Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

ZAKUMAPETO

Kugonjetsa Cizoloŵezi Coseŵeletsa Malisece

Kugonjetsa Cizoloŵezi Coseŵeletsa Malisece

Kuseŵeletsa malisece ndi cizoloŵezi coipa cimene Mulungu amadana naco. Cizolowezici cimasonkhezela munthu kufuna kudzisangalatsa yekha, ndipo cimam’pangitsa kuganiza zinthu zoipa. Munthu amene amaseŵeletsa malisece amayamba kuona ena monga kothetsela cabe cilakolako cake ca kugonana. Iye saona kugonana kukhala njila yoonetselana cikondi kwa anthu okwatilana, koma monga njila yothetsela cabe cilakolako cake ca kugonana ndi yopezela cisangalalo ca kanthawi. Koma cisangalalo cimene amapeza sicikhalitsa. M’malo mwa kucititsa ziwalo za thupi kuti zikhale zakufa “ku dama, zinthu zodetsa, cilakolako [coipa] ca kugonana,” kuseŵeletsa malisece kumadzutsa ziwalo zimenezo.—Akolose 3:5.

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Okondedwanu, . . . tiyeni tidziyeletse ndipo ticotse cinthu ciliconse coipitsa thupi kapena mzimu, kwinaku tikukwanilitsa kukhala oyela poopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Ngati mumavutika kutsatila malangizo amenewa, musataye mtima. Yehova nthawi zonse ndi “wokonzeka kukhululuka” ndi kukuthandizani. (Salimo 86:5; Luka 11:9-13) Ndithudi, ngati mumavutika mumtima koma mumacita khama kuti muleke cizoloŵezi cimeneci ngakhale kuti nthawi zina mungalephele, mumaonetsa kuti muli ndi maganizo abwino. Ndiponso kumbukilani kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziŵa zonse.” (1 Yohane 3:20) Mulungu saona macimo athu cabe, koma amaona munthu yense wathunthu. Popeza kuti amatidziŵa bwino kwambili, iye mwacifundo amamva mapemphelo athu ocokela pansi pa mtima opempha cikhululukilo. Conco, musaleme kupempha Mulungu modzicepetsa ndi mocokela pansi pa mtima monga mmene mwana amacitila kwa atate ake akakumana ndi vuto. Yehova adzakupatsani cikumbumtima coyela. (Salimo 51:1-12, 17; Yesaya 1:18) Komabe, muyenela kucita zinthu mogwilizana ndi mapemphelo anu. Mwacitsanzo, muyenela kuyesetsa kupewa kupenyelela zinthu zamalisece za mtundu uliwonse ndikuceza ndi anthu akhalidwe loipa. *

Ngati vuto lanu loseŵeletsa malisece lipitilizabe, muyenela kuuza kholo lanu lacikristu kapena Mkristu aliyense wokhwima kuuzimu amene ndi mnzanu wodalilika. *Miyambo 1:8, 9; 1 Atesalonika 5:14; Tito 2:3-5.

^ par. 2 Pofuna kupewa kugwilitsila nchito kompyuta mosayenelela, mabanja ambili amaika kompyuta yao pa malo oonekela kwa onse m’nyumba. Ndiponso, mabanja ena amagula mapulogalamu a pakompyuta amene amapangitsa kuti zinthu zoipa zisaloŵe mu kompyuta yao. Komabe, mapulogalamu a pakompyuta ndi osadalilika kwenikweni.

^ par. 1 Kuti mudziŵe njila zina zothandiza za mmene mungathetsele vuto loseŵeletsa malisece, onani nkhani yakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa  . . . Kodi Ndingathetse Bwanji Cizolowezi Cimeneci?” mu Galamukani! ya November 2006 ndi buku la Cingelezi lakuti Young People Ask—Answers That Work, Volume 1 patsamba 178 mpaka 182.