Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Sindiyenera Kugonana ndi Aliyense Mpaka N’talowa M’banja?

N’chifukwa Chiyani Sindiyenera Kugonana ndi Aliyense Mpaka N’talowa M’banja?

Mutu 5

N’chifukwa Chiyani Sindiyenera Kugonana ndi Aliyense Mpaka N’talowa M’banja?

“Ndimafuna n’tagonana ndi mwamuna kuti ndidziwe mmene zimakhalira.”—Anatero Kelly.

“Ndimadzikayikira chifukwa sindinagonanepo ndi mtsikana mpaka pano.”—Anatero Jordon.

“KODI sunagonepo ndi aliyense mpaka pano?” Funso limeneli lingakuchititseni mantha. M’madera ambiri wachinyamata amene sanagonanepo ndi aliyense amaonedwa ngati wotsalira ndiponso wopepera. N’chifukwa chake achinyamata ambiri amakhala atagonapo ndi munthu wina asanafike zaka 20.

Kukopeka ndi Chilakolako Chawo Komanso Kulimbikitsidwa ndi Anzawo

Ngati ndinu Mkhristu, mukudziwa kuti Baibulo limakuuzani kuti ‘mupewe dama.’ (1 Atesalonika 4:3) Komabe, mungaone kuti kudziletsa n’kovuta. Mnyamata wina dzina lake Paul, anati: “Nthawi zina ndimangoyamba kuganiza za kugonana popanda chifukwa chenicheni.” Koma dziwani kuti n’kwachibadwa kumva choncho nthawi zambiri.

Komabe, zimachititsa manyazi kwambiri kuti anthu azikuseka nthawi zonse kuti sunagonanepo ndi munthu. Mwachitsanzo, kodi mungamve bwanji anzanu atakuuzani kuti sindinu mwamuna kapena mkazi weniweni chifukwa simunagonanepo ndi munthu? Ellen anati: “Anzako amakuchititsa kuganiza kuti kugonana n’kosangalatsa ndiponso koyenera.” Iye anapitiriza kuti: “Anthu amakukayikira ngati sunagonanepo ndi aliyense.”

Koma pankhani yokhudza kugonana musanalowe m’banja, pali mfundo inayake imene anzanuwo sanganene. Mwachitsanzo, Maria, amene anagonapo ndi chibwenzi chake, anati: “Pambuyo pogonana naye, ndinachita manyazi kwambiri. Ndinakhumudwa kwambiri ndi zomwe tinachitazo.” Zinthu zoterezi zimachitika kawirikawiri ngakhale kuti achinyamata ambiri sazindikira zimenezi. Kunena zoona, kugonana musanalowe m’banja kumasokoneza maganizo kwambiri ndipo zotsatira zake n’zoopsa.

Komabe, mtsikana wina dzina lake Shanda anafunsa kuti, “N’chifukwa chiyani Mulungu amapatsa achinyamata chilakolako chogonana, koma akudziwiratu kuti safunika kugonana mpaka atalowa m’banja?” Limeneli ndi funso labwino kwambiri. Koma taganizirani izi:

Kodi chilakolako champhamvu chomwe inuyo mumakhala nacho ndi chogonana basi? Ayi. Yehova Mulungu anakulengani m’njira yoti muzitha kulakalaka ndi kuganizira zinthu zosiyanasiyana.

Kodi mumachita panthawi yomweyo chinthu chilichonse chimene thupi lanu lafuna? Ayi, chifukwa chakuti Mulungu anakulengani m’njira yoti muzitha kudziletsa.

Motero, kodi tikuphunzirapo chiyani? Mwina simungathe kuletsa thupi lanu kulakalaka zinthu zina, koma mungathe kudziletsa kuti musachite zinthu zomwe mukulakalakazo. Choncho, kugonana ndi munthu mukangokhala ndi chilakolako chogonana n’kulakwa ndiponso n’kupanda nzeru chifukwa zili ngati kumenya munthu nthawi iliyonse pamene mwakwiya.

Mfundo ndi yakuti, Mulungu safuna kuti tizigwiritsa ntchito molakwika chilakolako chogonana. Baibulo limati: “Aliyense wa inu akhale woyera mwa kudziwa kusunga thupi lake m’chiyero ndi ulemu.” (1 Atesalonika 4:4) Monga mmene palili “mphindi yakukonda ndi mphindi yakudana,” palinso nthawi yomvera chilakolako chanu cha kugonana ndiponso nthawi yodziletsa. (Mlaliki 3:1-8) Kwenikweni, inuyo muli ndi udindo wonse pa zilakolako za thupi lanu.

Koma kodi mungatani munthu wina atakusekani, n’kukufunsani modabwa kuti, “Kutereku sunagonepo ndi aliyense mpaka pano?” Zikatero musachite mantha. Munthu amene akungofuna kukunyozani mungamuuze kuti: “Inde, ndipo ndimasangalala kwambiri kuti sindinagonepo ndi munthu aliyense.” Kapena mungamuuze kuti, “Zimenezo sizikukukhudza ndipo sindikambirana ndi aliyense nkhani imeneyi.” * (Miyambo 26:4; Akolose 4:6) Komabe, mwina mungaone kuti m’pofunika kumuuza zambiri munthu amene akukufunsaniyo. Ngati ndi choncho, mungathe kum’fotokozera mfundo za m’Baibulo zimene mumatsatira pankhaniyi.

