Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 17

“Dzilimbitseni Pamaziko a Cikhulupililo Canu Coyela Kopambana”

“Dzilimbitseni Pamaziko a Cikhulupililo Canu Coyela Kopambana”

“Podzilimbitsa pamaziko a cikhulupililo canu coyela kopambana, . . . pitilizani kucita zinthu zimene zingacititse Mulungu kukukondani.”—YUDA 20, 21.

1, 2. Ndi nchito yomanga iti imene mukugwila? Nanga n’cifukwa ciani mufunika kuigwila mwakhama?

YELEKEZANI kuti mukugwila nchito yomanga nyumba mwakhama. Mwagwila nchito imeneyi kwa nthawi yaitali ndithu, ndipo mudzapitilizabe kuigwila. Ndi zoona kuti nchito imeneyi ndi yovuta, koma ndi yokhutilitsa. Ndipo zivute zitani, ndinu okonzeka kugwilabe nchito imeneyi mwakhama cifukwa imakhudza moyo wanu ndi tsogolo lanu. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti nyumba yophiphilitsa imeneyi ndinu amene.

2 Wophunzila Yuda anagogomezela mfundo yakuti tifunika kudzilimbitsa tokha mwa kuuzimu. Pamene iye analimbikitsa Akristu “kupitiliza kucita zinthu zimene zingacititse Mulungu kuwakonda,” anafotokozanso cimene cingatithandize kucita zimenezo. Iye anakamba kuti tiyenela ‘kudzilimbitsa pamaziko a cikhulupililo cathu coyela kopambana.’ (Yuda  20, 21) Kodi ndi zinthu zina ziti zimene muyenela kucita kuti mulimbitse cikhulupililo canu ndi kukhalabe m’cikondi ca Mulungu? Tiyeni tione zinthu zitatu zimene muyenela kucita pa nchito yanu yomanga imeneyi ya kuuzimu.

PITILIZANI KULIMBITSA CIKHULUPILILO CANU PA MALAMULO OLUNGAMA A YEHOVA

3-5. (a) Kodi Satana amafuna kuti muziwaona motani malamulo a Yehova? (b) Kodi malamulo a Mulungu tiyenela kuwaona motani? Nanga kuwaona mwanjila imeneyo kuyenela kutikhudza bwanji? Pelekani fanizo.

3 Coyamba, tifunika kulimbitsa cikhulupililo cathu pa malamulo a Mulungu. Panthawi yonse imene mwaphunzila buku lino, mwadziŵa malamulo ambili olungama a Yehova pa nkhani ya makhalidwe abwino. Kodi malamulo amenewa mumawaona bwanji? Satana amafuna kukusoceletsani kuti muziona malamulo a Yehova ndi mfundo zake kuti ndi zovuta ndi zopanikiza. Kuyambila pamene Satana anaona kuti msampha umenewu ndi wothandiza m’munda wa Edeni, iye wakhala akuugwilitsila nchito. (Genesis 3:1-6) Kodi mudzagwidwa mumsampha umenewu? Yankho lake limadalila mmene inu mumaonela zinthu.

4 Tiyelekezele kuti muli kumalo okongola osungilako nyama, ndiyeno mwaona kuti mbali ina anaichinga ndi mpanda wawaya, wautali ndi wolimba. Koma inu muona kuti mbali imene anachingayo ndi yokongola kwambili. Poyamba, mungaone kuti mpandawo ndi wopanda phindu, ndipo ukukulepheletsani kuona zinthu zina. Ndiyeno pamene muyang’ana mu mpandawo, mukuona mkango waukali ukuŵendelela nyama. Tsopano mwadziŵa kuti colinga ca mpandawo ndi kukutetezani. Kodi pali wina woopsa amene akukuŵendelelani? Mau a Mulungu amati: “Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso. Mdani wanu Mdyelekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.”—1 Petulo 5:8.

