Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndizipeza Ndalama?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizipeza Ndalama?

Mutu 18

Kodi Ndingatani Kuti Ndizipeza Ndalama?

“Ndikufuna ndalama zoti ndigulire galimoto.”—Anatero Sergio.

“Ndimakonda kugula zinthu.”—Anatero Laurie-Ann.

“Pali zinthu zina zabwino zomwe ndikuzifuna, koma makolo anga sangakwanitse kundigulira.”—Anatero Mike.

MWINA inunso muli ndi zifukwa ngati zimenezi zomwe mukufunira ndalama. Kapena mukufuna ndalama kuti muzithandiza pabanja panu. Ngakhale kuti simungathandize pabanja panu, kudzigulira nokha zovala kapena zinthu zina kungapepukitse udindo wa makolo anu wogula zofunika pabanjapo.

Zoona zake n’zakuti m’pofunika ndalama kuti muthe kugula zinthu zanu kapena zothandizira banja lanu. Ngakhale kuti Yesu analonjeza kuti Yehova adzathandiza anthu amene ‘akufuna Ufumu wa Mulungu choyamba,’ Mkhristu aliyense amafunikabe kugwira ntchito kuti apeze zosowa zake. (Mateyo 6:33; Machitidwe 18:1-3; 2 Atesalonika 3:10) Ndiyeno kodi mungatani kuti muzipeza ndalama? Mfundo ina yofunika kuiganizira kwambiri ndi yakuti, kodi mungatani kuti kufunafuna ndalama kusasokoneze ubwenzi wanu ndi Mulungu?

Zimene Mungachite Kuti Mupeze Ntchito

Ngati mukufunitsitsa chinthu chimene makolo anu sangakwanitse kukugulirani, mungachite bwino kupeza ntchito kuti mugule nokha chinthucho. Uzani makolo anu kuti mukufuna ntchito. N’kutheka kuti angasangalale kwambiri ndi maganizo anuwo. Ngati iwo atavomereza komanso ngati malamulo a m’dziko lanu akukulolani kugwira ntchito, mfundo zinayi zotsatirazi zingakuthandizeni kupeza ntchito.

Dziwitsani ena kuti mukufuna ntchito. Uzani anthu oyandikana nawo nyumba, aphunzitsi anu ndiponso achibale anu kuti mukufunafuna ntchito. Ngati mukuchita manyazi kuwafotokozera, mungathe kungowafunsa ntchito imene anagwirapo panthawi imene anali ndi zaka ngati zanuzo. Anthu ambiri akadziwa kuti mukufunafuna ntchito, sizingavute kuti mudziwe kumene akufuna kulemba anthu ntchito.

Lankhulani ndi aliyense amene mwamva kuti akufuna kulemba anthu ntchito. Lemberani kalata kapena imbirani foni kulikonse kumene mwamva kuti akufuna kulemba anthu ntchito. Mungadziwe zimenezi kudzera mu nyuzipepala, pa Intaneti ndi malo ena olengezerapo zinthu m’masitolo ndi kusukulu. Mnyamata wina dzina lake Dave anati: “Umu ndi mmene ndinapezera ntchito. Nditawerenga mu nyuzipepala, ndinatumizira mabwanawo chikalata chofotokoza zinthu zondiyenereza kugwira ntchitoyo komanso ndinawaimbira foni.” Ngakhale atapanda kukulembani ntchito imeneyo, mwina kuchita zimenezi kungathandize mabwanawo kuganizira ntchito ina imene angakulembeni yomwe sanailengeze.

