​—Luka 15:17.

Kodi tingatani ngati amene wachotsedwayo ndi wachibale? Wachibale wathu amene timamukonda akachotsedwa, zimakhala zovuta kwambiri kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Kodi m’bale wathu akachotsedwa tizichita naye bwanji zinthu? Sitingafotokoze zonse zimene muyenera kuchita ndi munthu ameneyu, koma tiyeni tikambirane mfundo ziwiri zofunika kwambiri.

Nthawi zina zingatheke kuti munthu wochotsedwayo mukukhala naye limodzi. Popeza kuchotsedwa sikuthetsa chibale, mungapitirize kumachita naye zinthu za masiku onse za pabanjapo. Komabe, chifukwa cha zimene wachita, munthuyo amakhala kuti wathetsa ubale wauzimu umene anali nawo ndi achibale ake okhulupirira. Choncho, achibale ake okhulupirirawo sangapitirize kuchitira naye limodzi zinthu zauzimu. Mwachitsanzo, wochotsedwayo sayenera kuyankhapo pamene banjalo likuchita Kulambira kwa Pabanja. Komabe, ngati wochotsedwayo ndi mwana wamng’ono, makolo amakhalabe ndi udindo womuphunzitsa ndi kumulangiza. Choncho, makolo achikondi angakonze zoti aziphunzira naye Baibulo. *​—Miyambo 6:​20-22; 29:17.

Nthawi zina zingatheke kuti wachibale wanu wochotsedwa simukukhala naye nyumba imodzi. N’zoona kuti nthawi zina pangafunikire kuti mukumane naye ndi kuchitira limodzi zinthu zina zapachibale. Komabe, simuyenera kuchita zimenezi kawirikawiri. Achibale okhulupirika a munthuyu, sayenera kupereka zifukwa pofuna kusonyeza kuti sikulakwa kuchita zinthu ndi munthu wochotsedwa amene sakhala naye nyumba imodzi. Koma chifukwa chokhala okhulupirika kwa Yehova ndi gulu lake, iwo amatsatira malangizo a m’Malemba pa nkhani ya anthu amene achotsedwa mumpingo. Kukhulupirika kwawo pa nkhani imeneyi kungasonyeze kuti amamufunira zabwino wochotsedwayo ndipo zingamuthandize kuti aone ubwino wa chilango chimene walandira. *​—Aheberi 12:11.

^ ndime 1 Mfundo za m’Baibulo zimene tiyenera kutsatira munthu akachotsedwa, n’zimenenso tiyenera kutsatira munthu akadzilekanitsa ndi mpingo.

^ ndime 2 Kuti mudziwe zambiri za mmene mungachitire ndi mwana wamng’ono amene wachotsedwa ndipo akukhalabe pakhomo pomwepo, onani Nsanja ya Olonda ya October 1, 2001, patsamba 16 ndi 17, komanso ya November 15, 1988, tsamba 20, ndiponso Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2002, patsamba 3 ndi 4.

^ ndime 3 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya mmene muyenera kuchitira ndi achibale amene achotsedwa, onani malangizo a m’Malemba mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1988, patsamba 26 mpaka 31, ndi ya March 15, 1982, patsamba 26 mpaka 31.