5 Satana ndi mdani woopsa. Popeza kuti Yehova safuna kuti Satana ationonge mwakuuzimu, wakhazikitsa malamulo kuti atiteteze ku “zocita zacinyengo” zambili za woipayo. (Aefeso 6:11) Conco, pamene tiganizila malamulo a Mulungu, tiyenela kuwaona monga umboni wakuti Atate wathu wakumwamba amatikonda. Kuona malamulo a Mulungu mwanjila imeneyi, kumatiteteza ndipo timakhala acimwemwe. Mtumwi Yakobo analemba kuti: “Woyang’anitsitsa m’lamulo langwilo limene limabweletsa ufulu, amene amalimbikila kutelo, adzakhala wosangalala policita.”—Yakobo 1:25.

6. Kodi njila yabwino koposa yolimbitsila cikhulupililo canu pa malamulo olungama a Mulungu ndi mfundo zake ndi iti? Pelekani citsanzo.

6 Kutsatila malamulo a Mulungu ndi njila yabwino koposa yotithandiza kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa Wotipatsa Malamulo ndi kudalila nzelu zopezeka m’malamulo ake. Mwacitsanzo, “cilamulo ca Kristu” cimaphatikizapo lamulo la Yesu lakuti tiyenela kuphunzitsa anthu ‘zinthu zonse zimene [iye] watilamulila.’ (Agalatiya 6:2; Mateyu 28:19, 20) Ndiponso Akristu sanyalanyaza lamulo lakuti tiyenela kusonkhana kuti tilambile Mulungu ndi kulimbikitsana. (Aheberi 10:24, 25) Malamulo a Mulungu amaphatikizaponso langizo lakuti tiyenela kupemphela kwa Yehova nthawi zonse, ndiponso mocokela pansi pa mtima. (Mateyu 6:5-8; 1 Atesalonika 5:17) Pamene titsatila malamulo amenewa, timazindikila kuti Mulungu amatipatsa malamulo cifukwa cakuti amatikonda. Kutsatila malamulo ake kumatipangitsa kukhala ndi umoyo wosangalala ndi wokhutila umene sitingaupeze kwina kulikonse m’dziko lovutali. Cikhulupililo cathu pa malamulo a Mulungu cimalimba kwambili tikamasinkhasinkha mmene tapindulila cifukwa cotsatila malamulowo.

7, 8. Kodi Mau a Mulungu amalimbikitsa bwanji anthu amene amada nkhawa kuti m’kupita kwa nthawi angalephele kumvela malamulo ake?

7 Anthu ena nthawi zina amada nkhawa kuti m’kupita kwa nthawi angalephele kumvela malamulo a Yehova. Amaopa kuti mwina angacite chimo. Ngati inunso mumaganiza conco, nthawi zonse muzikumbukila mau awa akuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, amene ndimakucititsani kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo. Zingakhale bwino kwambili mutamvela malamulo anga! Mukatelo mtendele wanu udzakhala ngati mtsinje, ndipo cilungamo canu cidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.” (Yesaya 48:17, 18) Kodi munayamba mwaganizilapo mmene mau amenewa alili olimbikitsa?

8 Palembali, Yehova akutikumbutsa kuti zinthu zimatiyendela bwino ngati timamumvela. Iye walonjeza mapindu aŵili amene tidzapeza tikakhala omvela. Loyamba, mtendele wathu udzakhala ngati mtsinje wabata, wokhala ndi madzi ambili amene saphwila. Laciŵili, cilungamo cathu cidzakhala ngati mafunde a m’nyanja. Mukakhala m’mbali mwa nyanja ndi kuyang’ana mmene mafunde amayendela, mumadziŵa kuti mafundewo ndi acikhalile ndipo adzapitiliza kuyenda m’nyanja imeneyo kwamuyaya. Yehova wanena kuti, cilungamo canu naconso sicidzatha ngati mumumvela. Malinga ngati muyesetsa kukhala okhulupilika kwa iye, sadzalola kuti mugwedezeke. (Ŵelengani Salimo 55:22.) Kodi malonjezo ogwila mtima amenewa salimbitsa cikhulupililo canu pa Yehova ndi malamulo ake olungama?

