Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndinalakwa Chiyani Kuti Ndidwale Chonchi?

Kodi Ndinalakwa Chiyani Kuti Ndidwale Chonchi?

Mutu 8

Kodi Ndinalakwa Chiyani Kuti Ndidwale Chonchi?

“Ukakhala mwana umaganiza kuti palibe choipa chilichonse chimene chingakuchitikire. Koma kenako ukadwala matenda aakulu, m’pamene umadziwa kuti zoterezi zingathe kuchitikira wina aliyense. Ndipo zikatero umangoona ngati ndiwe kankhalamba kodwaladwala.”—Anatero Jason.

ALI ndi zaka 18, Jason anam’peza ndi matenda amene amatupitsa matumbo ndipo amachititsa kuti m’mimba muzipweteka kwambiri. Mwina inunso mukudwala matenda enaake aakulu kapena ndinu wolumala. N’kutheka kuti zimenezi zimachititsa kuti muzilephera kuvala, kudya, kapena kupita ku sukulu.

Ngati mukudwala matenda aakulu mungamve ngati muli nokhanokha m’ndende. Mungayambe kuganiza kuti mwachimwira Mulungu kapena kuti Mulungu akukuyesani. Komabe, Baibulo limati: “Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yakobe 1:13) Tonsefe timadwala ndipo timakumana ndi ‘zotigwera m’nthawi mwake.’—Mlaliki 9:11.

N’zosangalatsa kudziwa kuti Yehova Mulungu walonjeza dziko latsopano mmene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Ngakhale anthu amene anamwalira, adzaukitsidwa n’kudzakhala ndi moyo m’dziko latsopano. (Yohane 5:28, 29) Koma kodi panopa mungatani kuti musamadandaule ngakhale mukudwala?

Musamadandaule. Baibulo limati: “Mtima wosekerera uchiritsa bwino.” (Miyambo 17:22) Ena amaganiza kuti akamadwala kwambiri sayenera kuseka kapena kusangalala. Koma moyo mungaumvebe kukoma mukamakonda kuseka ndiponso mukamacheza ndi anthu akhalidwe labwino. Pezaninso zinthu zina zimene zingakuthandizeni kukhala ndi moyo wosangalala. Kumbukirani kuti chimwemwe ndi mbali ya chipatso cha mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22) Mukamachita zimenezi mudzakhala wosangalala ngakhale mukudwala.—Salmo 41:3.

Chitani zimene mungathe. Baibulo limati: “Kulolera kwanu kudziwike kwa anthu onse.” (Afilipi 4:5) Mtima wololera ungakuthandizeni kuti musamadandaule kwambiri komanso kuti musamadzitayirire. Ngati mungathe, muzichita masewera olimbitsa thupi kuti muzimvako bwino. N’chifukwa chake m’zipatala zina amalimbikitsa achinyamata amene akudwala kuti azichita masewera olimbitsa thupi. Nthawi zambiri masewera abwino olimbitsa thupi amathandiza kuti muyambe kupezako bwino mwamsanga komanso kuti musamadandaule kwambiri. Apa mfundo ndi yakuti, m’pofunika kuona mmene zinthu zilili pamoyo wanu ndi kuchita zimene mungakwanitse.

Musadandaule ndi mmene ena amakuonerani. Kodi mungatani ngati ena akukunenani chifukwa cha mmene mulili? Baibulo limati: “Mawu onsetu onenedwa usawalabadire.” (Mlaliki 7:21) Nthawi zina mumangofunika kunyalanyaza zimene anthu ena akunenazo. Pali zinthu zinanso zimene mungachite kuti ena asamakuneneni. Mwachitsanzo, ngati anthu ena akuoneka kuti akumangika kukhala pafupi ndi inu chifukwa chakuti mukuyendera njinga ya anthu olumala, mungawathandize kuti akhale omasuka. Mwina mungayambitse nkhani inayake pofuna kuwafotokozera zimene zinakuchitikirani kuti muziyenda panjinga ya anthu olumala.

