Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 7

Tidzipereke Monga Akhristu

Tidzipereke Monga Akhristu

(Aheberi 10:7, 9)

1. Yehova analengatu

Chilengedwe chonse,

Dzikoli ndi mlengalenga

Zonsezi ndi zake.

M’lungu watipatsa moyo

Wasonyeza kuti

Ndi woyenera kum’tamanda

Ndiponso kum’lambira.

2. Yesu anabatizidwa

Nanena m’pemphero:

‘Ndabwera kuti ndichite

Chifuniro chanu.’

Anatuluka m’Yo’dano

Monga wodzozedwa,

Kuti atumikire M’lungu

Monga wodzipereka.

3. Yehova, ife tabwera

Kukutamandani.

Tadzipereka kwa inu

Ndipo tadzikana.

Munapereka Mwana’nu,

Nalipira dipo.

Tasiyatu zofuna zathu,

Tizichitano zanu.

(Onaninso Mat. 16:24; Maliko 8:34; Luka 9:23.)