Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chitsanzo Chabwino—Yosefe

Chitsanzo Chabwino—Yosefe

Chitsanzo Chabwino​—Yosefe

Yosefe anakumana ndi chiyeso chachikulu. Mkazi wa mbuye wake ankamunyengerera mobwerezabwereza kuti agone naye. Tsiku lina mkaziyo anayesa kumunyengerera, koma Yosefe sanatengeke. Iye anayankha motsimikiza kuti: ‘Ndingachitirenji choipa chachikulu chimenechi, ndi kuchimwira Mulungu?’ Mkaziyo atalimbikira mpaka kufika pomugwira, Yosefe sanachite manyazi kuthawa, kutuluka m’nyumbamo. Yosefe anasonyeza kuti anali munthu wamakhalidwe abwino.Genesis 39:7-12.

Mwina inunso mungakumane ndi munthu amene angakunyengerereni kuti mugone naye. Kudziletsa pakokha sikokwanira kuti mukane kuchita zimenezo. Choyamba, muyenera kufunitsitsa kukondweretsa Mlengi wanu, Yehova Mulungu. Mofanana ndi inu, Yosefe anali ndi chilakolako cha kugonana. Koma anaona kuti si bwino kuchimwira Mlengi wake chifukwa chotsatira chilakolako chake. Inunso muyenera kukhala wotsimikiza kuti kuchita khalidwe lililonse lodetsa n’kuchimwira Mulungu ndipo kumabweretsa mavuto. Choncho, yesetsani kuti mukhale wamakhalidwe abwino ngati Yosefe.