Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Makolo Dziwani Izi:

Makolo Dziwani Izi:

Makolo Dziwani Izi:

Achinyamata akamakula amakumana ndi mavuto ambiri ndipo zimenezi zimawachititsa mantha. Inuyo monga makolo mwina mungafune kuti ana anu asakumane ndi mavuto koma zimenezi n’zosatheka. Komabe mungathe kuwalimbikitsa. Ndi udindo wanu kuwathandiza mpaka atakula n’kukhala odzidalira.

Mwina mungaone kuti zimenezi n’zovuta. Inde n’zovutadi, chifukwa ana sachedwa kusintha. Mwana wanu amene ankakonda kucheza nanu angasinthe mwadzidzidzi n’kusiyiratu kulankhula nanu. Kapenanso mwana wanu wamkazi amene ankakonda kukutsatirani kulikonse angayambe kuchita manyazi kuyenda nanu.

Koma musamaone ngati simungathe kuthandiza ana anu. Mungathe kupeza malangizo okuthandizani inuyo komanso ana anu. Malangizowa mungawapeze m’Mawu a Mulungu, Baibulo.

Bukuli lakonzedwa kuti lithandize mwana wanu kutsatira malangizo a m’Baibulo. Zam’katimu zomwe zili patsamba 4 ndi 5 zikuthandizani kudziwa nkhani zimene zili m’bukuli. Koma si zokhazi, bukuli lili ndi zinthu zinanso zambiri monga izi:

(1) Bukuli lakonzedwa kuti wowerenga azinena maganizo ake. M’malo ambiri mwana wanu aziyankha mafunso komanso kulemba maganizo ake. Mwachitsanzo bokosi lakuti “Mmene Mungakonzekerere” lomwe lili patsamba 132 ndi 133 lithandiza mwana wanu kuganizira mavuto amene angakumane nawo komanso zimene angachite pothana ndi mavutowo. Bukuli lili ndi zigawo 9 ndipo kumapeto kwa chigawo chilichonse kuli tsamba lakuti “Mfundo Zanga.” Patsamba limeneli mwana wanu azilembapo maganizo ake pa zimene wawerenga m’chigawo chilichonse.

(2) Bukuli likulimbikitsa kulankhulana. Mwachitsanzo, patsamba 63 ndi  64 pali bokosi lakuti “Kodi Ndingafunse Bwanji Bambo kapena Mayi Anga Nkhani Zokhudza Kugonana?” Komanso kumapeto kwa mutu uliwonse kuli bokosi lakuti “Mukuganiza Bwanji?” Bokosili likubwereza mfundo za m’mutu uliwonse komanso lili ndi mfundo zoti banja lingakambirane. Mutu uliwonse uli ndi bokosi lakuti “Zoti Ndichite” ndipo mbali yomaliza m’bokosili ndi yakuti: “Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi:” Mbaliyi ikulimbikitsa achinyamata kuti azifunsa malangizo kwa makolo awo akakhala ndi vuto.

Chenjezo: Kuti ana anu alembe zakukhosi kwawo m’bukuli, musamaone zimene alemba. Anawo akafuna angathe kukusonyezani okha zimene alembazo.

Pezani buku lanu ndipo liwerengeni mofatsa. Mukamawerenga bukuli muzikumbukira mavuto amene munkakumana nawo muli wachinyamata. Kambiranani zimenezi ndi mwana wanu ngati zili zoyenera. Zimenezi zidzachititsa kuti ana anu akuuzeni zakukhosi kwawo. Ndipo anawo akamalankhula, muziwamvetsera. Ngakhale kuti anawo sangafune kuti mukambirane nawo, iwo amadziwa kuti malangizo anu ndi abwino kwambiri kuposa a anzawo. Choncho yesetsani kulankhulana nawobe.

Ndife osangalala kutulutsa buku la malangizo a m’Baibulo limeneli ndipo tikukhulupirira kuti bukuli lithandiza kwambiri inuyo ndi ana anu.

Ofalitsa