Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kuulula Zimene Ndimachita Mseri?

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kuulula Zimene Ndimachita Mseri?

Mutu 16

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kuulula Zimene Ndimachita Mseri?

□ Kumwa mowa

□ Kucheza ndi anthu omwe makolo anu amaona kuti si abwino

□ Kumvera nyimbo zoipa

□ Kupita ku zisangalalo za achinyamata okhaokha

□ Kuchita chibwenzi mobisa

□ Kuonera mafilimu oipa kapena kuchita masewera oipa a pakompyuta

□ Kutukwana

KODI mumachita zinthu zimene tatchulazi mwamseri? Ngati ndi choncho, n’zosakayikitsa kuti mukudziwa kuti zimene mumachitazo ndi zoipa. Mwinanso chikumbumtima chanu chimakuvutitsani. (Aroma 2:15) Komabe kuulula zimene mumachita mseri n’kovuta. Mwinanso zinthu zingaipe kwambiri ngati mutawauza makolo anu. Koma kodi mukudziwa kuti zimene mukuchitazo ndi chiphamaso? N’chifukwa chiyani mumachita zinthu mwamseri?

Kodi Mumafuna Ufulu Wochita Nokha Zinthu?

Baibulo limati: “Mwamuna adzasiya atate wake ndi amake.” (Genesis 2:24) Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito kwa akazi. Aliyense akamakula amafuna kumasankha yekha zochita. Koma makolo akamawaletsa achinyamata kuchita zinthu zimene makolowo akuona kuti n’zoipa, achinyamatawo safuna kumvera.

N’zoona kuti makolo ena amakhwimitsa zinthu kwambiri. Mtsikana wina dzina lake Kim anati: “Makolo athu satilola kuonera filimu ina iliyonse, ndipo bambo amatiletsa ngakhale kumvetsera nyimbo.” Achinyamata akamaletsedwa kuchita zinthu, amayamba kusirira anzawo omwe makolo awo amawalola kuchita zinthu mwaufulu.

Mtsikana wina dzina lake Tammy anafotokoza kuti achinyamata ambiri amachita zinthu mwamseri kuti azikondedwa ndi anzawo. Iye anati: “Ndikakhala kusukulu ndinkatukwana n’cholinga choti ndisamachite zinthu zosiyana ndi anzanga. Ndinayambanso kusuta fodya ndiponso kumwa mowa mwauchidakwa. Kenako ndinayamba kuchita zibwenzi mozembera makolo anga.”

Zimenezi zinachitikiranso mnyamata wina dzina lake Pete. Iye anati: “Ndinakulira m’banja la Mboni za Yehova. Koma sindinkafuna kuti anzanga azindiseka kuti ndine wa Mboni. Choncho, ndinkachita zinthu zoti anzangawo azindikonda. Akandifunsa chifukwa chimene sindinkalandilira mphatso zokhudzana ndi maholide achipembedzo, ndinkangowanamiza.” Pang’ono ndi pang’ono Pete anayamba kuchita zinthu zotsutsana ndi Baibulo ndipo mapeto ake anachita tchimo lalikulu.

Palibe Chinsinsi

Anthu sanayambe lero kuchita zinthu mwamseri. Aisiraeli ena anali ndi moyo wachiphamaso. Koma mneneri Yesaya anawachenjeza kuti: “Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wawo, ndi ntchito zawo zili mumdima, ndipo amati Ndani ationa ife? ndani atidziwa ife?” (Yesaya 29:15) Aisiraeliwo anaiwala kuti Mulungu ankaona zimene iwo ankachita. Patapita nthawi Mulungu anawalanga.

N’chimodzimodzinso masiku ano. Ngakhale mutabisira makolo khalidwe lanu loipa, simungathe kumubisira Yehova Mulungu. Lemba la Aheberi 4:13 limati: “Palibe cholengedwa chobisika pamaso pake. Zinthu zonse zili pambalambanda ndi zoonekera poyera pamaso pake. Inde, pamaso pa uyo amene tidzayenera kuyankha kwa iye.” Choncho palibe chimene munthu angapindule ngati atabisa khalidwe loipa. Dziwani kuti n’zosatheka kumusangalatsa Mulungu ngati mumangopita ku misonkhano yachikhristu mwachiphamaso. Yehova amadziwa ngati ‘anthu akumulemekeza ndi milomo yawo, koma mtima wawo uli kutali ndi iye.’—Maliko 7:6.

