Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nyimbo 19

Mulungu Watilonjeza Paradaiso

Mulungu Watilonjeza Paradaiso

(Luka 23:43)

1. M’lungu wathu watilonjeza

Paradaiso wam’tsogolo.

Adzachotsa uchimo, imfa,

Zopweteka ndi misozi.

(KOLASI)

Paradaiso adzafika.

Ndipo sitikukayika.

Khristu adzakwaniritsa

Chifuniro cha Mulungu.

2. Cholinga cha Mulungu n’choti

Yesu aukitse anthu.

Monga Yesu analonjeza,

‘Udzakhala m’Paradaiso.’

(KOLASI)

Paradaiso adzafika.

Ndipo sitikukayika.

Khristu adzakwaniritsa

Chifuniro cha Mulungu.

3. Yesu Mfumu, analonjeza

Paradaiso padzikoli.

Tiyamika Atate wathu

Mochokera mumtimamu.

(KOLASI)

Paradaiso adzafika.

Ndipo sitikukayika.

Khristu adzakwaniritsa

Chifuniro cha Mulungu.

(Onaninso Mat. 5:5; 6:10; Yoh. 5:28, 29.)