Musataye mtima. Yesu atakumana ndi mavuto, anapemphera kwa Mulungu, mwachikhulupiriro, ndipo ankaganiza kwambiri zabwino zimene zinali m’tsogolo mwake, osati za mavuto amene anali kukumana nawo. (Aheberi 12:2) Mavuto amene anakumana nawo anam’phunzitsa zambiri. (Aheberi 4:15, 16; 5:7-9) Komanso sankakana ena akafuna kumuthandiza ndi kumulimbikitsa. (Luka 22:43) Iye ankaganizira za mmene angathandizire anthu ena m’malo mongoganiza za mavuto ake.—Luka 23:39-43; Yohane 19:26, 27.

Yehova “Amasamala za Inu”

Kaya mukudwala matenda otani, musaganize kuti Mulungu amakuonani ngati munthu wopanda ntchito. Yehova amaona kuti anthu amene amayesetsa kumusangalatsa ndi ofunika kwambiri. (Luka 12:7) Iye “amasamala za inu” panokha ndipo amasangalala mukamamutumikira ngakhale mukudwala kapena ndinu wolumala.—1 Petulo 5:7.

Choncho musalephere kuchita zinthu zofunika chifukwa cha mantha kapena kukayikakayika. Muzidalira Yehova Mulungu nthawi zonse. Iye amadziwa mavuto anu ndiponso mmene mukumvera. Komanso angakupatseni “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti ikuthandizeni kupirira. (2 Akorinto 4:7) Idzafika nthawi imene simudzadandaula kwambiri ndi matenda anu. Izi n’zimene zinam’chitikira Timothy, mnyamata wina amene anam’peza ndi matenda enaake amene amachititsa kuti munthu azimva kutopa nthawi zonse. Panthawiyi n’kuti ali ndi zaka 17. Iye anati: “Lemba la 1 Akorinto 10:13 limafotokoza kuti Yehova sangalole kuti tikumane ndi mavuto amene sitingathe kuwapirira. Ndimaona kuti, ngati Mlengi anachita kunena kuti angandithandize kupirira, ineyo ndi ndani kuti nditsutsane naye?”

Kodi Mungathandize Bwanji Munthu Amene Akudwala?

Koma mungamuthandize bwanji munthu amene akudwala kapena wolumala? Njira yabwino kwambiri ndiyo ‘kukhala achifundo.’ (1 Petulo 3:8) Yesetsani kumvetsa mmene munthuyo akumvera. Onani vuto lakelo monga mmene iyeyo akulionera osati monga mmene inuyo mukulionera. Mtsikana wina dzina lake Nina, yemwe anabadwa ali wolumala msana, anati: “Popeza ndimaoneka wamng’ono, ndipo ndimayendera njinga ya anthu olumala, anthu ena amayankhula nane ngati akulankhula ndi kamwana ndipo zimenezi zimandiwawa kwambiri. Koma ndimasangalala ndi zimene ena amachita, amakhala pansi akamalankhula nane n’cholinga choti tizilankhulana bwinobwino.”

Popanda kuganizira za kudwala kapena kulumala kwawo mungathe kuona kuti anthuwa simukusiyana nawo kwenikweni. Ndipo ‘mungawagawire mphatso yauzimu’ polankhula nawo bwino. Zimenezi zingakuthandizeninso inuyo chifukwa ‘mudzalimbikitsana.’—Aroma 1:11, 12.

WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI, M’BUKU LOYAMBA, MUTU 13

LEMBA LOFUNIKA

“Pamenepo . . . wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:23, 24.

MFUNDO YOTHANDIZA

Kudziwa bwino matenda anu kungakuthandizeni kuti musamachite mantha. Choncho, fufuzani zambiri zokhudza matendawo. Funsani adokotala kuti akuthandizeni kumvetsa zinthu zimene simukuzimvetsa.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Ngati mukudwala kapena ndinu wolumala, sindiye kuti Mulungu akukulangani. Zimenezi zimachitika chifukwa cha kupanda ungwiro kumene tonsefe tinatengera kwa Adamu.—Aroma 5:12.

ZOTI NDICHITE

Kuti ndisamadandaule ndi kulumala kapena matenda anga ndiyenera kuchita izi: ․․․․․

Chinthu chimodzi chimene ndingakwanitse kuchita ndi ichi: ․․․․․

Munthu wina akandinyoza chifukwa cha mmene ndilili, ndingasonyeze kuti sindikudandaula mwa kuchita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

Kodi mungagwiritse ntchito bwanji mfundo zimene zili m’nkhani ino kuthandiza munthu wolumala kapena amene ali ndi matenda aakulu?

