Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Ngati Ndikusowa Ocheza Nawo?

Kodi Ndingatani Ngati Ndikusowa Ocheza Nawo?

Mutu 9

Kodi Ndingatani Ngati Ndikusowa Ocheza Nawo?

Kunja ndiye kwacha bwino, koma ine ndilibe chochita chilichonse. Anzanga onse apita kokasangalala ndipo andisiya ndekha. Anzako akapanda kukuitana kuti mupitire limodzi kokasangalala, mtima umakupweteka kwambiri. Ndimaganiza kuti, ‘Mwina ineyo ndili ndi vuto n’chifukwa chake anthu safuna kucheza nane.’

MWINA zimene tafotokozazi zakuchitikiranipo kambirimbiri. Mumamva ngati anzanu amakuthawani chifukwa chakuti muli ndi vuto linalake. Mukati mulankhule mumangochita chibwibwi. Ndipo mukakhala nawo limodzi mumalephera kucheza chifukwa cha manyazi. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti munthu uzichita kulephera ndi kucheza komwe?

Yesetsani kupeza njira yoti muzicheza ndi anzanu m’malo momangokhala nokhanokha. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

Vuto Loyamba: Kudziona ngati wosafunika. Achinyamata ena amadziona kuti ndi osafunika. Iwo amaona kuti palibe aliyense amene amawakonda ndipo sanganene chilichonse chomveka. Kodi inunso mumamva choncho? Vuto limenelitu lingachititse kuti muzilephera kucheza ndi anzanu.

Njira yothetsera vutoli: Musamadziderere. (2 Akorinto 11:6) Ganizirani mofatsa ‘zinthu zimene mumachita bwino.’ Ganiziraninso za luso kapena makhalidwe abwino amene muli nawo ndipo alembeni pansipa.

․․․․․

Inde simungalephere kukhala ndi zina zimene mumalakwitsa, ndipo ndi bwino kudziwa mfundo imeneyi. (1 Akorinto 10:12) Koma inuyo mukudziwa kuti pali zinthu zina zimene mumachita bwino. Kuganizira zimenezi kungakuthandizeni kuona kuti ndinu wofunika.

Vuto Lachiwiri: Manyazi. Mwina mumafuna kucheza ndi anzanu koma mpata ukapezeka, mumauma pakamwa. Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Elizabeth, anati: “Ndimachita manyazi nthawi zonse. Zimandivuta kwambiri kucheza ndi anthu pamisonkhano yachikhristu ndipo ndimasirira anthu amene amacheza momasuka ndi ena.” Ngati ndinu wamanyazi monga Elizabeth, zingakuvuteni kucheza ndi ena momasuka.

Njira yothetsera vutoli: Muzichita chidwi ndi anthu ena. Muzikhala womasuka koma musayembekezere kuti muchite kufanana ndi anthu amene amamasuka kwambiri ndi anthu. Pezani munthu mmodzi amene mungayambe kucheza naye. Mnyamata wina dzina lake Jorge, anati: “Mungayambe kucheza naye pom’patsa moni kapena kum’funsa mmene ntchito yake ikuyendera. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mum’dziwe bwino.”

Mfundo imene ingakuthandizeni ndi yakuti: Musamangocheza ndi anthu amsinkhu wanu okha. Anthu ena otchulidwa m’Baibulo amene ankachezera limodzi anali amisinkhu yosiyana, monga Rute ndi Naomi, Davide ndi Jonatani ndiponso Timoteyo ndi Paulo. (Rute 1:16, 17; 1 Samueli 18:1; 1 Akorinto 4:17) Kumbukiraninso kuti pocheza, anthu ena amalankhulapo osati inu nokha ayi. Ndiponso pocheza, anthu ambiri amasangalala mukamawamvetsera. Choncho musamachite manyazi kucheza ndi anzanu chifukwa nawonso azilankhulapo.

Lembani mayina a anthu awiri achikulire amene mukufuna kuti muzicheza nawo.

․․․․․

Yesani kupeza njira yoti mucheze ndi mmodzi wa anthu amenewa. Mukamayesetsa kudziwana bwino ndi “gulu lonse la abale,” simungasowe anthu ocheza nawo.—1 Petulo 2:17.