Lembani CV yanu ndi kutumizira anthu osiyanasiyana. Lembani chikalata chotchedwa CV, chofotokoza mbiri yanu, maphunziro anu, ntchito zimene mukudziwa ndiponso zimene munagwirapo. Kodi mukuganiza kuti palibe zimene mungalembe? Taganizani mofatsa. Kodi munayamba mwasamalirapo mwana wa anthu ena kapena m’bale wanu wamng’ono makolo anu atachoka? Zimenezo zikutanthauza kuti ndinu wodalirika. Kodi munayamba mwathandizapo bambo anu kukonza galimoto kapenanso zinthu zina? Zimenezo zingasonyeze kuti muli ndi luso lokonza zinthu. Kodi mumadziwa kutayipa kapena kugwiritsa ntchito kompyuta? Kodi kusukulu munakhozapo bwino kwambiri phunziro linalake la ntchito zamanja? Mabwana ambiri angasangalale ndi zinthu ngati zimenezi, choncho zilembeni pa CV yanu. Perekani CV yanuyo kwa mabwana amene akufuna kulemba anthu ntchito, komanso pemphani anzanu ndiponso achibale anu kuti aipereke kwa mabwana enanso.

Dzilembeni nokha ntchito. Taganizirani za m’dera lanu. Kodi mungachite zinthu zinazake zofunika m’deralo zimene palibe aliyense amene akuchita? Mwachitsanzo, ngati mumakonda ulimi, mungathe kumalima ndiwo zamasamba n’kumagulitsa. Ngati mumadziwa kukonza zipangizo zamagetsi, mungathe kumakonzera anthu zipangizo zoterozo. Kapenanso mungagwire ntchito inayake yooneka ngati yonyozeka, monga kuchita ganyu pakhomo la munthu. Mkhristu sachita manyazi kugwira ntchito ndi manja ake. (Aefeso 4:28) Ndi zoona kuti kugwira ntchito ngati zimenezi kumafuna kuti munthu akhale wakhama ndiponso wodzipereka.

Komabe, chenjezo pankhaniyi ndi lakuti: Musathamangire kuyamba ntchito yodzilemba nokhayo musanafufuze bwinobwino. (Luka 14:28-30) Lankhulani ndi makolo anu choyamba. Komanso funsani anthu ena amene anachitapo ntchito yoteroyo. Kodi pangafunike kuti muzikhoma msonkho? Kodi mungafunike kukhala ndi chilolezo kapena chiphaso cha ntchitoyo? Mungachite bwino kukafunsa zimenezo kuboma.—Aroma 13:1.

Muzichita Zinthu Moganiza Bwino

Tiyerekezere kuti mukufuna kukwera njinga mutanyamula zinthu zambirimbiri m’manja, monga chikwama cha kusukulu, mpira ndiponso katundu wina. Mukanyamula katundu wambiri mungalephere kukwera njingayo. Ndi mmenenso zingakhalire ngati mutayamba ntchito yofuna zambiri. Mungathe kumakhala wofooka komanso simungamakhoze bwino kusukulu ngati ntchito yanuyo ndi yofuna kuganiza kwambiri, nthawi yambiri ndiponso nyonga zambiri. Komanso mfundo yofunika kuiganizira kwambiri ndi yakuti mukhoza kumalephera kupita kumisonkhano yachikhristu, kuphunzira Baibulo ndiponso kulalikira. Mtsikana wina dzina lake Michèle anati: “Ndakhala ndikulephera kufika pamisonkhano chifukwa choweruka kusukulu komanso kuntchito nditatopa kwambiri.”

Musalole kuti mtima wofuna ndalama usokoneze moyo wanu. Yesu ananena kuti anthu “amene amazindikira zosowa zawo zauzimu” ndi omwe amakhaladi osangalala. (Mateyo 5:3) Ndipo ananenanso kuti: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Mtsikana wina dzina lake Maureen anatsatira malangizo amenewa. Iye anati: “Sindifuna kutanganidwa ndi zinthu zakuthupi. Ndimadziwiratu kuti ngati nditatanganidwa nazo kwambiri, ubwenzi wanga ndi Mulungu ndi womwe ungasokonezeke.”