“TIYENI TIYESETSE MWAKHAMA UTI TIKHALE OKHWIMA MWAUZIMU”

9, 10. (a) N’cifukwa ninji Mkristu aliyense ayenela kukhala ndi colinga cokhala wokhwima kuuzimu? (b) Kodi kukhala ndi maganizo a kuuzimu kumatithandiza bwanji kukhala acimwemwe?

9 Caciŵili cimene muyenela kucita pa nchito yanu yomanga ya kuuzimu, cili m’mau ouzilidwa akuti: “Tiyeni tiyesetse mwakhama kuti tikhale okhwima mwauzimu.” (Aheberi 6:1) Kukhala okhwima kuuzimu ndi colinga cabwino kwa Mkristu. Nthawi ino n’zosatheka kukhala angwilo, koma n’zotheka kukhala okhwima kuuzimu. Ndiponso Akristu amapeza cimwemwe coculuka potumikila Yehova ngati ndi okhwima kuuzimu. N’cifukwa ciani zili conco?

10 Mkristu wokhwima kuuzimu amaona zinthu mmene Yehova amazionela. (Yohane 4:23) Paulo analemba kuti: “Otsatila zofuna za thupi amaika maganizo ao pa zinthu za thupi, koma otsatila za mzimu amaika maganizo ao pa zinthu za mzimu.” (Aroma 8:5) Munthu amene amaika maganizo pa zinthu za thupi sakhala wacimwemwe kwenikweni cifukwa cakuti amakhala wodzikonda, wosaona patali, ndi wokonda zinthu zakuthupi. Munthu amene amaika maganizo pa zinthu za kuuzimu amakhala wacimwemwe cifukwa amakonda Yehova, “Mulungu wacimwemwe.” (1  Timoteyo 1:11) Munthu wa maganizo otelo amafuna kukondweletsa Yehova, ndipo amakhala wacimwemwe ngakhale pamene akuyesedwa. Amatelo cifukwa ciani? Cifukwa cakuti ziyeso zimatipatsa mwai woonetsa kuti Satana ndi wabodza, ndi kutithandiza kukhala okhulupilika, ndipo zimenezi zimakondweletsa Atate wathu wakumwamba.—Miyambo 27:11; ŵelengani Yakobo 1:2, 3.

11, 12. (a) N’ciani cimene Paulo anakamba ponena za ‘mphamvu za kuzindikila’ za Mkristu? Nanga liu lomasulidwa kuti “zaphunzitsidwa” limatanthauza ciani? (b) N’ciani cimene mwana amafunikila kucita kuti aphunzile kugwilitsila nchito thupi lake? Ndipo woseŵela bola amafunika kucita ciani kuti akhale katswili?

11 Kuti munthu akhale wokhwima mwakuuzimu, ayenela kuphunzitsa mphamvu zake za kuzindikila. Ganizilani lemba ili: “Cakudya cotafuna ndi ca anthu okhwima mwauzimu, amene pogwilitsa nchito mphamvu zao za kuzindikila, aphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.” (Aheberi 5:14) Pamene Paulo anakamba kuti mphamvu zathu za kuzindikila ‘zaphunzitsidwa’, anagwilitsila nchito liu la Cigiriki limene anthu ambili m’nthawi ya atumwi anali kuligwilitsila nchito m’mabwalo a maseŵela m’dziko la Greece. Liu limeneli lingamasulidwenso kuti ‘kuphunzitsidwa ngati katswili wa maseŵela.’ Tsopano ganizilani zimene kuphunzila kumeneko kumaphatikizapo.

