Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chitsanzo Chabwino—Lidiya

Chitsanzo Chabwino—Lidiya

Chitsanzo Chabwino​—Lidiya

Ngakhale kuti Lidiya anali atangokhala kumene wophunzira wa Yesu, iye anaitanira Paulo ndi anzake kunyumba kwake popanda kupemphedwa. (Machitidwe 16:14, 15) N’chifukwa chake anali ndi mwayi wogwirizana ndi Paulo ndiponso anzake aja. Ndipo Paulo ndi Sila atatuluka ku ndende, anapitanso ku nyumba kwa Lidiya—Machitidwe 16:40.

Kodi inunso mungatsatire chitsanzo cha Lidiya poyesetsa kudziwana ndi anthu? Kodi mungachite bwanji zimenezi? Musapupulume. Yambani kulankhula ndi munthu mmodzi. Mukapita ku misonkhano yachikhristu, yesetsani kulankhulana ndi munthu mmodzi m’malo mocheza ndi anthu ambiri nthawi imodzi. Pochezapo muzikhala wansangala. Ngati mukusowa chonena, mufunseni mafunso kapena muuzeni zilizonse zimene zakuchitikirani. Muzimvetsera akamalankhula. M’kupita kwanthawi mudzayamba kulankhula momasuka. Dziwani kuti anthu amakonda kucheza ndi munthu wachifundo ndiponso wokoma mtima. (Miyambo 16:24) Lidiya anapeza anzake abwino chifukwa chakuti anali wachifundo ndi wokonda kuchereza alendo. Ngati mutatsatira chitsanzo cha Lidiya, inunso mungapeze anzanu abwino.