N’zoona kuti m’madera ena, achinyamata amafunikira kugwira ntchito kwa maola ambiri kuti azithandiza pabanja pawo. Koma ngati inu simukufunikira kutero, palibe chifukwa choti muzigwira ntchito kwa maola ambiri. Akatswiri ambiri amati sibwino kuti mwana wa sukulu azigwira ntchito maola oposa 20 pamlungu chifukwa zimabwezera m’mbuyo maphunziro ake. Ena amati ndi bwino kuti mwana wa sukulu azigwira ntchito maola 8 kapena 10 pamlungu. Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja awiri oti tho pali vuto ndi kungosautsa mtima.”—Mlaliki 4:6.

Kumbukirani kuti “chinyengo champhamvu cha chuma” chingathe kukusokonezani kuti musakhale ndi chidwi pa zinthu zauzimu. (Maliko 4:19) Choncho ngati mwayamba ntchito yoti muzigwira mukaweruka kusukulu n’cholinga choti muzipeza ndalama, konzani ndandanda yabwino yokuthandizani kuti muziika zinthu zauzimu patsogolo. Pempherani kwa Yehova Mulungu ndipo iye angakuthandizeni kuti mupitirize kukhala wolimba mwauzimu.

WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 21

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi mumatha kugwiritsa ntchito bwino ndalama kapena ndalamazo zimakulamulirani? Onani mmene mungazigwiritsire ntchito moyenera.

LEMBA LOFUNIKA

“Moyo wa [munthu waulesi] ukhumba osalandira kanthu; koma moyo wa akhama udzalemera.”—Miyambo 13:4.

MFUNDO YOTHANDIZA

Tumizani CV yanu ku makampani osiyanasiyana ngakhale kuti sanalengeze kuti akufuna kulemba anthu ntchito.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

M’madera ena, amalengeza ntchito imodzi yokha pantchito 8 zilizonse zimene akufuna kulemberapo anthu.

ZOTI NDICHITE

Kuti ndipeze ntchito mwamsanga ndingachite izi: ․․․․․

Ndingachepetse nthawi imene ndimagwira ntchito kufika pa maola pamlungu. ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani mukufuna kuti muzipeza ndalama?

● Kodi ndi mavuto otani amene mungakumane nawo mukayamba ntchito?

● Kodi mungatani kuti muziona bwino nkhani zokhudza ndalama?

[Mawu Otsindika patsamba 153]

“Ngati nthawi zonse mumaona kuti mungakhale wosangalala chifukwa cha zinthu zimene mungakhale nazo, ndiye kuti mukudzinamiza. Zinthu zatsopano zimene mungazifune zizitulukabe. Choncho, muyenera kukhutira ndi zinthu zimene muli nazo.”—Anatero Jonathan

[Bokosi patsamba 155]

Ndalama N’zofunika, Koma Musazikonde Kwambiri

Mpeni ndi chipangizo chothandiza kwambiri kukhitchini. Koma mpeni womwewo ungavulaze mwana kapena munthu wamkulu amene sakuugwiritsa ntchito bwino. N’chimodzimodzinso ndi ndalama. Ngati mukudziwa kuzigwiritsa ntchito bwino zingakuthandizeni kwambiri. Koma ngati simukudziwa, zingakuvulazeni. N’chifukwa chake mtumwi Paulo anatichenjeza kuti tisamakonde ndalama. Pofunafuna ndalama, anthu ena amanyalanyaza ubwenzi wawo ndi anzawo, amanyalanyaza mabanja awo, ndipo ngakhalenso ubwenzi wawo ndi Mulungu. Pochita zimenezi, iwo ‘amadzibweretsera zopweteka zambiri.’ (1 Timoteyo 6:9, 10) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tikuphunzirapo kuti tizigwiritsa ntchito bwino ndalama. Inde, ndalama n’zofunika, koma tisazikonde kwambiri.

[Chithunzi patsamba 153]

Kuchita zinthu zambiri panthawi imodzi kungakusokonezeni