Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chitsanzo Chabwino—Paulo

Chitsanzo Chabwino—Paulo

Chitsanzo Chabwino​—Paulo

Mtumwi Paulo ankadziwa zinthu zimene angathe kuchita komanso zimene sangathe. Iye anati: “Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili nane.” Paulo anali ndi mtima wofuna kuchita zinthu zabwino n’chifukwa chake ananena kuti: “Mu mtima mwanga ndimasangalala kwambiri ndi chilamulo cha Mulungu.” Koma kodi vuto lake linali chiyani? Iye ananena kuti: “Ndimaona chilamulo china . . . chikumenyana ndi chilamulo cha m’maganizo mwanga ndi kundipanga kapolo wa chilamulo cha uchimo chimene chili m’ziwalo zanga.” Paulo sankasangalala chifukwa panali zinthu zina zimene ankalakwitsa. Iye anadandaula kuti: “Munthu wovutika ine!”—Aroma 7:21-24.

Kodi mukalakwitsa zinthu, mumaona kuti ndinu munthu wolephera? Umu ndi mmenenso Paulo ankamvera nthawi zina. Koma Paulo ankadziwanso kuti Khristu anafera anthu ngati iyeyo. Choncho iye ananena kuti: ‘Mulungu adzandipulumutsa kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.’ (Aroma 7:25) Paulo ankaona kuti Yesu anamufera iyeyo payekha. Iye anati: “Mwana wa Mulungu . . . anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.” (Agalatiya 2:20) Mukakhumudwa, muziganizira dipo la Yesu. Ndipo mukalakwitsa zinthu zinazake, muzikumbukira kuti Khristu anafera anthu ochimwa, osati anthu angwiro.