Katswili wa maseŵela amalimbitsa thupi lake mwa kuliphunzitsa

12 Tikabadwa, thupi lathu limakhala kuti silinaphunzile kucita zinthu. Mwacitsanzo, khanda silizindikila pamene pali miyendo ndi manja ake. Ndiye cifukwa cake limayendetsa manja ake uku ndi uku ngakhale kudzimenya kumaso, cakuti limacita kudzidzimuka ndi kulila. Koma m’kupita kwa nthawi, khandalo likayamba kugwilitsila nchito ziwalo zake, limaphunzila kucita zinthu bwinobwino. Pambuyo pake mwanayo amayamba kukwaŵa, kuyenda, kenako amayamba kuthamanga. * Koma bwanji za katswili wa maseŵela? Mwacitsanzo, mukaona katswili wa bola amene amamenya bola mwaukatswili, mumadziŵa kuti anaphunzila mokwanila. Luso lake silinabwele mwamwai, koma anatailapo nthawi yoculuka kuphunzila maseŵelawo. Baibulo limakamba kuti kucita maseŵela olimbitsa thupi “n’kopindulitsa pang’ono.” Koma cofunika koposa ndi kuphunzitsa mphamvu zathu za kuzindikila.—1 Timoteyo 4:8.

13. Kodi mphamvu zathu za kuzindikila tingaziphunzitse bwanji?

13 M’buku lino takambilana zambili zimene zingakuthandizeni kuphunzitsa mphamvu za kuzindikila, kuti mukhalebe wokhulupilika kwa Yehova monga munthu wa kuuzimu. Popanga zosankha tsiku ndi tsiku, muyenela kupemphela ndiponso kuganizila mfundo za Mulungu ndi malamulo ake. Popanga cosankha ciliconse, dzifunseni kuti: ‘Kodi malamulo kapena mfundo za m’Baibulo zimati bwanji pankhaniyi? Nanga ndingazigwilitsile nchito motani? Kodi n’ciani cingakondweletse Atate wanga wakumwamba?’ (Ŵelengani Miyambo 3:5, 6; Yakobo 1:5.) Cosankha ciliconse cimene mungapange mwanjila imeneyi, cidzakuthandizani kuphunzitsa mphamvu zanu za kuzindikila. Kucita zimenezi kudzakuthandizani kukhalabe munthu wauzimu.

14. Ndi njala yotani imene tiyenela kukhala nayo kuti tikule mwa kuuzimu? Nanga tiyenela kusamala za ciani?

14 Ngakhale munthu wokhwima kuuzimu afunika kupitilizabe kukula kuuzimu. Kuti munthu akule mwakuthupi, amafunikila kudya. Ndiye cifukwa cake Paulo anati: “Cakudya cotafuna ndi ca anthu okhwima mwauzimu.” Conco, cinthu cofunika kuti mulimbitse cikhulupililo canu ndi kupitiliza kudya cakudya cotafuna ca kuuzimu. Kugwilitsila nchito bwino zimene mumaphunzila ndi cinthu canzelu, ndipo Baibulo limati: “Nzelu ndiyo cinthu cofunika kwambili.” Motelo, tiyenela kukhala ndi njala ya coonadi camtengo wapatali cimene Atate wathu amatipatsa. (Miyambo 4:5-7; 1 Petulo 2:2) Tikakhala ndi cidziŵitso ndi nzelu zaumulungu, sitiyenela kukhala odzikweza. Conco, tiyenela kudzipenda nthawi zonse kuti tione ngati kunyada kapena cofooka cina cazika mizu ndi kukula mumtima mwathu. Paulo analemba kuti: “Pitilizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’cikhulupililo. Pitilizani kudziyesa kuti mudziŵe kuti ndinu munthu wotani.”—2 Akorinto 13:5.

15. N’cifukwa ciani cikondi n’cofunika kuti tikule kuuzimu?

15 Mukamaliza kumanga nyumba, sindiye kuti nchito yatha. Muyenela kupitiliza kuikonza ndipo mwina m’kupita kwa nthawi mungafune kumangilako cipinda cina. Kodi cofunika n’ciani kuti tikhwime ndi kukhalabe olimba kuuzimu? Cofunika koposa ndi cikondi. Tiyenela kukulitsa cikondi cathu pa Yehova ndi Akristu anzathu. Ngati tilibe cikondi, cidziŵitso cathu ndi nchito zathu zonse zidzakhala zacabecabe monga belu longolila. (1 Akorinto 13:1-3) Tikakhala ndi cikondi, tidzakhala Mkristu wokhwima ndipo tidzapitilizabe kukula kuuzimu.

