Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

ZAKUMAPETO

Kodi Tiyenela Kucita Bwanji ndi Munthu Wocotsedwa?

Kodi Tiyenela Kucita Bwanji ndi Munthu Wocotsedwa?

Wacibale kapena mnzathu wapamtima akacotsedwa mumpingo cifukwa cocita macimo mosalapa, zimatipweteka mtima kwambili. Mmene timacitila ndi malangizo a m’Baibulo pa nkhani imeneyi, zingaonetse kuti timakondadi Mulungu ndi kulemekeza makonzedwe ake kapena iyai. * Tiyeni tikambilane mafunso ena amene tingakhale nao pa nkhani imeneyi.

Kodi tiyenela kucita bwanji ndi munthu wocotsedwa? Baibulo limati: “Muleke kuyanjana ndi aliyense wochedwa m’bale, amene ndi wadama, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, wolalata, cidakwa, kapena wolanda, ngakhale kudya naye munthu woteleyu ayi.” (1 Akorinto 5:11) Ponena za munthu amene “amacita zosemphana ndi zimene Kristu amaphunzitsa,” timaŵelenga kuti: “Musamulandile m’nyumba zanu kapena kumupatsa moni. Aliyense amene wamupatsa moni akugaŵana naye nchito zake zoipazo.” (2 Yohane 9-11) Sitiyenela kukambilana zinthu za kuuzimu kapena kuceza ndi anthu ocotsedwa. Nsanja ya Olonda ya March 15, 1982, patsamba 24, inanena kuti: ‘Kungopatsa moni munthu ndiye poyambila kuceza naye kapenanso kukhala naye pa ubwenzi. Kodi tingafune kuyamba kucita zimenezi ndi munthu wocotsedwa?’

Kodi tiyenela kum’pewelatu munthu wocotsedwa? Inde, ndipo pali zifukwa. Coyamba, ngati tipewa wocotsedwayo, timaonetsa kuti ndife okhulupilika kwa Mulungu ndi kuti timakhulupilila Mau ake. Timamvela Yehova osati cabe pamene zinthu zili zofewa, koma ngakhale pamene zinthu zili zovuta. Cikondi cathu pa Mulungu cimatilimbikitsa kumvela malamulo ake onse, podziŵa kuti iye ndi wacilungamo, wacikondi, ndi kuti malamulo ake amatipindulitsa kwambili. (Yesaya 48:17; 1 Yohane 5:3) Caciŵili, kuleka kuyanjana ndi munthu wosalapa kumateteza ifeyo ndi mpingo wonse mwakuuzimu. Kumathandizanso kuti makhalidwe athu ndi a Akristu ena onse mumpingo asaipe ndiponso kumateteza mbili ya mpingo. (1 Akorinto 5:6, 7) Cacitatu, ngati titsatila mfundo za m’Baibulo molimba mtima tingathandizenso munthu wocotsedwayo. Mwa kugwilizana ndi cigamulo ca komiti yaciweluzo, tingathandize wocimwayo kuona kuipa kwa zimene anacita ponyalanyaza uphungu umene akulu anali kum’patsa. Kupewa kuceza ndi munthu wocotsedwa kungamuthandize kuti ‘nzelu zibwelemo’ ndi kuona kuipa kwa chimo limene anacita, ndipo kungam’pangitse kuyamba kukonzanso ubwenzi wake ndi Yehova.—Luka 15:17.

Kodi tingacite ciani ngati tili ndi wacibale wocotsedwa? Wacibale wathu akacotsedwa, zingakhale zovuta kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova. Kodi tiyenela kucita motani ndi wacibale wocotsedwa? Sitingakwanitse kunena zonse zimene tingacite. Koma tiyeni tikambilane zinthu ziŵili zofunika kwambili zimene tingacite.

Mwina munthu wocotsedwayo angakhale kuti amakhala nyumba imodzi ndi acibale ake. Popeza kucotsedwa kwake mumpingo sikuthetsa cibale, io angapitilize kucitila limodzi zinthu zimene amacita monga banja masiku onse. Koma cifukwa ca khalidwe lake, wocotsedwayo wasankha kuthetsa ubale wake wakuuzimu ndi acibale ake amene ndi Mboni za Yehova. Motelo, acibale ake okhulupilika kwa Yehova, sayenela kucita naye zinthu zokhudza kulambila. Mwacitsanzo, ngati banja likumana kuti liphunzile Baibulo, wocotsedwayo sayenela kuyankhapo. Komabe, ngati wocotsedwayo ndi mwana wamng’ono, makolo ali ndi udindo wopitiliza kumuphunzitsa ndi kumulanga. Conco, makolo acikondi angakonze zakuti aziphunzila Baibulo ndi mwanayo. *Miyambo 6:20-22; 29:17.

Nthawi zina, munthu wocotsedwayo angakhale kuti amakhala kutali ndi acibale ake. Ngakhale kuti nthawi zina mungafunikile kukamba naye zinthu zina zokhudza banja lanu, simuyenela kucita zimenezo kaŵilikaŵili. Akristu okhulupilika sayenela kupeza zifukwa zosayenela zolankhulila ndi wacibale wocotsedwa amene amakhala kutali. Koma kukhulupilika kwao kwa Yehova ndi ku gulu lake, kuyenela kuwalimbikitsa kulemekeza malangizo a m’Malemba okhudza munthu wocotsedwa. Kukhulupilika kwao kwa Yehova pa nkhani imeneyi, kumaonetsa kuti amafunila zabwino munthu wolakwayo, ndipo kungamuthandize kupindula ndi cilango cimene anapatsidwa. *Aheberi 12:11.

^ par. 3 Mfundo za m’Baibulo pa nkhani imeneyi zimagwilanso nchito kwa anthu amene adzilekanitsa okha ndi mpingo.

^ par. 2 Kuti mudziŵe zambili pa nkhani yokhudza ana aang’ono ocotsedwa amene akali kukhala panyumba, onani Nsanja ya Olonda ya October 1, 2001, patsamba 16 mpaka 17, ndi ya November 15, 1988, tsamba 20.

^ par. 3 Kuti mudziŵe zambili zokhudza mmene tingacitile ndi acibale ocotsedwa, onani malangizo a m’Malemba amene ali mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1988, patsamba 26 mpaka 31, ndi ya March 15, 1982, patsamba 26 mpaka 31.