Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 77

Muzikhululuka

Muzikhululuka

(Salimo 86:5)

1. Mwachikondi M’lungu

Mwa Yesu anakonza

Kuti tikhululukidwe

Ndi kuthetsadi imfa.

Ngati tilidi olapa,

Ndipo titamupempha,

Pogwiritsa ntchito

Dipo Atikhululukira.

2. Ngati titsanzira

Mulungu wakumwamba

Kukhululukira ena

Tidzakhululukidwa.

Tikhale ololerana,

Tisakhale odana

Koma olemekezana

Komanso okondana.

3. Tikhale n’chifundo,

Chidzatithandizadi

Kusasunga chakukhosi

Kapenanso chidani.

Tikatsanzira Yehova

Maka chikondi chake

Tidzakhululukirana

Tidzafanana naye.

(Onaninso Mat. 6:12; Aef. 4:32; Akol. 3:13.)