Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 98

Fesani Mbewu za Ufumu

Fesani Mbewu za Ufumu

(Mateyu 13:4-8)

1. Akapolonu a Yehova

Amene mwadzipereka,

Bwerani kuntchito ya ’Mbuye

Ndipo muzimutsanzira.

Muzifesa mbewu za cho’nadi

M’mitima ya omvetsera.

Mukakhulupirika kwa Mulungu

Inde mudzamulemekeza.

2. Mbewu zina zomwe mufesa

Zidzagweratu pamwala.

Zidzakuladi kwa kanthawi

Pambuyo pake n’kufota.

Minga ikatsamwitsa cho’nadi

Amatengeka ndi dziko.

Zina zidzapeza nthaka yachonde

Ndiponso zidzakula bwino.

3. Kuti ntchito iyende bwino

Khama lanu n’lofunika.

Mukaleza mtima ndi anthu

Angakhozedi kusintha.

Mwa kukhala atcheru mungathe

Kuwathetseradi mantha.

Mungakolole zipatso makumi

Atatu kapena kuposa

(Onaninso Mat. 13:19-23; 22:37.)