Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 16

Thawirani ku Ufumu wa Mulungu

Thawirani ku Ufumu wa Mulungu

(Zefaniya 2:3)

1. Bwerani kwa Yehova ofatsanu,

Zinthu zolungamadi muchite.

Tsiku la Yehova likadzafika

Mwina mungadzabisike.

(KOLASI)

Thawirani ku ’fumu wa M’lungu,

Khalani mbali yake.

N’kumene mudzapeza chitetezo.

M’mvereni, musachedwe.

2. Anjala ya choonadi nonsenu

Mudzamva chisoni mpaka liti?

Bwerani kwa Yehova m’pulumuke

Pansi pa Yesu khalani.

(KOLASI)

Thawirani ku ’fumu wa M’lungu,

Khalani mbali yake.

N’kumene mudzapeza chitetezo.

M’mvereni, musachedwe.

3. Tukulani mitu mosangalala,

Onanitu Ufumu wayamba.

Landirani kuwala kwa Yehova,

Muopeni iye yekha!

(KOLASI)

Thawirani ku ’fumu wa M’lungu,

Khalani mbali yake.

N’kumene mudzapeza chitetezo.

M’mvereni, musachedwe.

(Onaninso Sal. 59:15; Miy. 18:10; 1 Akor. 16:13.)