Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 10

“Ine Ndilipo! Nditumizeni”

“Ine Ndilipo! Nditumizeni”

(Yesaya 6:8)

1. Lero anthu akunyoza

Dzina labwino la M’lungu.

Ena am’yesa wankhanza,

Nati: “Kulibe Mulungu.”

Ndani adzaliyeretsa

Dzina la Mulungu wathu?

“Ndilipo nditumizeni.

Ndidzaimbira nokhanu

(KOLASI)

Sindingachitirenso mwina.

Nditumizeni Mbuye.”

2. Anthu akutonza M’lungu

Ndikumati ndi wochedwa.

N’kumalambira mafano

Ena eti Kaisara.

Ndani adzawachenjeza

Za nkhondo yomalizayo?

“Ndilipo nditumizeni.

Ndidzachenjeza oipa.

(KOLASI)

Sindingachitirenso mwina.

Nditumizeni Mbuye.”

3. Anthu ofatsa ’kulira,

Zoipa zikuchuluka.

Iwo akufunafuna

Choonadi chomasula.

Ndani adzawatonthoza?

Ndani adzawathandiza?

“Ndilipo, nditumizeni.

Ndidzaphunzitsa ofatsa.

(KOLASI)

Sindingachitirenso mwina.

Nditumizeni Mbuye.”

(Onaninso Sal. 10:4; Ezek. 9:4.)