IKANI MAGANIZO ANU PA CIYEMBEKEZO CIMENE YEHOVA WATIPATSA

16. Kodi Satana amalimbikitsa maganizo otani? Nanga Yehova watipatsa citetezo cotani?

16 Tiyeni tikambilane cinthu cina cimene mungacite pa nchito yanu yomanga imeneyi. Kuti mukhale wotsatila weniweni wa Kristu, muyenela kuteteza maganizo anu. Wolamulila wa dziko lino, Satana, ndi katswili pakupangitsa anthu kukhala ndi maganizo ofooketsa, okaikila ena, ndi opanda ciyembekezo. (Aefeso 2:2) Maganizo amenewa ndi oopsa kwa Mkristu cifukwa amakhala monga matabwa ogwila mtenje amene ayamba kufumbwa. Koma zosangalatsa n’zakuti, Yehova watipatsa cida cofunika cimene cingatiteteze. Cida cimeneci ndi ciyembekezo.

17. Kodi Mau a Mulungu amaonetsa bwanji kuti ciyembekezo n’cofunika?

17 Baibulo limachula zida zosiyanasiyana za nkhondo ya kuuzimu, zimene tifunika kukhala nazo polimbana ndi Satana ndi dzikoli. Cida cina cofunika kwambili pa nkhondoyi ndi cisoti, cimene ndi “ciyembekezo cacipulumutso.” (1 Atesalonika 5:8) M’nthawi za m’Baibulo, msilikali anali kudziŵa kuti popanda cisoti sangapulumuke pa nkhondo. Nthawi zambili cisoti cimeneco cinali cansimbi, ndipo mkati mwake anali kumatamo cikumba. Cisotico cinali kuteteza mutu wake ku mivi iliyonse imene ingaponyedwe kwa iye. Monga mmene cisoti cimatetezela mutu, ciyembekezo cingatetezenso maganizo anu.

18, 19. Ndi citsanzo cotani cimene Yesu anapeleka pankhani yokhala ndi ciyembekezo? Ndipo tingatengele bwanji citsanzo cake?

18 Yesu anapeleka citsanzo cabwino kwambili pa nkhani ya kukhala ndi ciyembekezo. Kumbukilani mavuto amene anakumana nao usiku wake womaliza padziko lapansi. Mnzake wapamtima anamupeleka kwa adani ake cifukwa cofuna ndalama. Mnzake wina anam’kana kuti samudziŵa ngakhale pang’ono. Anzake ena anamuthaŵa. Anthu a mtundu wake anamukana, ndi kuumilila kuti iye aphedwe mwankhanza ndi asilikali a Roma. Inunso mungavomeleze kuti Yesu anakumana ndi mayeselo aakulu kwambili, amene aliyense wa ife sangakumane nao. Nanga n’ciani cinamuthandiza kupilila? Lemba la Aheberi 12:2 limayankha kuti: “Cifukwa ca cimwemwe cimene anamuikila patsogolo pake, anapilila mtengo wozunzikilapo. Iye sanasamale kuti zocititsa manyazi zimucitikila, ndipo tsopano wakhala pansi kudzanja lamanja la mpando wacifumu wa Mulungu.” Yesu anayang’anabe pa “cimwemwe cimene anamuikila patsogolo pake.”

19 Kodi Yesu anamuikila cimwemwe cotani patsogolo pake? Yesu anadziŵa kuti kupilila kwake kudzathandiza kuti dzina loyela la Yehova liyeletsedwe. Anadziŵanso kuti kupilila kwake kudzapeleka umboni waukulu koposa wakuti Satana ndi wabodza. Palibe ciyembekezo cina cimene cikanapatsa Yesu cimwemwe coculuka kuposa zimenezi. Iye anadziŵanso kuti Yehova adzamudalitsa kwambili cifukwa cokhala wokhulupilika, ndi kuti patsogolo pake adzasangalala kukhalanso ndi Atate wake. Yesu anali ndi ciyembekezo cosangalatsa cimeneci panthawi zovuta kwambili. Tiyenela kucita cimodzimodzi. Ifenso tili ndi cimwemwe cimene caikidwa patsogolo pathu. Yehova wapatsa aliyense wa ife mwai wothandiza kuyeletsa dzina lake lalikulu. Tingaonetse kuti Satana ndi wabodza mwa kusankha Yehova kukhala wolamulila wathu wamkulu. Ndipo tidzakhalabe m’cikondi ca Atate wathu, mosasamala kanthu za mavuto ndi ziyeso zimene tingakumane nazo.