Kodi mumadziwa kuti anthu amene amachita zinthu mwamseri amakhumudwitsa Yehova? Aisiraeli atasiya kumvera Chilamulo cha Mulungu, iwo ‘anamvetsa chisoni Woyera wa Isiraeli.’ (Salmo 78:41, NW) Masiku anonso Yehova amamva chisoni akaona achinyamata ena amene ‘analeredwa m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake,’ akuchita zinthu zoipa mwamseri.—Aefeso 6:4.

Ululani

Ngati simuulula zimene mukuchita mseri, ndiye kuti mukulakwira Mulungu, makolo anu ndiponso mukudzilakwira nokha. N’zoona kuti ngati mutaulula mungachite manyazi ndiponso mungalandire chilango, komabe ndi bwino kuulula. (Aheberi 12:11) Mwachitsanzo, ngati muli ndi chizolowezi chonama, makolo anu angasiye kukukhulupirirani. Choncho makolo akamakukhwimitsirani zinthu, musamadabwe. Komabe, kodi kuulula machimo anu n’kofunika kwambiri chifukwa chiyani?

Tayerekezerani kuti inuyo ndi makolo anu mukuyenda m’nkhalango yowirira kwambiri. Makolo anuwo akuuzani kuti muziwatsatira pambuyo. Koma inu mwawazembera n’kupita mbali inayake yoopsa. Ndiyeno mwapezeka kuti mwagwera m’zithaphwi ndipo mukulephera kutulukamo. Kodi mungachite manyazi kukuwa kuti makolo anu akuthandizeni? Kodi mungachite mantha kuti makolo anu akukalipirani chifukwa chosamvera lamulo lawo? Ayi. M’malo mwake mungakuwe kwambiri kuti akumveni ndi kukupulumutsani.

Chimodzimodzinso ngati mumachita zinthu mwamseri, mukufunikira kuthandizidwa mwamsanga. Komabe, dziwani kuti simungasinthe zinthu kuti zikhale mmene zinalili poyamba. Koma mungathe kusintha tsogolo lanu kuti likhale labwino. Ngakhale zitakhala zovuta bwanji, ndi bwino kuuza makolo anu zimene mumachita mseri. Ngati simuchita zimenezo khalidwe lanu lingawonongeke kwambiri ndiponso mungawononge mbiri ya anthu a m’banja lanu. Koma mukalapa ndi mtima wonse, Yehova adzakukhululukirani.—Yesaya 1:18; Luka 6:36.

Choncho, auzeni makolo anu zoona. Sonyezani kuti mukumvetsa mmene zawakhudzira. Ndipo mverani malangizo awo. Mukachita zimenezo, iwo adzasangalala kwambiri ndiponso mudzasangalatsa Yehova Mulungu. Komanso inuyo mudzakhala ndi chikumbumtima choyera.—Miyambo 27:11; 2 Akorinto 4:2.

M’MUTU WOTSATIRA

Ngati mumacheza bwino ndi anzanu a kusukulu, kodi muyenera kudziwa chiyani za anzanuwo?

LEMBA LOFUNIKA

“Wobisa machimo ake sadzaona mwayi; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.”—Miyambo 28:13.

MFUNDO YOTHANDIZA

Musamaone zolakwa zanu ngati zazing’ono, komanso musamadziimbe mlandu kwambiri. Muzikumbukira kuti Yehova ndi Mulungu wokhululuka.—Salmo 86:5.

KODI MUKUDZIWA  . . . ?

Munthu akamadziimba mlandu chifukwa cholakwitsa zinazake ndi chizindikiro choti atha kusintha. Koma amene amapitirizabe kuchita zinthu zoipa amawononga chikumbumtima chake. Kenako chikumbumtimacho sichigwiranso ntchito ngati mmene limachitira khungu limene lapsa ndi moto.—1 Timoteyo 4:2.

ZOTI NDICHITE

Ngati ndimachita zinthu zinazake mwamseri, ndiyenera kuuza anthu awa: ․․․․․

Ndikapatsidwa malangizo, ndiyenera kuchita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi n’chifukwa chiyani achinyamata ena amachita zinthu mwamseri?

● Kodi chingachitike n’chiyani ngati munthu akuchita zinthu mwamseri?

● Kodi ubwino wosiya kuchita zinthu mwamseri ndi wotani?

[Mawu Otsindika patsamba 140]

“Ndikuona kuti ndi bwino kuti achinyamata azisonyeza kuti amatsatira mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo. Ayenera kuchita zimenezi mwamsanga, chifukwa akachedwa zinthu zingawavute kwambiri.”​—Anatero Linda

[Chithunzi patsamba 141]

Ngati mukulephera kutuluka m’moyo wachiphamaso, muyenera kupempha thandizo