Ngati mukudwala matenda aakulu, kodi mungaganizire zinthu zabwino ziti kuti mukhalebe wosangalala?

Kodi mukudziwa bwanji kuti kudwala kapena kulumala si chizindikiro chakuti Mulungu akukulangani?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 75]

DUSTIN, wazaka 22, anati:

“Atandiuza kuti ndiyamba kuyenda panjinga ya anthu olumala, ndinalira kwambiri kwinaku mayi anga atandikumbatira. Nthawi imeneyi ndinali ndi zaka 8 zokha basi.

Ndili ndi matenda ofooketsa thupi moti manja anga anafa. Chifukwa cha matendawa, amachita kundiveka, kundisambitsa ndi kundidyetsa. Ndipo zimandivuta ngakhale kunyamula manja anga. Komabe, pali zambiri zimene ndimatha kuchita. Ndimalalikira nthawi zonse ndipo ndine mtumiki wothandiza mumpingo mwathu. Sindiganizira kwambiri za vuto langali chifukwa munthu ukamatumikira Yehova umakhala ndi zambiri zochita ndiponso umakhala ndi chiyembekezo. Ineyo ndikuyembekezera kuti m’dziko latsopano la Mulungu, ‘ndidzadumpha ngati nswala.’”—Yesaya 35:6.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 75]

TOMOKO, wazaka 21, anati:

“Ndinali ndi zaka zinayi zokha pamene dokotala anandiuza kuti tsiku lililonse ndizibayidwa jakisoni wa matenda a shuga kwa moyo wanga wonse.’

N’zovuta kwa munthu wodwala matenda a shuga kuti azikhala ndi shuga wokwanira m’thupi mwake. Nthawi zambiri ndimafunikira kudya ngakhale kuti ndilibe njala, ndipo nthawi zinanso amandiuza kuti ndisadye ngakhale kuti ndili ndi njala. Moti panopo, ndabayidwa majakisoni okwanira 25,000 ndipo m’manja ndi m’ntchafu mwanga muli zipsera zokhazokha. Koma makolo anga andithandiza kwambiri. Sadandaula chilichonse ndipo anandiphunzitsa kukonda zinthu zauzimu. Yehova wandichitiranso zabwino zambiri. Ndikakhala kuti ndikupeza bwino, ndimayamikira Mulungu pochita utumiki wa nthawi zonse.”

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 76]

JAMES, wazaka 18, anati:

“Anthu ambiri zimawavuta kucheza ndi munthu wa chilema ngati ineyo.

Anthu ambiri amachita chidwi ndi maonekedwe a munthu, choncho poti ndili ndi matenda amene amalepheretsa munthu kukula, ndimayesetsa kuchita zinthu zoti anthu asamaganize kuti ndikungomveka besi koma ndine kamwana. Sindidandaula ndi mmene ndimaonekera, koma ndimangovomereza kuti ndi mmene ndilili basi ndipo ndimasangalala ndi moyo. Ndimaphunzira Baibulo ndi kupemphera kwa Yehova kuti andithandize. Makolo ndiponso abale anga amandilimbikitsa nthawi zonse. Pakali pano ndikuyembekezera nthawi imene Mulungu adzachotse matenda onse. Ngakhale kuti ndine wolumala, sindilola kuti ndizilephera kuchita zinthu.”

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 76]

DANITRIA, wazaka 16, anati:

“Ndinkadziwa ndithu kuti sindili bwino chifukwa ndinkati ndikanyamula kapu ya madzi ndinkamva kupweteka kwambiri.

Munthu ukamadwala matenda opweteketsa minofu umamva ululu kwambiri. Ndimafuna kucheza ndi anzanga monga mtsikana wina aliyense, koma panopa zimenezi n’zosatheka. Ngakhale kugona kwenikweniku kumandivuta. Komabe, sindikayika kuti Yehova amandithandiza kuchita zinthu bwinobwino ngakhale ndikudwala. Ngakhale zinali zovuta, ndinakwanitsa kuchita upainiya wothandiza. Koma sindilimbana ndi kuchita zimene sindingakwanitse. Mayi anga amandikumbutsa mfundo imeneyi ndikayamba kuchita zinthu zimene sindingakwanitse.”