20. N’ciani cingakuthandizeni kukhalabe ndi maganizo oyenela ndi ciyembekezo colimba?

20 Yehova ndi wokonzeka kupeleka mphoto kwa atumiki ake okhulupilika, ndipo amalakalaka kutelo. (Yesaya 30:18; ŵelengani Malaki 3:10.) Iye amasangalala kupatsa atumiki ake zokhumba za mtima wao malinga ngati n’zoyenela. (Salimo 37:4) Conco, ikani maganizo anu pa malonjezo a Mulungu a mtsogolo. Musalole maganizo ofooketsa, oipa ndi opotoka a dziko la Satana kukulefulani. Ngati muona kuti mzimu wa dziko lino ukuloŵelela m’maganizo ndi mumtima mwanu, pemphelani ndi mtima wonse kwa Yehova kuti akupatseni “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” Mtendele wa Mulungu umenewu, udzateteza mtima wanu ndi maganizo anu.—Afilipi 4:6, 7.

21, 22. (a) Ndi ciyembekezo cosangalatsa citi cimene a “khamu lalikulu” ali naco? (b) Pa zinthu zonse zimene Akristu amayembekezela, kodi inu mumafunitsitsa kuti mukaone ciani? Nanga mwatsimikiza mtima kucita ciani?

21 Muli ndi ciyembekezo cabwino kwambili cimene muyenela kuciganizila. Ngati ndinu wa “khamu lalikulu” limene  ‘lidzatuluka m’cisautso cacikulu,’ ganizilani za moyo umene  mudzakhala nao posacedwapa. (Chivumbulutso 7:9, 14) Satana ndi ziŵanda zake akadzacotsedwa, mudzakhala ndi mpumulo umene panthawi ino simungaumvetsetse. Ndani wa ife amene  sanavutikepo ndi cisonkhezelo coipa ca Satana? Cifukwa cakuti kudzakhala kulibe cisonkhezelo cimeneco, tidzasangalala kugwila nchito yokonza dziko lapansi kukhala paladaiso mu ulamulilo wa Yesu ndi olamulila anzake a 144,000. Timasangalala kwambili kudziŵa kuti matenda onse ndi zofooka za m’thupi  zidzacotsedwapo, tidzalandila okondedwa athu kucokela kumanda ndi kukhala ndi moyo monga mmene Mulungu anafunila poyamba. Pamene tidzakhala angwilo, tidzalandila mphoto ina yaikulu yolonjezedwa pa Aroma 8:21. Mphoto imeneyo ndi “ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.”

22 Yehova afuna kuti mukakhale ndi ufulu woculuka umene panthawi ino simungaumvetsetse. Kuti mukapeze ufulu umenewo, muyenela kukhala womvela. N’cifukwa cake muyenela kucita khama kwambili kumvela Yehova tsiku ndi tsiku. Motelo, yesetsani kudzilimbitsa nokha pamaziko a cikhulupililo canu coyela kopambana kuti mukhalebe m’cikondi ca Mulungu kwamuyaya.

^ par. 12 Asayansi amakamba kuti pamene anthufe tikula timayamba kukhala ndi mphamvu yotithandiza kudziŵa pamene pali manja ndi miyendo yathu. Mwacitsanzo, mphamvu imeneyi imakuthandizani kuomba m’manja ngakhale pamene mwatseka maso anu. Wodwala wina amene mphamvu imeneyi inaonongeka, anali kulephela kuimilila, kuyenda ngakhale kukhala tsonga.