Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 18

Chikondi cha Mulungu N’chosatha

Chikondi cha Mulungu N’chosatha

(Yesaya 55:1-3)

1. Chikondi cha M’lungu.

Ndithudi ndi chachikulu.

Iye anapereka

Mwana wake kwa ife

Kuti tipeze moyo,

Tipepezenso chimwemwe.

(KOLASI)

Inu nonse aludzu,

Dzamweni kwaulere.

Madzi opatsa moyo;

N’chifundo cha M’lungu.

2. Chikondi cha M’lungu.

Ntchito zake ndi umboni.

Watikonda popatsa

Mwana wake Ufumu

Pokwanitsa pangano.

Ufumu wake wadza.

(KOLASI)

Inu nonse aludzu,

Dzamweni kwaulere.

Madzi opatsa moyo;

N’chifundo cha M’lungu.

3. Chikondi cha M’lungu.

Nafenso tichisonyeze.

Tithandize ofatsa,

Kufuna chilungamo.

Tilalike kwa onse,

Uthenga wotonthoza.

(KOLASI)

Inu nonse aludzu,

Dzamweni kwaulere.

Madzi opatsa moyo;

N’chifundo cha M’lungu.

(Onaninso Sal. 33:5; 57:10; Aef. 1:7.)