Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 106

Tikhale pa Ubwenzi ndi Yehova

Tikhale pa Ubwenzi ndi Yehova

(Salimo 15)

1. Ndani angakhale

Bwenzi lanu M’lungu?

Ndani mungakhulupirire,

Angakhale nanu?

Ndi onse amene

Amakukondani,

Amakukhulupirirani,

Okonda cho’nadi.

2. Ndani angakhale

Bwenzi lanu M’lungu?

Ndani angafike

Kumpando wanu wachifumu?

Ndi onse

Amene amakumverani,

Olemekeza dzina lanu,

Okulambirani.

3. Timakuuzani

Zamumtima mwathu,

Ndipo timamva

Kuti tili pafupidi nanu.

Ndi inu tifuna

Kukhala mabwenzi.

Palibiretu bwenzi

Lomwe lingakuposeni.

(Onaninso Sal. 139:1; 1 Pet. 5:6, 7.)