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 77]

ELYSIA, wazaka 20, anati:

“Ndinali wanzeru kwambiri m’kalasi. Koma panopa ndimavutika ngakhale kuwerenga, ndipo nthawi zina zimenezi zimandikhumudwitsa kwambiri.

Matenda ofooketsa thupi amachititsa kuti munthu azilephera kugwira ntchito ngakhale zimene zimaoneka ngati zosavuta. Sutha ngakhale kudzuka kumene. Komabe sindinalole kuti matenda amenewa azindilepheretsa kuchita zinthu zofunika kwambiri pamoyo wanga. Ndimawerenga Baibulo tsiku lililonse, ngakhale kuti nthawi zina ndimangowerenga mavesi ochepa chabe kapena ndimapempha munthu wina kuti andiwerengere. Ndimayamikira kwambiri makolo anga ndiponso abale anga. Nthawi ina bambo anga anakana kupatsidwa udindo winawake pamsonkhano wachigawo n’cholinga choti tidzayendere limodzi. Iwo sanadandaule ndi zimenezi. Ananena kuti udindo wawo waukulu ndi kusamalira banja lawo.”

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 77]

KATSUTOSHI, wazaka 20, anati:

“Ndimangobanika mwadzidzidzi n’kuyamba kukuwa ndi kunjenjemera kwambiri. Ndimapezeka kuti ndamwaza zinthu ndiponso kuswa chilichonse chimene chandiyandikira.

Ndinayamba kudwala matenda a khunyu ndili ndi zaka zisanu. Mwezi uliwonse ndimagwa mwina mpaka ka 7. Ndimamwa mankhwala tsiku lililonse, ndipo mankhwalawa amandifooketsa kwambiri. Komabe, sindimangoganizira kwambiri za matenda angawa. M’malo mwake, ndimaganiziranso za anthu ena. Mumpingo mwathu muli achinyamata awiri amene akuchita utumiki wa nthawi zonse ndipo amandithandiza kwambiri. Nditamaliza sukulu ndinawonjezera nthawi imene ndimalalikira. Matenda a khunyu amachititsa kuti munthu azikhala ndi maganizo tsiku ndi tsiku. Ndikayamba kumva choncho, ndimayesetsa kupuma mokwanira ndipo tsiku lotsatira ndimamva bwino.”

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 78]

MATTHEW, wazaka 19, anati:

“N’zovuta kuti anzako azikulemekeza ngati akuona kuti iweyo penapake sipali bwino.

Ndimafuna kusewera ndi anzanga, koma sindingathe chifukwa ndimadwala matenda a muubongo omwe amaumitsa ziwalo ndipo ndimayenda movutikira. Komabe sindiganizira kwambiri za zinthu zimene sindingathe kuchita. Ndimalimbikira kuchita zinthu zimene ndingathe, monga kuwerenga. Ku Nyumba ya Ufumu n’kumene ndimakhala mosangalala kwambiri chifukwa kulibe aliyense amene amandinyoza. Ndimasangalalanso kudziwa kuti Yehova amandikonda chifukwa cha makhalidwe anga abwino. Panopo, sindidzionanso ngati ndine wolumala. Ndimangodziona ngati munthu amene ali ndi vuto linalake limene akufunika kulipirira.”

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 78]

MIKI, wazaka 25, anati:

“Poyamba ndinkatha kuchita masewera olimbitsa thupi. Koma ndisanakwanitse m’komwe zaka 20, ndinayamba kumva ngati ndakalamba kale.

Ndinabadwa ndi matenda a mtima. Vutoli linadziwika ndisanafike zaka 20. Papita zaka 6 chindipangireni opaleshoni komabe sindichedwa kutopa ndipo mutu umandipweteka nthawi zonse. Komabe, ndimayesetsa kuchita zimene ndingathe. Mwachitsanzo, ndimachita utumiki wa nthawi zonse polemba makalata ndi kulalikira pa telefoni. Ndiponso chifukwa cha matendawa, ndaphunzira kupirira ndi kuzichepetsa.”

[Chithunzi patsamba 74]

Matenda aakulu angakuchititseni kumva ngati muli m’ndende koma Baibulo limapereka chiyembekezo chakuti matenda adzatha