Vuto Lachitatu: Khalidwe losasangalatsa. Munthu amene amadziona ngati amadziwa zonse, samva zonena za ena. Ndiponso pali anthu ena amene nthawi zonse amakonda kutsutsa maganizo a anzawo ndipo amafuna kuti aliyense azichita zimene iwo akufuna. Popeza munthu wotere ‘amapambanitsa kukhala wolungama,’ sagwirizana ndi aliyense amene sachita zimene iye akufuna. (Mlaliki 7:16) N’zodziwikiratu kuti inuyo simungafune kucheza ndi munthu wotere. Mwina n’kuthekanso kuti anzanu safuna kucheza nanu chifukwa chakuti inuyo ndi amene muli ndi khalidwe lotere. Baibulo limati: “Chitsiru chichulukitsanso mawu.” Ndipo limanenanso kuti: “Pochuluka mawu zolakwa sizisoweka.”—Mlaliki 10:14; Miyambo 10:19.

Njira yothetsera vutoli: Muziganizira ena. (1 Petulo 3:8) Muzimvetsera modekha mnzanu akamalankhula ngakhale musakugwirizana ndi zimene akunenazo. Musalimbane ndi mfundo zimene simukugwirizana nazozo. Ngati mukuona kuti m’pofunika kunena maganizo anu pamfundo zimene simukugwirizana nazozo, yesani kufotokoza maganizo anuwo modekha ndiponso mwanzeru.

Muzilankhula bwino ndi ena chifukwa ndi mmene inunso mungafunire kuti anthu azilankhula nanu. Baibulo limati: “Muzichita zinthu zonse popanda kung’ung’udza ndi kutsutsana.” (Afilipi 2:14) Anzanu sangakonde kucheza nanu ngati mumakonda kuwatsutsa, kuwagemula ndiponso kuwanyoza kapena kuwaona ngati amalakwitsa zinthu nthawi zonse. Anthu angamasangalale kucheza nanu ngati ‘nthawi zonse mawu anu amakhala achisomo, okoleretsa ndi mchere.’—Akolose 4:6.

Musayembekezere Kuti Aliyense Angakhale Mnzanu

Mwina pamfundo zimene takambiranazi, mwapezapo njira zimene zingakuthandizeni kucheza ndi ena. Komabe sindiye kuti zikatero aliyense angakhale mnzanu. Yesu ananena kuti anthu ena angadane nanu ngakhale mutachita zabwino bwanji. (Yohane 15:19) Choncho sizingatheke kuti aliyense akhale mnzanu.

Komabe muzingoyesetsa kukhala munthu wabwino n’kumatsatira mfundo za m’Baibulo. Baibulo limanena kuti Samueli ankafunitsitsa kuchita zinthu zokondweretsa Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, “Yehova ndi anthu omwe anam’komera mtima.” (1 Samueli 2:26) Inunso mungakhale ngati Samueli ngati mukuyesetsa kukondweretsa Mulungu.

WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 8

Kuti mudziwe zambiri, onerani DVD  yakuti “Young People Ask—How Can I Make Real Friends?” DVD imeneyi ikupezeka m’zinenero zoposa 40

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi mungatani ngati mnzanu wapamtima wayamba kudana nanu?

LEMBA LOFUNIKA

“Wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.”—Miyambo 11:25.

MFUNDO YOTHANDIZA

Yesetsani kupeza zonena. Mwachitsanzo, ngati mnzanu wakufunsani kuti: “Zikuyenda?” Musangoyankha kuti: “Ee zikuyenda,” koma fotokozani mmene zikuyendera ndipo m’funseninso mnzanuyo kuti nayenso afotokoze.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Baibulo limasonyeza kuti Mose, Yeremiya ndi Timoteyo anali anthu amanyazi.—Eksodo 3:11, 13; 4:1, 10; Yeremiya 1:6-8; 1 Timoteyo 4:12; 2 Timoteyo 1:6-8.

ZOTI NDICHITE

Vuto lalikulu limene limandilepheretsa kucheza ndi anzanga ndi lakuti: ․․․․․

Ndingathetse vuto limeneli pochita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani Akhristu ena amasowa anthu ocheza nawo?

● Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzidziona kuti ndinu wofunika?

● Kodi mungamulimbikitse bwanji mng’ono wanu amene ali ndi vuto lolephera kucheza ndi anthu?

[Mawu Otsindika patsamba 88]

“Mlongo wina ankayesetsa kuti azicheza nane koma ineyo sindinkamusamala. Koma nditayamba kucheza naye, ndinaona kuti sindinkachita bwino kumunyalanyaza. Iye anakhala mnzanga wapamtima ngakhale kuti anali wamkulu ndipo ndinkasiyana naye zaka 25.”—Anatero Marie

[Chithunzi patsamba 87]

Mungapeze njira yokuthandizani kuti muyambe kucheza ndi anzanu