Kodi mukuganizira njira zinanso zimene mungayankhire munthu amene wakufunsani monyoza kuti, “Kutereku sunagonepo ndi aliyense mpaka pano?” Ngati ndi choncho, lembani njira zimenezo m’munsimu.

․․․․․

Mphatso Yamtengo Wapatali

Kodi Mulungu amamva bwanji anthu akagonana asanalowe m’banja? Tayerekezerani kuti mwagula mphatso yoti mupatse mnzanu. Koma musanam’patse mphatsoyo, mnzanuyo akuitsegula, n’cholinga chongofuna kuona kuti ndi yotani. Kodi mungasangalale nazo? Ndiyeno taganizirani mmene Mulungu angamvere ngati mutagonana ndi munthu musanalowe m’banja? Iye amafuna kuti mudikire mpaka mudzalowe m’banja kuti mudzasangalale ndi mphatso ya kugonana.—Genesis 1:28.

Kodi muyenera kutani mukakhala ndi chilakolako chogonana? Mwachidule, tinganene kuti muyenera kudziletsa ndipo mukhoza kuchitadi zimenezi. Pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni. Iye angakupatseni mzimu wake kuti ukuthandizeni kudziletsa. (Agalatiya 5:22, 23) Musaiwale kuti Yehova “sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.” (Salmo 84:11) Wachinyamata wina dzina lake Gordon anati: “Ndikayamba kuganiza kuti palibe cholakwika kugonana ndisanalowe m’banja ndimaganizira kaye mavuto amene angabwere pamoyo wanga wauzimu. Ndiyeno ndimaona kuti ngakhale tchimo litakhala losangalatsa chotani siliyenera kusokoneza ubwenzi wanga ndi Yehova.”

Mfundo ndi yakuti palibe chodabwitsa kukhala wosagonana ndi munthu mpaka mutalowa m’banja. Kuchita zachiwerewere n’koopsa ndiponso kumamuchotsera munthu ulemu. Choncho, musalole kuti maganizo a dzikoli akuchititseni kuganiza kuti inuyo muli ndi vuto chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Mukapewa kugonana ndi munthu mpaka mutalowa m’banja, mudzakhala ndi thanzi labwino, simudzavutika ndi maganizo, ndipo koposa zonse, mudzakhala ndi ubwenzi wabwino ndi Mulungu.

WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 24

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 N’zochititsa chidwi kuti Yesu sanayankhe chilichonse Herode atam’funsa funso. (Luka 23:8, 9) Nthawi zambiri ndi bwino kusayankha mafunso opanda pake.

LEMBA LOFUNIKA

Ngati wina . . . wasankha mu mtima mwake kukhalabe [wosagonana ndi munthu], achita bwino.1 Akorinto 7:37.

MFUNDO YOTHANDIZA

Pewani kucheza ndi anthu amakhalidwe oipa ngakhale atamanena kuti muli nawo chipembedzo chimodzi.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Kawirikawiri anthu achiwerewere sasintha khalidwe lawo ngakhale atalowa m’banja. Koma anthu amene amatsatira mfundo za Mulungu zamakhalidwe abwino asanalowe m’banja, amakhalanso okhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wawo.

ZOTI NDICHITE

Kuti ndisagone ndi munthu aliyense mpaka nditalowa m’banja, ndiyenera kuchita izi: ․․․․․

Anzanga akamandivutitsa kuti ndigonane ndi munthu, ndizichita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

N’chifukwa chiyani ena amaseka anthu amene sanagonanepo ndi munthu aliyense?

N’chifukwa chiyani kukhalabe osagonana ndi munthu n’kovuta?

Kodi ubwino wosagonana ndi munthu aliyense mpaka mutalowa m’banja ndi wotani?

Kodi mng’ono wanu mungamufotokozere motani ubwino wosagonana ndi munthu mpaka atalowa m’banja?

[Mawu Otsindika patsamba 51]

“Kukumbukira nthawi zonse kuti ‘wadama kapena wopanda chiyero sadzalowa konse mu ufumu wa Mulungu,’ kumandilimbikitsa kupewa chiwerewere.”(Aefeso 5:5)—Anatero Lydia

[Chithunzi patsamba 49]

Zimene Munalemba

Kodi Zotsatirapo Zake Zimakhala Zotani Kwenikweni?

Anzanu komanso zosangalatsa zotchuka sizitchula mavuto amene angabwere chifukwa cha kugonana musanalowe m’banja. Taonani zochitika zitatu zotsatirazi. Kodi mukuganiza kuti achinyamatawa chingawachitikire n’chiyani kwenikweni?

● Mnyamata wina kusukulu akudzitama kuti wagonapo ndi atsikana ambirimbiri. Iye akuti n’zosangalatsa ndipo palibe vuto lililonse. Koma kodi n’chiyani kwenikweni chingachitikire mnyamatayu ndiponso atsikanawo? ․․․․․

● Filimu ina ikutha ndi achinyamata awiri osakwatirana akugonana ngati njira yosonyezerana chikondi. Ngati anthu atachitadi zimenezi, kodi zotsatirapo zake zingakhale zotani? ․․․․․

● Mwakumana ndi mnyamata winawake wokongola kwambiri ndipo akukupemphani kuti mugone naye. Iye akuti palibe aliyense amene angadziwe zimenezi. Ngati mutalola kugona naye n’kubisa zomwe mwachitazo, kodi zotsatirapo zake zingakhale zotani kwenikweni? ․․․․․

[Chithunzi patsamba 54]

Kugonana ndi munthu musanalowe m’banja, kuli ngati kutsegula mphatso musanapatsidwe